Umboni wa Kusungidwa kwa Umulungu
MAWU owuziridwa a Mulungu atumizidwa kwa ife molongosoka, ndipo kaamba ka kusungidwa kozizwitsa koteroko tiyenera kuyamikira choyambirira Mkonzi wa Baibulo. Pali mwinamwake mamanusikripiti 6,000 a Malemba onse Achihebri kapena mbali za iwo ndi ena 5,000 a Malemba Achikristu a Chigriki.
“Mawu a [Yehova] akhala chikhalire.” (1 Petro 1:25) Koma kodi nchiyani chomwe kufufuza kwamakono kwavumbula ponena za kusungidwa kwa Mawu ake Opatulika?
Ndi Lemba Lodalirika Motani?
Kokha kodi ndi lodalirika chotani lemba la Malemba Achikristu a Chigriki? Odalirika koposa, mosayerekezeka tero titalingalira zolembedwa zina zomwe zapulumuka kuchokera ku zinthu zakale. Nsonga imeneyi inawunikiridwa m’bukhu lakuti Auf den Spuren Jesu (M’mapazi a Yesu), lolembedwa ndi Gerhard Kroll. Mkonziyo anasonyeza, mwachitsanzo, kuti kokha mapepala a gumbwa asanu ndi limodzi anasungidwa a zolembera za wanthanthi wa Chigriki Aristotle (zana lachinayi B.C.E.), mokulira zokhala ndi masiku a zana la khumi C.E. kapena pambuyo pake. Ntchito za Plato (zana lachinayi B.C.E.) zinali zabwinoko. Pali mamanusikripiti khumi a ntchito zake omwe ali ndi deti la kuchokera lisanakwane zana la 13. M’nkhani ya Herodotus (zana lachisanu B.C.E.), pali chifupifupi zidutswa za gumbwa 20 zokhala ndi deti kuchokera m’zana loyamba C.E. ndi pambuyo pake. Mamanusikripiti oyambirira athunthu a ntchito zake ali ndi deti la kuchokera m’zana la khumi. Ndipo mamanusikripiti oyambirira kwambiri a ntchito za Josephus ali ndi deti la kubwerera kokha ku zana la 11.
M’kusiyana ndi ichi, lemba la Malemba Achikristu a Chigriki (lotsirizidwa m’zana loyamba C.E.) liri lotsimikiziridwa ndi zidutswa zochokera ku zana lachiŵiri ndi makope okwanira kuchokera ku zana lachinayi. Mogwirizana ndi Kroll, pali mapepala a gumbwa 81 kuchokera ku zana la 2 mpaka 7, mamanusikripiti a zilembo zazikulu 266 kuchokera ku zana la 4 mpaka 10, ndi mamanusikripiti a kalembedwe ka chikhwakhwaza 2,754 kuchokera ku zana la 9 mpaka 15, limodzinso ndi zosonkhanitsidwa 2,135. Zonsezi zimatithandiza ife kukhazikitsa lemba la Malemba Achikristu a Chigriki. Chotero, inde, ilo ndithudi limatsimikiziridwa bwino.
Chidutswa Chofunika Koposa cha Uthenga Wabwino wa Yohane
Ndani amene angayembekezere kupeza mbali ya mtengo koposa ya manusikripiti ya Baibulo mu unyinji wa zinyalala? Komabe, kumeneko ndi kumene chidutswa cha mtengo woposa cha mutu 18 wa Uthenga Wabwino wa Yohane chinapezedwa. Tsopano chodziŵika monga John Rylands Papyrus 457 (P52), chikusungidwa mu Manchester, England. Ndimotani mmene icho chinapezedwera, ndipo nchifukwa ninji chiri chofunika chotero?
Pa kusintha kwa zana, ofukula zinthu zofotseredwa pansi anakumba unyinji wa zidutswa za gumbwa, kuphatikizapo makalata, malisiti, mapembedzero, ndi zolembera za chiŵerengero cha anthu, limodzi ndi malemba ena ambiri, kunja kwa mzinda wa Oxyrhynchus mu boma la El Faiyûm, Igupto. Zambiri za izo zolembedwa mu Chigriki, zonsezo zinasungidwa kwa zaka mazana angapo mu m’chenga wowuma.
M’chaka cha 1920, kusonkhanitsidwa kwa mapepala a gumbwa amenewa kunapezedwa ndi John Rylands Library of Manchester. Zaka khumi ndi zinayi pambuyo pake, wophunzira C. H. Roberts, m’kusankha kupyola zina za zidutswazo, anapeza mawu ochepera omwe anawoneka kukhala ozoloŵereka kwa iye. Tangolingalirani kusangalatsidwa kwake pamene iye anazindikira kuti iwo anali ochokera m’Yohane mutu 18, mbali za maversi 31 mpaka 33 zikumakhala pa mbali imodzi ya chidutswacho ndi mbali za maversi 37 ndi 38 ku mbali ina (kuseri). Chidutswa cha gumbwa chimenechi chinatsimikizira kukhala mbali yakale koposa yodziŵika ya manusikripiti iriyonse ya Lemba Lachikristu la Chigriki yopezedwa. Yolembedwa m’zilembo zazikulu za Chigriki zotchedwa uncials, iyo inayambira kuchokera ku theka loyambirira la zana lachiŵiri la Nyengo yathu ya Chisawawa.
Chidutswa chimenechi chiri ndi muyeso wa kokha masentimita 8.9 ndi 6.4. Ndimotani mmene chiriri chothekera kuika tsiku chidutswa cha gumbwa chimenechi molongosoka chotero? Kwakukulukulu mwa kusanthula mtundu wa kalembedwe, phunziro lokziŵika monga paleography. Kalembedwe ka manja konse kamasintha mwapang’onopang’ono mkati mwa zaka, ndipo kuli kusintha kumeneku kumene kumasonyeza utali wa kukhalapo kwa manusikripiti, ndi kusiyana kwa kulakwa kwa zaka zina mbali zonse ziŵiri. Manusikripiti yokwanira kwa imene chidutswacho chiri mbali yaing’ono yotero chotero inalembedwa moyandikira koposa ku nthaŵi ya kulembedwa kwa cholembera choyambirira cha Uthenga Wabwino wolembedwa ndi Yohane iyemwini. Mwachidziŵikire, mpatawo unali wochepera monga zaka 30 kapena 40. Tingakhalenso otsimikizira kuti cholembera cha Yohane sichinasinthidwe kotheratu ndi alembi a pambuyo pake, popeza kuti lemba la chidutswalo limagwirizana chifupifupi ndendende ndi lija lopezedwa m’mamanusikripiti atsopano koposa.
Kumayambiriro kwa kupezako, osuliza anatsutsa kuti Uthenga Wabwino wa Yohane sunali kulembedwa kowona mtima kwa mtumwi wa Yesu koma kunalembedwa nthaŵi ina pambuyo pake, kulinga ku mapeto kwa zana lachiŵiri. Mosiyanako, tsopano chiri chachimvekere kuchokera ku chidutswa chimenechi kuti Uthenga Wabwino wa Yohane unakhalako mu Igupto m’theka loyamba la zana lachiŵiri C.E., osati monga mpukutu, koma mu mtundu wa bukhu la makedzana. Ndi chozizwitsa chotani nanga kuti chidutswa cha gumbwa chowoneka chopanda phindu chimenechi chingakhalitse chete osuliza mokhutiritsa chotero!
[Bokosi patsamba 31]
GUMBWA
GUMBWA ndi chomera chomwe chimakula m’madzi osazama, osayenda kapena m’madambo ndipo m’mphepete mwa mitsinje yoyenda pang’onopang’ono, monga ngati Nile. (Yobu 8:11) Pepala la gumbwa lingakhale linagwiritsiridwa ntchito monga chinthu cholembapo kumayambiriro m’nthaŵi ya Abrahamu. Pambuyo pake, kupangidwa kwake kunali imodzi ya maindasitale akulu a Aigupto akale. M’kupanga iyo, iwo anatsatira dongosolo lopepuka. Utali wa chithime chamkati unadulidwa kukhala luzi lowonda ndi kuyalidwa kumbali ndi kumbali, ndi muyalo wina utamamatizidwa mopingasa. Izi kenaka zinali kupanikizidwa ndi kupindidwa kukhala pepala, kuwumikidwa m’dzuwa, ndipo kwa nthaŵi ndi nthaŵi kokongoletsedwa ndi pumice, zikamba, kapena m’nyanga. Mapepala akanalumikizidwa kupanga mpukutu, avereji ya utali ukumakhala pakati pa mamita anai ndi asanu ndi imodzi, ngakhale kuti imodzi yasungidwa yomwe iri ndi utali wa mamita 41. Mosiyanitsa, masambawo akakhoza kupindidwa kupanga bukhu longa la makedzana, mtundu wa manusikripiti yotchuka kwambiri pakati pa Akristu oyambirira.
[Bokosi patsamba 31]
CHIKOPA CHOPUNTHIDWA ndi CHIKOPA CHOLEMBAPO
BUKHU la Makedzana la Alexandrine la m’zana lachisanu, lomwe poyambirira linali ndi Baibulo lonse, liri lolembedwa pa chikopa. Kodi chinthuchi nchiyani, ndipo kodi icho chimasiyana bwanji ndi chikopa chopunthidwa?
Kuchokera ku nthaŵi zakale, chikopa chopunthidwa chinali kupangidwa kuchokera ku chikopa cha nkhosa, chikopa cha mbuzi, kapena chikopa cha ng’ombe. Chinali kukonzedwa mwa kuchotsa ubweya ku zikopa zotsukidwa, zimene kenaka zinali kufutukulidwa pa mitengo kuti ziwume. (Yerekezani ndi 2 Timoteo 4:13.) Pofika mazana achitatu ndi chinayi a Nyengo yathu ya Chisawawa, kusiyana pakati pa mtundu wa chinthucho kunalandiridwa, chochindikalako chikupitirizabe kudziŵika monga chikopa chopunthidwa, chofewakocho monga chikopa. Ponena za chikopa, kokha zikopa zofewa za ng’ombe yaing’ono kapena ng’ombe zobadwa zakufa kale kapena ana a nkhosa zinali kugwiritsiridwa ntchito. Izo zinatulutsa chinthu cholembapo chopyapyala, chosalala, cholembapo choyera chomwe chinali kugwiritsiridwa ntchito kaamba ka mabukhu ofunika koposa kufikira kupangidwa kwa kusindikiza, kaamba ka kumene kugwiritsira ntchito kwa pepala kunali kotsika mtengo ndipo kwabwinopo.