Kuchita Upainiya Mphepete mwa Amazon
NKHALANGO ya Amazon! Chifupifupi aliyense anamva ponena za iyo. Koma ochepera akhala ndi mwaŵi wa kupita ndi kukaiwona iyo. Mkati mwa zaka khumi zapitazo, ngakhale kuli tero, unyinji wa apainiya, kapena atumiki a nthaŵi zonse, achita kokha chimenecho. Ngakhale chofunika koposa, iwo atenga mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu kumeneko. Mwa kugwiritsira ntchito bwato la Watch Tower Society El Refugio (Chipulumutso), iwo adutsa nkhalango ya Amazon kupyolera mwa cholowanecholowane wa mitsinje yomwe imadutsanadutsana kumpoto cha kum’mawa kwa Peru.
Ndi gawo losangalatsa chotani nanga mmene iri lakhalira! Mafuko ambiri a Amwenye ali omwazikana mkati mwa gawo lalikulu limeneli. Machacras ang’ono, kapena minda, imapezeka kukwera ndi kutsika mitsinjeyo, mphepete mwa magombe, ndi kumbuyo kwambiri mu ziyangoyango za mdima za nkhalangoyo. Ngakhale kuti ali opatulidwa, anthu amenewanso ayenera kukhala ndi mwaŵi wa kukhala ndi uthenga wa Baibulo wa moyo.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
Pafupi ndi mzinda wa nkhalango ya Iquitos, mitsinje yaikulu iŵiri—Ucayali ndi Marañón yofulumira ndi yowopsya—imabwera pamodzi kupanga Amazon wamphamvu. Ikumasokoneza mopitiriza, kupindikapindika, ndi kupanga phokoso, mitsinje imeneyi imadya m’magombe awo ndi kugwetsera mitengo yaikulu m’mafunde ake a njala. Magombe a m’chenga amapangidwa mkati mwa usiku, motero kusintha njira ya mafunde.
Pamene inali kumayenda motsika ndi mtsinjewo mphepete mwa Ucayali, El Refugio mwadzidzidzi inalowa m’gombe la mchenga lomizidwa pang’ono. Kuima kosayembekezerekako kunapangitsa ziwalo zokweramo za gululo kukhala zosakhazikika bwino, koma kugwiririra ku zingwe ndi mitengo ya bwatolo kunawasunga iwo kusagwera m’madzi. Kaputeni anayendetsa bwatolo mobweza m’mbuyo, koma osaphula kanthu. Ilo linatitimira. Chotero abale asanu ndi mmodziwo omwe anali m’bwatolo anapinda matilauzi awo, kulumphira m’gombe la m’chengalo, ndi kuyamba kuchotsa mabokosi 40 a mabukhu kuti apeputseko katunduyo. Mwadzidzidzi, chiwalo cha gululo chinafuula: “Chenjerani! Nsato ya m’madzi ikukwera pa bwato.” Motsimikizirika, njoka yobiriwira mowala ya utali wa mamita aŵiri inali kukwera m’mphepete mwa bwatolo. Koma ndi kugwedeza kofulumira kwa ngombo, iyo inabwerera m’madzi. Mwamsanga, ndi katunduyo atapeputsidwa, bwatolo linamasuka ndipo linayambanso kuyandama.
Njira Zolalikira Zolinganizidwa
El Refugio si bwato lalikulu, ndipo ndithudi siiri yothamanga kwambiri. M’chenicheni, imayenda pang’onopang’ono kwambiri pamene ikuyenda molimbana ndi mafunde othamanga. Kuti akhoze kukwaniritsa gawo la mkati, chotero, apainiyawo akulitsa makonzedwe a kachitidwe. Asanasiye nyumba zawo mu mzinda wa Iquitos, iwo amayesa kupeza chomwe chiri kutsogolo m’dera lapadera lomwe akukhumba kukwaniritsa. Mwa kufunsa anthu omwe ali nzika za kumaloko, iwo amakhala okhoza kupanga mapu a mwamsanga a midzi ndi chacras m’gawo limenelo. Mitsinje yaing’ono kapena ngalande zimalembedwa kaamba ka maulendo a pambali. Chotero, ngati dera losankhidwalo liri ndi midzi yambiri, bwatolo lingakhale losayenda kwa mlungu umodzi kapena iŵiri. Kaŵirikaŵiri, anayi a apainiya asanu ndi mmodziwo akakhoza kukwaniritsa minda yomwazikanayo, pamene kaputeni ndi apainiya ena otsalawo anali kuyenda mkati mwa nkhalangoyo, kumene watolo silingapite. Ichi chimapangidwa mwa kukonza kaamba ka njira pa kampani ya ndege ya mafuta yomwe imapita ku msasa.
Misasa imeneyi iri m’malo olambulidwa mkati kumene kukumba kofufuza kaamba ka mafuta kumachitidwa mokhazikika. Amuna zana limodzi kapena owonjezereka angapezedwe mu msasa woterowo. Mbonizo zimapanga makonzedwe kulankhula kwa amunawo pa nthaŵi ya chakudya cha madzulo, pa mapeto a maora ogwira ntchito. Mu msasa umodzi, msasa wodyeramo unatsimikizira kukhala bwalo losonkhanira labwino koposa. Amunawo anamvetsera, ndipo angapo pambuyo pake anafunsa mafunso ponena za mavuto a makhalidwe omwe anali kuyang’anizana nawo pamene anali kutali kwambiri ndi mabanja awo. Ndi mwaŵi wabwino chotani nanga umenewo wa kupereka lingaliro la BAibulo pa chiyero cha makhalidwe abwino! Pambuyo pa gawo la mafunso ndi mayankholo, amuna ambiri anapempha maBaibulo ndi zothandizira kuphunzira Baibulo. Maina anatengedwa, ndipo pambuyo pake maphunziro anayambitsidwa ndi ena a amuna amenewa ndi mabanja awo mu Iquitos. Misasa inayi ya mafuta inagwiriridwapo ntchito m’njira imeneyi—itatu kupyolera mwa kuyenda pa ndege ndi umodzi ndi ulendo wa El Refugio.
Nthaŵi iriyonse pamene caserío, kapena mudzi waung’ono, unawonedwa m’mphepete mwa gombe, apainiyawo anali kumangirira bwatolo ku chinthu chapafupi kwambiri chokhazikika chokhoza kulikhazikitsa ilo. Anali munthu wanzeru wa gululo, ngakhale ndi tero, yemwe anayesa gombelo asanalumphe. Mtumbira wa dothi wowonekera wolimba wa gombe umene mtsinjewo unawunjika umawoneka kukhala wachisungiko koma ungakhale wodzaza ndi zozizwitsa. Wolumpha wosakaikirayo angadzipeze iyemwini atamira kufikira m’chiwuno m’matope!
Pamene ali achisungiko pa gombe, abalewo amadutsa kupyola gulu la nthaŵi zonse la ana okhala ndi chilakolako chofuna kudziŵa, omafuula ndi kuyang’ana kaamba ka kalonga wa mudzi. Iwo mwachidule amalongosola kwa iye chifuno cha ulendo wawo ndi kufunsa kugwiritsira ntchito sukulu ya kumaloko kapena malo apakati osonkhanira a mudziwo kaamba ka nkhani ya Baibulo. Kaŵirikaŵiri, chilolezo chinali kukperekedwa. Zilengezo zinali kupangidwa ndi pakamwa pamene anawo anamwazikana m’njira zonse kufalitsa chiitanocho. Kumayambiriro kwa nkhaniyo, tsiku limathedwa kulalikira ku msasa ndi msasa. Anthuwo ali aubwenzi ndipo ochereza ndipo amalandira mofunitsitsa mabukhu anthu a Baibulo. Pamene ndalama siziriko, mabukhuwo amasinthanitsidwa ndi nkhasi, anyani, nkhuku, parrots, zipatso, kapena ngakhale duwa lokongola koposa.
Pamene nthaŵi ilola, maulendo obwereza amapangidwa masana. Awo amene amasonyeza chikondwerero chapadera amafunsidwa kubweretsa mecheros yawo, kapena nyali, ndi parafini ndi kuyatsa muuni. Mwachisawawa, pofika ora lachisanu ndi chiŵiri, onse akhala kale pansi, ndi nyali zawo m’dzanja limodzi ndi Baibulo lawo m’dzanja lina. Pambuyo pa kutha kwa nkhaniyo, mafunso ayamba. Kodi Mboni za Yehova zimakhulupirira mu moto wa helo? Ndimotani mmene zikhulupiriro za Mboni zimasiyanirana nd zija za chipembedzo cha Chikatolika? Ambiri akondweretsedwa kupeza mayankho mu maBaibulo awo.
Zokumana Nazo Zotenthetsa Mtima
Pamapeto pa nkhani imodzi yoteroyo, mwamuna ndi mkazi wake anabwera kwa mpainiyayo ndi misozi m’maso mwawo. “Abale, takhala tikuyembekezera kwa nthaŵi yaitali kumva mawu onga amene tamva usiku uno,” mwamunayo anatero. “Timakonda dziko lathu ndi lingaliro la paradaiso wa pa dziko lapansi kumene tingakhale moyandikira ku ilo. Tsopano, ndani amene mwanena kuti adzapita kumwamba?” Chiri ndithudi chotenthetsa mtima kukhala kutali m’nkhalango ya Amazon, makilomita ochulukira kuchoka ku malo “otsungula,” ndi kupeza onga nkhosa oterowo.
Apainiyawo amayesera kugawira mabukhu mu unyinji, popeza kuti chingatenge nthaŵi yaitali asanabwererenso ku midziyo. Tsiku lina, atabwerera ku Iquitos, mwamuna wa pa bwato la mu mtsinje anaimika mmodzi wa abalewo ndi kufunsa kaamba ka unyinji wina wa mabukhu asanu ndi atatu. Nchiyani chomwe chinachitika ku unyinji wake woyambirira? Limodzi ndi limodzi, anansi ake odzacheza anabwereka mabukhuwo. Zinthu zoŵerenga ziri zosowa m’nkhalangoyo. Mwanjira imeneyo, mabukhu afikira malo amene apainiyawo iwo eni sanawafikire. Ndi mzimu wake, Yehova mwakutero akuwona ku icho kuti zofalitsidwa zathu Zachikristu zafika m’manja olondola.
Pa mudzi umodzi waung’ono, aŵiri a abalewo anakhala ndi bwatolo pamene enawo anatsatira kanjira kopita m’nkhalango. Mitengo yaikulu inatseka kutsogoloko, kuthetseratu kuwala kwa dzuŵa, pamene mbalame za mitundu yambiri zinaitana mobwerezabwereza mkati mwa zitsamba zobiriwira. Pambuyo pa kuyenda kwa mphindi 15, Mbonizo zinafika ku malo olimiridwa bwino. Chinatenga chifupifupi ora limodzi kuitanira pa misasa yonse kumeneko. Pamene abalewo anali okonzekera kupita, mwamuna wina anawafikira ndi kuwapempha kukhala usiku wonse, popeza kuti anali ndi mafunso ambiri. Chotero mmodzi wa apainiyawo anatsala kumbuyo pamene ena onsewo anabwaerera ku bwatolo.
Mpainiyayo analingalira kuti nkhani ya Baibulo iperekedwe madzulo. Chotero anawo anatimizidwa, kutsatira njira zimene abalewo anaphonya, kukaitana anansi. Pa nthaŵiyo, phunziro la Baibulo linatsogozedwa m’mudzimo, mwa kugwiritsira ntchito mitu ya bukhu lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya yomwe inakwaniritsa mafunso amene mwamuna wocherezayo anafunsa. Pamene kuzizira kwamadzulo kunakuta pa chophimba chotentha, choimikira cha mitengo ya nsungwi mwadzidzidzi chinaphulika kukala phokoso lalikulu. Mazana onsewo a mbalame zotchedwa parakeet anawonekera kukhala akuyamba kuyimba pa nthaŵi imodzi, akumawoneka kukhala akulonjera kuzizira kwa madzulowo.
Pofika kumayambiriro kwa madzulo, achikulire 20 ndi ana ambiri anali atasonkhana mozungulira mlankhuliyo. Nyali yowala yogwiritsira ntchito gasi inapereka kuwunikira kwabwino koposa kaamba ka kuŵerenga, koma inakokanso mazana a tizirombo tamunkhalango. Chifupifupi pakati pa nkhaniyo, mlankhuliyo anameza kamodzi! Pambuyo pa mkhalidwe wa kusokonezeka kwa phokoso lopambanitsa, kuseka, ndi kumvera chifundo, iye anapitiriza, kubweretsa nkhaniyo ku mapeto ake a chipambano. Pa nthaŵiyo, manyazi onse anali atatha ndipo kukambitsirana kwa umoyo kunayambika.
Mnansi womalizira atachoka, munthu wokondwererayo anaika mosquito net pa khoma limodzi la pulatiformu ya pabwalo ya nyumba yake, yomwe inamangidwa pa mitengo chifulpifupi mita imodzi ndi theka pamwamba. Akumasiya mpainiyayo kuti akhazikike pansi pa netiyo, mwamunayo anasonkhanitsa nyama zake ndi kuzitsekera izo pansi pa pulatiformuyo kaamba ka chitetezero kuchokera ku zowukira za m’nkhalango. Pamene mbaleyo anakhala pamenepo pambuyo pa kupereka ziyamiko za pemphero kwa Yehova kaamba ka kuyang’anira kwake kwa chisamaliro, phokoso la m’nkhalango mwamsanga linamunyengetera iye kugona.
Sichinawonekere kukhala nthaŵi yaitali pamene mbaleyo anakhalanso tsonga. Tambala anali atalira, ndipo chinamvekera ngati kuti mbalameyo inali pansi pa kama yake. Iyo inalidi. Choyamba tambalayo analira, kenaka galu anakuwa, potsatira nkhukundembo inameza ngwidyo, ndipo potsirizira mbuzi inatulutsa mawu. Kutsatira ichi, mitundu yonse ya mbalame inayamba kulira kwawo kwa m’mawa. Tsiku latsopano linali litayamba.
Pamapeto pa kufisula kosangalatsa, mbaleyo ananyamuka kutsatira kanjirako kukagwirizana ndi anzake. Kokha patsogolo iye anawona chomwe chinawoneka ngati mtengo waukulu mopingasa kanjirako. Kuyang’ana kosamalitsa kunawonetsa iyo kukhala nsato yaikulu, motsimikizirika ya utali wa mamita asanu ndi atatu. Mpainiyayo mochenjera anayenda moizungulira iyo ndi kufika mwa chisungiko ku bwatolo.
Chitsutso cha Atsogoleri Achipembedzo Chithetsedwa
Mudzi wotsatirawo sunali wolandira kwenikweni. Pamene bwatolo linayenda ulendo wake ku malo oimira, abalewo anadabwitsidwa kuwona gulu lalikulu litasonkhana pa gombe. Otsogozedwa ndi wansembe Wachikatolika, iwo anathamangitsa bwatolo, akumafuula kuti sanafune mabukhu aliwonse a Baibulo. Chotero abalewo anapitiriza nd kumangirira pa malo kokha kunsi kwa mudziwo.
Sipanapite nthaŵi yaitali pamene ngalawa yonyamula nthochi inatuluka m’mudzimo. Pamene inali kudutsa, abalewo anaitana amuna atatu amene anali kuyendetsa ngalawayo kuima pafupi ndi El Refugio. Pamene iwo anatero, apainiya atatu anakwera m’ngalawayo ndi kuyamba kuchitira umboni. Mwiniwake wa ngalawayo anafuna kudziŵa chifukwa chimene wansembeyo sanafunire Mbonizo kuima pa mudziwo, ndipo apainiyawo anayankha kuti iwo sanawone chifukwa chimene wansembe sakafunira anthu kumvetsetsa Baibulo. Mwachitsanzo, ncholakwa chotani chimene chingatulukepo kucokera m’kuŵerenga Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo? Pamene amunawo anayang’ana m’bukhulo, iwo sakanatha kuliika pansi.
Tsiku lotsatira, ngalawa zambiri zinatsatira El Refugio. Chofalitsidwa cha Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo chinapangitsa chisangalalo m’mudziwo. Abalewo anawuzidwa kuti mwa kuyenda mtunda waufupi cha mkati mwa mudzi iwo akafika pa kanjira komwe kakawatsogolera iwo m’mudzimo ndi njira ya kumbuyo. Pamene anafika kumeneko ndi kuyamba kupita ku khomo ndi khomo, apainiyawo anasangalala ndi kulonjeredwa kwabwino koposa. Ambiri a anthu a m’mudziwo anatenga unyinji wonse wa mabukhuwo, zochulukira ku kukwiyitsidwa kwa wansembe wa kumaloko.
Nyumba ya Ufumu Yakutali Imangidwa
M’kupita kwa nthaŵi apainiya olimba mtimawo anafikira pa malo mu Amazon pamene malire a maiko atatu amakumanira. Midzi itatu, yonse mkati mwa mtunda waufupi kuchokera ku wina ndi unzake, imapanga malo otanganitsidwa a za malonda pamenepo. Iwo ali Caballococha mu Peru, Leticia mu Colombia, ndi Tabatinga kumbali ya Brazil. Kulowa mu uliwonse wa mizindayo kumapezedwa mopepuka, popeza kuti kuli lamulo lochepera la chiphaso cholowera m’dziko mkati mwenimweni mwa nkhalangoyo.
Pa Tabatinga, chinadziŵidwa kuti alongo achipainiya aŵiri achiBrazil anali kugwira ntchito mu mzindawo. Iwo anapangitsa gulu lochepera kukhala lokondweretsedwa m’kusonkhana pamodzi koma analibe malo okumanira. Alongo aŵiriwo anafunsa abalewo kukhala ndi kupereka nkhani m’gawolo, chomwe anachita mwachimwemwe. Kukambitsirana kosiyanasiyana kunasonyeza kuti panali zopereka zokwanira pakati pa gululo kugula mitengo kumanga chimango chaching’ono pa malo omwe anaperekedwa. alongowo anali atapeza kale malo opala matabwa ku mtunda kwa mtsinjewo kumene munthu wokondwerera analonjeza mtengo wabwino pa matabwa. Chinatenga maulendo aŵiri pa El Refugio kubweretsa matabwawo. M’masiku 15, manja ofunitsitsa anamanga Nyumba ya Ufumu yaikulu mokwanira kukhala anthu 80. Gulu la pa bwatolo linagawira atril yawo yeniyeni, kapena tebulo la mlankhuli, ndi mabenchi angapo kutenga gulu losangalatsidwalo. Anali achimwemwe chotani nanga kukhala ndi malo awo awo osonkhanira pamalizira pake!
Padakali gawo lokulira lakuti likutidwe mphepete mwa Amazon ndi mitsinje yake yolunzanitsa. awo amene amalabadira chiitano cha munthu wa ku Makedoniya cha “kulalikira mbiri yabwino” m’malo akutali amenewa adalitsidwa mokulira. (Machitidwe 16:9, 10) Tsopano El Refugio iri ndi ziwalo zatsopano za apainiya. Iwo nawonso ali ndi chidaliro chotheratu chakuti Yehova adzatsogoza ndi kuwachinjiriza iwo mu utumiki wawo wopatulika.
[Mapu patsamba 25]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
COLOMBIA
Leticia
PERU
Iquitos
Amazon
Marañón
Ucayali
BRAZIL
Tabatinga
[Zithunzi patsamba 26]
Apainiya okwera “El Refugio” abweretsa chowonadi chopatsa moyo kwa anthu m’mphepete mwa Amazon