Chidziŵitso pa Nyuzi
Phunziro Lolakwika
Kwa zaka khumi zapitazo, koleji mu New York State yakhala ikupereka kosi pa kugonana kwa anthu komwe kungapezere ophunzira zipambano zitatu za koleji. Ophunzira “akufunidwa kupita ‘pa ulendo’ kukalankhula ndi achigololo, kuchezera malo okhalako ogonana ofanana ziwalo kapena kufunafuna malo owonetsa umaliseke,” akusimba tero wolemba m’danga la New York Post. Bukhu lophunziridwa m’kalasi likunenedwa kupereka malangizo otheratu pa kudzilowetsa m’kugonana kwa mkamwa ndi kulimbikitsa kuchita mphyotomphyoto. Mogwirizana ndi Post, monga mbali ya phunziro la m’kalasi, ophunzira akusonyezedwa filimu yomwe imasonyeza “anthu aŵiri akugonana,” limodzinso ndi “kuwonetsedwa kwa ziwalo za thupi za mwamuna ndi mkazi.” Kodi nchiyani chomwe chikachotsedwa mowonjezereka ku mkhalidwe wa kuyera ndi ubwino?—Afilipi 4:8, 9.
Pamene kuli kwakuti anthu achichepere afunikira kudziŵa zenizeni za moyo ndi kukhala ndi mkhalidwe woyera kulinga ku zoterozo, makolo ali ndi thayo lokulira la kupereka malangizo oterowo. (Miyambo 22:6) Kosi ya sukulu iriyonse yomwe imalimbikitsa kugonana kunja kwa ukwati ndipo imafuna ophunzira kuwona mafilimu oipa ndi kuchezera ogonana ofanana ziwalo ndi achigololo sikakhoza, ndithudi, kulandiridwa kwa alambiri owona a Mulungu. Baibulo limalongosola momvekera awo ochita dama, chigololo, ndi kugonana kwa ofanana ziwalo kukhala anthu a “m’zilakolako za mitima yawo ku zonyansa,” odzilowetsa m’chomwe chiri “chamanyazi.” Ponena za zinthu zoterezi, Baibulo likulamula kuti: “Thawani dama.” Chomwe chiri choposerapo, ilo limati: “Dama . . . lisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu.”—Aroma 1:24-32; 1 Atesalonika 4:3; Aefeso 5:3, 5; Agalatiya 5:19, 21.
Chiyembekezo Chonama
Anthu ofunafuna “popitira paumwini kwenikweni” kulowa mu imfa akutembenukira mkhalidwe wozoloŵereka wa kuika maliro m’kuyanja kachitidwe kakale ka kuwumitsa mtembo, ikusimba tero The Wall Street Journal. Mtengo wokulira wa $7,500 “udzapangitsa kasitomalayo kuviikidwa kwa miyezi iŵiri mu vinyo, masamba ndi zosungitsa za mankhwala, wokutidwa ndi mafuta onunkhira ndi kuikidwa m’nsalu yowumikira, fiberglass, polyethylene ndi pulasita,” ikutero Journal. Zokometsera za golidi kapena miyala ya mtengo wapatali yozokotedwa pa bokosi la mtembo la mkuwa lolinganizidwa ku mlingo wa thupi zimagulidwa pa $100,000 ndi kuposapo.
Komabe, sikuli kokha kupatulika kwa kuwumitsako komwe kukukoka makasitomala. Munthu mmodzi ananena kuti “ngati chiri chowona monga mmene Akristu ena amanenera kuti pa Tsiku la Chiweruzo Kristu adzatiitana ife kuchoka m’manda, kenaka ndifunikira kukhala mu mkhalidwe wabwino womwe ndingakhoze.”
Mofanana ndi Aigupto akale omwe anakhulupirira kuti thupi lifunikira kusungidwa kaamba ka kubwerera kwa moyo mu moyo wa pambuyo pake, anthu oterowo kaŵirikaŵiri amazika chiyembekezo chawo pa chiphunzitso chakuti moyo uli wosafa. Atsogoleri a chipembedzo aphunzitsa kuti pa Tsiku la Chiweruzo, matupi a olungama ndi oipa adzagwirizanitsidwanso ndi miyoyo yawo yeniyo kukagawana m’madalitso a kumwamba kapena kutayidwa ku moto wa helo.
Komabe, chiphunzitso cha kukhala ndi moyo wosafa sichimaphunzitsidwa m’Baibulo. M’malomwake, Baibulo limaphunzitsa kuti moyo umafa. “Moyo wochimwawo—ndiwo udzafa.” (Ezekieli 18:4) Chotero, chiyembekezo cha m’Baibulo kaamba ka moyo wa mtsogolo chimadalira, osati pa kupulumuka kwa moyo wosafa, koma pa kuwukitsa kwa Mulungu munthu wokhala ndi zikhoterero za moyo wake weniweni ndi thupi loyenerera lokhala ndi zizindikiro zofananazo ndi zikumbukiro zonga zimene anali nazo pamene anafa. Molondola, Yesu anakhoza kunena kuti: “Ikudza nthaŵi imene onse ali m’manda adzamva mawu ake nadzatulukira.”—Yohane 5:28, 29.
“Sali Mbali ya Dziko”
Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., inakumana ndi Bungwe Lolinganiza la Mzinda wa New York chaka chatha kukafunsa utali wa malo pa chimango cha nyumba zosanjikana 19 zogonamo. Pamene kuli kwakuti ochulukira a ziwalo za bungwelo anatsutsa ntchitoyo, mavoti aŵiri oyanja kusintha kwa malirewo anaponyedwa ndi Woyang’anira wa Mzinda wa New York Edward Koch. Mu ndemanga yolongosola maziko a chigamulo chake, Woyang’anira Mzinda Koch anawona kuti “Mboni za Yehova . . . zingalingaliridwe kokha kukhala anansi abwino . . . ndimawasunga iwo pa malo aulemu koposa.” Iye kenaka anawonjezera kuti: “Ndawuzidwa kuti kaamba ka zifukwa za chipembedzo iwo samavota m’masankho aliwonse ndipo mwinamwake chimenecho chiri chimodzi cha mavuto a ntchitoyi, chifukwa chakuti chiri chovuta kwa munthu wosavota kupambana m’nkhani ya mkangano mu imene nduna zosankhidwa zikuvutitsidwa ndi chiŵerengero chokulira cha anthu.”
Woyang’anira Mzinda Koch afunikira kuyamikiridwa kaamba ka kulimba mtima kwake ndi kupanda tsankho poyang’anizana ndi otsutsa ochulukira chotero. Ngakhale kuti zinthu zikanakhala zosiyana ngati Mboni za Yehova zinagawanamo mu masankho a ndale zadziko, iwo sangasonkhezeredwe kuchoka pa kaimidwe kawo ka uchete pa nkhani za ndale zadziko—mosasamala kanthu za kukulira kwa mtengowo. Kwa Akristu owona kaimidwe kali komvekera bwino. Yesu ananena kuti: “Iwo sali mbali ya dziko, monga momwedi ine sindiri mbali ya dziko.”—Yohane 17:16, NW.