Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 2/15 tsamba 31
  • Chilungamo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chilungamo
  • Nsanja ya Olonda—1989
Nsanja ya Olonda—1989
w89 2/15 tsamba 31

Chilungamo

Kuli kusungirira kapena kulamulira kwa chimene chiri cholondola m’njira yabwino ndi yopanda tsankho ndipo mogwirizana ndi muyezo. Liwu la Chihebri mishpatʹ, kaŵirikaŵiri lotembenuzidwa “chilungamo” kapena “chiweruzo” (NW, RS), lingaperekenso lingaliro la makonzedwe achindunji (Eks. 26:30), mwambo (Gen. 40:13), lamulo (2 Mbiri. 4:20), kapena njira yokhazikika (Lev. 5:10) yochitira zinthu.

Mawu aŵiri a Chihebri otembenuzidwa kaŵirikaŵiri kukhala “chilungamo” mu King James Version (tseʹdheq ndi tsedha·qahʹ) amaikidwa kaŵirikaŵiri kukhala “chilunjiko” mu New World Translation. (Gen. 18:9; Yobu 8:3) Pamene kuli kwakuti chilungamo chiri ndi kugwirizanitsidwa kwa lamulo, kwakukulukulu palibe kusiyana pakati pa chilungamo ndi chilunjiko.​—Yerekezani ndi Amosi 5:24.

Liwu limodzi la Chigriki lotembenuzidwa “m’chigwirizano ndi chilungamo” (NW) limasonyeza chinachake chomwe chiri “cholungama” (KJ, RS) kapena choyenerera. (Aroma 3:8; Aheb. 2:2) “Chiweruzo” ndi “kubwezera” ali matanthauzo oyambirira a mawu aŵiri ena a Chigriki oikidwa nthaŵi zina kukhala “chilungamo.”​—Mat. 12:20, NW, RS; Luka 18:7, NW.

Woweruza wamkulu ndi Mpatsi wa Lamulo (Yes. 33:22), Yehova Mulungu, “ali wokonda chilunjiko ndi chilungamo.” (Sal. 33:5, NW) “Chilungamo ndi kuchuluka kwa chilunjiko iye sadzanyalanyaza.” (Yobu 37:23, NW) Ichi chimatsimikizira kuti iye sadzalekerera okhulupirika ake. (Sal. 37:28) Yehova samasonyeza tsankho m’kuchita ndi zolengedwa zake, koma amalandira ndi kupereka madalitso pa awo onse omuwopa iye ndi kuchita m’chilunjiko. (Mach. 10:34, 35) Aliyense payekha ndi mitundu amapatsidwa chilango kapena kufupidwa mogwirizana ndi machitidwe awo. (Aroma 2:3-11; Aef. 6:7-9; Akol. 3:22–4:1) Chilungamo cha Yehova chimalinganizidwanso ndi chifundo, mwakutero kupereka mwaŵi kaamba ka anthu ndi mitundu kutembenuka kuchoka ku njira zawo zoipa ndipo mwakutero kuthaŵa kuperekedwa kwa ziweruzo zake zoipa.​—Yer. 18:7-10; Ezek. 33:14-16.

Nzeru ya Yehova iri yokulira koposa ija ya anthu opanda ungwiro, ndipo munthu, osati Mulungu, ayenera kuphunzira njira ya chilungamo. (Yes. 40:14) Chotero munthu sali m’malo a kuweruza machitidwe a Mulungu kukhala olungama kapena osalungama, koma ayenera kuphunzira kugwirizanitsa kulingalira kwake ku muyezo wa chilungamo umene Yehova wavumbula m’Mawu ake. Anatero Mulungu kwa Aisrayeli kuti: “Inu, nyumba ya Israyeli, kodi njira zanga nzosayenera? Njira zanu si ndizo zosayenera?” (Ezek. 18:29) Ndiponso, ulengi wa Yehova umachotsapo maziko aliwonse a kukaikira kulunjika kwa ntchito zake.​—Aroma 9:20, 21; onaninso Yobu 40:8–41:34.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena