‘Sindinakhalepo Wachimwemwe Kuposa Mmene Ndiriri Tsopano’
Imeneyo inali ndemanga ya mkazi yemwe anagwiritsira ntchito uphungu woperekedwa m’bukhu la Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Iye anali ndi mavuto a mu ukwati ndipo anayamba kukambitsirana zimenezi ndi mkazi yemwe ankayeretsa nyumba yake. Mtsikana woyeretsayo akulemba kuti:
“Uphungu uliwonse womwe ndinapereka kwa iye unali mwachindunji wochokera m’bukhulo. Potsirizira pake ndinamuuza iye kuti ndinali ndi bukhu lomwe angalipeze kukhala lokondweretsa. Ndinalongosola mmene linandithandizira ine ndi kuti linali ndi nzeru zofala zambiri zochokera m’Baibulo. Masiku oŵerengeka pambuyo pake, ndinalankhula kwa iye pa lamya ndipo ndinadziŵitsidwa kuti iye ndi mwamuna wake analiŵerenga ilo ndipo anagamulapo kuchitirana wina ndi mnzake mwaubwino pang’ono.
“Madzulo ano iye anaitana kachiŵirinso kundiuza ine, pakati pa zinthu zina, kuti moyo wawo sunakhalepo wachimwemwe kuposa mmene uliri tsopano. Iwo aŵerenga bukhulo pamodzi, kufufuza ilo m’Baibulo, ndipo kugwiritsira ntchito maprinsipulo opezeka mu ilo.”
Ngati inu mukhumba thandizo m’kupangitsa ukwati wanu kukhala wachimwemwe koposa, inu mungapindule kuchokera ku bukhuli. Landirani kope mwa kudzaza ndi kutumiza kapepalaka.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba, la masamba 192 Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Ndatsekera K10 (Zambia).