Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 3/1 tsamba 3
  • Mmene Mungazindikirire Atumiki Owona a Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungazindikirire Atumiki Owona a Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zofunika kaamba ka Atumiki Owona
  • Kodi Atumiki a Mulungu Ndani Lerolino?
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kodi Ndani Kwenikweni Amene Ali Atumiki a Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Akazi a Mboni za Yehova Amaphunzitsa Mawu a Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Mtumiki Ndani?
    Galamukani!—2000
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 3/1 tsamba 3

Mmene Mungazindikirire Atumiki Owona a Mulungu

ZINACHITIKA mu 1948. Atumiki aŵiri, omwe anali Mboni za Yehova, anali pa ulendo m’basi yophwasuka pa msewu wa mabampu, akuchokera mu mzinda wa kumpoto kwa Spain kulinga ku Mapiri a Pyrenees. Iwo anali pa ulendo wawo kukachezera mtumiki wakutali. Pamene basi inaima pa malo a pafupi ndi mudzi umene mtumikiyo ankakhala, iwo anamuwona iye akuwayembekezera ndi bulu wake. Koma iwo anawonanso chapafupi ndi iye gulu lachilendo​—Alonda a Boma anayi okonzekeretsedwa bwino ndi mfuti ndi wansembe! Pamene atumikiwo anali kupita m’kanjira kakang’ono kotsikira ku mudziwo, mmodzi wa Alondawo anatulutsa mfuti yake ndi kufuula, “Manos arriba!” (Manja m’mwamba!) Alendowo anamangidwa. Chifukwa ninji? Wansembeyo anali atawuza Alondawo kuti alendowo anali zigawenga​—bodza lenileni! Monga chotulukapo, atumiki atatu onsewo anaikidwa m’ndende.

Kodi chimenechi chimatsimikizira chiyani? Kuti sionse omwe amadzinenera kukhala ansembe kapena atumiki amene amakhala atumiki owona a Mulungu. M’chenicheni, kaŵirikaŵiri pamakhala kusiyana kwakukulu pakati pa atumiki owona ndi onyenga. Kodi ndi ziti zomwe ziri zofunika zazikulu kaamba ka atumiki owona?

Zofunika kaamba ka Atumiki Owona

Tanthauzo lenileni la “kutumikira” liri “kupereka thandizo kapena utumiki.” Atumiki Achikristu owona ayenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kuti Baibulo liri Mawu owuziridwa a Mulungu. (Yohane 17:17) Ngakhale kuli tero, chofunika chenicheni chimenecho sichiri chokwanira. Ayeneranso kukhala ndi chidziwitso chabwino ndi kumvetsetsa kwa Baibulo. Koma sayenera kugwiritsira ntchito chidziŵitso chimenecho mwadyera​—kaamba ka phindu la iwo okha. Ayeneranso kukhala alaliki achangu a Uthenga Wabwino​—mbiri yabwino yonena za Ufumu wa Mulungu ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’paradaiso ya dziko lapansi.​—Yohane 17:3; Salmo 37:11, 29.

Mofananamo, chenicheni chakuti Mboni za Yehova zikulalikira mbiri yabwino ya Ufumu osati kokha mu Spain koma kuzungulira dziko lonse chiri m’kukwaniritsidwa kwa chimene Yesu analosera kaamba ka nthawi ya mapeto a dongosolo iri lakale loipa la kachitidwe ka zinthu. Iye ananena kuti: “Ndipo mbiri yabwino imeneyi ya Ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”​—Mateyu 24:14, 33, 34, NW.

Chofunika china chenicheni kaamba ka atumiki owona chiri chakuti, monga mmene Yesu ananenera, iwo sayenera “kukhala mbali ya dziko”; chotero, iwo sayenera kukhala m’ndale zadziko. (Yohane 15:19) Iwo ayeneranso kukhala odzichepetsa kwenikweni, achikondi, ndi okoma mtima, nthawi zonse okonzekera kuthandiza oyenerera omwe ali m’kusowa.​—1Akorinto 13:1, 4; 1 Petro 5:6.

Iyi ndi nkhani yaikulu kwenikweni. Kusiyanitsa pakati pa atumiki owona ndi onyenga iri nkhani ya moyo ndi imfa. Iri yofunika kwambiri tero! Mu Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri, Yesu anachenjeza kuti: “Yang’anirani mupeŵe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma mkati mwawo ali afisi olusa.”​—Mateyu 7:15.

Komabe, atumiki owona a Mulungu alibe kokha mathayo ndi zofunika komanso ali ndi mwaŵi wochuluka. M’chenicheni, monga gulu, iwo ali a mwaŵi koposa, opambana kwenikweni, ndipo gulu lachimwemwe koposa pa dziko lapansi lerolino, monga mmene mudzawonera m’nkhani yotsatira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena