Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 7/15 tsamba 26-29
  • Kufikira Chitokoso cha Gawo Lakale Koposa pa Dziko Lapansi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufikira Chitokoso cha Gawo Lakale Koposa pa Dziko Lapansi
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Kufikira Chitokosocho
  • Chipatso cha Ufumu Chatulutsidwa
  • Ziŵerengero Zapamwamba Zatsopano m’Gawo Lakale Koposa
Nsanja ya Olonda—1989
w89 7/15 tsamba 26-29

Kufikira Chitokoso cha Gawo Lakale Koposa pa Dziko Lapansi

“UFUMU wakumwamba wayandikira.” Kwa olengeza 370 a “mbiri yabwino” mu Boma la Israyeli lamakono, kulalikira uthenga umenewo kuli ndi tanthauzo lapadera. Chifukwa ninji? Chifukwa kunali kuno kumene uthenga wa Ufumu unalalikidwa choyamba ndi Yesu Kristu zaka zina 2,000 zapitazo. (Mateyu 4:17; 24:14) Chimenecho chimapangitsa Israyeli kukhala gawo lakale koposa pa dziko lapansi m’limene mbiri yabwino ikulalikidwa.

Kuyambira pa chiyambi penipeni, ngakhale kuli tero, iri lakhala gawo lopereka chitokoso. Ngakhale kuti ambiri anasonyeza chikondwerero mu uthenga wa Yesu, ochepera anapita kuposa pamenepo. (Yohane 6:2, 66) Lerolino, chitokoso chiri mu kukula kwa chipembedzo, mwambo, ndi kawonedwe ka ndale zadziko.

Ku mbali imodzi, pali Aluya 2.2 miliyoni. Pakati pawo pali otchedwa Akristu, Asilamu okangalika ndi osakangalika, ziŵalo za chikhulupiriro cha Druze, ndi odzinenera kukhala osakhulupirira mwa kukhalapo kwa Mulungu. Iwo alinso osiyana m’njira zambiri mwa ndale zadziko, ena omayanja kukhazikitsidwa kwa boma lodzilamulira la Palestina mu West Bank ndi Gaza Strip.

Ku mbali ina, kuli Ayuda a Chiisrayeli 3.5 miliyoni, nawonso ogawanikana m’njira zambiri. Ena anasamuka kuchokera ku Morocco, Yemen, Iraq, ndi Syria. Ena anabwera kuchokera ku Europe ndi Russia. Enanso anachokera ku India, America, Ethiopia, South Africa, ndi kwina kwake. Iwo amakhala m’midzi yokhala ndi makhalidwe ndi miyambo yawo yawo limodzinso ndi kutanthauzira kwawo kwapadera kwa Chiyuda ndi mmene amachitira icho.

Pali, mwachitsanzo, rabi wamkulu kaamba ka Ayuda a Ashkenazi (a ku Europe) ndi wina kaamba ka Ayuda a Sephardic (a ku Middle East). Pamene kuli kwakuti ochulukira amasonyeza chikondwerero chokulira m’nkhani za ndale zadziko, pali Ayuda achipembedzo mozama omwe samazindikira nkomwe kukhalapo kwa Boma la Israyeli ndipo amakana kupereka misonkho. Kenaka pali opulumuka a Chipululutso, ambiri omwe akuzunzidwabe ndi tsoka lawo lapita, aliyense wokhala ndi chokumana nacho chake chokhwethemula mtima kuchisimba. Mowonjezereka, kachiŵirinso, ambiri akudzinenera kukhala osakhulupirira mwa kukhalapo kwa Mulungu, akumamamatira ku kusiyana kokulira kwa nthanthi zaumwini. Nkhosi yokha yomwe ikusungirira unyinji wa Ayuda pamodzi iri kupulumuka kwawo monga anthu ndi gulu la ndale zadziko.

Kufikira Chitokosocho

Pambuyo pa kulekeka kwa zaka zoposa 1,800, ntchito yolalikira Ufumu inayambidwanso kuno pa mlingo wochepera mu 1913. Pa nthaŵi imeneyo, mwamuna wachichepere wokondweretsedwa m’Baibulo anayamba kufesa mbewu za Ufumu mu Ramallah, chifupifupi makilomita 16 kumpoto kwa Yerusalemu. Kuchokera kumeneko mbiri yabwino inafalikira kwa nzika za Chiluya za ku Beit-Jala ndi Haifa. Mwamsanga pambuyo pa Nkhondo ya Dziko II, alongo aŵiri omwe anali Mboni a chiyambi cha Chiyuda anayambitsanso ntchitoyo mu gawo la Tel Aviv/​Jaffa. Lerolino, pali mipingo isanu ndi umodzi ndi magulu aŵiri a Mboni za Yehova otumikira mu Haifa, Tel Aviv, Betelehemu, Ramallah, Lodi, ndi m’gawo la Beereseba.

Monga mmene zinaliri zaka mazana 19 apitawo, utumiki wa ku nyumba ndi nyumba udakali njira yokhutiritsa koposa ya kupeza omwe ali okondweretsedwa m’mbiri yabwino. (Luka 8:1; yerekezani ndi Machitidwe 5:42.) M’chenicheni, kuyerekezedwa ndi maiko ena, chiri chosangalatsa kuchitira umboni m’njira imeneyi kuno. Mwachisawawa, anthu ali ofunitsitsa kudziŵa ponena za uthenga wathu ndipo amaitanira mkati olalikira a Ufumu kaamba ka kukambitsirana. Kufunitsitsa kudziŵa kumeneku kaŵirikaŵiri kumatsogolera ku kugawiridwa kwa magazini athu ndi mabukhu ena a Baibulo. Kaŵirikaŵiri, zofalitsira zoterozo zimaperekedwa kuchokera kwa mnansi mmodzi kupita kwa mnansi wina, kutulukapo m’kuphunzira chowonadi cha Baibulo kwa anthu ena.

Kufunitsitsa kudziŵa kumodzimodziku, ngakhale kuli tero, kaŵirikaŵiri kumakhala chiwopsyezo ku mbewu zosalimba za chowanadi m’mitima ya atsopano. (Mateyu 13:20, 21) Anansi, mabwenzi, ndipo makamaka atsogoleri a chipembedzo amachita kuthekera kwawo kutsendereza, kuseka, kuwopsyeza, ndipo m’nkhani zina kuchitira choipa mwakuthupi awo omwe amasonyeza chikondwerero mu uthenga wa Ufumu. Monga chotulukapo, ena atayikiridwa ntchito, pamene ena alekedwa kotheratu ndi mabwenzi ndi banja. Awo omwe amaima nji ndi kukhala Mboni za Yehova ayenera kupirira moto wa chitsutso.​—Yerekezani ndi Yohane 9:22.

Chitsutso chimabweranso m’njira zina. Mboni za chiyambi cha Chiyuda zawukiridwa ndi gulu lowukira. Ofesi ya nthambi ndi Nyumba ya Ufumu mu Tel Aviv ndi Nyumba ya Ufumu mu Haifa zakhala chandamale cha kutentha moto. Tsopano pali chitsenderezo chokulira ponse paŵiri kwa Mboni za Chiluya ndi za Chiyuda kutenga mbali mu mkangano wa ndale zadziko pa kukhazikitsidwa kwa boma la Palestina. Akumasungilira kaimidwe ka uchete m’nkhani zoterozo, abale mwamachenjera amalongosola kuti palibe nthumwi ya umunthu yomwe iri yokhoza kuthetsa mavuto a mtundu wa anthu ovutitsidwa. M’malomwake, m’kutsanzira Mtsogoleri wawo, Yesu Kristu, Mbonizo zimaloza ku Ufumu wa Mulungu monga yankho lokha.​—Yohane 17:16; 18:36.

Chipatso cha Ufumu Chatulutsidwa

Mosasamala kanthu za zitokoso m’gawo lochitira umboni lakale koposa limeneli, awo “akumva mawu nawadziŵitsa” amabweretsa chipatso cha Ufumu m’munda umenewo. (Mateyu 13:23) “Pali anthu omwe ali aludzu kaamba ka chowonadi, okonda chilungamo omwe m’chenicheni amachifunafuna icho,” anawona tero mtumiki wa nthaŵi zonse wokhala ndi kuzoloŵera. “Iwo sakusonkhezeredwa ndi malingaliro kapena zididikizo kuchokera kwa ena. Pamene mwaŵi wa kuphunzira chowonadi ukantha, iwo mofulumira amaugwira uwo.” Zokumana nazo zambiri zimachitira umboni nsongayi.

Woleredwa m’malo a chipembedzo mu Grisi, Benvenida anasangalatsidwa mwakuya ndi chimene Baibulo limanena ponena za “mapembedzedwe oyera ndi osadetsedwa,” otchedwa, “kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo, ndi kudzisungira mwini osachita mawanga ndi dziko lapansi.” (Yakobo 1:27) Monga mtsikana wachichepere Wachiyuda, iye sanakumane ndi chirichonse koma “tsoka pambuyo pa tsoka,” monga mmene iye anachiikira icho. Iye anapirira zovuta za kulamulira kwa Nazi ndi nkhondo ya chiweniweni, mu imene iye anatayikiridwa mwamuna wake. Koma chiyembekezo chake cha kupeza anthu owona mtima ndi opanda chinyengo sichinazimiririke nkomwe.

Pambuyo posamukira ku Israyeli mu 1949, Benvenida analondola ntchito ya kukhala namwino kufikira kuleka kwake ntchito mu 1974. “Mkati mwa nthaŵi yonseyo,” iye ananena kuti, “ndinapitiriza kudzifunsa inemwini kuti: ‘Kodi ali kuti anthu aja abwino ndi owona mtima amene Baibulo limalongosola? Nkuti komwe kuli chilungamo m’dziko lino?’” Iye anatenga Chiyuda, kupezeka pa sunagoge ndi kusunga Sabata ndi matchuthi. Koma kujeda ndi kukangana pakati pa ziŵalo za mpingo wake wa kumaloko kunampangitsa iye kukhalabe ndi njala yokulirapo kaamba ka “mapembedzedwe oyera ndi osadetsedwa.”

Pomalizira pake, mu 1985, pa umodzi wa maulendo a pa chaka a Benvenida ku malo a za umoyo mu Grisi, mkazi yemwe anali Mboni wolandira thandizo kumeneko anayambitsa kukambitsirana ndi iye. Kukambitsirana kwakutali kunayambika. Usiku umodzimodziwo, Benvenida anapezeka pa msonkhano wake woyamba pa Nyumba ya Ufumu ya kumaloko ndipo anasangalatsidwa mwakuya ndi kutentha ndi kuwona mtima kwa abale ndi alongowo.

Benvenida anapitiriza phunziro lake pamene anabwerera ku Israyeli, ndipo chifupifupi chaka chimodzi ndi theka pambuyo pake, iye anabatizidwa m’kuchitira chithunzi kudzipereka kwake mwa Mulungu wa chowonadi, Yehova. “Pomalizira pake,” iye ananena kuti, “pambuyo pa zaka zonsezi ndipo pa msinkhu wa zaka 70, ndinapeza anthu odekha ndi odzichepetsa amene Baibulo limalankhula ponena za iwo, awo omwe amachita ndi ine monga munthu. Tsopano, tsiku lirilonse lomwe ndimakhala ndi moyo liri tsiku lachimwemwe ndi chifuno!”

Moshe anali wofunafuna chowonadi wina wongodikirira ‘kumva liwu la mbusa wabwino.’ (Yerekezani ndi Yohane 10:14-16.) Ngakhale kuti Moshe nthaŵi zonse anali wokonda Malemba, kunali kuchokera m’kope la “Chipangano Chatsopano” limene mbale wake anali pafupi kutaya mmene iye anaphunzira ponena za Yesu Kristu, ndipo anasangalatsidwa mwakuya. Nthaŵi ina pambuyo pake, Moshe anagwirizana ndi wogwira naye ntchito m’phunziro la Baibulo ndi Mboni ndi kupezekapo pa nkhani yoperekedwa ndi mlankhuli wochezera. “Ichi ndi chimene ndinafuna kumva nthaŵi zonse!” anafuula tero pambuyo pa msonkhano woyamba umenewo.

Pambuyo pa kubwerera m’mbuyo koyambirira, kupita patsogolo kwa Moshe kunali kofulumira. Mkati mwa miyezi isanu ndi umodzi, iye anabatizidwa. Ngakhale kuli tero, kupita patsogolo kwake kunabweretsa chitsutso kuchokera ku banja lake, makamaka mkazi wake. Ichi chinawonekera pamene iye, monga mwana wamkulu koposa m’banjalo, anakana kutenga mbali m’mapemphero a mwambo pa maliro a atate wake. M’kuwonjezerapo, mabwenzi ndi achibale anawuza mkazi wake kuti iye angachite bwino ‘kuchita chinachake mofulumira’ iye asanasamutsire zonse ku mpingo. “Ndinathetsa mantha ake mwa kudzipereka kuika nyumba m’dzina lake,” anachitira ndemanga tero Moshe. Ndipo mwa kundandalitsa moyenerera nthaŵi yake, iye anali wokhoza kusungirira kulinganizika kwa chimwemwe pakati pa banja lake ndi mathayo a mpingo.

Ngakhale kuli tero, siachibale onse amene anatsutsa chowonadi. Nehai anagawana chimene anaphunzira kuchokera m’Baibulo ndi mwamuna wake, Hanna, amene pa nthaŵiyo anali wokangalika koposa m’ndale zadziko. Mwamsanga, onse aŵiri anazindikira kuti Ufumu wa Mulungu uli chiyembekezo chokha kaamba ka mtundu wa anthu wotsenderezedwa. Chotero iwo anakhala atumiki odzipereka a Yehova ndi kuyamba kuchitira umboni pakati pa mabanja Achiluya mu Haifa ndi midzi yozungulira. Mwapadera iwo anachitira umboni pakati pa mabanja awo enieni ofutukulidwa, anthu ena 252 onse pamodzi.

Kodi ichi chakhala chitokoso? Inde, popeza kuti pambali pa kufunika kuyendetsa galimoto kwa ora limodzi ndi theka ulendo uliwonse ku midzi ya Chiluya kukapanga kufikira, kuleza mtima kokulira ndi chipiriro zinafunikira. “Nthaŵi zina osiyanasiyana amakuwuza kuti safuna kumva zowonjezereka. Pamene chimenecho chichitika, mudzayenera kuleka kulankhula. Pambuyo pake, mwinamwake mochenjera mungaloŵe m’nkhaniyo kachiŵirinso. Chiri chofanana ndi kukankhidwira kunja motulukira pa khomo la kutsogolo ndi kuloŵanso mkati kupyolera pa zenera,” anachitira ndemanga tero Hanna. Zonsezi zapereka malipiro. Kufikira ku nthaŵi ino, 24 a achibale ake 36 apafupi asonyeza chikondwerero chosamalitsa m’Malemba, ndipo 13 a iwo akuphunzira Baibulo ndi Hanna kapena Mboni zina. Kufikira ku tsiku lino, asanu a achibale ake apafupi limodzinso ndi ana ake apereka miyoyo yawo kwa Yehova, ndipo atatu ena akupita patsogolo kulinga ku nsonga imeneyo.

Ziŵerengero Zapamwamba Zatsopano m’Gawo Lakale Koposa

Zokumana nazo zotenthetsa mtima zonga izi zikuwonjezeka muno mu Israyeli, ndipo ziyembekezo kaamba ka kukula ziri zosangalatsa koposa. Mu 1988 chiŵerengero cha olengeza a Ufumu chinafika pa chiŵerengero chapamwamba cha 370. Avereji ya maphunziro a Baibulo otsogozedwa mwezi uliwonse m’nyumba za anthu okondweretsedwa chinadumpha kuchokera pa 89 mu 1979 kufika ku 301 mu 1988​—chiwonjezeko cha 240 peresenti!

Zonsezi zimabweretsa chimwemwe chokulira kwa Mboni za Yehova m’dziko lakale limeneli. Tikuyang’ana kutsogolo ku madalitso owonjezereka kuchokera kwa Mulungu wathu, Yehova, pamene tikupitiriza ndi ntchito yopanga ophunzira m’gawo lakale koposa pa dziko lapansi.

[Zithunzi pamasamba 26, 27]

Pamwamba: Garden Tomb, Yerusalemu

Kulamanzere: Msika ndi zochitika za m’khwalala mu Israyeli

Pansi: Ofesi ya nthambi mu Tel Aviv

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena