Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 10/1 tsamba 22-26
  • Kumapeza Chomchitira Yehova Nthaŵi Zonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumapeza Chomchitira Yehova Nthaŵi Zonse
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kaimidwe Kauchete
  • Gawo Langa Latsopano​—Ndende
  • Kutuluka
  • Wandende Wankhondo
  • Kulalikira kwa Anthu Onse
  • Kufutukula Utumiki Wanga
  • Yehova, Linga Lolimba
  • Kupeza Zinthu Zowonjezereka Zomchitira Yehova
  • Ndinali Wandale Tsopano Ndinasanduka Mkristu Wosakhudzidwa N’zandale
    Galamukani!—2002
  • Munthu Sakhala ndi Moyo ndi Chakudya—Chokha Mmene Ndinapulumukira M’ndende za Chipani cha Nazi
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Ndakhala Ndikudikirira Ufumu Womwe “Suli Mbali ya Dziko Lino”
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kuyesetsa Kukhala “Wantchito Wopanda Chifukwa Cha Kuchita Manyazi”
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 10/1 tsamba 22-26

Kumapeza Chomchitira Yehova Nthaŵi Zonse

Monga momwe yasimbidwira ndi Jean Queyroi

INALI nyengo yachirimwe yosangalatsa kalelo mu 1939. Malo ozungulira Martigny, gawo la Chiswiss la Valais, linali loŵala m’dzuŵa la August. Pamwamba pathu panali malo ena okwezeka koposa mu Alps, onga ngati Grand Combin yokutidwa ndi chipale chofeŵa, ikumafika ku utali wa mamita 4,314. Ndinali kusangalala ndi kuchereza kwa banja Lachikristu kwa masiku oŵerengeka, ndipo tinathera yochulukira ya nthaŵi yathu kukwera mapiriwo pamodzi. Ndinamva ngati kuti ndinali kale m’Paradaiso.

Posakhalitsa inafika nthaŵi ya kutsazika ndi kubwerera ku Paris. Ndinagula nyuzipepala kuti ndiŵerenge m’sitima, ndipo mbiri yochititsa mantha inandizizwitsa. Mkhalidwe wa dziko unali utanyonyotsoka mokulira, ndipo nkhondo inali yosapeŵeka.

Ndinayambanso ntchito yanga pa ofesi ya Watch Tower Society mu Paris, kumene ndinakhala ndikutumikira koposa chaka chimodzi. Koma masiku oŵerengeka pambuyo pake, ndinalandira chidziŵitso cha kuitanidwa ndi kulamulidwa kufika ku malo a anthu a nkhondo a Fort of Vincennes, kum’mawa kwa Paris. Moyo wanga unali pafupi kusintha mokulira.

Kaimidwe Kauchete

Pa September 3, 1939, Falansa ndi Great Britain inalengeza nkhondo pa Jeremani. Ndinafika ku Vincennes ndi kutenga kaimidwe kanga pa nkhani yauchete Wachikristu. Mwamsanga ndinadzipeza inemwini ndiri m’galimoto ya pambali ya njinga yamoto yankhondo yoyendetsedwa ndi msilikali wachichepere yemwe anapatsidwa malamulo a kundipereka ine ku Fort of Charenton yapafupipo. Mosasamala kanthu za phokoso la njinga yamotoyo, msilikali wachichepereyo, yemwe anadziŵa chifukwa chimene ndinali kutumizidwira kumeneko, anayesera kundithandiza. Iye anandipempha kuti: “Queyroi, chonde usalole izo kukuchitikira. Usakane kumenya, kupanda apo zinthu sizidzakhala bwino ndi iwe.” Ndinafulumira kumutsimikizira kuti ndinalibe mantha.

Kenaka unafika usiku wanga woyamba m’lumande ya ndende. Lumandeyo inali ya mamita aŵiri ndi mita imodzi ndi theka ndipo inali ndi mabulangeti oŵerengeka ndi thabwa logonapo. Munalibe zowunikira. Ndinawunikira pa zomwe ndingamchitire Yehova mu mkhalidwe umene ndinali. Pamene ndinadzuka, ndinapeza kuti munalibiretu zenera ling’ono loloŵetsa kuwala kwa tsiku. Kwa kota la ola tsiku lirilonse, ndinaloledwa kutuluka kunja kukasamba, kuperekedwa ku chosambira ndi sajenti wonyamula mfuti yaing’ono, kutsagana ndi asilikali aŵiri okhala ndi mfuti. Anali kundichita monga mpandu wowopsya!

Asilikali osiyanasiyana anandibweretsera chakudya. Iwo anazizwitsidwa ndi kaimidwe kanga, ndipo ichi chinandipatsa mwaŵi wa kumchitira chinachake Yehova. Ndinapereka umboni wabwino, ndipo posakhalitsa ena a iwo anandilezera mtima ndipo anandipatsa machisa, makandulu, ndiponso chakudya chowonjezereka. Poyambapo Baibulo langa linali linalandidwa, koma ndiyamikira ofisala, yemwe analibweza ilo. Ndinayamikira chotani nanga kuŵerenga mawu ake a mtengo wake ndi kuwala kwa kandulu!

Pambuyo pake ndinasamutsidwira ku ndende yankhondo yomwe kulibekonso, pa rue du Cherche-Midi, mu Paris. Ndinabindikiritsidwa, chotero ndinakhala ndi nthaŵi yochuluka ya kusinkhasinkha pa mkhalidwe wanga.

Ndinali ndi zaka 27 ndipo ndinali nditatumikira Yehova nthaŵi yonse kwa zaka ziŵiri. Banja langa linakumana choyamba ndi Mboni za Yehova kupyolera mu kuwulutsa kwa pa Radio Vitus, siteshoni yamseri mu Paris. Mmenemo munali mu 1933. Ndinatenga kaimidwe kanga ka chowonadi mu 1935, pambuyo pa kumaliza utumiki wa nkhondo wokakamizidwa. Ndinabatizidwa mu Lucerne, Switzerland, mu August 1936.

Makolo anga, mbale wanga, mlongo wanga, ndi ine tinali kusonkhana ndi mpingo womwe unalimo wokha mu Paris. Mbale Knecht, yemwe panthaŵiyo anali kuyang’anira ntchito mu Falansa, ankalimbikitsa Mboni zachichepere kuloŵa mu utumiki wa nthaŵi zonse. Monga chotulukapo, mu April 1938, mbale wanga, mlongo wanga, ndi ine tinasankha kukhala apainiya, kapena aminisitala a nthaŵi zonse. Gawo lathu linali Auxerre, tauni yokhala pa mtunda wa chifupifupi makilomita 154 kum’mwera cha kum’mawa kwa Paris. Mlongo wanga Jeannette anachitira umboni m’taunimo, ndipo mbale wanga Marcel ndi ine tinatchova njinga kupita ku midzi yozungulira mkati mwa mtunda wa chifupifupi makilomita 30 mbali zonse. Kalelo ntchito yolalikira inkachitidwa kwakukulukulu mwa kugaŵira mabukhu a Baibulo, popanda kupanga maulendo obwereza. Ndidakakumbukirabe mmene ichi chinandiipira.

Mu June 1938 ndinaitanidwa kukagwira ntchito pa ofesi ya Watch Tower Society mu Paris. Pa nthaŵiyo ogwira ntchitowo, kapena banja la Beteli, mu Falansa linapangidwa ndi chifupifupi ziŵalo khumi, ndipo ndinagaŵiridwa kuthandiza mu Dipatimenti Yotumiza Mabukhu. Ndinkagwira ntchito kumeneku pamene ndinaitanidwa kaamba ka utumiki wankhondo ndi kulandira “gawo latsopano.”

Gawo Langa Latsopano​—Ndende

Kuyambira pachiyambi ndinazindikira kuti ngati sindinafune njira zomchitira chinachake​—mosasamala kanthu kuti nchochepa motani​—Yehova pamene ndinali m’ndende, chikhulupiriro changa chikafooka mwamsanga. Koma posapita nthaŵi ndinali wokhoza kupanga mwaŵi wa kulankhula za chowonadi cha Mawu a Mulungu. Patangopita milungu yoŵerengeka pambuyo pa kufika kwanga pa ndende ya Cherche-Midi, ndinasamutsidwira ku chipinda chokhala ndi andende ena. Kumeneko ndinakumana ndi wophunzira lamulo yemwe anaikidwa m’ndende chifukwa chobwerera mochedwa kuchokera ku tchuthi chake cha nkhondo. Munalinso wophunzira maphunziro aumulungu Wachikatolika yemwe anaikidwa m’ndende chifukwa cha kuba. Atatufe tinasangalala ndi kukambitsirana kotalikira kwa chowonadi cha Baibulo.

Tsiku lina ndinawona wandende ali yekha pa ngodya ya bwalo. Pamene ndinamfikira, ndinawona kuti anali kuŵerenga. Ndinalankhula kwa iye. Iye anatembenuka ndi kundisonyeza Baibulo lake. Tangolingalirani! Iye anali mmodzi wa Mboni za Yehova! Anali wa mbadwa Yachipolish, wotchedwa Ceglarski, ndipo mofanana ndi ine, anali m’ndende chifukwa cha uchete wake. Pomalizira pake ndinapeza bwenzi Lachikristu! Mungalingalire mmene aŵirife tinasangalalira. Tsopano tikanatha kusangalala ndi maola ochulukira a kukambitsirana komangirira.

M’ndende mmenemu tinali kuloledwa kuyenda pabwalo kwa maola angapo pa tsiku, chotero ndinakhoza kulankhula ndi andende angapo omwe anasangalala kumva uthenga wa Baibulo. Nthaŵi zina ngakhale ena a alondawo anagwirizana nafe m’kukambitsiranako. Ndinali nditapeza chomchitira Yehova. M’chenicheni, ndende inakhala gawo langa latsopano lolalikiramo, ndipo tsopano ndinali kuchita maola a upainiya, ngakhale kuti sindinali kuwachitira ripoti. Komabe chimenecho sichinandivutitse.

Kutuluka

Miyezi inapita popanda zochitika zenizeni​—yotchedwa Nkhondo Yachinyengo. Koma iyi inatha mu May 1940, pamene Ajeremani aawukira Falansa. Mu June akuluakulu Achifalansa anasamutsa andende onse a mu Paris chifukwa cha magulu ankhondo Achijeremani omayandikira. Tinalongedwa m’magalimoto aakulu ankhondo ndi kutengedwa kupita ku Orleans, tauni yomwe inali pa mtunda wa makilomita oposa 100 kum’mwera kwa Paris. Pambuyo pa kupuma kwa kanthaŵi kochepa, ponse paŵiri andende wamba ndi ankhondo anaikidwa pamodzi ndi kulangizidwa kupitiriza kuyenda pansi kulinga kum’mwera cha kum’mawa m’mphepete mwa gombe la kumpoto kwa mtsinje wa Loire. Alonda okhala ndi zida anali kuyang’anira gululo. Ulendowo unali wovuta mkati mwa kutentha kwa dzuŵa la June.

Pakati pathu panali apandu, ndipo alondawo analandira malangizo a kuwombera mfuti aliyense amene anaima, kugwa, kapena sanali wokhoza kupitiriza kuyenda. Pa tsiku lachitatu, Mbale Ceglarski anayamba kudwala sunstroke. Kumuleka iye kukanatanthauza imfa. Alondawo anandilola, limodzi ndi thandizo la andende ena kumuika iye m’bulangeti, ndipo tinamunyamula. Tsiku lotsatira anamvako bwino ndipo anali wokhoza kupitiriza kuyenda pansi.

Tisanafike pa Briare, tauni yaing’ono yokhala ku gombe la kumpoto kwa Loire, gulu lathu linakumana ndi unyinji wa anthu olemedwa ndi zochulukira za zinthu zawo zimene ananyamula kapena kuzikoka m’ngolo. Iwo anali kuthaŵira kum’mwera kuthaŵa magulu ankhondo Achijeremani omayandikira. Tinali okhoza kuzindikira ku mlingo winawake kutuluka kwa anthu wamba popeza kuti zikwi zikwi zinali kuthaŵa kupulumutsa miyoyo yawo.

Kenaka tinapeza kuti alonda athu anasoŵa, ndipo tinali tokha. Kodi nchiyani chomwe tikachita tsopano? Chinali chosatheka kuwoloka mtsinje wautali wa Loire ndi kupitiriza ulendo wathu kulinga kum’mwera chifukwa chakuti maulalo onse anali ataphwanyidwa. Gulu lathu laling’ono (lopangidwa ndi Mbale Ceglarski, andende ena aŵiri, ndi ine) tinasankha kubwerera ku Paris.

Tinapeza akavalo ena osiyidwa, ndipo tinawakwera iwo monga mmene tikathera. Ndinali nditavulala pa bondo ndipo ndinkalephera kupinda mwendo wanga, chotero mabwenzi anga anandithandiza ine kukwera pamsana pa kavaloyo. Kenaka tinapeza kuti kavalo wanga anali kutsimphinanso! Chotero kayendedwe kanali kochedwerako pamene kavalo wanga anali kutsimphina. Chikhalirechobe, ulendo wathu unatha mwadzidzidzi. Tinali titangoyenda kokha makilomita oŵerengeka pamene tinakumana mwachindunji ndi gulu lankhondo Lachijeremani lopatuka ku gulu lalikulu, ndipo mpolisi wachisilikali anatilamulira kutsika. Zonse zomwe tinakhoza zinali kusintha alonda!

Wandende Wankhondo

Mwamsanga pambuyo pa kugwidwa kwathu, Mbale Ceglarski ndi ine tinapatulidwa, ndipo iye anakhalabe wandende wa Ajeremani kufikira mapeto a nkhondo. Pamapeto pa miyezi yoŵerengeka m’ndende pa malo ankhondo a Joigny, pakati pa Falansa, ndinathamangitsidwira ku Stettin, doko lomwe kale linkatchedwa East Prussia. Ilo tsopano liri doko Lachipolish la Szczecin.

Popeza kuti ndinali m’ndende ya nkhondo Yachifalansa mu imene Ajeremani anandigwira, ndinaikidwa m’msasa wandende wankhondo, kumene mikhalidwe sinali yoipa monga mmene inaliri m’misasa yachibalo. Msasawo unali malo okonzeramo ndege wokhala ndi andende 500, oyang’aniridwa ndi alonda okhala ndi zida. Andendewo anali kugwira ntchito zosiyanasiyana mu mzinda mkati mwa tsiku ndipo anali kubwezedwa ku msasawo madzulo. Chotero kodi ndimotani mmene ndikapezera chomchitira Yehova, pamene anthu onsewo anali kunja tsiku lonse?

M’malo okonzera ndegewo, munali bolodi lalikulu pamene chidziŵitso chikanaikidwa, ndipo ndinapempha chilolezo cha kugwiritsira ntchito malo aang’ono pa bolodilo. Ndinapeza pepala, ndipo pambuyo pa kulisalaza ilo bwino lomwe, ndinalembapo malemba aafupi angapo pa nkhani za Baibulo. Pansi pake, ndinalongosola kumene ndikapezeka ndi nthaŵi imene aliyense wokondweretsedwa mu uthenga wa Ufumu wa Mulungu akanabwera ndi kundiwona.

Kulalikira kwa Anthu Onse

Njira imeneyi inabweretsa zotulukapo zabwino. Posapita nthaŵi ndinali wokhoza kupangitsa misonkhano iŵiri madzulo aliwonse yokhala ndi asanu ndi mmodzi, asanu ndi atatu, ndipo nthaŵi zina ngakhale khumi opezekapo. Kukambitsirana kwathu kaŵirikaŵiri kunatha mu ola limodzi kapena ochulukirapo, kudalira pa mafunso omwe anafunsidwa. Kwa nthaŵi ndi nthaŵi, mlonda Wachijeremani wolankhula Chifalansa ankagwirizana nafe.

Popeza kuti ndinali ndi Baibulo limodzi lokha, ndinalembera ku Red Cross mu Geneva, kuwapempha iwo kunditumizira Mabaibulo ochulukira monga momwe ankanathera. Nthaŵi inapita, koma pomalizira pake ndinalandira mtokoma wanga woyamba wa Mabaibulo akale. Tsiku lina ndinawuzidwa kupita ku ofesi ya msasawo chifukwa chakuti mlendo, woimira wa Red Cross, anafuna kundiwona. Zinachitika kuti iye anali minisitala Wachiprotesitanti. Iye adaganiza kuti ndinalinso m’Protesitanti. Iye anakhumudwitsidwa pamene anadziŵa kuti ndinali mmodzi wa Mboni za Yehova!

Komabe, iye anali wachifundo ndipo anandiyamikiradi chifukwa cha zomwe ndinkachita. Ananditsimikizira kuti ndingapitirize kuoda Mabaibulo ndipo ndidzawalandira iwo. Izi zinalidi zowona. Chotero, ndinali wokhoza kugaŵira chifupifupi Mabaibulo 300 mkati mwa nthaŵi yomwe ndinakhala mumsasawo. Pamapeto pa nkhondo, chinali chosangalatsa chotani nanga kudziŵa kuti wandende Wachibelgian wotchedwa Wattiaux, yemwe ndinamuchitirako umboni mumsasa wa Stettin, anatenga kaimidwe kake kaamba ka chowonadi!

Mkati mwa kugwidwa kwanga mu Jeremani, ndinali ndi mwaŵi wa kulandira mitokoma ya zakudya kuchokera ku banja langa. Mwamsanga ndinapeza kuti mtokoma uliwonse unabisanso unyinji wa chakudya chauzimu cha mtengo wake. Mlongo wanga analemba pa taipi nkhani zochokera mu Nsanja ya Olonda pa pepala lopsyapsyala kwenikweni ndi kubisa izo m’mapaketi a makaroni. Alondawo sanazitulukire konse izo. Ndinalandiradi kope la bukhu lakuti Children mu mtokoma wa chakudya. Ilo linatsimikizira kukhala lothandiza koposa mu utumiki wanga.

Kufutukula Utumiki Wanga

Pokhala makanika, m’kupita kwa nthaŵi ndinagaŵiridwa kugwira ntchito pa garaji yokonza matalakitala. Chifupifupi Ajeremani 20, ochulukira a iwo omwe anali okalamba osakhoza kulembedwa ntchito mu utumiki wa nkhondo, anali kugwira ntchito kumeneko. Chotero ndinapanga zoyesayesa kuphunzira Chijeremani pang’ono. Chikhumbo changa cha mtima wonse chinali kufutukula utumiki wanga kuti usalekezerenso ku kulalikira kwa andende olankhula Chifalansa okha.

Komabe, ndinayenera kuchita mochenjera, chifukwa chakuti antchito Achijeremani anali kuwopa kulongosola malingaliro awo mwapoyera. Chotero ndinalankhula kwa iwo mmodzi ndi mmodzi. Mwachisawawa, iwo analidziŵadi Baibulo ndipo anamva za Mboni za Yehova. Ena anadziŵadi kuti Mboni zambiri zinatumizidwa ku misasa yachibalo.

Tsiku lirilonse mu garajimo, ndinkapanga maulendo kulankhula kwa antchito anzanga ponena za chowonadi. Ena anali osonyeza chiyanjo kulinga ku uthengawo, koma osati mwamuna yemwe anali woyang’anira. Mosakaikira ndinachita mopambanitsa pamene ndinalemba Jehovas Zeugen (Mboni za Yehova) pa benchi lake logwirirapo ntchito kumthandiza iye kumvetsetsa amene ndinali. Mwamunayo anawoneka kukhala wamantha pamene anawona icho ndipo anafuta mwamsanga. Koma sanandipatse chilango. Pamene nthaŵi inapita, antchito ena anakhala aubwenzi. M’chenicheni, iwo anandibweretsera chakudya chochulukira kotero kuti ndinali wokhoza kugaŵana ndi andende ena kumsasako.

Yehova, Linga Lolimba

M’zaka zonsezi, ndaphunzira kuti tingamchitire chinachake Yehova ndi anthu anzathu, mosasamala kanthu za mmene mikhalidwe ingakhalire yovuta. Stettin inaphulitsidwa nthaŵi zingapo ndi magulu Ogwirizana. Tinayesera kubisala m’maenje okwiriridwa ndi matabwa ndi dothi. Izi zinapereka kokha chisungiko chachinyengo, popeza kuti unyinji wa andendewo anafera m’maenje amenewo. Mkati mwa kuwukira kochitidwa ndi ndege, nthaŵi zina ndinali kumva dzanja litandigwira mumdima, ndi kundileka mwamsanga kuwukirako kutatha. Sindinadziŵe konse yemwe anali. Mwachidziŵikire, andende ena anaganiza kuti ndinali ndi chitetezo chapadera chifukwa ndinalankhula ponena za Mulungu.

Mkati mwa kuwukira kumodzi kochitidwa ndi ndege, msasa wathu unatenthedwa kotheratu ndi mabomba amoto. Pamene tinatsala tokha m’makwalala a tauniyo, tinachitira umboni zochitika zambiri zowopsya. Anthu wamba ovutika ndi kupsya kosaneneka analumphira m’makwawa a Mtsinje wa Oder womwe unayenda kudutsa m’Stettin. Pamene minkhole yakupsya imeneyi inatuluka m’madzimo, phosphorus inapitirizabe kuwatentha iwo. Ambiri anafa.

Chifukwa cha kuyandikira kwa magulu ankhondo Achirussia, tinalamulidwa kuchoka mu Stettin ndi kupanga ulendo wathu kulinga kumadzulo ku Neubrandenburg ndipo kenaka kupita ku Güstrow. Titalenjekeka pamwamba pa talakitala yaikulu, tinayenda pamsewu kumene mizinga Yachisoviet inali kugwa kwa nthaŵi ndi nthaŵi. Pomalizira pake akasinja Achirussia anakumanizana nafe pa Güstrow. Magulu ankhondo opereka chiwopsyezo a ku Soviet anali olamulira a tauniyo kwa mlungu umodzi. Magulu ankhondo Achibritish anali kuyandikira, ndipo pamene anali kudikirira kaamba ka magulu ankhondowo kuti akumane, akuluakulu Achisoviet analekanitsa andende ankhondo ndi andende wamba. Iwo anasunga ena a andendewo ndi kubwezera otsalawo (kuphatikizapo ine) kwa Mabritish.

Amenewo ndiwo anali mapeto a loto lowopsyalo. Milungu yoŵerengeka pambuyo pake, ndinadzipeza inemwini ndiri pa pulatifomu ya malo oima sitima pa Gare du Nord mu Paris. Kunangocha kumene. Munali mkati mwa May 1945, ndipo ndinali nditabwereranso pomalizira, pambuyo pa miyezi 69 ya ukapolo.

Kupeza Zinthu Zowonjezereka Zomchitira Yehova

Mu 1946 Sosaite inandiitananso kutumikira pa Beteli, pa nthaŵiyo yokhala mu Montmorency, kunja kwa tauni kumpoto kwa Paris. Miyezi yoŵerengeka pambuyo pake, Mbale Paul Dossman ndi ine tinagaŵiridwa kuchezera mipingo mu Falansa monga oyang’anira amadera. Panthaŵiyo, munali Mboni 2,000 zokha m’dziko lonselo. Lerolino, zoposa zaka 40 pambuyo pake, pali ofalitsa oposa chikwi zana limodzi.

Pambuyo pake ndinaitanidwanso ku Beteli, pa nthaŵiyo yokhala m’malo okhala anthu a Paris. Mu 1949, pambuyo polimbikitsidwa ndi abale achimishonale aŵiri ochokera ku Ingalande, ndinayamba kuphunzira Chingelezi​—ndiyenera kuvomereza kuti, ndinazichita movutikiradi. Chaka chotsatira, ndinaitanidwa ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower.

Pamene ndinabwerera ku Falansa, ndinatumikira kwakanthaŵi m’ntchito yadera, ndipo kenaka Sosaite inandifunsa kutumikira monga m’mishonale mu Afirika. Pa nthaŵiyo, ndinali nditakwatira Titica, mlongo wa mbadwa Yachigriki. Tinakhala mu Senegal kwa zaka zisanu ndipo tinakhala ndi mwaŵi wa kuwona mpingo woyamba ukupangidwa mu Dakar. Chifukwa cha zovuta zaumoyo, tinakakamizika pambuyo pake kubwerera ku Falansa.

Tsopano ndiri m’chaka changa cha 50 mu utumiki wa nthaŵi zonse ndipo ndakhala ndi chisangalalo zaka zonsezi cha kuthandiza anthu oposa zana limodzi kutenga kaimidwe kawo kaamba ka chowonadi. Yehova wapitirizadi kukhala wabwino ndi wowoloŵa manja kwa ine. Ndaphunzira kuchokera ku zokumana nazo za moyo kuti mosasamala kanthu za mmene mkhalidwe wathu ungakhalire, nthaŵi zonse tingapeze njira ya kutamandira ndi kulemekezera Mulungu wathu, Yehova.

[Chithunzi patsamba 23]

Jean Queyroi ndi mkazi wake, Titica

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena