Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 10/15 tsamba 29
  • Chidziŵitso pa Nyuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziŵitso pa Nyuzi
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchinjiriza Chiŵaŵa
  • Chilengedwe Chonse Chopangidwa
  • Kugonana kwa Ofanana Ziŵalo ndi Akatolika
  • Kodi Akristu Ayenera Kuda Ochita Mathanyula?
    Galamukani!—1997
  • Umathanyula—Kodi Ngwoipa Kwambiridi?
    Galamukani!—1995
  • Kugonana kwa Ofanana Ziŵalo—Kodi Nchiyani Chimene Chiri Thayo la Atsogoleri Achipembedzo?
    Galamukani!—1989
  • Thambo Lathu Lodabwitsali—Kodi Linangokhalako Mwamwayi?
    Galamukani!—2000
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 10/15 tsamba 29

Chidziŵitso pa Nyuzi

Kuchinjiriza Chiŵaŵa

Poyang’ana pa kukwera kosalekeza kwa chiŵaŵa pakati pa amsinkhu wa zaka za pakati pa 13 ndi 19, magazine a American Health akusimba kuti “kumenyana ndi mabwenzi, am’kalasi imodzi ndi anansi kumapanga wakupha Na. 1 wa achichepere m’matauni ndiponso wakupha Na. 2 wa achichepere onse mu Amereka.”

Mwa kuyesayesa kulimbana ndi zikhoterero zachiŵaŵa zimenezi, bungwe lopereka uphungu la ku Boston likupereka kosi imene imakhozetsa ophunzira ake kuseŵera madrama aafupi olembedwa a chiŵaŵa. Mwa njira imeneyi, iwo “amayamba kuzindikira machitidwe ogwirizanitsidwa ndi chiŵaŵa” ndipo, akulongosola tero mtsogoleri wa programuyo, amakhala okhoza “kuwona machitidwe aukali amenewo mwa iwo eni.”

Ophunzirawo amaphunzira za kachitidwe kathupi kulinga ku mkwiyo, kuthamanga kowonjezereka kwa adrenaline yomwe imafooketsa kudziletsa, ndi phindu la kukambitsirana m’kuthetsa mkwiyo “thupi lonse lisanayambukiridwe.” Iwo amaphunzira kuti mwakufunsa mafunso ndi kulankhula mwabata ndi modziletsa, mkangano wowopsya ungapeŵedwe.

Ophunzira Baibulo azindikira kwa nthaŵi yaitali kuti chiŵaŵa chimabala chiŵaŵa ndi kuti, “mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Baibulo limatilangiza kuchokapo, pachiyambi penipeni, pamene tiyang’anizana ndi mkwiyo wothekera kutha moipa. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Chiyambi cha ndewu chifanana ndi kutsegulira madzi; tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.”​—Miyambo 17:14.

Chilengedwe Chonse Chopangidwa

Kumapeto kwa May akatswiri a zachilengedwe 200, kuphatikizapo opata mphotho ya Nobel oŵerengeka, anakumana mu Blois, Falansa. Msonkhano wotha mlungu umodzi unali wa kusekerera phwando la chaka cha 25 cha kupezedwa kwa ‘CP violation,” kulakwira malamulo kolingaliridwa kukhala kokhazikitsa kulinganiza kwabwino pakati pa zinthu zokhudzika ndi zosakhudzika.

Koma nthanthi imeneyi imapereka mavuto ochulukira monga omwe imathetsa. Kugwira mawu Profesa wa ku Soviet Andrei Linde, International Herald Tribune inasimba kuti: “Chodabwitsa,” iye anatero, “nchakuti kusagwirizana kumeneku kunatulutsa chilengedwe choikidwa kale mwadongosolo.” Atafunsidwa kaya “CP violation” inasonyeza chifuno chirichonse m’chilengedwe chonse, katswiri wa zam’mlengalenga Wachifalansa Jean Audouze ananena kuti: “Masiku ena ndimaganiza kuti inde, masiku ena ayi. Chilengedwe chonse sichiri cholingana. Ndipo chilengedwe chonse chiri chopangidwa. Ndipo zinthu ziŵiri zimenezi ziri zodabwitsa. Chilengedwe chonse sichiri chinthu chomwe chinakhalako mosalinganiza.”

Chilengedwe chonse sichinakhaleko mwangozi kapena mosalinganiza. Genesis 1:1 amati: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Chilengedwe chonse chiri cha dongosolo chifukwa chakuti Yehova, Mlengiyo, “sali Mulungu wachisokonezo,” koma Yemwe ntchito yake ndi “yangwiro.”​—1 Akorinto 14:33; Deuteronomo 32:4; yerekezani ndi Yesaya 40:26; 42:5.

Kugonana kwa Ofanana Ziŵalo ndi Akatolika

Papa mobwerezabwereza wanena kuti kaimidwe kalamulo ka Tchalitchi Chachikatolika pa mkhalidwe wa kugonana kwa ofanana ziŵalo kali kakuti iko kuli mkhalidwe woipa. Monga mmene akulongosolera, “chitaganya cha Akristu oyambirira ndithudi sichinali cholekelera.” Sabishopu Achikatolika onse ndi ansembe amene amavomereza zimenezi.

Kuchiyambi kwa 1989, bishopu Wachifalansa Jacques Gaillot ananena kuti iye anali kungobwereza mawu a Yesu pamene analemba kuti “ogonana ofanana ziŵalo akutitsogolera kuloŵa ufumu wa Mulungu.”

Komabe, chimene Bishopu Gaillot analephera kutchula chinali chakuti Yesu ankasonya kwa akazi achigololo olapa​—osati omachitabe chigololo​—kukhala awo okaloŵa Ufumu wa Mulungu motsogolera atsogoleri Achiyuda oipa a m’tsiku lake.​—Mateyu 21:28-32.

Mofananamo, wansembe Wachispanya José Ramón Carrasco posachedwapa analemba m’nyuzipepala ya Madrid El País kuti “Yesu Kristu sanavomereze konse ogonana ofanana ziŵalo. . . . Pamene analankhula za chikondi, ananena za chikondi cha mnansi ndipo sanalunjikitse kuti kaya anansiwo anafunika kukhala mwamuna kapena mkazi, kapena ndi mtundu wanji, mkhalidwe kapena njira yomukondera.”

Komabe, cholembera cha Baibulo chimasonyeza kuti Yesu sanasonye ku maunansi a kugonana kwa ofanana ziŵalo. M’fanizo lake la Msamariya Wabwino, iye analongosola chimene kwenikweni chikondi cha mnansi chinatanthauza kukhala, kusonyeza chikondwerero chopanda mpeni ku mphasa mu ubwino wa ena.​—Luka 10:29-37.

Baibulo limalongosola ponena za ochita kugonana kwa ofanana ziŵalo kuti: “Musanyengedwe; a makhalidwe oipa, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena ogonana ofanana ziŵalo . . . sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.”​—1 Akorinto 6:9-11, Revised Standard Version, matembenuzidwe Achikatolika.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena