Kodi Mungalikhulupirire Baibulo?
“NKOSALAKWIKA mpang’ono pomwe kunena kuti ngati mwakumana ndi winawake amene amanena kuti sakhulupirira m’chisinthiko, munthuyo ali mbuli, wopusa kapena wamisala.” Kodi ndimotani mmene mawu ameneŵa a katswiri wa zamoyo Richard Dawkins akukuyambukirirani? Ngati mumalikhulupirira Baibulo, mwachidziŵikire mumakhulupirira chilengedwe osati nthanthi ya chisinthiko. Kodi zimenezo zimatanthauza kuti, monga wokhulupirira Baibulo, ndinu mbuli, wopusa, kapena wamisala?
Lingaliraninso ndemanga iyi: “Akatswiri a Chipangano Chatsopano atsimikizira popanda chikaiko chirichonse kuti Yesu wa m’zolembera zoyambirira Zachikristu ku mlingo winawake ali nthano ya kulingalira Kwachikristu.” Mawu ameneŵa a mu The Weekend Australian analankhulidwa ndi Dr. Robert W. Funk, profesa wa pa yunivesite wa maphunziro achipembedzo ndiponso mkonzi wa mabukhu ambiri pa mamasulidwe achipembedzo.
Dr. Funk anayambitsa projekiti yodziŵika monga Jesus Seminar, gulu la akatswiri a Baibulo oposa zana limodzi amene onse pamodzi anasanthula mosamalitsa zonena za Yesu zolembedwa m’Baibulo. Pakati pa zinthu zina, iwo anamaliza kuti Pemphero la Ambuye silinapangidwe ndi Yesu; kuti Yesu sananene kuti ofatsa akalandira dziko lapansi kapena kuti opanga mtendere akatchedwa ana a Mulungu; ndikuti sananene kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira ine . . . sadzamwalira nthaŵi yonse.”—Yohane 11:25, 26; Mateyu 5:5, 9; 6:9, 10.
Ngakhale kuti zopeza zawo zingakudabwitseni, siziri zachilendo. Izo ziri zotulukapo za kusuliza Baibulo kwamakono, ndipo malingaliro ofananawo aphunzitsidwa m’maseminale achipembedzo kwa nthaŵi yaitali. Mwinamwake mwadzizoloŵeretsa kumva asayansi akupangitsa Baibulo kudzitsutsa. Koma tsopano pamene atsogoleri achipembedzo akaikira kuwona kwake kwa cholembedwa cha Baibulo, mungalingalire kaya ngati iri nthaŵi ya kupendanso kaimidwe kanu. Kodi nkwanzeru kukhulupirira Baibulo pamene mwachiwonekere anzeru ambiri m’mbali yachipembedzo sakutero?