Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 1/15 tsamba 32
  • Iye Anachititsidwa Chidwi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Iye Anachititsidwa Chidwi
  • Nsanja ya Olonda​—1990
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 1/15 tsamba 32

Iye Anachititsidwa Chidwi

Pamene ankayenda paulendo pa sitima ya m’mzinda ya New York chirimwe chatha, mkazi wina wachichepere anali kuŵerenga bukhu la Revelation​—Its Grand Climax At Hand! Mwamuna wokhala pafupi naye anawona bukhulo, ndipo pamene mkaziyo ankatsegula masamba, mwamunayo anachititsidwa chidwi ndi zithunzi zokongola. Iye anati: “Ha, bukhulo likuwonekadi lokondweretsa!”

“Inde, liridi tero,” anayankha tero mkaziyo. “Ilo limalongosola bukhu la Baibulo la Chibvumbulutso, mutu ndi mutu.”

“Kodi ndingapeze motani imodzi ya iwo?” mwamunayo anafuna kudziŵa.

“Kuchokera kwa Mboni za Yehova,” mkaziyo anayankha tero. Komano anapitirizabe nati: “Mudziŵa, kope iri ndiri nalo n’latsopano, ndipo liri pa $3 yokha, tero ndingakuloleni kulitenga.”

Iye mwamsanga anaturutsa ndalama mthumba lake ndi kulandira bukhulo. Nthaŵi imeneyo, sitimayo inaima, ndipo anafunikira kutuluka mofulumira.

Bukhu lochititsa chidwi limeneli lachikuto cholimba, la ukulu wa tsamba wofanana ndi magazine ino, limapereka kulingalira kwa vesi ndi vesi kwa bukhu lonse Labaibulo la Chibvumbulutso. Ilo limapereka kuzindikiridwa komvekera ndi kwanzeru kwa zirombo, njokayo, mkazi wachigololo wamkulu, ndi mbali zina zophiphiritsira za Chibvumbulutso. Mudzawona tanthauzo la tsiku lathu. Tumizani kaamba ka ilo.

Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la masamba 320 Revelation​—Its Grand Climax At Hand! Ndatsekeramo K60 (Zambia).

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena