Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 1/15 tsamba 25-31
  • Kudzipereka Kwaumulungu—Kopindulitsa Zinthu Zonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudzipereka Kwaumulungu—Kopindulitsa Zinthu Zonse
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Piątek w Poznaniu (Lachisanu mu Poznan)
  • Sobota w Chorzowie (Loŵeruka mu Chorzów)
  • Niedziela w Warszawie (Sande mu Warsaw)
  • Tikulandirani ku Misonkhano Yachigawo ya “Kudzipereka Kwaumulungu”
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Onjezerani Kudzipereka kwa Mulungu pa Chipiriro Chanu
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Wonjezerani Pachipiriro Chanu Kudzipereka Kwaumulungu
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Londolani Kudzipereka Kwaumulungu Monga Akristu Obatizidwa
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 1/15 tsamba 25-31

Kudzipereka Kwaumulungu​—Kopindulitsa Zinthu Zonse

MBONI ZA YEHOVA zimadziŵa kuti “kudzipereka kwaumulungu kupindula zinthu zonse” ndipo nkofunika kaamba ka kulambira kowona. (1 Timoteo 4:8, NW) Popanda iko, chipembedzo chimangokhala mwambo. Chotero “Kudzipereka Kwaumulungu” linali dzina loyenerera kaamba ka mpambo wawo wa misonkhano yachigawo imene inayamba June yapita.

Mu August, itatu ya misonkhano yoteroyo inachitidwira mu Poland m’chisangalalo choposadi. Iyo inachitika pambuyo pakuti Mboni za Yehova zapatsidwa kuzindikiridwa kwalamulo mu May. (Kaamba ka tsatanetsatane wonena za misonkhano ya ku Poland, onani Galamukani! ya December 22, 1989, Chingelezi.) Tiyeni tibwereremo mu programu ya msonkhano monga mmene inachitidwira mu Poland.

Piątek w Poznaniu (Lachisanu mu Poznan)

Polirira mkate ndi ufulu, anthu achiwawa 50,000 anaukira mu Poznan mu June 1956. Ichi chinatulukapo imfa 50 ndi kupangidwa kwa boma latsopano la Poland. Mosiyana kwenikweni, zaka 33 pambuyo pake, mumkhalidwe wozindikiridwa ndi mkate wauzimu wa mwana alilenji ndi ufulu Wachikristu, Akristu amtendere anakumana kumeneko kukamvetsera nkhani pa “Kutumikira Mulungu Wofuna Kudzipereka Kokwanira,” umene unali mutu wa Lachisanu. Chiŵerengero chapamwamba cha 40,442 anasonkhana kumeneko pa Sande.

Pambuyo pa nkhani yolonjera ya tcheyamani wa msonkhano ndi kufunsa anthu “Otsogoza Moyo Wokhala ndi Kudzipereka Kwaumulungu Kotheratu,” uphungu wopindulitsa unaperekedwa m’nkhani yakuti “Pewani Milomo Yovulaza.” Nchopepuka chotani nanga kuti nkhani wamba itembenuke kukhala miseche yovulaza! Ndipo miseche yovulaza ingatsogolere ku kuneneza kwakupha. Koma asanakambe za anthu ena, Akristu ofikapo, olakalaka kusungirira mtendere ndi umodzi, amadzifunsa mwanzeru iwo eni kuti: ‘Kodi Yesu akadanena zimenezi? Kodi nzofunika kunenedwa? Kodi zimenezi zidzamangirira? Kodi chifukwa changa nchiti chozisimbira?’

Chapadera ku misonkhanoyo mu Poland chinali nthaŵi yoikidwa pambali tsiku lirilonse kumvetsera ku maripoti operekedwa ndi Mboni zochokera m’maiko ena. Zokumana nazo zosimbidwa ndi nthumwi zoimira maiko 24 osiyanasiyana zinagogomezera chenicheni chakuti pali banja la mitundu yonse logwirizana mowonadi m’kuzindikira chenicheni chakuti “Yehova Amafuna Kudzipereka Kotheratu.” Popeza kuti Mulungu ali woyenerera kulandira kudzipereka koteroko, atumiki ake ayenera kukhala osagawanikana m’chikondi ndi kulambira. Chitsanzo cha Yesu chimasonyeza kuti sipayenera kukhala mitima iŵiri ponena za kudzipereka kotheratu.

Kudzipereka kwaumulungu kumaphatikiza chirichonse chimene timachita. Chotero, kukambitsirana kwa mbali zitatu kunachenjeza Akristu “Kupewa Kupanduka” m’zakudya ndi zakumwa, kavalidwe ndi kapesedwe, ndi zosangulutsa. Madyaidya ndi uchidakwa ziri mitundu ina ya umbombo imene imazimiriritsa nzeru zauzimu, kupangitsa mavuto aumoyo, kubweretsa makhalidwe oipa, ndi kutsogolera ku ngozi. Masitayelo akavalidwe onkitsa​—opanda chikatikati, okopa, achilendo, kapenadi ozizwitsa​—ayenera kupewedwa. Zovala zazikulu kwambiri, zosasamala mopambanitsa, kapena zothina nzosayenerera. Nsonga siiri kaya chovalacho nchafashoni, koma kaya chiri choyenerera kwa mtumiki wa Mulungu. Ndipo zosangulutsa zimene ziri zogwirizanitsidwa ndi kuwukira, chiwawa, mankhwala ogodomalitsa, kuchita ula, kapena chisembwere cha kugonana siziri za Akristu.​—Afilipi 1:27.

Lachisanu masana programu inayamba ndi nkhani yakuti “‘Kapolo Wokhulupirika’ ndi Bungwe Lake Lolamulira.” Pokhala ndi chidaliro m’chimvero cha zolengedwa zake zokhulupirika, Yehova amapatsa ulamuliro. Mwana wake naye amateronso. Kuchokera pakati pa atsatiri ake odzozedwa, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” iye wasankha oŵerengeka kutumikira monga bungwe lolamulira lowoneka ndi maso. (Mateyu 24:45) M’zaka za zana loyamba, gulu limeneli linapangidwa ndi atumwi ndi amuna achikulire ena angapo mu Yerusalemu.

M’nthawi zamakono Bungwe Lolamulira lazindikiridwa mwathithithi ndi ziwalo za alembi a Watch Tower Society ndi bungwe lake la otsogolera. Koma Bungwe Lolamulira limasiyana ndi chigwirizanocho chalamulo, monga mmene mlankhuli anasonyezera kuti: “Popeza kuti kukhalapo kwa chigwirizanocho kuli kwalamulo laboma kotheratu, chokhala ndi malikulu omangidwa pa dziko, icho chingathetsedwe ndi Kaisala, Boma.” Siziri tero ndi Bungwe Lolamulira, limene siliri chipangizo chalamulo laboma koma ziwalo zomwe “zaikidwa kupyolera mwa mzimu woyera pansi pa chitsogozo cha Yehova ndi Kristu.” Chotero, Bungwe Lolamulira limapitirizabe kugwira ntchito ndi kulandira chilikizo losayerekezeka la Mboni za Yehova dziko lonse.

Ku misonkhano ya ku Poland kunapezeka ziwalo 5 za Bungwe Lolamulira lomwe pali pano liri ndi amuna 12. Mmodzi wa iwo anapereka nkhani yaikulu yakuti, “Chifukwa Chimene Tiyenera Kuphunzira Chinsinsi Chopatulika cha Kudzipereka Kwaumulungu.” Mu iyo chinadziwidwa kuti chinsinsi cha kudzipereka kwaumulungu sichirinso chinsinsi, popeza kuti “chinadzakhala munthu Yesu.” Mlankhuli analongosola mbali zisanu ndi imodzi za chinsinsi chopatulika chimenechi chotchulidwa pa 1 Timoteo 3:16, ndi kunena kuti: “Chiyamikiro chathu cha chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu chiyenera kutitsogolera nthawi zonse kutsatira mapazi a Yesu mosamalitsa.”

Nkhani zosiirana ziŵiri zinachimveketsa kuti kudzipereka kwaumulungu kumafunikira kwa achichepere ndi achikulire mofananamo. Makolo ali ndi thayo la kupatsa ana awo cholowa chauzimu mwa kuwaphunzitsa kukulitsa nzeru yozindikira chabwino ndi choipa. Phunziro labanja lopindulitsa, kuphatikizapo kukambitsirana kotsimikiza kwa mavuto apaubwana, kuli kofunika. Nthawi zonse khalani ogalamuka ku zizindikiro zosonyeza ngozi, makolo afunikira kuchinjiriza ana ku mayanjano oipa, ngakhale mkati mwa mpingo.

Kumbali ina, ngati achichepere ati akhale ndi miyoyo yopindulitsa, ayenera kuyang’ana kwa Kristu, amene ‘anawasiira chitsanzo chotsatira mapazi ake mosamalitsa.’ (1 Petro 2:21) Moyenerera, iwo anafunsidwa kuti: “Ngati munaleredwa m’chowonadi, inu mumadziŵa zimene mumakhulupirira, koma kodi mumadziŵa chifukwa chake?” Iwo analimbikitsidwa kupanga chowonadi kukhala chawochawo mwa kudzitsimikizira iwo eni kuti Baibulo ndilo Mawu a Mulungu ndikuti Mboni za Yehova ziridi ndi chowonadi.

M’maiko ambiri nkhani imeneyi inatha ndi kutulutsidwa kwa bukhu la masamba 320 lotchedwa Questions Young People Ask​—Answers That Work. (Chonde onani bokosi lotsaganalo, “‘Mphatso Yochokera kwa Yehova’ kaamba ka Achichepere.”) Chikuyembekezeredwa kuti achichepere mu Poland ndi maiko ena a ku Eastern Europe nthawi ina adzakhalanso okhoza kupindula kuchokera mu uphungu wabwino umene bukhu limeneli liri nawo mwa kuliŵerenga m’chinenero cha kwawo.

Sobota w Chorzowie (Loŵeruka mu Chorzów)

Chorzów ali malo apakati a maindasitale m’kati mwa dera lokumbamo malasha la kumwera kwa Poland. Migodi yamalasha ya Silesia yakhala phindu la zachuma ku deralo. Koma nkhani yokambirana yaikulu pakati pa anthu 65,710 pa Slaski Stadium, August yatha inali phindu la mtundu wokulirapo.

“Kudzipereka Kwaumulungu Kumatanthauza Phindu Lalikulu,” mutu wa Loŵeruka, unadzalongosoledwa ndi mlankhuli woyamba m’gawo lamasana. (1 Timoteo 6:6) Kuwona kwake kwa mawu a mlankhuli kunatsimikiziridwa ndi kufunsa anthu amene anapeza phindu lokulira m’miyoyo yawo mwa kulondola kudzipereka kwaumulungu.

Mkati mwa programu ya mmawa, mapindu a kulondola kudzipereka kwaumulungu anagogomezeredwa mu nkhani yosiirana. “Mwa Kuŵerenga Mokhazikika [Mawu a Mulungu] ndi Kuzindikira,” kufika patanthauzo la chimene tikuŵerenga, ndi kulingalira mwa pemphero mmene tingagwiritsire ntchito zimene timaphunzira, ife monga Akristu timakhala okhoza kulondola kudzipereka kwaumulungu “Mwa Kulola Kuwala Kwathu Kuwunika Nthawi Zonse.” (Yoswa 1:8) Chinadziŵidwa kuti ngati aliyense wa Mboni za Yehova kupyola dziko lonse akathera mphindi 15 patsiku akulankhula kwa ena mwamwaŵi, maola owonjezereka 327 miliyoni akatheredwa chaka chirichonse m’ntchito yolalikira Ufumu.

Kudzipereka kwaumulungu kumalondoledwanso “Mwa Kutsutsa Chiyeso.” Zinthu zonga zakudya, zakumwa, kugonana, kapena ndalama, ngakhale kuti sizoipa mwa izo zokha, zingakhale zoipa pansi pa mikhalidwe yosalondola. Njira yochinjirizira ndiyo kupewa kudziwunikira mosayenerera inu eni ku kukondetsa chuma kwa kudziko, zithunzi zamaliseche, mankhwala ogodomalitsa, ndi uchidakwa, limodzinso ndi kudzitanganitsa ndi zosangulutsa, zonga ngati nyimbo, maseŵera, ndi zochitachita za mayanjano. Pemphero n’lofunika koposa. Akristu afunikira kuphunzira kuda zimene ziri zoipa. Ichi nchoyenerera, popeza kuti mlankhuli wotsatira analoza kuti akayenera “Kusakhalanso Kaamba ka Chifuniro cha Munthu koma cha Mulungu.”

Anthu owonjezerekawonjezereka akusankhapo kuchitadi tero. Ichi chinawonekera pamene Mboni zatsopano 2,663 zinasonyeza poyera kugamulapo kwawo kwa “Kulondola Kudzipereka Kwaumulungu monga Akristu Odzipereka, Obatizidwa.” (Pa misonkhano yonse itatu mu Poland, opita ku ubatizo anafika ku chiwonkhetso cha 6,093.) Kuti asungirire chisangalalo mu utumiki wa Yehova, omwe anali pafupi kubatizidwa analimbikitsidwa kusinkhasinkha pa zifukwa zambiri zokhalira achisangalalo: Ubwenzi ndi Yehova, ubale wawo wa dziko lonse, ndi chiyembekezo cha moyo mu Paradaiso.

Chigonjero Chachikristu chinadzakambitsiridwa m’nkhani yakuti “Kuwonetsa Machitidwe a Kudzipereka Kwaumulungu​—Monga Amuna Pansi pa Umutu wa Kristu.” Amuna ochita kudzipereka kwaumulungu adzasamalira ntchito za banja m’njira yachikondi, Yachikristu. “Monga Akazi Osonyeza Kugonjera Koyenera,” alongo athu Achikristu adzakhala ochilikiza, osasonkhezera mitu yabanja molakwika kapena kulola zikhoterero za malingaliro kuwapatutsa kusapanga zosankha zanzeru. “Monga Ana Omvera Makolo,” achichepere adzaphunzira kumvera, kuchitira ndemanga pa misonkhano, ndi kugawanamo mu utumiki Wachikristu.

Ndi uphungu wabwino chotani nanga! Komabe, ndi momvetsa chisoni chotani nanga mmene chipembedzo chonyenga chalepherera kupereka chitsogozo cholondola choterocho! Chifukwa cha ichi, icho chimayenerera kutsutsidwa mwamphamvu, komwe kunkadza mu nkhani yakuti “Kuvumbula ‘Munthu Wosayeruzika.’” Munthu wa chinsinsi ameneyu anazindikiritsidwa kukhala “‘munthu’ wokhalamo ambiri, atsogoleri achipembedzo onse a Dziko Lachikristu la mpatuko.” Pokhala otchuka m’kuzunza kwawo atumiki a Mulungu, atsogoleri achipembedzo tsopano agwirizana ndi “ampatuko amakono, omwe kale ankadzitcha Mboni, [koma amene] abwerera ku masanzi a chiphunzitso cha Dziko Lachikristu ndipo agwirizana ndi kuledzera kwauzimu kwa Babulo Wamkulu m’kumenya ndi kuwukira gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru la Yehova.” Kuwomba mmanja kunasonyeza chivomerezo pamene mlankhuli analengeza kuti: “Tidzapitirizabe kuvumbula Babulo Wamkulu ndi ‘munthu [wake] wosayeruzika.’”

Ichi chimafunikira kulimba mtima, makamaka panthaŵi imene, mogwirizana ndi M. G. Henschel, chiwalo cha Bungwe Lolamulira, anthu ambiri “akupandukira Mulungu ndi Mawu ake, Baibulo.” Ngakhale kuti “kulemekeza Baibulo lerolino kuli kochepera kuposa ndi kale lonse,” Baibulo laima nji m’nthaŵi za kuyesa. Mlankhuli anatsutsa kuti “palibe bukhu lotulutsidwa ndi anthu okha limene lingakhale lozindikira mwakuya chotero ndi lolondola mokhazikika chotero.” Iye analenegza kuti “Mboni za Yehova zimalola Mawu a Mulungu kupereka mphamvu m’miyoyo yawo [ndipo] ubale wa mitundu yonse wotulukapo wa Akristu enieni uli umboni wamphamvu wakuti Baibulo liri Mawu owuziridwa a Mulungu.” Tsikulo linafikira mapeto osangalatsa ndi chilengezo cha bukhu latsopano lakuti The Bible​—God’s Word or Man’s?, lotulutsidwa m’zinenero zingapo.

Niedziela w Warszawie (Sande mu Warsaw)

Ochezera Warsaw kaŵirikaŵiri amapita kukawona chokumbutsa chozindikiritsa malo a Warsaw Ghetto yotchuka, kumene Anazi anasungira mazana a zikwi za Ayuda okonzekeredwa kuthetsedwa m’nthawi ya Nkhondo Yadziko ya II. Komabe, lokhala kokha pa mtunda woyenda mphindi zowerengeka ndi galimoto, ndilo Bwalo Lamaseŵera la X-Lecia kumene anthu 60,366 anadzala pa August 13, kudzamva malingaliro pa mutu wa pa Sande wakuti “Kanizani Kupanda Umulungu ndipo Khalani Ndi Kudzipereka Kwaumulungu.”​—Tito 2:12, NW.

Kukhala ndi moyo wa kudzipereka mwaumulungu kumatsutsa kuwonetsera mzimu wodzidalira wakudziko. Drama ya moyo weniweni yakuti “Dzigonjetsereni Inu Eni kwa Yehova,” yoperekedwa m’njira yotenthetsa maganizo kwenikweni ya ku Poland, inagogomezera kusintha kofunika koposa kumene Akristu afunikira kupanga kuti apeze chivomerezo cha Mulungu.

Chiwalo cha Bungwe Lolamulira chinagwira mawu 1 Akorinto 8:6, limene limanena kuti: “Kwa ife kuli Mulungu Mmodzi Atate.” Iye anadziwitsa kuti chiphunzitso chachikulu cha Chikristu sindicho Utatu, monga mmene ambiri amanenera, koma kulemekezedwa kwa Yehova mwa Ufumu wake wokhala pansi pa Kristu. “Chiphunzitso cha Utatu ndicho kugwa kuchoka pa chowonadi, mpatuko wake,” iye analongosola tero. Chotero, anthu amene amatcha Mariya kukhala amai wa Mulungu ndi Nkhoswe pakati pa Mulungu ndi anthu “samakhala ndi Mulungu m’chidziŵitso cholongosoka.” (Aroma 1:28) Moyenerera, “kulambira Mulungu molondola kumatanthauza kutsutsa chiphunzitso cha Utatu.” Kuwomba mmanja kunalonjera kutulutsidwa kwa broshuwa ya masamba 32, Czy wierzyć w Trójcę? (Should You Believe in the Trinity?) Ndi chiwiya chabwino chotani nanga cha kuvumbulira chinyengo cha chiphunzitso chonyoza Mulungu chimenechi!

Chipulumutso sichinabwere kwa minkhole ya ku Warsaw Ghetto. Koma lonjezo la Mulungu, monga mmene linalongosoledwera mu nkhani ya Baibulo, n’lakuti “Chipulumutso [Chiri] Pafupi kaamba ka Anthu a Kudzipereka Kwaumulungu!” (2 Petro 2:9) Izi ziridi tero ngakhale kuti Akristu ali minkhole ya chiwawa chokhala ndi mbali ziŵiri​—cha tsiku ndi tsiku ndi chija cholunjikitsidwa kwa iwo m’njira ya chizunzo. Akumaitanira chisamaliro pa kudzisanthula kwaumwini, mlankhuli anagogomezera kuti “chipulumutso chiri kokha kwa awo amene ali anthu a kudzipereka kwaumulungu, amene kudzipereka kwawo kuli kwenikweni, awo amene chimvero chawo chiri chisonyezero cha chikhulupiriro.”

Pambuyo pa kukumbutsa komalizira kwakuti “Khalani Achangu Mumzimu,” msonkhano unamalizidwa ndi kuperekedwa kodzutsa maganizo kwa mutu wakuti “Kuphunzitsidwa Kwathu Kopitirizabe Ndi Kudzipereka Kwaumulungu Kuli Kopindulitsa.” Kenaka osonkhana anatsegula mabuku awo anyimbo atsopano a m’chinenero cha ku Poland, otulutsidwa kumene pa makina osindikizira milungu ingapo kumbuyoko, ndipo mogwirizana anapereka “Pemphero la Chiyamikiro” m’njira ya nyimbo 45.

Pempherro lotsekera lapamtima linatsatira, ndipo kenaka phokoso la kuwomba mmanja linamveka pa Warsaw, Poznan, ndi Chorzów. Mu Warsaw kuwomba mmanja kwamphamvu kwa manja makumi a zikwi kunamvekera mosalekeza kwa mphindi 11. Palibe amene anafuna kuchokapo, ndipo kuwomba mmanja koturukapoko, kolongosoladi kukwezeka kwa khamu lalikululi la Mboni, mwa amene zikwi zambiri ankapezeka pa msonkhano wawo woyamba wa masiku atatu, kunalidi kozindikiritsa mwakuya chiyamikiro chawo kwa Yehova ndi gulu lake. Kunali ngati kuyankha ku Salmo 47:1, 2: “Ombani m’manja, mitundu yonse ya anthu; fuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuyimbitsa. Pakuti Yehova Wam’mwambamwamba ndiye woopsa; ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi.” Pamene chimodzi cha zochitika zokulira m’mbiri yamakono ya Mboni za Yehova chinafika kumapeto ake, abale ofunitsitsa amenewo anakonzekera kuyenda kubwerera kwao, mitima yawo ikumasefukira ndi chimwemwe ali ogamulapo kuwonjezera kuchitira umboni kokulira kwa Ufumu mogwirizana ndi chitsanzo cha mtengo wapatali cha Yesu cha kudzipereka kwaumulungu.

[Bokosi patsamba 27]

Zotulutsidwa Zatsopano zifulumiza ku ‘Machitidwe a Kudzipereka Kwaumulungu’

Bukhu latsopano lakuti The Bible​—God’s Word or Man’s? ndi broshuwa yakuti Should You Believe in the Trinity? onsewo anadzutsa zisonyezero zambiri za chiyamikiro. Mlongo wina akulemba ponena za broshuwa ya Trinity kuti: “Ndazizwitsidwa, kusangalatsidwa, ndi kukondweretsedwa nayo. Ndikuyamikani kaamba ka nthawi yokulira, nyonga, ndi ntchito imene inachitidwa posindikiza bukhu labwinoli.”

Mlongo winanso analemba ponena za bukhu lakuti The Bible​—God’s Word or Man’s kuti: “Ndifuna kukuyamikani kuchokera kunsi kwa mtima wanga kaamba ka bukhuli labwino koposa. Sindidziŵa, kodi mumaganizapo za ntchito ya luso koposa limene ilo liri? Kaŵirikaŵiri ndimachonga mawu ofunika. Koma mwandichita nazo popeza kuti liwu lirilonse ndilofunika. Ndangomaliza kumene mutu 5, komabe ndiyenera kunena kuti zikomo.”

[Bokosi patsamba 30]

‘Mphatso Yochokera kwa Yehova’ kaamba ka Achichepere

Mbali yapadera pa misonkhano mu United States ndi maiko ena ambiri inali chigawo cha pa Lachisanu masana, pamene achichepere a msinkhu wa zaka zapakati pa 10 ndi 19 anapemphedwa kukhala m’chigawo chopatulidwa. Pambuyo pa mpambo wa nkhani zapadera, aliyense anapatsidwa kope laulere la bukhu latsopano lotchedwa Questions Young People Ask​—Answers That Work. Padziko lonse, makope 8,840,000 anatulutsidwa m’zinenero 21, ndipo makalata a chiyamikiro mazanamazana akhala akulandilidwa!

“Pa misonkhano ya nthawi yapita, pakhala nkhani zoperekedwa kwa achichepere,” analemba tero wa zaka zapati pa 13 ndi 19, “koma chiyambukiro cha kutikhazika pamodzi tonsefe chinali chabwino koposa.” Akulembanso wachichepere wina kuti: “Ndidakhaladi m’chigawo cha achichepere. Ndinalimbikitsidwa kwenikweni ndi chimenechi kotero kuti, chiyambire pamenepo, ndakhala ndikulemba nsonga pa misonkhano, kuphunzira mowonjezereka, ndi kuthira ndemanga. Ndikuganizira za kubatizidwa m’dzinja lomwe likudzalo.”

Kwa achichepere ambiri, chokumana nachochi chinali chochitika cha m’mbiri. “Pamene mlankhuli analengeza kuti tinafunikira kukhala m’chigawo chapadera,” akukumbukira tero m’tsikana wachichepere, “ndinadziwa kuti chinachake chabwino koposa chidzachitika. Pamene analengeza kutulutsidwa kwa bukhuli, ndinadzimva wachimwemwe kwenikweni kotero kuti ndinafuna kulira. Ndinadziwa nthawi zonse kuti mumatisamalira achicheperefe, koma ichicho chinakuzamitsa iko mumtima mwanga. Bukhuli liri kokha chimene tinafunikira!”

“Linalembedwadi bwino,” akutero wachichepere wotchedwa Leah, “ndipo zithunzi ziri zenizeni ndipo zimakupangitsadi kuganiza.” Mabuku operekedwa pa msonkhano anali ndi uthenga wachidule wochokera ku Bungwe Lolamulira wolembedwa “Kwa Mboni za Yehova zachichepere zonse.” “Ndinakhudzidwa kwenikweni ndi chidziwitso chapadera chimenecho,” anatero Andreá wachichepere. “Kwa ine chimenecho ndikuchimva ngati wina wake amene Yehova wasankha kukhala naye kumwamba akumalankhuladi kwa ine!”

Ambiri anayamikiradi kuti bukhulo linaperekedwa monga mphatso. Kholo lina likukumbukira kuti: “Ndinagwetsa misozi. Abale, asanu a achichepere amenewo anali anga, a zaka za 11 kufika ku 16. Ndikanakhoza kugula mabuku aŵiri okha.” Wachichepere wotchedwa Mark akulemba kuti: “Ndinayamba kuwerengera unyinji umene unawonongedwa kuti mupatse kope kwa wachichepere aliyense, koma kenaka ndinazindikira kuti chitsogozo chimene chiri mkati mwake nchosakhoza kugulika ndi ndalama. Ngati bukhulo lithandiza wachichepere wopanduka mmodzi yekha kubwerera pa msewu wotsogolera ku moyo, kapena kuposapo, ngati lithandiza ambirife kukhalirira pa msewu umenewo, ilo linalidi loyenerera zotaikazo.”

Achichepere ambiri anayamba kupindula m’bukhuli kuchokera pompaja. “Ndinapezeka ku msonkhano wathu pa July 7-9,” akutero wachichepere wina, “ndipo podzafika pa Lolemba, July 10, ndinali nditalimaliza!” Winanso anati: “Mitu iŵiri yothera inandilimbikitsadi kuyamba kuwona moyo wanga mosamalitsa. Panthawi ina ndinafuna kubatizidwa koma ndinasintha maganizo anga. Tsopano pokhala nditalandira bukhuli labwino koposa, ndikuzindikira kuti ‘dziko likupita’ ndikuti ndifunikira kuchitapo kanthu tsopano lino.”

“Chifukwa chakuti nthawi zasintha,” analemba tero mtsikana wina wachichepere, “nthawi zonse ndinaganizira kuti achikulire sanadziwe mmene timadzimverera. Inu simudziwa mmene ndakhalira wachimwemwe podziwa kuti ndine wolakwa. Chisamaliro chanu pa ife achichepere chimandipangitsa kudzimva kuti ndimawerengeredwa.” Gulu la achichepere kuchokera ku Sweden linalemba kuti: “Tikudzimva kuti mumatimvetsetsa ife achichepere, ndipo tikudzimvanso oyandikana nanu koposa.”

Wachichepere wina anachiika bwino m’mawu aafupi pamene ananena kuti: “Ine ndi mbale wanga ndi mlongo tinakonda bukhulo. Tikudzimva kuti liri mphatso yochokera mwachindunji kwa Yehova.” Liri pemphero lathu kuti mphatsoyo idzapitirizabe kugwira ntchito kudalitsa achichepere owopa Mulungu!

[Tchati patsamba 29]

Kudzipereka Kwaumulungu kuli pa Kuwonjezeka mu Europe!

Chiŵerengero Chapamwamba cha Opezekapo Obatizidwa pa

Msonkhano

1979 1984 1989 1979 1984 1989

AUSTRIA 17,847 20,908 25,153 236 257 307

BELGIUM 23,185 28,456 30,622 234 248 429

BRITAIN 113,910 137,008 160,704 605 937 1,344

DENMARK 21,057 23,267 24,645 122 147 249

FINLAND 20,293 23,501 25,679 215 302 329

FRANCE 89,073 110,745 156,751 1,361 1,856 3,201

GERMANY 129,342 140,681 159,819 1,154 1,009 1,694

ITALY 117,163 169,328 240,041 2,515 3,769 6,295

LUXEMBOURG 1,141 1,327 3,131 8 12 61

NETHERLANDS 36,768 42,060 44,185 126 143 271

NORWAY 10,327 11,352 13,829 107 159 294

POLAND ​— 94,134a 166,518 ​— 3,140b 6,093

PORTUGAL 35,108 47,843 59,797 862 1,068 1,546

SPAIN 62,201 84,706 115,981 1,278 1,521 2,935

SWEDEN 21,286 25,204 30,943 279 323 410

SWITZERLAND 14,455 17,457 23,867 130 225 349

ZIWONKHETSO 713,156 977,977 1,281,665 9,232 15,116 25,807

[Mawu a M’munsi]

a Ziŵerengero za 1985

b Ziŵerengero za 1985

[Chithunzi patsamba 26]

Kutulutsidwa kwa broshuwa ya “Trinity” kunali magwero a chisangalalo mu Warsaw

[Chithunzi patsamba 31]

Mboni zodzipereka chatsopano mu Chorzów zikulondola kudzipereka kwaumulungu mwakubatizidwa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena