Londolani Kudzipereka Kwaumulungu Monga Akristu Obatizidwa
“Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, . . . tsata chilungamo, kudzipereka kwaumulungu.”—1 TIMOTEO 6:11, “NW.”
1. Kodi mungayankhe motani funso lakuti, Kodi ndiliti limene liri tsiku lofunika koposa m’moyo wanu? Kodi mwayankhiranji motero?
KODI ndiliti limene liri tsiku lofunika koposa m’moyo wanu? Ngati ndinu Mboni yobatizidwa ya Yehova, mosakaikira yankho lanu likakhala lakuti, ‘Ndithudi, tsiku limene ndinabatizidwa!’ Kunena zowonadi, ubatizo ulidi sitepe lofunika koposa m’moyo wanu. Uli chizindikiro chakunja chakuti mwapanga kudzipatulira kotheratu ndi kosasiyako kwa Yehova kuchita chifuniro chake. Ubatizo wanu umazindikiritsa tsiku la kuikidwa kwanu monga minisitala wa Mulungu Wam’mwambamwamba, Yehova.
2. (a) Kodi zingachitiridwe chitsanzo motani kuti ubatizo suli sitepe lomalizira limene mumatenga m’njira yanu Yachikristu? (b) Kodi ndi masitepe oyambirira ofunika otani amene munatenga musanabatizidwe?
2 Ngakhale ndi tero, kodi ubatizo uli sitepe lomalizira limene mumatenga m’njira yanu Yachikristu? Kutalitali! Kuti tichitire chitsanzo: M’maiko ambiri phwando la ukwati limazindikiritsa mapeto a nyengo ya kupanga mapulani ndi kukonzekera (ndipo kaŵirikaŵiri ya kutomerana). Pa nthaŵi imodzimodziyo, limazindikiritsa kuyambika kwa moyo pamodzi monga anthu okwatirana. Mofananamo, ubatizo wanu ndiwo pachimake pa nyengo ya kukonzekera mu imene munatenga masitepe ofunika angapo. Munapeza chidziŵitso cha Mulungu ndi Kristu. (Yohane 17:3) Munayamba kusonyeza chikhulupiriro mwa Yehova monga Mulungu wowona, mwa Kristu monga Mpulumutsi wanu, ndi m’Baibulo monga Mawu a Mulungu. (Machitidwe 4:12; 1 Atesalonika 2:13; Ahebri 11:6) Munasonyeza chikhulupiriro chimenecho mwa kulapa za njira yanu yakale ya kachitidwe ndi kutembenukira ku njira yolungama. (Machitidwe 3:19) Ndiyeno munapanga chosankha cha kudzipatulira inu eni kwa Yehova kuchita chifuniro chake. (Mateyu 16:24) Pomalizira pake, munabatizidwa.—Mateyu 28:19, 20.
3. (a) Kodi ndimotani mmene tingasonyezere kuti ubatizo wathu umazindikiritsa kuyambika kwa moyo wodzipatulira ku utumiki wa kwa Mulungu? (b) Kodi ndi mafunso otani amene amabuka, ndipo kodi nchifukwa ninji mayankhowo ayenera kukhala osangalatsa kwa ife?
3 Ngakhale ndi tero, ubatizo wanu suli mapeto koma chiyambi cha utumiki wopatulika wodzipatulira kwa Mulungu. Monga mmene katswiri wa Baibulo wina anadziŵitsira, moyo Wachikristu suyenera kukhala ‘kukangalika koyambirira kotsatiridwa ndi kukhwethemuka kosalekeza.’ Pamenepa, kodi ndimotani mmene mungasonyezere kuti kwa inu, ubatizo sumangoimira ‘kukangalika koyambirira’? Ziri mwa kulondola njira ya kudzipereka kwaumulungu kwa moyo wonse. Kodi kudzipereka kwaumulungu kumeneku nchiyani? Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kulondoledwa? Kodi ndimotani mmene mungakukulitsire mokwanira m’moyo wanu? Mayankhowo ayenera kukhala osangalatsa kwambiri kwa ife, popeza kuti tiyenera kukhala anthu ozindikiritsidwa ndi “machitidwe a kudzipereka kwaumulungu” ngati titi tidzapulumuke tsiku lomayandikira la chiweruzo cha Yehova.—2 Petro 3:11, 12, NW.
Tanthauzo la Kudzipereka Kwaumulungu
4. Kodi Paulo analangiza Timoteo kuchita chiyani, ndipo kodi nchiyani chimene chinali chowona ponena za Timoteo pa nthaŵiyi?
4 Nthaŵi ina pakati pa 61 ndi 64 C.E., mtumwi Paulo analemba kalata yake yoyamba yowuziridwa kwa wophunzira Wachikristu Timoteo. Pambuyo polongosola ngozi zimene chikondi cha ndalama chingatsogolereko, Paulo analemba kuti: “Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa zinthu izi. Koma tsata . . . kudzipereka kwaumulungu.” (1 Timoteo 6:9-11, NW) Mosangalatsa, pa nthaŵi imeneyi Timoteo n’kuti mwinamwake ali m’zaka zake za m’ma 30. Iye anali atayenda kale kwambiri ndi mtumwi Paulo ndipo adali atapatsidwa ulamuliro wa kuika oyang’anira ndi atumiki otumikira m’mipingo. (Machitidwe 16:3; 1 Timoteo 5:22) Komabe, Paulo analangiza Mkristu wachikulire, wodzipatulira ndi wobatizidwa ameneyu kulondola kudzipereka kwaumulungu.
5. Kodi mawu akuti “kudzipereka kwaumulungu” amatanthauzanji?
5 Kodi Paulo anatanthauzanji ndi mawu akuti “kudzipereka kwaumulungu”? Liwu loyambirira Lachigriki (eu·seʹbei·a) lingatembenuzidwe kutanthauza “waulemu wabwino.” Ponena za tanthauzo lake, timaŵerenga kuti: “Eusebeia limawoneka kamodzikamodzi m’lingaliro la kudzipereka kwaumwini kwa chipembedzo m’zolembedwa za m’nthawi yake . . . koma tanthauzo lake lofala la m’Chigriki cha nyengo Yachiroma linali ‘kukhulupirika.’ . . . Kwa Akristu eusebeia uli mtundu wapamwamba kwambiri wa kudzipereka kwa Mulungu.” (Christian Words, lolembedwa ndi Nigel Turner) Chotero monga mmene agwiritsiridwira ntchito m’Malemba, mawu akuti “kudzipereka kwaumulungu” amasonyeza ulemu kapena kudzipereka kokhala ndi kukhulupirika kwa Yehova Mulungu mwaumwini.
6. Kodi ndimotani mmene Mkristu amaperekera umboni wa kudzipereka kwake kwaumulungu?
6 Ngakhale ndi tero, kudzipereka kwaumulungu kumeneku sikuli kokha kudzimva kwa kulambira. Mongadi mmene “chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa,” momwemonso, kudzipereka kwaumulungu kuyenera kusonyezedwa m’moyo wa wina. (Yakobo 2:26) Mu New Testament Words, William Barclay analemba kuti: “Sikokha kuti [eu·seʹbei·a ndi mawu olingana nawo] amasonyeza kudzimva kwa mantha ndi ulemu, komanso amasonyeza kulambira kumene kumayenerera mantha amenewo, ndi moyo wa chimvero chachangu chimene chimayenera ulemuwo.” Eu·seʹbei·a imalongosoledwanso kukhala “kuzindikira kwenikweni kwa Mulungu m’mbali iriyonse ya moyo.” (The Second Epistle General of Peter and the General Epistle of Jude, lolembedwa ndi Michael Green) Pamenepa, Mkristu ayenera kupereka umboni wa kugwirizana kwake kwaumwini kwa Yehova mwa njira imene amatsogozera moyo wake.—1 Timoteo 2:2; 2 Petro 3:11.
Kuyesayesa Kwamphamvu Nkofunika
7. Kodi Paulo anatanthauzanji pamene anafulumiza Timoteo “kulondola” kudzipereka kwaumulungu ngakhale kuti anali wobatizidwa?
7 Ngakhale ndi tero, kodi nchiyani chimene chimaloŵetsedwamo m’kukulitsa ndi kusonyeza kudzipereka kwaumulungu? Kodi kuli kokha kubatizidwa? Kumbukirani kuti ngakhale kuti Timoteo anali wobatizidwa, anafulumizidwa “kulondola [m’chenicheni, ‘udzikulondola’]” iko.a (1 Timoteo 6:11, Kingdom Interlinear) Mwachidziŵikire, Paulo sanali kupereka lingaliro lakuti wophunzira Timoteo analibe kudzipereka kwaumulungu. M’malomwake, anali kugogomezera kwa iye kufunika kwa kupitiriza kukulondola ndi changu chowona mtima. (Yerekezerani ndi Afilipi 3:14.) Mwachiwonekere, kumeneku kunayenera kukhala kulondola kwa moyo wonse. Timoteo, mofanana ndi Akristu onse obatizidwa, angapange kupita patsogolo m’kusonyeza kudzipereka kwaumulungu.
8. Kodi Petro anasonyeza motani kuti kuyesayesa kwamphamvu kuli kofunika kwa Mkristu wodzipatulira, wobatizidwa wolondola kudzipereka kwaumulungu?
8 Kuyesayesa kwamphamvu nkofunika kwa Mkristu wodzipatulira, wobatizidwa kuti alondole kudzipereka kwaumulungu. Akumalembera Akristu obatizidwa amene anali ndi chiyembekezo cha ‘kukhala oyanjana nawo umulungu wake,’ mtumwi Petro anati: “Inde, kaamba ka chifukwa chimenechicho, mwa kuwonjezera kwanu molabadira kuyesayesa kwamphamphu konse, wonjezerani kuchikhulupiriro chanu ukoma, kuukoma wanu chidziŵitso, kuchidziŵitso chanu kudziletsa, kukudziletsa kwanu chipiriro, kuchipiriro chanu kudzipereka kwaumulungu.” (2 Petro 1:4-6, NW) Mwachidziŵikire, mlingo winawake wa chikhulupiriro ngwofunika kotero kuti tidzipereke kaamba ka ubatizo. Komabe, pambuyo pa ubatizo sitimafika kumathero, kudzikhutiritsa ife eni ndi Ukristu wapakamwa. M’malomwake, pamene tikupanga kupita patsogolo mu mkhalidwe Wachikristu, timafunikira kupitiriza kukulitsa mikhalidwe ina yabwino, kuphatikizapo kudzipereka kwaumulungu, kumene kungawonjezeredwe ku chikhulupiriro chathu. Petro akunena kuti zimenezi zimafunikira kuyesayesa kwathu kwamphamphu.
9. (a) Kodi ndimotani mmene liwu Lachigriki lotanthauza “kuwonjezera” limasonyezera ukulu wa kuyesayesa kofunika kukulitsa kudzipereka kwaumulungu? (b) Kodi Petro akutifulumiza kuchita chiyani?
9 Liwu Lachigriki limene Petro akugwiritsira ntchito kaamba ka “kuwonjezera” (e·pi·kho·re·geʹo) liri ndi chiyambi chosangalatsa ndipo limasonyeza ukulu wa kuyesayesa kofunika. Limachokera ku nauni yakuti (kho·re·gosʹ) imene kwenikweni imatanthauza “mtsogoleri wa gulu loimba.” Linalozera kwa winawake amene analipirira zowonongedwa za maphunziro ndi kusamalira gulu la oimba posonyeza seŵero. Anthu oterowo ankatenga thayolo mwaufulu chifukwa cha chikondi kaamba ka mzinda wawo ndipo analipirira zowonongedwazo ndi ndalama zawo. Kunali kunyada kwa anthu ameneŵa kuwononga mosasamala kuti apereke zonse zimene zinafunikira kaamba ka seŵero lolemekezeka. Liwulo linafikira kutanthauza “kuwonjezera, kupatsa mochulukira.” (Yerekezerani ndi 2 Petro 1:11.) Chotero Petro akutifulumiza kudziwonjezera kwa ife eni, osati kokha mlingo wa kudzipereka kwaumulungu, koma kusonyeza kokwanira kothekera kwa mkhalidwe wabwino umenewu.
10, 11. (a) Kodi nchifukwa ninji kuyesayesa kuli kofunikira kuti tikulitse ndi kusonyeza kudzipereka kwaumulungu? (b) Kodi ndimotani mmene tingapambanire kulimbanako?
10 Komabe, kodi nchifukwa ninji kuyesayesa koteroko kuli kofunika kuti tikulitse ndi kusonyeza kudzipereka kwaumulungu? Choyamba, pali kulimbana ndi thupi lochimwa. Popeza kuti “ndingaliro ya mtima wa munthu iri yoipa kuyambira pa unyamata wake,” sizopepuka kulondola moyo wa chimvero chachangu kwa Mulungu. (Genesis 8:21; Aroma 7:21-23) “Ndipo onse akufuna kukhala ndi kudzipereka kwaumulungu m’moyo ndi Kristu Yesu adzazunzidwa,” akutero mtumwi Paulo. (2 Timoteo 3:12, NW) Inde, Mkristu amene akukalimira kukhala ndi moyo m’njira imene imakondweretsa Mulungu ayenera kukhala wosiyana ndi dziko. Iye ali ndi miyezo yosiyana ya makhalidwe ndi zonulirapo zosiyana. Monga mmene Yesu anachenjezera, zimenezi zimadzutsa chidani cha dziko loipa.—Yohane 15:19; 1 Petro 4:4.
11 Mosasamala kanthu za izo, tingapambane kulimbanako, popeza kuti “Yehova amadziŵa kulanditsa anthu odzipereka mwaumulungu ku chiyeso.” (2 Petro 2:9, NW) Komabe, nafenso tiyenera kuchita mbali yathu mwakupitirizabe kulondola kudzipereka kwaumulungu.
Kukulitsa Kudzipereka Kwaumulungu
12. Kodi ndimotani mmene Petro akusonyezera zimene zikufunika kuti tikulitse kudzipereka kwaumulungu ku mlingo wokwanira?
12 Pamenepa, kodi ndimotani mmene mungakulitsire kudzipereka kwaumulungu kumeneku ku mlingo wokwanira? Mtumwi Petro akupereka mfungulo. Pa 2 Petro 1:5, 6, pondandalitsa mikhalidwe imene iyenera kuwonjezeredwa ku chikhulupiriro chathu, iye akundandalitsa chidziŵitso poyamba ndiyeno kudzipereka kwaumulungu. Poyambapo m’chaputala chimodzimodzicho, iye analemba kuti: “Mphamvu yake yaumulungu yatipatsa mwaulere zinthu zonse zimene zimakhudza moyo wa kudzipereka kwaumulungu, mwa chidziŵitso cholongosoka cha iye amene anatiitana.” (2 Petro 1:3, NW) Chotero Petro akugwirizanitsa kudzipereka kwaumulungu ndi chidziŵitso cholongosoka cha Yehova.
13. Kodi nchifukwa ninji chidziŵitso cholongosoka chiri chofunika m’kukulitsa kudzipereka kwaumulungu?
13 Kwenikwenidi, n’kosatheka kukulitsa kudzipereka kwaumulungu popanda chidziŵitso cholongosoka. Chifukwa ninji? Chabwino, kumbukirani kuti kudzipereka kwaumulungu nkolinga kwa Yehova mwaumwini ndipo kumasonyezedwa ndi njira imene timakhalira ndi miyoyo yathu. Chotero chidziŵitso cholongosoka cha Yehova nchofunika, popeza chimaloŵetsamo kumdziŵa iye mwaumwini, mwathithithi, kukhala wozoloŵerana kotheratu ndi mikhalidwe yake ndi njira zake. Kuposa apo, kumaloŵetsamo kukalimira kumtsanzira iye. (Aefeso 5:1) Ukulu umene timapita patsogolo kuphunzira ponena za Yehova ndi kusonyeza njira zake ndi mikhalidwe m’miyoyo yathu, ndiwo ukulu umene timamdziŵa bwinopo. (2 Akorinto 3:18; yerekezerani ndi 1 Yohane 2:3-6.) Izinso zimatulukapo chiyamikiro chozama cha mikhalidwe yabwino ya Yehova, mlingo wokwanira wa kudzipereka kwaumulungu.
14. Kuti tipeze chidziŵitso cholongosoka, kodi programu yathu ya phunziro laumwini iyenera kuphatikizapo chiyani, ndipo kodi nchifukwa ninji?
14 Kodi ndimotani mmene mumapezera chidziŵitso cholongosoka chimenecho? Palibe njira zachidule. Kuti tipeze chidziŵitso cholongosoka, tiyenera kukhala akhama m’kuphunzira Mawu a Mulungu ndi mabuku ozikidwa pa Baibulo. Phunziro laumwini loterolo liyenera kuphatikizapo programu yokhazikika ya kuŵerenga Baibulo, yonga ngati yomwe yandandalitsidwa mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki. (Salmo 1:2) Popeza kuti Baibulo liri mphatso yochokera kwa Yehova, zimene timachita m’phunziro Labaibulo laumwini zimasonyeza ukulu umene timayamikira mphatso imeneyo. Kodi zizoloŵezi zanu za phunziro laumwini zimasonyeza chiyani ponena za kuzama kwa chiyamikiro chanu kaamba ka zopereka zauzimu za Yehova?—Salmo 119:97.
15, 16. (a) Kodi nchiyani chimene chingatithandize kukulitsa mzimu wa chilakolako chauzimu kaamba ka phunziro Labaibulo laumwini? (b) Ngati phunziro Labaibulo laumwini liti litulukemo kukulitsa kwathu kudzipereka kwaumulungu, kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa pamene tikuŵerenga Mawu a Mulungu?
15 Kunena zowona, kuŵerenga ndi kuphunzira siziri zopepuka kwa ena. Koma ndi nthaŵi ndi kuyesayesa, mungakulitse chikhumbo chauzimu kaamba ka phunziro Labaibulo laumwini. (1 Petro 2:2) Pamene musinkhasinkha moyamikira pa zonse zimene Yehova Mulungu wakuchitirani, akukuchitirani, ndi zimene adzakuchitiranibe, mtima wanu udzakufulumizani kuphunzira zonse zimene mungathe ponena za iye.—Salmo 25:4.
16 Koma ngati phunziro Labaibulo laumwini loterolo liti litulukemo kukulitsa kwanu kudzipereka kwaumulungu, chonulirapo chanu sichidzakhala kungomaliza masamba a nkhanizo kapena kungodzaza maganizo anu ndi chidziŵitso. M’malomwake, pamene muŵerenga mbali ya Mawu a Mulungu, muyenera kutenga nthaŵi ya kusinkhasinkha pa nkhaniyo, kudzifunsa nokha mafunso onga ngati awa: ‘Kodi zikundiphunzitsanji ponena za mikhalidwe yokoma ya Yehova ndi njira zake? Kodi ndingakhale bwanji ngati Yehova m’mbali zimenezi?’
17. (a) Kodi tikuphunziranji ponena za chifundo cha Yehova m’bukhu la Hoseya? (b) Kodi kusinkhasinkha za chifundo cha Yehova kuyenera kutiyambukira motani?
17 Talingalirani chitsanzochi. Nthaŵi ina yapitayo gawo lathu logaŵiridwa la kuŵerenga Baibulo mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki linatitengera ku bukhu la Hoseya. Pambuyo poŵerenga bukhu Labaibulo limeneli, mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndikuphunziranji ponena za Yehova monga Munthu—mikhalidwe ndi njira zake—m’bukhuli?’ Njira imene lagwiritsiridwa ntchito ndi alembi a Baibulo apambuyo pake imasonyeza kuti timaphunzira zambiri ponena za chifundo chokoma mtima cha Yehova m’bukhu la Hoseya. (Yerekezani Mateyu 9:13 ndi Hoseya 6:6; Aroma 9:22-26 ndi Hoseya 1:10 ndi 2:21-23.) Kufunitsitsa kwa Yehova kwa kusonyeza chifundo kwa Israyeli kunasonyezedwa ndi zochita za Hoseya ndi mkazi wake, Gomeri. (Hoseya 1:2; 3:1-5) Ngakhale kuti kukhetsa mwazi, kuba, dama, ndi kulambira mafano zinali zofalikira mu Israyeli, Yehova ‘analankhula ndi mtima wa Israyeli.’ (Hoseya 2:13, 14; 4:2) Yehova analibe thayo la kusonyeza chifundo choterocho koma akatero “mwaufulu,” malinga ngati Aisrayeli anasonyeza kulapa kwa mtima wonse ndi kupatuka pa njira yawo yochimwa. (Hoseya 14:4; yerekezerani ndi Hoseya 3:3.) Pamene mukusinkhasinkha mwa njira imeneyi pa chifundo chapadera cha Yehova, chidzasonkhezera mtima wanu, kulimbitsa chigwirizano chanu chaumwini kwa iye.
18. Pambuyo posinkhasinkha za chifundo cha Yehova chogogomezeredwa m’Hoseya, kodi mungadzifunse chiyani?
18 Ngakhale ndi tero, zambiri nzofunika. “Odala ali akuchitira chifundo; chifukwa adzalandira chifundo,” anatero Yesu. (Mateyu 5:7) Chotero, pambuyo posinkhasinkha pa chifundo cha Yehova monga momwe chagogomezeredwa m’bukhu la Hoseya, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimotani mmene ndingatsanzire bwinopo chifundo cha Yehova m’zochita zanga ndi ena? Ngati mbale kapena mlongo amene wandichimwira kapena kundilakwira apempha chikhululukiro, kodi ndimakhululuka “ndi kukondwa mtima”?’ (Aroma 12:8; Aefeso 4:32) Ngati mukutumikira mu mpingo monga mkulu woikidwa, mungadzifunse kuti: ‘Pamene ndikusamalira nkhani zachiweruzo, kodi ndingamtsanzire motani Yehova, amene ali “wokhululukira,” makamaka pamene wolakwa apereka umboni weniweni wa kulapa kowona mtima?’ (Salmo 86:5; Miyambo 28:13) ‘Kodi ndiyenera kufunafuna chiyani monga maziko osonyezera chifundo?’—Yerekezani Hoseya 5:4 ndi 7:14.
19, 20. (a) Kodi nchiyani chimene chimatulukapo pamene phunziro Labaibulo lichitidwa mosamalitsa? (b) Kodi nchiyani chimene chiri thandizo lowonjezereka la kukulitsa kudzipereka kwaumulungu?
19 Kuŵerenga Baibulo kwanu kumakhala kopindulitsa chotani nanga pamene kwachitidwa mosamalitsa chotero! Mtima wanu udzakondwa ndi chiyamikiro kaamba ka mikhalidwe yabwino ya Yehova. Ndipo mwakupitirizabe kukalimira kutsanzira mikhalidwe imeneyi m’moyo wanu, mudzalimbitsa chigwirizano chanu chaumwini kwa iye. Mwakutero mudzakhala mukulondola kudzipereka kwaumulungu monga mtumiki wa Yehova wodzipatulira, wobatizidwa.—1 Timoteo 6:11.
20 Thandizo lowonjezereka m’kukulitsa mkhalidwe wabwino umenewu lingapezedwe mwa Yesu Kristu—chitsanzo changwiro cha kudzipereka kwaumulungu. Kodi ndimotani mmene kutsatira chitsanzo cha Yesu kungakuthandizireni ponse paŵiri m’kukulitsa ndi kusonyeza kudzipereka kwaumulungu? Nkhani ya patsamba 18 idzalongosola zimenezi ndi mafunso ogwirizana nawo.
[Mawu a M’munsi]
a Ponena za liwu Lachigriki lakuti di·oʹko (“kulondola”), The New International Dictionary of New Testament Theology ikulongosola kuti m’zolembedwa zodalirika liwulo “kwe[nikwenidi] limatanthauza kuthamangitsa, kulondola, kuthamangira, . . . ndipo mophi[phiritsira] kulondola chinachake mwachangu, kuyesa kufikira chinachake, kuyesa kupeza.”
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji ubatizo suli sitepe lomalizira limene mumapanga m’njira yanu Yachikristu?
◻ Kodi “kudzipereka kwaumulungu” kumatanthauzanji, ndipo kodi ndimotani mmene mumaperekera umboni wake?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuyesayesa kwamphamvu kuli kofunika kuti mukulitse kudzipereka kwaumulungu?
◻ Kodi mungakulitse motani kudzipereka kwaumulungu ku mlingo wokwanira?