Tikulandirani ku Misonkhano Yachigawo ya “Kudzipereka Kwaumulungu”
NDI mutu wabwino chotani nanga umene tiri nawo kaamba ka msonkhano wachigawo wa chaka chino: “Kudzipereka Kwaumulungu”! Ndipo ndi chitsanzo chabwino chotani nanga cha kudzipereka kwaumulungu chimene Yesu Kristu anakhazikitsa kaamba ka ife! Nchosadabwitsa kuti mtumwi Paulo anawuziridwa kulemba ponena za iye kuti: “Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anawonekera m’thupi, anayesedwa wolungama mu mzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m’dzdiko lapansi, wolandiridwa m’ulemerero.”—1 Timoteo 3:16.
Msonkhano wathu wachigawo udzatilimbitsa kukhala anthu a kudzipereka kwaumulungu kowona, monga mmene Yesu analiri. Chotero, choyamba cha zonse, tikufuna kutsimikizira kuti sitimalola chirichonse kusokoneza kudya kwathu phwando lauzimu limeneli. Chotero, tiyeni tikhale m’mipando yathu pa Lachisanu m’mawa pa 10:20 kuti tisangalale ndi kuperekedwa kwa kuimba ndipo mwakutero kukhala m’mkhalidwe wabwino wa maganizo kuti tipindule mokwanira kuchokera ku programu yotsatira. Mutu wosankhidwa kaamba ka tsiku loyamba ndi wakuti “Kutumikira Mulungu Wofuna Kudzipereka Kotheratu,” wozikidwa pa Eksodo 20:5. (NW) Nkhani ya tcheyamani iri yoyenerera koposa: “Tikulandirani, Anthu Inu a Kudzipereka Kwaumulungu!” Pa tsiku loyamba, tidzalimbikitsidwanso ndi nkhani zimene zimasonyeza chifukwa chimene Yehova amawumirira pa kudzipereka kwaumulungu ndi chifukwa chimene ife tifunikira kuphunzira chinsinsi cha kudzipereka kwaumulungu. Padzakhalanso chidziwitso chosangalatsa ponena za chizindikiritso cha Mulungu wowona. Ndiponso, m’chiyang’aniro cha mavuto amene achichepere athu amayang’anizana nawo, padzakhala uthenga wapadera kaamba ka iwo.
Mutu wa pa Loweruka uli wakuti “Kudzipereka Kwaumulungu Kumatanthauza Phindu Lalikulu,” wozikidwa pa 1 Timoteo 6:6. (NW) M’mawa, tidzalandira malangizo pa kokha chomwe chimatenga kulondola kudzipereka kwaumulungu. Ndipo, ndithudi, padzakhala nkhani ya ubatizo kaamba ka awo okonzekera kulowa njira ya moyo ya kudzipereka kwaumulungu. Loweruka masana tidzasindikiza m’maganizo athu chifuno cha kukhala okhulupirira kwa “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera,” ndipo kenaka tidzaphunzira mmene tingasonyezere zochita za kudzipereka kwaumulungu m’chomangira cha banja.
“Kanizani Kupanda Umulungu ndi Kukhala ndi Kudzipereka Kwaumulungu,” wotengedwa kuchokera pa Tito 2:12, uli mutu wa pa Sande. M’mawa, tidzalandira malangizo a panthaŵi yake kutichenjeza motsutsana ndi “munthu wosayeruzika” ndi motsutsana ndi kusokera m’nkhani za chakudya ndi chakumwa, kapesedwe, ndi zosangulutsa. (2 Atesalonika 2:3) Imeneyi idzatsatiridwa ndi drama yamakono kugogomezera kufunika kwa kudzigonjetsera ife eni kwa Mulungu. Nkhani ya Baibulo m’masana idzapereka mbiri yabwino yakuti chiwombolo chiri pafupi kaamba ka anthu a kudzipereka kwaumulungu. Phwando lathu lauzimu lidzatsekedwa ndi kukambitsirana kosonyeza kuti “Kuphunzitsidwa Kwathu Kopitirizabe ndi Kudzipereka Kwaumulungu Kuli Kopindulitsa.”
Chotero bwerani okonzekera kudzatsatira m’Baibulo lanu zilozero za alankhuli ndi kulemba nsonga zosangalatsa kuchokera ku nkhanizo m’bukhu lolembamo nsonga. Kulemba nsonga kuli thandizo lokulira ku kupereka chisamaliro ndi kupindula mokwanira kuchokera ku chimene wina amamvetsera. Ndipo lolani kuti tisanyalanyaze konse chenicheni chakuti ntchito yokulira imafunika kuti msonkhano ugwire ntchito mokwanira ndi mwatawatawa ndipo kuti manja ambiri amapeputsa ntchito. Mwa kudzipereka mwaufulu kuthandiza, tidzazindikira chimwemwe chokulira cha kupatsa.—Machitidwe 20:35.
Chotero lolani kuti kudzipereka kwathu kwaumulungu kutikakamize kubwera ku msonkhano uwu ndi kutisonkhezera kupeza zochulukira kuchokera ku iwo. Lolani kuti tipite olimbikitsidwa ndi ogamulapo kutsogoza miyoyo ya kudzipereka kwaumulungu mokwanira mowonjezereka koposa.