Kupeza Chimwemwe—Koma Kuti?
YESU ananena kuti: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) Msungwana wachichepere wowona mtima ku Middle East anali wozindikira kusoŵa kwake kwauzimu ndipo anafunafuna kukondweretsa Mulungu. Pomalizira, anapeza chimwemwe—koma kuti? Tidzamlola kuti afotokoze.
“Ndinakulira m’banja Lachimaron lachipembedzo kwambiri Lachikatolika. Anafe tinaphunzitsidwa kupemphera madzulo aliwonse patsogolo pa mafano owumbidwa, ndipo kuchokera ku ubwana ndinali ndi chikhumbo cha kutumikira Mulungu.
“Pa msinkhu wa 17, ndinapita kusukulu ya convent kuti ndikakhale m’viringo, ndikumaganiza kuti imeneyi ikakhala njira yokhutiritsira chikhumbo changa. Komabe, ndinawona zinthu zambiri pakati pa aviringo zimene zinandivutitsa maganizo. Iwo anajedana. Ophunzira sankapatsidwa chakudya chokwanira, pamene kuli kwakuti aviringo anasangalala ndi chakudya chabwino koposa. Ndipo panali machitachita achisembwere pakati pa aviringo ndi wansembe. Pokhala wokhumudwitsidwa moipitsitsa, ndinachoka pa conventpo pambuyo pa miyezi isanu ndi inayi ndi kubwerera kwathu.
“Ndinali ndidakali ndi mafunso ambiri osayankhidwa, ndipo pamene sindinapeze mayankho ake okhutiritsa, ndinafika pa mlingo wakusasamala ponena za chipembedzo. Kenaka, mu 1982, pamene ndinali 22, mbale ndi mlongo wanga akuthupi ankaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Makolo anga ndi ine tinali otsutsa kwa iwo. Mbale wanga anavutika ndi kuzunzidwa kochuluka, kumenyedwa, ndi kuikidwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chake chatsopano. Ngakhale kuli tero, chimene chinandikondweretsa chinali masinthidwe aakulu amene anawapanga m’moyo wake. Ndiponso, iye anapereka mayankho anzeru am’Baibulo ku mafunso amene ndinkawafunsa kwa nthaŵi yaitali. Chotero ndinayamba kuŵerenga Baibulo mwamseri pandekha nthaŵi yausiku.
“Tsiku lina ndinatsatira kukapenyerera msonkhano wa Mboni za Yehova. Ndinakondweretsedwa ndi chikondi chosonyezedwa kumeneko. Panalibe kusiyana pakati pa olemera ndi osauka. Mboni zimakhala mogwirizana ndi zimene zimaphunzitsa. Ndinakhutiritsidwa kuti anali nacho chowonadi.
“Kungotha msonkhanowo, ndinapempha mmodzi wa iwo kuphunzira nane. Ndinawuza mkaziyo kuti ndinangofuna kuphunzira, osati kupezeka ku misonkhano kapena kupita ku ulaliki. Komabe, mwamsanga ndinazindikira kuti ndinali kuphunzira chowonadi. Ndinapemphera ndi kusankha kutumikira Yehova. Pa October 28, 1983, mbale wanga, mlongo wanga, ndi ine tinabatizidwa. Tsopano ndinapeza njira yokhutiritsira chikhumbo changa chotumikira Mulungu chimene ndinali nacho kuchokera kuubwana.
“Miyezi iŵiri pambuyo pa ubatizo, ndinayamba upainiya wothandizira, ndipo miyezi isanu ndi itatu pambuyo pake ndinakhala mpainiya wokhazikika. Pambuyo pa chaka chimodzi ndi theka, ndinaitanidwa kukatumikira pa ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova, yotchedwa Beteli, zimene ndinachita pa maziko apakanthaŵi kwa zaka ziŵiri. Ndinakondweretsedwa ndi kudzichepetsa kosonyezedwa ndi onse. Abale amathayo aakulu anakhaladi ndi phande m’ntchito yotsuka mbale pambuyo pa chakudya chamadzulo.
“Pa March 14, 1988, ndinakhala chiŵalo chanthaŵi zonse cha banja la Beteli. Inali nthaŵi yosangalatsa chotani nanga! Inde, ndinapeza chimwemwe. Kuti? Pakati pa Mboni zodzipatulira za Yehova! Tsopano ndikudzimva ngati wamasalmo yemwe anati: ‘Tsiku limodzi m’mabwalo anu likoma koposa [zaka chikwi kwinakwake, NW].’”—Salmo 84:10.