Galamukani! Woyamikiridwa Mofala
Galamukani! akufalitsidwa m’zinenero 55, ndipo ali ndi avareji yakusindikiza makope 11,930,000 pa imodzi. Aŵerengi kuzungulira dziko lonse amasangalala nayo ndi kupindula nayo, monga zavumbulidwa ndi makalata awo achiyamikiro. Ofesi yanthambi ya Watch Tower mu Thailand inalandira pempho lotsatirali:
“Sukulu yathu imalandira mokhazikika magazine a Galamukani! [mu Chithai], ndipo tawona kuti kope la September 8, 1988, liri pa nkhani ya ‘Makolo,’ imene makolo onse okhala ndi ana opita kusukulu ayenera kuiŵerenga. Chotero tikufuna kuti mutitumizire makope 250-400, ngati aliko, kuti tikawagaŵire pa kukumana kotsatira kwa makolo/aphunzitsi.”
Mkazi wina waku Roanoke, Virginia, U.S.A., akulemba kuti: “Ndine Mbaptist wokhulupirika . . . , koma ndinatola imodzi ya mapepala anu Galamukani! m’Nyumba Yochapiramo yapafupi ndipo ndaunikiridwa mokulira. Ndasangalala kuiŵerenga. Pano ndikutsekera [cheke cha $5], chimene ndifuna kuti munditumizire sabuskripishoni ya Galamukani! ya chaka chimodzi.”
Tiganiza kuti nanunso mudzapindula ndi kusangalala ndi nkhani zochititsa chidwi za mu Galamukani!
Chonde tumizani sabuskripishoni ya chaka chimodzi ya Galamukani! Ndatsekeramo K62.50 (Zambia) kaamba ka makope 12 a magazineŵa (kope limodzi pamwezi).