Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 6/15 tsamba 32
  • “Nyimbo Zimene Zimachiritsa”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Nyimbo Zimene Zimachiritsa”
  • Nsanja ya Olonda​—1990
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 6/15 tsamba 32

“Nyimbo Zimene Zimachiritsa”

Mkazi wa ku Spanya analembera nthambi ya Jeremani ya Watch Tower Society kuti: “Ndiri woyamikira kwenikweni kwakuti ndinafunikiradi kulemba kukuwuzani ponena za icho.” Kodi anayamikiranji?

“Ndakhala m’Spanya kwa zaka pafupifupi zisanu ndi zinayi,” akulongosola tero, “ndipo chaka chimodzi ndi theka zapitazo, aŵiri a achichepere anu anayamba kuphunzira Baibulo ndi ine. Pokhala nditaŵerenga m’nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yonena za nyimbo zomwe zimachiritsa, ndinawafunsa kundipezera makasetiwo.

“Nthaŵi ina pambuyo pake, podzimva wopsyinjika ndikuŵaŵa kwina, ndinaliza nyimbozo. Panali kusiyana kotani nanga! Kwakanthaŵi kochepa kokha, kuŵaŵa kwamaganizoko kunatha, ndipo maganizo anga anawongokera molingalirika. Ndinasangalala chotani nanga kukhala ndi makaseti a nyimbo ameneŵa! Chiyambire nthaŵiyo, kaŵirikaŵiri ndaŵamvetsera pogona usiku. Izo ndi nyimbodi zochiritsa.”

Ambiri ayamikira alubamu ya Sing Praises to Jehovah, yomwe iri ndi makaseti asanu ndi atatu a nyimbo zoimbidwa pa piano. Ngati ndinu wokondweretsedwa kupeza alubamuyi, dzazani ndikutumiza kapepala kotsatiraka.

Iyi ndi mbali ya ntchito yophunzitsa Baibulo ya dziko lonse imene imachilikizidwa ndi zopereka zaufulu.

Ndingakonde kulandira alubamu ya Sing Praises to Jehovah yokhala ndi makaseti tepu anyimbo asanu ndi atatu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena