“Pambuyo Pake Anapatsanso Mwamuna Wake”
KODI Adamu analipo pamene njoka inalankhula kwa Hava ndi kum’nyenga kulakwira Mulungu? Baibulo silimasonyeza chimenechi. Genesis 3:6 (NW) imasimba kuti Hava “anatenga chipatso chake, ndi kuchidya. Pambuyo pake anapatsanso china kwa mwamuna wake pamene anali naye.” Komabe, matembenuzidwe ena a Baibulo amapereka lingaliro losiyana. King James Version imamasulira lembalo motsatiramu: “Iye anatenga zipatso zake, nadya, ndipo anapatsanso mwamuna wake amene ali naye; ndipo anachidya.”
Mneni wa Chihebri wotembenuzidwa “anapatsa” ali mkamvedwe kosakhala kapanthaŵiyo ndipo wagwirizanitsidwa ndi liwu lapadera logwirizanitsa zinthu lakuti “ndipo” [Chihebri, waw], motero kusonyeza tsatanetsane wosakhala wapanthaŵiyo kapena kutsatizana kwanzeru. Chotero, New World Translation imatembenuza kukhalapo kosiyanasiyana kwa waw, imene imagwirizanitsa ndandanda ya zochitika pa Genesis 3:6, osati kokha ndi “ndipo” komanso ndi mawu ena otembenukira ku chinthu china, onga ngati “ndiponso,” “chotero,” ndi “pambuyo pake.” Motero New World Translation iri ndi maziko enieni a kutembenuza kwapamwambako.
Kodi Adamu akanapenyerera osalankhulapo kanthu pa kukambirana kwa pakati pa mkazi wake ndi njokayo, akumamvetsera ku bodza ndi nkhani ya chinyengo ya woukira wosawoneka wokhala kumbuyo kwa njokayo? Mosangalatsa, katswiri wa Baibulo wa Chijeremani J. P. Lange akukana lingaliro limeneli ndipo akuthirira ndemanga kuti: “Kukhalapo kwa mwamunayo m’chochitika cha kuyesako, ngakhale kukhala kwake chete, nkosalingalirika.” Ndipo polongosola mawu akuti “ndi mkaziyo,” wothirira ndemanga Wachiyuda B. Jacob akutchula kuti iko “[sikumatanthauza] yemwe anaimirira ndi mkaziyo (mkati mwa kachitidwe kapapitako kapena pamene anadya).”
Kukambirana kwa Hava ndi njokayo kunavumbula kuti mwamuna wake anamdziŵitsa ponena za lamulo la Mulungu la kusadya za mtengowo. (Genisis 3:3) Chotero monga mutu wa Hava, Adamu anakwaniritsa thayo limenelo. Mdyerekezi ananyalanyaza makonzedwe a Mulungu aumutu ndipo mochenjera anatenga mwaŵi wa chenicheni chakuti Hava anali yekha. Mkaziyo pambuyo pake anayankha kuti: “Njoka inandinyenga ine ndipo ndinadya.” (Genesis 3:13) Hava ananyengedwa chifukwa chakuti anakhulupirira bodza, koma ichi sichinalungamitse kuchimwa kwakeko. Chitsanzo cha chenjezoli chimafotokoza mwafanizo kuti sitingakhale ndi chodzikhululukira chakuchita chinachake cholakwika m’maso mwa Yehova.—1 Timoteo 2:14.