Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 6/15 tsamba 30
  • Chidziŵitso pa Nyuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziŵitso pa Nyuzi
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nkulengezeranji?
  • Kudyerera Masuku Kugonana
  • Kodi Mkristu “Wabwinopo” Ndani?
  • Carici Coona ndi Maziko Ace
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kodi ma Lutheran AchiGerman ali Mtundu Wowopsyezedwa?
    Galamukani!—1988
  • Ziyembekezo za Mtsogolo Kaamba ka chiProtestanti—Ndi Inu!
    Galamukani!—1988
  • Gawo 22: 1900 kupita mtsogolo—Chipembedzo Chonyenga Cholakidwa ndi Nthaŵi Yake Yapita!
    Galamukani!—1989
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 6/15 tsamba 30

Chidziŵitso pa Nyuzi

Kodi Nkulengezeranji?

Kusa lengeza kwa opita ku tchalitchi kwafotokozedwa ndi akuluakulu ena kukhala kochititsidwa ndi kucheperachepera kwa umembala wa tchalitchi pakati pa zipembedzo zazikulu. Kudera nkhaŵa vutoli mu 1988 kunafulumiza United Church of Christ kutenga kukhala chonulirapo cha zaka zinayi cha nkhani ya “kukula kwa ulaliki ndi umembala.”

St. Petersburg Times ikusimba kuti zipembedzo zazikulu zina mu United States, kuphatikizapo Presbyterian Church ndi Episcopal Church, zachita mofananamo. Komabe, kufufuza kwa posachedwapa kwa mipingo yoposa 200 ya United Church of Christ kunavumbula kuti ambiri a ziŵalo zake 1.6 miliyoni amasonyeza chikondwerero chochepera m’kulankhula ndi ena ponena za chikhulupiriro chawo. Chiŵalo chimodzi chinafunsa kuti: “Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulankhula kwa ena ngati tikuchita zabwino?” China chinati: “Ngati mumakhala ndi moyo mogwirizana ndi chikhulupiriro chanu, simufunikira kulankhula ponena za icho.”

Komabe, m’bukhu lake lakuti American Mainline Religion, mthandizi wa mkonzi Wade Clark Roof anavomereza kuti “mmene anthu amalankhulira ponena za chipembedzo chawo ndi miyoyo yauzimu kumagwirizana kwakukulukulu ndi kupulumuka kwa chikhulupiriro chenichenicho.”

Ngati “kuchita zabwino” ndi kukhala ndi “chikhulupiriro” nkokwanira kukondweretsa Mulungu, kodi nchifukwa ninji mtumwi Paulo analemba kuti: “Tsoka kwa ine ngati sindilengeza mbiri yabwino”? Iye analongosola kwa akhulupiriri anzake mu Roma kuti: ‘Ngati mudzavomereza mkamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Pakuti ndi mtima munthu akhulupira kutengapo chilungamo; ndi mkamwa abvomereza kutengapo chipulumutso’​—1 Akorinto 9:16, NW; Aroma 10:9, 10.

Kudyerera Masuku Kugonana

Zoposa theka za nkhani zosangulutsa 1,100 zomwe zinawonekera m’mabuku osiyansiyana a ku Japan, kuphatikizapo a ana, zinasonyeza machitachita a kugonana, anatero Profesa Mamoru Fukutomi. Iye anatsogolera kufufuza mu Tokyo kwa magazine oposa 390 ndi mabuku ena ogulidwa m’mwezi umodzi.

‘Kusonyezedwa kochuluka kwa kachitidwe ka kugonana,’ akutero Profesa Fukutomi, ‘kumatsatira zisonyezero zazithunzi za amuna akukakamiza akazi ozengereza [muunansi wa kugonana] ndipo akazi potsirizira pake amavomereza mokangalika.’ Pafupifupi 80 peresenti ya zithunzi 6,861 m’magazine otchuka a ku Japan zomwe zinasanthulidwa “zinasonyeza akazi okhala mumkhalidwe wodzetsa chilakolako cha kugonana,” ikusimba tero The Daily Yomiuri. Pamene kuli kwakuti akazi ambiri m’zithunzizo “anavala zovala zamkati, zovala zosambira kapena kukhala maliseche” ndipo 40 peresenti okha anali ovala, 75 peresenti ya zithunzi za amuna zofufuzidwa zinali zovala.

Kodi kudyerera masuku kugonana koteroko kudzayambukira achichepere motani? Bukhu la Baibulo la Miyambo limafotokoza mwachithunzi mwamuna wachichepere “wopanda kulingalira kwabwino” wokopeka kunka kunyumba ya wachigololo. (Miyambo 7:7, Reference Bible, mawu ammunsi) Ndipo kodi imati bwanji za mkazi wa chigololoyo? “Mwina ali kumakwalala, mwina ali kumabwalo, nabisalira pamphambano zonse. Ndipo anagwira mnyamatayo, nampsopsona.” (Miyambo 7:8-13) M’nthaŵi zamakono ngakhale tsamba losindikizidwa ‘limabisalira kugwira’ wachichepere. Komabe, Baibulo likulangiza kuti: ‘Mtima wako usapatukire ku njira ya mkaziyo, usasochere m’mayendedwe ake.’​—Miyambo 7:25.

Kodi Mkristu “Wabwinopo” Ndani?

“Mosasamala kanthu za chosankha chimene Mkristu angapange, kaya kukakhala msilikali kapena wotsutsa weniweni, kukakhala kolakwika kwa iye kudziganizira yekha kukhala ndi Chikristu chenicheni kuposa ena, kapena ngakhale kukaikira, kuchilikiza kaimidwe kosiyana ndi kake, popeza kuti enanso ndi Akristu.”

Ndemangayi inatulutsidwa ndi Evangelical Lutheran Church Council ya ku Jeremani mu July 1989. Chifukwa ninji? Akuluakulu anati inalinganizidwira kutsutsa kaimidwe kotengedwa ndi ena m’tchalitchi kakuti kutsutsa kwa chikumbumtima ndiko “chizindikiro chowona” kwenikweni cha kukhala Mkristu kuposa utumiki wa nkhondo. Pamene kuli kwakuti tikuvomereza kuti Akristu angathetse nkhondo mwa “kudzipatula mwaumwini ku chiwawa,” Church Council inatsutsa kuti ichi chingachitidwenso mwakumenyera chiwawa ndi mphamvu zankhondo n’cholinga cha kutsimikizira mtendere.

M’bukhu lake lakuti History of Christianity, Edward Gibbon analemba kuti Akristu a m’zaka za zana loyamba “anakana kutengamo phande lokangalika lirilonse m’kulamulira kwa boma kapena kutetezera kwa nkhondo kwa ufumuwo,” ndikuti “kunali kosatheka kuti Akristu, popanda kukana ntchito yawo yopatulika koposa, apitirize nkukhala msilikali, woweruza, kapena akalonga.”

Chotero, funso silakuti ndani yemwe ali Mkristu “wabwinopo” koma kaya ngati munthu wolondola njira yosiyana ndi Chikristu choyambirira alidi Mkristu nkomwe. Paulo analemba kuti: ‘Pakuti pakuyendayenda m’thupi, sitichita nkhondo monga mwathupi, (pakuti zida zankhondo yathu siziri zathupi.)’​—2 Akorinto 10:3, 4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena