Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 3/8 tsamba 22-23
  • Kodi ma Lutheran AchiGerman ali Mtundu Wowopsyezedwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi ma Lutheran AchiGerman ali Mtundu Wowopsyezedwa?
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nchifukwa Ninji Akuchoka?
  • Ziyembekezo za Mtsogolo Kaamba ka chiProtestanti—Ndi Inu!
    Galamukani!—1988
  • “Ngati Lipenga Lipereka Mawu Osazindikirika . . . ”
    Galamukani!—1988
  • Kodi Siali a Dziko Lapansi?
    Galamukani!—1995
  • Carici Coona ndi Maziko Ace
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Galamukani!—1988
g88 3/8 tsamba 22-23

Kodi ma Lutheran AchiGerman ali Mtundu Wowopsyezedwa?

Ndi mlembi wa Galamukani! mu Federal Republic of Germany

OWONERERA ena angakhale anadabwitsidwa kumva mawu otsatirawa pa wailesi ya kanema ya chiGerman: “Tchalitchi cha Lutheran sichidzakhala ndi mtsogolo mulimonse.” Yozizwitsa koposa inali nsonga yakuti iwo anayambira pafupi ndi malo enieni omwe anabweretsa Martin Luther m’yambitsi wa tchalitchi chimenecho ndi tate wa Kukonzanso.a

Zowona, Tchalitchi cha United Evangelical Lutheran cha ku Germany chiri ndi chifupifupi ziwalo mamiliyoni 25, chimene chiri, kulingana ndi kuŵerengera kwa anthu a boma kochitidwa posachedwapa, chiri unyinji wowirikiza 45 womwe umapita ku magulu ena a chiProtestanti utaikidwa pamodzi mu Germany. Chikhalirechobe, tchalitchi chikugwa, chomwe chaimiridwa bwino lomwe ndi zotsala zowonongedwa za Kaiser Wilhelm Memorial Church mu West Berlin.

Mu 1961, yoposa 50 peresenti ya anthu onse a chiGerman anali a Lutheran. Podzafika 1970, chiŵerengerocho chinali 49 peresenti, podzafika 1980, 46 peresenti. Kenaka zinthu zinawonekera kukhala zikuwongokera. Nyuzipepala ya nthaŵi zonse ya chiGerman inasimba kumayambiriro kwa 1981 kuti: “Tchalitchi cha Lutheran mu Germany chawongokerako kuchokera ku kubwerera m’mbuyo kwake kwa zaka khumi zapitazo. . . . Kuchoka kwa ziwalo za tchalitchi . . . kwachititsa kutaikiridwa kwa kuwala kwa unyinji.”

Koma ziŵerengero za ziwalo kaamba ka 1984 zinasonyeza kulongosola kumeneku kukhala kosakhala kwenikweni. Zoyerekezera tsopano ziri zakuti tchalitchicho chidzataya ziwalo zina 4,500,000 mkati mwa zaka khumi. Chotero, podzafika chaka cha 2030, kokha gulu lowirikiza katatu kapena kucheperapo la chiŵerengero cha dziko lidzakhala a Lutheran.

Nchifukwa Ninji Akuchoka?

Pa programu yomwe yangotchulidwa kumene ya wailesi ya kanema mu 1986, zomwe zinali kale ziwalo za tchalitchi zisanu ndi ziŵiri zinapereka zifukwa zawo kaamba ka kusamvana: kutsutsana kwa tchalitchi ku maseŵera a pa Sande, kuchirikiza kwake kwa ndalama kwa omenyera ufulu a chiKomyunisiti, kaimidwe kake ku malamulo ochinjiriza a boma, kuchotsa kwake kwa apasitala aŵiri a kugonana kwa ofanana ziwalo, ndi kunyalanyaza kwake kwa kusamalira zinyama. Wina anatsutsa kakonzedwe mu kamene ndalama zolipira zotaika za tchalitchi zimachotsedwa ku malipiro a ziwalozo. Mwapadera, kokha aŵiri anatchula Mulungu. Ndipo komabe, kodi chimenecho sichimene kokha chipembedzo chikufunikira?

China chachikulu, chomwe chiri ngakhale chovuta kuposa kuchepa mu chiŵerengero, anatero Johannes Hansen, katswiri wa za chipembedzo wotsogolera mu Lutheran, chiri “kugwa kowona kwa mkhalidwe wa chipembedzo wa ziwalo za tchalitchi.” Ichi chiri tero kaamba ka nsonga yakuti pa Sande ya nthaŵi zonse ochepera pa 6 peresenti ya iwo amapezeka ku misonkhano ya tchalitchi, m’mizinda yaikulu ngakhale oŵerengeka. Kokha mmodzi mwa anayi amalingalira kupezeka ku tchalitchi kapena kuŵerenga Baibulo monga chofunika cha Mkristu. M’chenicheni, chifupifupi asanu ndi atatu mu khumi amanena kuti kukhala mu Lutheran wabwino munthu amangofunikira kubatizidwa ndi kutsimikiziridwa, kukhala ndi moyo wabwino ndi kukhulupiriridwa. Nchosadabwitsa kuti Frankfurter Allgemeine Zeitung inadziŵitsa m’nkhani yake ya mkonzi kuti: “Ngozi kaamba ka tchalitchi cha Lutheran simachokera ku chiŵerengero chake koma imachokera ku kusoweka kwake kwa thanzi lauzimu”!

Ziwalo za tchalitchi zomwe zimasowa thanzi lauzimu zimawona tchalitchi chawo mwatsatanetsatane. Izo zimakhumbira mbiri yake yakale yolemera, kunyada kaamba ka nyumba zake zokongola, ndi kutenga mwaŵi wa mapindu a zamayanjano omwe icho chimapereka. Chitadza pa “kufunafuna Mulungu” ngakhale kuli tero, ambiri amasankha kumufunafuna iye m’chilengedwe m’malo mwa tchalitchi. Ichi chinatsogolera mtsogoleri wa tchalitchi kufunsa ndi chikaikiro chifukwa chimene iwo samangopitiriza ndi kukhala ndi misonkhano ya pa maliro ikuchitidwa ndi Dipatimenti ya za m’Nkhalango m’malo mwa tchalitchi.

“Chomwe chikuwoneka kukhala chikusowa,” inachitira ndemanga tero magazini ina ya ku U.S. zaka zingapo zapita, “chiri chikondi kaamba ka Mulungu ndi chowonadi chake chomwe chinadziŵikitsa chiLutheran choyambirira.” Nchifukwa ninji a Lutheran ambiri amawona tchalitchi chawo kukhala osati china chirichonse koma kokha kachitidwe kolondola ka kubatiza makanda, kutsimikizira uchichepere, ndi mapwando achikwati a achikulire? Nchifukwa ninji iwo amafunafuna Mulungu m’chilengedwe ndi kutembenukira ku tchalitchi kokha pamapeto a moyo kaamba ka “kuikidwa mwaulemu”? Nchifukwa ninji pali kusoweka kwa thanzi lauzimu?

[Mawu a M’munsi]

a Kunena zenizeni, Luther anabadwa ndi kuthera moyo wake wonse mu chimene tsopano chiri German Democratic Republic, yodziŵika mofala monga East Germany.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena