Kodi Siali a Dziko Lapansi?
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU GERMANY
“SIALI a dziko lapansi monga ine sindili wa dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Ndi mawu amenewa Yesu analongosola uchete weniweni wa otsatira ake m’nkhani za ndale. Kodi odzitcha Akristu amafikira muyezo umenewu lerolino?
Talingalirani ndemanga za panyuzi zotsatirazi ponena za kudziloŵetsa kwa Dziko Lachikristu mu amene kale anali German Democratic Republic (GDR), amene analamuliridwa ndi boma Lachikomyunizimu kufikira pamene linathetsedwa mu 1990.
● “Popeza kuti tsopano Tchalitchi cha Lutheran mu GDR chakhala paulemerero kwa kanthaŵi monga mayi wa kupandukira boma kwamtendere, kutchuka kwake pakati pa anthu kukutsika mofulumira. Ambiri amachiona kukhala kwakukulukulu mzati wa bomalo ndi malo ogwirirapo ntchito a Stasi (Bungwe Lotetezera la Boma).”—Die Zeit, November 1991.
● “Matchalitchi a m’zigawo osiyanasiyana a Lutheran . . . asonyeza kuzizwa poona kuyanjana kwa antchito a tchalitchi ndi ziŵalo zake ndi a Stasi.”—Evangelische Kommentare, January 1991.
● “Atsogoleri a Tchalitchi [cha Lutheran] amamva madandaulo akuti ansembe sanali kusamaliranso anthu awo mmene anachitira kale, chifukwa cha kutanganitsidwa ndi za ndale.”—Süddeutsche Zeitung, February 1990.
● “Weizsäcker [pulezidenti wakale wa Federal Republic of Germany] ananena kuti Tchalitchi [cha Lutheran] nthaŵi zonse chinachita mbali ya kuthandiza mu unansi wa za ndale wa Maboma aŵiri a Germany.”—Wetterauer Zeitung, February 1992.
Kuloŵerera m’ndale sikunali kwa Tchalitchi cha Lutheran chokha. “Pafupifupi tchalitchi chilichonse [Chachiprotesitanti] chinaloŵereredwa ndi atumiki a Stasi,” inasimba motero The European. Manfred Stolpe, amene The European imamutcha kukhala “wolankhulira wamkulu wa tchalitchi chachiprotesitanti kwa akuluakulu a komyunizimu,” anati m’kudzikanira kwake: “Ndikanagwirana chanza ndi Mdyerekezi ngati kuteroko kukanachirikiza cholinga chathu.”
Guardian ya London inasimba za unansi wathithithi pakati pa atsogoleri achipembedzo ndi Amafia mu Italy. Iyo inati: “Tchalitchi ndi Cosa Nostra zakhalira pamodzi mwamtendere kwa nthaŵi yaitali kwakuti tchalitchi kaŵirikaŵiri chimaimbidwa mlandu wa kudziloŵetsa m’machitachita aupandu.”
Toronto Star inali ndi nkhani yonena za kuchita zinthu kwa pakati pa ansembe ena a Orthodox ya ku Russia ndi KGB yakale. Lipotilo likunena kuti: “Kuvumbulidwa kwa kugwirizana kwa tchalitchi ndi boma la komyunizimu ndiko nkhonya yosakaza koposa. . . . Zolembedwa za mu akaundula a KGB . . . zimasonyeza kuti akuluakulu a tchalitchi sanangotaya makhalidwe awo komanso anali ofunitsitsa kuleretsa molakwa atsogoleri awo achipembedzo a kumaiko akunja.”
Pamene kuli kwakuti matchalitchi a Dziko Lachikristu akupitiriza kudziloŵetsa m’ndale, Akristu enieni akumamatira ku chilangizo cha Yesu cha kusakhala a dziko lapansi.