Pamene Agogo Ake Anamwalira
Nakubala wa ku Virginia Beach, Virginia, analemba motere kuchiyambi kwa chaka chino: “Mwezi watha atate wanga anamwalira. Iwo ndi mwana wanga wamwamuna wamng’ono kwambiri ankakondana kwambiri, mosasamala kanthu za mtunda womwe unali pakati pawo. Pamene ndinamudziŵitsa kuti agogo ake amwalira, iye anayamba kulira momvetsa chisoni.
“Mwamsanga ndinafunafuna katrakiti kakuti Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Akufa Okondedwa? Mwamsanga nditakapeza, pamene nkhope yake inali idakali yonyowa ndi misozi, ndinayamba kumuŵerengera iko. Pamene ndinamaliza, iye anachitako bata. Ndikuthokoza kaamba ka chidziŵitso chamtengo wake choterocho, chomwe chinali chofunikadi panthaŵi yowawitsa imeneyi.”
Mungalandire trakiti yotonthoza imeneyi, limodzi ndi ena, mwakungodzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Ndingakonde kulandira katrakiti kakuti Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Akufa Okondedwa? limodzi ndi ena. (Kunja kwa Zambia, lemberani ku nthambi ya Watch Tower yakumaloko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 2.)