Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 9/15 tsamba 30-31
  • Chifukwa Chake Réunion Ili ndi Nyumba Zaufumu Zambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Réunion Ili ndi Nyumba Zaufumu Zambiri
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Kodi Nchifukwa Ninji Kuli Nyumba Zaufumu Zambiri?
  • Zopinga Zolakidwa
  • Chitamando Chinka kwa Yehova
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 9/15 tsamba 30-31

Chifukwa Chake Réunion Ili ndi Nyumba Zaufumu Zambiri

PAFUPIFUPI makilomita 640 kum’mawa kwa Madagascar, chisumbu chaching’ono cha Réunion chimabuka mwadzidzidzi m’Nyanja yaikulu ya India. Ngakhale kuti nchautali wa makilomita 60 ndipo chotambalala makilomita 50, chisumbucho nchodziŵika chifukwa cha matanthwe ake otentha ndi kuwala kwa moto kwa nthaŵi ndi nthaŵi. Phiri lalitali kwambirili, lautali wa mamita 3,069 pamwamba pa malekezero a nyanja, ndithanthwe loleka kuphulika lotchedwa Piton des Neiges (Phiri la Chipale Chofeŵa). Kumbali ya kum’mwera cha kum’mawa kwa chisumbucho kuli thanthwe lotentha kwambiri lautali wa mamita 2,625 lotchedwa molondola kukhala Piton de la Fournaise (Phiri la Ng’anjo). Chimakhala chochititsa chidwi chotani nanga pamene liphulika usiku! Misewu yambiri imadutsa mokhotakhota kutsika ndi materezi opendekeka, kupereka mawonekedwe othetsa phuma a chimene chadziŵika kukhala kukongola kwadzawoneni kwa Réunion.

Kodi Nchifukwa Ninji Kuli Nyumba Zaufumu Zambiri?

Komabe, kukongola kwenikweni kwa Réunion kuli m’njira imene anthu ambiri apachisumbupo avomerezera ku “mbiri yabwino ya ufumu” yolalikidwa ndi Mboni za Yehova. (Mateyu 24:14, NW) Ntchito yawo yolalikira inayamba mu 1960, pamene aminisitala a nthaŵi zonse aŵiri anafika kuchokera ku Falansa. Tsopano, zaka 30 pambuyo pake, Mboni 1,665 nzotanganitsidwa kufalitsa uthenga Waufumu pakati pa nzika 582,000​—chiŵerengero cha Mboni imodzi kwa anthu 350 alionse pa chisumbucho.

Kukula koteroko kwafunikira kumangidwa kwa malo osankhanira oyenerera kotero kuti Mbonizo zipitirize kulambira kwawo ndi kuphunzitsa kwauzimu. (Ahebri 10:24, 25) Pakali pano, mipingo 13 mwa 19 ya Réunion yamanga kale Nyumba Zaufumu zawo. Chifukwa cha mphepo zamkuntho zobwerezabwereza m’derali, nyumbazi nzolimba zimene zimafunikira nthaŵi yaitali​—ndi zowonongedwa​—kuti zimangidwe. Chotero kodi zatheka bwanji kumanga nyumba zoterozo, popeza kuti Mboni zambiri pachisumbucho zimalandira malipiro ochepa ndipo ziri ndi mabanja aakulu owachilikiza? M’mawu a Baibulo, yankho nlakuti ‘mkono wa Yehova siwaufupi.’​—Yesaya 59:1.

Zopinga Zolakidwa

Mwachitsanzo, talingalirani mmene Yehova anafulumizira mitima ya anthu kuthandiza kumanga Nyumba Yaufumu m’tauni yaing’ono ya Saint-Louis, yokhala kumbali ya kum’mwera cha kum’mawa kwa Réunion. Pamene makonzedwe anavomerezedwa choyamba, Mboni yachichepere inauza mphunzitsi wake wa kalasi yomanga nyumba zolimba kuti Nyumba Yaufumu ikamangidwa ndi antchito aufulu. Mphunzitsiyo sanapereke kokha mautumiki ake komanso anabweretsa kalasi lake lonse kudzathandiza kukumba maziko. Pambuyo pake, iye anapereka zitsulo zofunikira kaamba ka mazikowo.

Pamene antchito aufulu oposa zana limodzi anabwera patsiku latchuthi chakudziko kuti adzawake konkiri pa malo a mamita 190 m’mbali zonse zinayi, anadabwitsidwa kupeza kuti madzi anatsekedwa ndi akulu a mumzindawo. Kodi iwo akakonzekera motani konkiriyo popanda madzi? Mmodzi wa antchitowo amene anadziŵa mkulu wa dipatimenti ya ozima moto analingalira kuti akafotokoza tsokalo kwa munthu wachifundoyo. Kanthaŵi pang’ono, galimoto lalikulu lozima moto linafika pamalopo. Galimotolo linali ndi madzi okwanira kaamba ka ntchitoyo, ndipo dipatimenti ya ozima motoyo inalola kuti galimotolo likhale pamalopo kwa tsiku lathunthu! Momvekera, antchito aufulu onse anasonkhezeredwa kuika mtima wawo pantchitoyo.

Thandizo la Yehova linali lowonekera m’njira imene zopinga zina zinalakidwira. Mwachitsanzo, panthaŵi ina ya kumangako, denga linali lokonzekera kuti liikidwe zoikira magetsi zapadera 22 zimene zinaodedwa miyezi isanu ndi itatu kuchiyambi. Koma kampaniyo inadziŵitsa abalewo kuti mtundu umene ankaufuna unaleka kupangidwa. Kodi akachitanji? Kodi kapangidwe konseko ndi denga zinayenera kusinthidwa? Ayi, popeza kuti panthaŵi yabwino, abalewo anamva za munthu wina womanga amene anali ndi magetsi ofananawo kaamba ka ntchito yake imene sinachitike.

“Kodi muli nawo angati?” iye anafunsidwa motero.

Iye anayankha kuti, “pafupifupi 25.”

Mosatayanso nthaŵi, magetsiwo anagulidwa ndi kuikidwa.

Pamene ntchitoyo inkapita patsogolo, munthu yemwe anangoyamba kumene kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova anakondweretsedwa kwabasi ndi nyumba yabwinoyo.

“Tandiuzani,” iye anafunsa tero, “kodi pali chinachake chimene mukufuna?”

“Inde,” anayankha motero mbale wina. “Tikufunikira ziwiya zokuzira mawu.”

Panthaŵi yomweyo, munthu wokondwerera chatsopanoyo anatulutsa bukhu lake la ndalama ndi kupereka ndalama zokhala pang’ono kukwanira kaamba ka ziwiya zokuzira mawu zatsopano. Zopereka zoterozo, limodzi ndi ngongole yoolowa manja kuchokera ku malikulu a Watch Tower Society mu United States, zinathandiza mpingowo kumaliza Nyumba Yaufumu yabwino imeneyi.

Kumaliza zonsezi, Mpingo wa Saint-Louis unakondweretsedwa kukhala ndi Mbale Carey W. Barber, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, kubwera ndi kupereka Nyumba Yaufumuyo mu December 1988. Mbale Barber adandandalitsidwa kuchokera ku malikulu a Sosaite mu Brooklyn, New York, kudzapereka nyumba ya nthambi yatsopano pachisumbu choyandikana nacho cha Mauritius. Pamene abale a mu Saint-Louis anamva za ichi, m’milungu itatu yokha, anasonkha ndalama zokwanira kulipirira ulendo wake wapandege ndi wa chiŵalo cha Komiti ya Nthambi ya Mauritius kuchoka ku Mauritius kupita ku Réunion. Chifukwa cha kukula komwe kwachitika chiyambire nthaŵi imeneyo, Mpingo wa Saint-Louis wagaŵidwa. Mipingo iŵiri tsopano ikugwiritsira ntchito Nyumba Yaufumu yatsopanoyo.

Chitamando Chinka kwa Yehova

Kodi bwanji ponena za mipingo ina mu Réunion? Chifukwa cha chivomerezo chabwino ku ntchito yolalikira Ufumu, chiŵerengero cha pamisonkhano pa Nyumba Zaufumu chawonjezeka kuchoka pa 150 mpaka 200 peresenti ya chiŵerengero cha Mboni za Yehova zonse pachisumbucho. Chotero nchowonekera chifukwa chake Nyumba Zaufumu zambiri zikufunika mu Réunion. Kwenikweni, nyumba zitatu zowonjezereka zamangidwa chiyambire ija ya ku Saint-Louis, ndipo chimenecho chafikitsa chiwonkhetso chonse ku 13 mwa mipingo 19 imene iri pa chisumbupo.

Kaamba ka zonsezi, chitamando chinka kwa Yehova, amene ananeneratu kuti: ‘Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.’ (Yesaya 60:22) Mofanana ndi m’mbali zina za dziko lapansi, ulosi umenewu wakhala wowona pachisumbu chokongolachi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena