“Kuchirimika Monga Gulu Limodzi Lankhosa” mu Chad
Mofanana ndi Akristu anzawo padziko lonse, Mboni za Yehova mu Chad zimayamikira misonkhano yapachaka imene imakonzedwera kuwamangirira mwauzimu. Panopa pali mbiri ya ulendo wonka ku mipambo ya masiku a msonkhano wapadera yochitidwira kumbali yakum’mwera kwa dziko lamkati limeneli, pakati pa Afirika.
Chifukwa cha mtunda ndi kuvuta kwa kayendedwe, misonkhano mu Chad kaŵirikaŵiri imachitidwa m’magulu aang’ono, nthaŵi yochitidwa imadalira pa nyengo. Kuyambira June mpaka September, nyengo ya mvula imapangitsa kuyenda kukhala kovuta ndipo mmalo ena kosatheka konse. Masiku a msonkhano wapadera amachitidwa mvula yamphamvu itatha. Matchuthi a kothera kwa chaka ngoyenerera kaamba ka msonkhano wachigawo waukulu. Ndipo mvulayo isanayambenso mu June, misonkhano yadera ya masiku aŵiri imachitidwa.
ANALI masana a tsiku la Sande lotentha ndi lachinyontho. Nyumba Yaufumu ya ku N’Djamena, likulu la Chad, inadzaza ndi anthu 184. Mosasamala kanthu za chitungucho, iwo anali kupereka chisamaliro chosagawanika ku nkhani yaikulu yakuti, “Kuchirimika mu Mzimu Umodzi.” M’mawa mmenemo anali achimwemwe kuchitira umboni anthu atatu akusonyeza kudzipereka kwawo kwa Yehova Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi. Uwu unali msonkhano woyamba wa masiku a msonkhano wapadera asanu ndi limodzi amene woyang’anira woyendayenda wakumaloko ndi ine tinapatsidwa mwaŵi wakutumikira.
Mutu wa mipambo yakuti, “Kuchirimika Monga Gulu Limodzi Lankhosa,” unayamikiridwa mwapadera ndi Mboni 267 mu Chad. Iwo amakhala kutali ndi Akristu anzawo m’maiko ena. Komabe, kulandira kwawo chakudya chauzimu chofananacho ndikusamaliridwa m’njira yofanana kumawalimbikitsa kupitirizabe kugwira ntchito mogwirizana ndi abale awo padziko lonse. Uphungu wogwira ntchito wa programuyi unawalimbitsanso iwo kuchirimika motsutsana ndi chisonkhezero chaupalu cha dziko la Satana ndi mkuntho wa chizunzo kapena chitsutso.
Mu N’Djamena
Mpingo woyamba wa Mboni za Yehova mu Chad unapangidwa mu N’Djamena mu 1964. Tsopano uli ndi ofalitsa a mbiri yabwino Yaufumu oposa 90. Chidali chosangalatsa kuyang’ana m’gululo ndikuwona ambiri amene akhala akutumikira mokhulupirika chiyambire masiku oyambirira a ntchito mu Chad. Mbale wina adali ndi akazi atatu pamene anaphunzira choyamba chowonadi cha Baibulo. Posakhalitsa iye anawona kufunika kwa kugwirizanitsa moyo wake ndi miyezo ya Baibulo. Iye anakwatira mwalamulo mkazi wake woyamba nalekana ndi enawo, ngakhale kuti anapanga makonzedwe akuwasamalira iwo. Iye anabatizidwa mu 1973 ndipo wakhala wokangalika m’ntchito chiyambire nthaŵiyo.
Mkulu wina yemwe analimo ndi mbali m’programuyo anapyola chiyeso chowopsya cha chikhulupiriro. Mu 1975 boma la nthaŵi imeneyo linkakakamiza kutengamo mbali m’miyambo ina yomwe inazikidwa pa kulambira akufa; munthu yemwe anakana kugwirizana nawo akanaphedwa. Pamene mbaleyo anachirimika nakana kupotoza chikhulupiriro chake, akuluakulu aulamuliro anayamba kumfunafuna. Kusintha kwa boma panthaŵi yoipitsitsayo ndiko kunampulumutsa.
Pamsewu Wonka ku Pala
Titachoka ku N’Djamena, ulendo wonka kum’mwera kukatumikira misonkhano isanu yotsala unayambika. Tinadzera kaŵirikaŵiri m’njira imeneyo koma m’nyengo youma yokha. Tsopano, kumapeto kwa September kumapeto kwa nyengo yamvula, zinthu zonse zinali zobiriŵira ndi zogudira. Inali nthaŵi yabwino yoyenda. Tinadutsa minda yambiri yamapira. Ngala zake zokhala pamapesi aataliwo ondandama m’mphepete mwa msewu zinkayamba kucha. Posachedwapa akakololedwa, kuyanikidwa, ndikusungidwa m’nkhokwe zomata zomwe zimakongoletsa dzikolo. Mapira ndiwo chakudya chachikulu cha anthu ambiri a ku Chad. Amasinjidwa. Kenaka ufawo umaphikidwa nsima namadyera therere kapena ndiwo zotendera.
Pamene tinkanka kum’mwerako tinawona minda yambiri ya thonje. Chifukwa chakuti dzikolo nlathyathyathya kumbali iyi ya dzikoli, minda yochita maluwayo inawoneka ngati kuti ikufika kumalekezero adziko. Posachedwapa mabanja onse adzabwera m’mindamu kudzatola thonjelo ndimanja. Thonje ndilo mbewu yobweretsa ndalama zambiri mu Chad, matani 133,000 anakololedwa mu 1988. Pamene madzulo ankayandikira, nkuti tikudutsa Nyanja ya Léré. Panopa dzikolo nlamapiri ndipo lokongola kwabasi, makamaka panthaŵi ino ya chaka. Pokhala pamenepo panthaŵi yabwino, tinali okhoza kugula nsomba yotchedwa carp yongowedzedwa kumene imene inakazingidwa mphepete mwa msewuwo. Chinali chakudya chimene wolandira mlendo aliyense angakhale wonyadira kuchipereka.
Chinthu china chimene chimapangitsa kuyenda kukhala kovuta kwambiri m’nyengoyi nchakuti kutagwa mvula, zochinga zimaikidwa m’misewu kuletsa magalimoto. Chifukwa ninji? Kuti atetezere misewu. Chotero mitima yathu inada nkhaŵa pamene tinawona mtambo ukukhala wakuda bii kutsogolo kwathu. Kunenadi zowona sitinakondwere ndi kumanga msasa pamvula m’mphepete mwa msewu. Koma chofunika koposa, tikanachedwa kaamba ka tsiku la msonkhano wapadera wotsatira. Mwachimwemwe, mvula yamphamvu koposa yomalizira imeneyi siinagwe mu msewuwo. Ngakhale kuti tinafunikirabe kudikirira kwakanthaŵi pamalo ochinga angapo, tinafika mwachisungiko usiku umenewo ku Pala, tauni yokhala ndi anthu pafupifupi 32,000. Nzosangalatsa zotani nanga zomwe zinatiyembekezera kumeneko! Thambo lopanda mwezilo linatitheketsa kuwona bwino nyenyezi ndi Mlalang’amba, chowoneka chochitsa chidwi chimene anthu okhala mumzinda samachiwona konse. Zinatikumbutsa za chifukwa chake tiyenera kukhala ochirimika—kulemekeza Mlengi Wamkulu wa chilengedwe chozizwitsachi.
Mipingo iŵiri yaing’ono ndi gulu lokhala kutali linasonkhana pa Pala. Abale atatu achichepere anayenda mtunda wa makilomita 100 kubwera kumsonkhanoko. Popeza kuti misonkhano ya kum’mwera imakhala yaing’ono ndipo kuli akulu ochepa, mbali zina za programu zinajambulidwa pamsonkhano wa ku N’Djamena ndikuseŵeredwanso. Ichi chimatsimikizira programu yabwino ngakhale kuti pali anthu ochepa okha opezekapo. Tinali osangalala kukhala ndi munthu mmodzi waubatizo.
Gulu Lachangu ku Kélo
Wotsatira unali ulendo waufupi wonka ku Kélo, kumene anthu 194 anasonkhana kaamba ka programu pa Sande. Mabanja ambiri okhala ndi ana aang’ono anayenda mtunda wa makilomita oposa 30 kudzapezekapo. Anthu aŵiri odzipereka chatsopano anafunikira kubatizidwa. M’nyengo youma, ubatizo kaŵirikaŵiri umapereka vuto ngati msonkhano sunachitidwire pafupi ndi mtsinje; chotero, anthu ambiri anabatizidwira mu mgolo. Koma kukhalapo kwathu kumapeto kwa nyengo yamvula kunapangitsa zinthu kukhala zokhweka. Komabe, kunali koyenera kuyenda pagalimoto kwamtunda woposa makilomita 20 kunka kumalo abwino.
Mmodzi wa opita ku ubatizowo anali msungwana wachichepere amene chikhulupiriro chake chinayesedwa kowopsya. Banja lake limamulonjeza kukwatiwa ndi mwamuna amene sanali wokondwerera m’kuphunzira Baibulo. Ndiponso, mwamunayo anafuna kuti agwirizane mwamwambo osati mwa ukwati walamulo. Popeza kuti anali wofunitsitsa kupereka chikole chachikulu, banja la msungwanayo linamkakamiza kwambiri. Iye anachita kusamukira kwinakwake kwakanthaŵi kuthaŵa kugwirizana kosakhala Kwamalemba kumene banja lake linkafuna. Iye anachirimika kupyola zonsezi ndipo anapanga kupita patsogolo kwabwino. Chibatizikire, chitsutso cha banja lake chalekeka. Tikuyamikira Yehova kuti tiri ndi anthu okhulupirika oterowo pakati athu.
Abalewa kuno ali ndi zifukwa zina zokhalira oyamikira kwa Yehova. Chad anavutika ndi nkhondo yachiweniweni yowopsya ndipo kenaka, mu 1984, mudali njala yaikulu. Mkulu wakonko akukumbukira kuti nthaŵi ina njalayo iri mkati, anayang’ana m’Nyumba Yaufumu ndikuzizwa ngati aliyense wa awo omwe analipowo akakhala akali ndimoyo m’miyezi yoŵerengeka. Komabe, gulu la Yehova linapereka thandizo lachakudya, kuthetsa tsoka lawo. Kuyamikira kwawo zimenezo kukuwonekera tsopano muutumiki wawo wachangu. Muli mzimu wamphamvu wa upainiya mu Kélo. Mu October 1989, ofalitsa Aufumu oposa mbali imodzi mwa zitatu anakonza zochita zawo kotero kuti angakhale ndi phande m’ntchito yolalikira ya nthaŵi zonse.
Chokumana nacho chawo cha njala chinawaphunzitsa kuti nawonso ayenera kukhala ooloŵa manja. Chaka chatha mkulu wina mumpingo wakomweko anadwala mwadzidzidzi namwalira. Iye anasiya banja la ana asanu ndi anayi, chitsirizira anali ndi miyezi yoŵerengeka yokha. Mkazi wake anayang’anizana ndi chitsenderezo cha banja chakutengamo mbali m’miyambo yokhuza maliro yoloŵetsamo kulambira akufa. Abalewo anampatsa chilikizo lofunikira, kotero kuti anali wokhoza kupeŵa chitsenderezo chopambanitsa. Kenaka mpingo unagwirira ntchito pamodzi kumanga nyumba yake ndi ya ana achichepere, kuwonjezera pa kuthandiza mwakuthupi m’njira zina. Ichi chinatulukapo m’kuperekedwa kwa umboni wabwino m’tauniyo, kusonyeza chotulukapo chachimwemwe cha ntchito Yachikristu.—Machitidwe 20:35.
Koumra, Doba, ndi Bongor
Malo oimapo athu otsatira anali Koumra. Misewu yogangatidwa bwinoyo inaupanga ulendo wa makilomita 300 kukhala wopepuka. Tiri panjira, tinadutsa mzinda wa Moundou, malo apakati a indasitale okhala ndi anthu oposa chikwi zana limodzi. Anthu makumi asanu ndi aŵiri mphambu mmodzi anasonkhana mu Koumra. Mbale wachichepere amene sanaphunzirepo konse kusukulu analankhula papulatifomu. Iye analongosola mmene programu yophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba yophunzitsidwa pa Nyumba Yaufumu inamthandizira ndi kumpatsa chidaliro chofunikira. Iye tsopano amachititsa maphunziro m’Baibulo ndi anthu ena anayi.
Titamaliza tsiku la msonkhano wapadera mu Koumra, tinayamba kubwerera ku N’Djamena, ndipo malo athu oimapo otsatira anali pa Doba kaamba ka msonkhano wachisanu mu mpambo wathu. Anthu ena omwe anapezekapowo anagwidwa ndi mvula yomalizira ndipo anafunikira kugona m’mphepete mwa msewu. Komano, aliyense anafika panthaŵi yake kaamba ka kuyambika kwa programu pa Doba. Anthu makumi asanu ndi mmodzi anasonkhana, ndipo munthu mmodzi anadzipereka yekha kaamba ka ubatizo.
Malo oimapo omalizira anali mu Bongor. Ili ndi dera lodzala mpunga, ndipo tinazizwitsidwa kuwona mmene dzikolo liriri la thyathyathya. Chiŵerengero cha anthu opezekapo pa Bongor chinafikitsa chiwonkhetso cha onse amene anamva programuyo mu Chad ku 630. Ndipo pokhala ndi aŵiri ena omizidwa, chiwonkhetso cha anthu obatizidwa chinakwana asanu ndi anayi.
Kubwerera kwathu ku N’Djamena kunatsiriza ulendo wa makilomita pafupifupi 2,000. Chinali chosangalatsa kusonkhana ndi atumiki a Mulungu omwe anali ochirimika kwa zaka zambiri, limodzinso ndi kukumana ndi achatsopano ambiri omwe akukupanga kupita patsogolo kodabwitsa. Changu chawo kaamba ka uminisitala chinali cholimbikitsa mwapadera. Mu October 1989, panali chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 267 mu Chad, chiwonjezeko choposa 20 peresenti kuposa chaka chatha.
Ogwirizana Ngakhale Kuti Ali Kutali
Kuyenda m’dzikolo kunatipangitsa kumvetsetsa chitokoso chimene chiripo pofalitsa mbiri yabwino m’dziko mmene zinenero zoposa 200 zimalankhulidwa. Ngakhale kuti Chifrenchi ndi Chiluya ndizo zinenero zalamulo za ku Chad, pa msonkhano uliwonse wa masiku a msonkhano wapaderawo, programu inafunikira kutembenuzidwa kuchoka m’Chifrenchi kunka m’chinenero chosiyana. Ngakhale zinali choncho, anthu ambiri amene anabwera ku msonkhanowo sankalankhula chinenero cha chigawocho, choncho chidali chovutabe kuwathandiza kuti amve programu.
Mmalo onse amene tinachezera, abale ndi alongo athu anatilandira bwino. Mwachisawawa zakudya zinali nsima ya ufa wamapira kapena wampunga ndi ndiwo zomwe zatchulidwa poyambirirapo. Nthaŵi zina msungwana wachichepere ankabweretsa chakudyacho pa tray yovindikiridwa ndi nsalu yowala. Tray imeneyo inadendekeredwa, ndipo tinafunikira kukhumbira kulemekezeka kwake.
Anthu ambiri a kumpoto kwa Chad kwakulukulu ndi Asilamu; anthu akum’mwera ndi Akatolika, Protestanti, kapena okhulupirira mzimu. Boma liri ndi lamulo la ufulu wa chipembedzo, ndipo ndife achimwemwe kukhala okhoza kusonkhana pamodzi mwaufulu.
Programu ya tsiku la msonkhano wapadera inathandiza gulu lochepa la Mboni mu Chad kumvetsetsa kuti ngakhale kuti iwo ali kutali ndi abale awo m’mbali zina za dziko, iwo ngwogwirizanadi nawo m’gulu limodzi lankhosa. Iyo inawatheketsa iwo ‘kuchirimika mu mzimu umodzi’ mosasamala kanthu za zitsenderezo ndi chitsutso zimene amakumana nazo.—Afilipi 1:27.