Nkhani za Baibulo Zimene Zimasangalatsa Ana
Chiŵalo cha mpingo Wachiprotestanti m’Puerto Rico chinalembera Watch Tower Society kuti: “Ndine mphunzitsi wa ana pa sukulu yophunzitsa Baibulo. Mkati mwa chaka chapitachi, zinandichitikira zotsatirazi.
“Mabuku omwe ndinkagwiritsira ntchito kuphunzitsa ana Baibulo adatha, chotero ndinadzifunsa kuti: ‘Kodi ndichitenji tsopano?’ Pamene ndinayang’ana m’mashelufu m’chipinda changa m’mene ndiri ndimabuku pafupifupi zana limodzi, ndinawona bukhu lachikasu lokhala ndi mutu wakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Ndinasankha kugwiritsira ntchito bukhu limeneli.
“Ndinapukuta fumbi ndikuyamba kuligwiritsira ntchito pa Sande iriyonse m’kuphunzitsa kwanga. Anawo anasangalala ndi bukhulo, ndipo tinali tisanamalize kwenikweni mutu umodzi pamene iwo anafuna kuti tiyambe wina. Chotulukapo: Chaka chinatha, ndipo ndinamaliza bukhu lonselo. Anawo anali achimwemwe kwabasi, ndipo ineyo ndikuthokoza kwenikweni. Liridi bukhu lokongola, lomvekera bwino ndi lolondola.”
Tikulingalira kuti nanunso mudzalikonda bukhu lokhala ndi zithunzithunzi zokongola, ndi zilembo zazikulu. Nkhani zake za Baibulo zokwanira 116 zimadziŵitsa woŵerengayo chifuno cha Baibulo. Nkhani zimenezi ziri mwadongosolo la kuchitika kwa zinthuzo. Mudzapeza zimenezi kukhala zothandiza kwenikweni m’kuphunzira, pamene zinthu zinachitika mogwirizanitsa ndi zochitika zina. Ngati mungakonde kulandira bukhu lothandiza limeneli lamasamba 256, chonde lembani ndi kutumiza kapepala kali pansipa.
Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba la Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. (Kunja kwa Zambia, lemberani ku nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 2.)