Galamukani! Imayambukira Miyoyo
Galamukani! imafalitsidwa m’zinenero 64, ndipo imasindikizidwa pa avareji ya magazini 12,980,000 pa kope limodzi. Aŵerengi ake padziko lonse amasangalala nayo ndikupezamo phindu, monga momwe makalata awo achiyamikiro akusonyezera. Ofesi yanthambi ya Watch Tower m’Ghana, Kumadzulo kwa Afirika, inalandira ndemanga zotsatirazi:
“Ndine mmodzi wa aŵerengi okhazikika a magazini anu Abaibulo a Galamukani!, othokozedwa kwambiri ndi ophunzitsa. Zamkati mwa magaziniŵa zasonkhezera moyo wanga mwanjira zambiri! Nthaŵi zonse ndimakonda kuwaŵerenga motengeka kwambiri kwakuti ndimanyalanyaza chakudya nthaŵi iriyonse pamene nditenga kope, ngakhale kuti ndine wa Tchalitchi cha Roma Katolika.”
Tikulingalira kuti mosasamala kanthu za kuzama kwanu m’chipembedzo chanu, nanunso mudzapindula ndi nkhani zochititsa chidwi za m’Galamukani!
Ndingakonde kuti munditumizire magazini a Galamukani! kunyumba kwanga. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 2.)