Dalirani pa Nyonga Yopatsidwa ndi Mulungu
Mfundo Zazikulu Zochokera m’Timoteo Wachiŵiri
YEHOVA amapatsa atumiki ake mphamvu kuti apirire ziyeso ndi chizunzo. Ndipo Timoteo ndi Akristu ena anafunikira nyonga yopatsidwa ndi Mulungu chotani nanga! Moto unasakaza Roma mu 64 C.E., ndipo panamveka mphekesera kuti Wolamulira Nero ndiye anauchititsa. Kuti adzichinjirize, iye anatulira Akristu mlanduwo, ndipo mwachiwonekere ichi chinayambitsa funde la chizunzo. Kukuwonekera kuti panthaŵiyo (pafupifupi 65 C.E.), mtumwi Paulo anaponyedwanso m’ndende m’Roma. Ngakhale kuti anayang’anizana ndi imfa, iye kenaka analemba kalata yake yachiŵiri kwa Timoteo.
Kalata ya Paulo inakonzekeretsa Timoteo kutsutsa ampatuko ndi kuima nji pamaso pa chizunzo. Inamlimbikitsa kupita patsogolo mwauzimu ndikusimba za mikhalidwe ya Paulo m’ndende. Kalatayo inathandizanso oiŵerenga kudalira pa nyonga yopatsidwa ndi Mulungu.
Vutikani ndi Masautso Ndipo Phunzitsani ndi Chifatso
Mulungu amapereka nyonga kuti tipirire chizunzo monga alengezi a mbiri yabwino. (1:1-18) Paulo sanamuiŵale konse Timoteo m’mapemphero ake, ndipo anakumbukira chikhulupiriro chake chopanda chinyengo. Mulungu anapatsa Timoteo si ‘mzimu wa mantha; komatu wa mphanvu ndi chikondi ndi chidziletso.’ Chotero sanachite manyazi pochitira umboni ndi kuvutika ndi masautso kaamba ka mbiri yabwino. Iye anasonkhezeredwanso ‘kugwira chitsanzo cha mawu a moyo’ omvedwa kwa Paulo, mongadi momwe tiyenera kumamatira mosamalitsa ku chowonadi Chachikristu ngakhale kuti ena akuchifufunuka.
Zinthu zimene Paulo anaziphunzitsa zinafunikira kuikiziridwa kwa amuna okhulupirika omwe akaphunzitsa ena. (2:1-26) Timoteo anafulumizidwa kukhala msirikali wabwino wa Kristu, wokhulupirika povutika ndi masautso. Paulo iyemwini anavutika m’maunyolo a m’ndende kaamba ka kulalikira mbiri yabwino. Iye analimbikitsa Timoteo kuchita bwino koposa kuti akhale wantchito wovomerezedwa wa Mulungu, natsutse mawu opanda pake amene akalakwira chimene chiri chopatulika. Ndipo anauzidwa kuti kapolo wa Ambuye ayenera kulangiza ena ndi chifatso.
Lalikirani Mawu!
Nyonga yopatsidwa ndi Mulungu ikakhala yofunikira kuyang’anizana ndi masiku otsiriza ndi kusunga chowonadi Chamalemba. (3:1-17) Kuchokera mwa anthu osapembedza mukauka anthu ‘ophunzira nthaŵi zonse koma osakhoza konse kupeza chizindikiritso cha chowonadi.’ ‘Anthu oipa ndi onyenga [oterowo] adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.’ Komabe, Timoteo anafunikira ‘kukhalabe mu izi zimene anaziphunzira.’ Tiyenera kutero nafensotu, podziŵa kuti ‘lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iriyonse yabwino.’
Timoteo anafunikira kutsutsa ampatuko ndi kutsiriza uminisitala wake. (4:1-22) Iye akatero ‘mwakulalikira mawu’ ndikuwatsatira. Ichi chinali chofunika kwambiri, popeza kuti mpingo unayang’anizana ndi “nyengo yovuta,” (NW) chifukwa chakuti ena ankaphunzitsa chiphunzitso chonama. Mboni za Yehova nazonso tsopano zimamamatira ku Mawu a Mulungu, kuwalalikira mofulumira mumpingo ndi kwa anthu okhala kunja, ngakhale m’mikhalidwe yovuta. Paulo ‘anasunga chikhulupiriro,’ ngakhale kuti anakanidwa ndi ena. Koma ‘Ambuye anampatsa mphamvu, kuti mwa iye kulalikidwa kwa mbiri yabwino kungatsirizidwe mokwanira.’ Nafenso tidaliretu pa nyonga yopatsidwa ndi Mulungu ndikupitirizabe kulalikira mbiri yabwino.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 31]
Msirikali Wabwino: Paulo anafulumiza Timoteo kuti: ‘Umve zoŵaŵa pamodzi nane monga msirikali wabwino wa Kristu Yesu. Msirikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usirikali.’ (2 Timoteo 2:3, 4) Msirikali Wachiroma woyenda pansi ‘anavutika ndi zoŵaŵa’ ponyamula zida zolemera, nkhwangwa, mtanga, kamba wamasiku atatu, ndi zinthu zina. (Bukhu 3 la Josephus lakuti Wars of the Jews, mutu 5) Iye sanalondole mapindu achuma, amene sakakondweretsa mbuye wake, ndipo zowonongedwa zake zinalipiriridwa. Mofananamo, Mkristu amavutika ndi mayeso chifukwa chokhala ‘msirikali wabwino wa Kristu.’ Ngakhale kuti iye angagwire ntchito yakudziko kuti achite mathayo Amalemba, sayenera kudziloŵetsa mopambanitsa m’zinthu zakuthupi kotero kuti aleka kumenya nkhondo yauzimu. (1 Atesalonika 2:9) Pochitira umboni kunyumba ndi nyumba, iye amamenyetsa ‘lupanga la mzimu, ndiko kuti, mawu a Mulungu,’ ndipo amathandiza anthu kumasuka ku chinyengo chachipembedzo. (Aefeso 6:11-17; Yohane 8:31, 32) Popeza kuti moyo uli pachiswe, asirikali Achikristu onse apitirizebe kukondweretsa Yesu Kristu ndi Yehova Mulungu mwanjira imeneyi.