Panali Pambuyo Pake Pomwe Sanaganizire!
CHINALI chaka cha 609 B.C.E. Kumaloko kunali ku Yerusalemu. Mlankhuliyo adali mneneri Yeremiya. Iye ananeneratu za chiwonongeko cha mzinda wake wopatulika wokondedwa, Yerusalemu, chiwonongeko chomwe chinkadza chifukwa chakuti Ayuda anafulatira Yehova ndipo anadzimiza m’kulambira milungu yonyenga. Iwo anadziloŵetsa m’kulambira konyansa kwa kugonana pamalo okwezeka, anapereka nsembe zomwera kwa milungu yachikunja, analambira dzuŵa ndi mwezi ndi nyenyezi, anafukizira Baala, napereka ana awo nsembe kwa Moleki.—1 Mafumu 14:23, 24; Yeremiya 6:15; 7:31; 8:2; 32:29, 34, 35; Ezekieli 8:7-17.
M’maso mwawo Yeremiya anawoneka kukhala woitanira tsoka, wodzipereka mopambanitsa, wosakhutira ndi chirichonse ndi aliyense. Kwa zaka 38 Yeremiya anakhala akuwachenjeza; ndipo nzika za Yerusalemu zinakhala zikumseka kwa zaka 38. Kufikira nthaŵiyi, anthuwo anakhala akukana Yehova, akumati sanali munthu wofunika kuda naye nkhaŵa. Iwo anati: ‘Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa’ natinso, “Yehova wataya dziko, Yehova sapenya.”—Zefaniya 1:12; Ezekieli 9:9.
Mneneri Yeremiya ndi Ezekieli anakhala akulalikira za chiwonongeko cha Yerusalemu, koma palibe chimene chinachitika. Chotero Aisrayeli sanakhulupirire kuti masomphenya amenewo akakwaniritsidwa m’tsiku lawo, akumati: ‘Masiku achuluka, ndi masomphenya alionse apita pachabe?’ Koma yankho la Yehova ku funsoli linali lakuti: ‘Masiku ayandikira . . . Pakuti ine ndine Yehova, ndidzanena, ndi mawu ndidzanenawo adzachitika, osazengerezekanso; pakuti m’masiku anu, nyumba yopanduka inu, ndidzanena mawu ndi kuwachita.’—Ezekieli 12:22-25.
Mu 609 B.C.E., inafika nthaŵi ya Yehova yakukwaniritsa mawu ake. Mzinda wa Yerusalemu unalaliridwa ndi magulu ankhondo Achibabulo pambuyo pakuti Yeremiya anakhala akupereka chenjezo kwa pafupifupi zaka makumi anayi. Miyezi khumi mphambu isanu ndi itatu pambuyo pake malingawo anagumulidwa, kachisi anatenthedwa, ndipo anthu ambiri anatengedwera kundende m’Babulo. Monga momwe kunanenedweratu, mzindawo unawonongedwa ndi lupanga ndi njala ndi mliri.—2 Mafumu 25:7-17; 2 Mbiri 36:17-20; Yeremiya 32:36; 52:12-20.
Yeremiya anali wolondola. Anthuwo anali olakwa. Panali pambuyo pake pomwe sanaganizire! Masomphenyawo sanali a zaka zakutsogolo. Anali a m’tsiku lawo.
Iyitu simbiri wamba. Zimene zinachitikira Yerusalemu zinali zaulosi. Zinachitira chithunzi chinachake chomwe chikudza. Chikristu Chadziko chamakono chimadziveka dzina la Kristu ndikunena kuti chili muunansi wapangano ndi Mulungu; komabe chimayenda m’mapazi a nzika za Yerusalemu wakale. Kwakukulukulu, matchalitchi a Chikristu Chadziko amaphunzitsa ziphunzitso zachikunja, ngodetsedwa ndi chisembwere chakugonana, amachilikiza ziŵembu zandale zadziko, amachilikiza nkhondo zadziko, kulandira chisinthiko ndikukankhira pambali Mulungu monga Mlengi, kusekerera nsembe za mamiliyoni a ana osabadwa zoperekedwa pa guwa lansembe la zoyenerera, ndipo mwachisawawa amatengera nthanthi za anthu, akumanena kuti Baibulo ndi nthano ndi nthanthi.
Monga momwedi anthu a m’Yerusalemu anamsekera Yeremiya, momwemonso Chikristu Chadziko chimaseka Mboni za Yehova lerolino. Chenjezo la Mbonizo la chiwonongeko cha Armagedo chikudzacho limanyalanyazidwa kukhala lopanda pake. Chikristu Chadziko chimati, ‘Mulungu alibe kanthu ndi dziko lapansi. Mlekeni adzilamulira kumwamba; ife tidzilamulira dziko lapansi. Ndipo ngati Armagedo ibwera, siidzachitika mu mbadwo wathu. Tinaimvapo kale nkhani imeneyo. Sitidzanyengedwa ndi zimenezo!’
Kodi kumeneku kudzakhala kudzibwereza kwa mbiri? Kodi idzakhala nthaŵi ina imene mamiliyoni adzazindikira kuti panali pambuyo pake pomwe sanaganizire?