Ino Ndiyo Nthaŵi Yakumfuna Yehova
‘Yehova m’mwamba ana ŵeramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna [Yehova, “NW”].’—SALMO 14:2.
1, 2. (a) Kodi ambiri amamulingalira motani Mulungu wowona, Yehova? (b) Kodi timadziŵa bwanji kuti Yehova akudziŵa za kusakondweretsedwa kwa anthu?
LEROLINO, Mulungu wowona, Yehova, akukanidwa ndi osakhulupirira Mulungu, osadziŵa, olambira milungu yonyenga, ndi mamiliyoni amene amati amakhulupirira Mulungu koma amamkana ndi ntchito zawo. (Tito 1:16) Ambiri amakhulupirira monga momwe anachitira wanthanthi Wachijeremani wa m’zaka za zana la 19 Nietzsche kuti “Mulungu ngwakufa.” Kodi Yehova sakudziŵa za kusakondweretsedwa kwakukulu kumeneku? Ayi, popeza kuti anauzira Davide kulemba kuti: ‘Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe [Yehova, NW]. Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino.’—Salmo 14:1.
2 Davide anapitiriza kuti: ‘Yehova m’mwamba anaŵeramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna [Yehova, NW].’ Inde, Mfumu Ambuye amadziŵa awo amene akufuna kumdziŵa ndi kumtumikira. Chotero, kumfuna kwathu tsopano nkofunika. Kudzatanthauza kusiyana pakati pa moyo wosatha ndi kuzimiririka kosatha.—Salmo 14:2; Mateyu 25:41, 46; Ahebri 11:6.
3. Kodi ndikuthekera kotani komwe kulipo kaamba ka mtsogolo?
3 Chotero, tingawone chifukwa chake kuli kofunika motero kuti tithandize ena kufuna Yehova tsopano. Padakali anthu mamiliyoni ambiri omwe sanakumanepo ndi mmodzi wa Mboni za Yehova kapena kumvapo “mbiri yabwino ya ufumu.” Ndipo sitikudziŵa kuti kaya chiŵerengero cha ‘khamu lalikulu’ chidzafika pati ‘chisautso chachikulu’ chisanachitike. Koma palidi kuthekera kwakuti anthu owonjezereka adzamfuna ndikumpeza Yehova Mulungu mtsogolomo kusanakhale kuchedwa. Tsopano funso nlakuti, Kodi tingachitenji kuti tithandize ambiri owonjezereka kumpeza Mulungu?—Mateyu 24:14, NW; Chibvumbulutso 7:9, 14.
4, 5. M’kufunafuna kwawo mulungu, kodi anthu ambiri amakondanji?
4 Anthu ambiri m’dziko lerolino adakafunafunabe, koma kodi akufunafunanji? Ochepera akumfunadi Mulungu wowona yekha, Yehova. Ambiri amakonda mulungu yemwe amamvana ndi zikhumbo zawo zaumwini ndi malingaliro olakwa. Monga momwe wofufuza zolingalira za anthu wa ku U.S. George Gallup, Jr., anafotokozera kuti: “Inu ndithudi simumapeza kusiyana kwenikweni pakati pa opita kutchalitchi ndi osapita kutchalitchi m’nkhani za kunama, kuthaŵa msonkho, ndi kuba, kwakukulukulu chifukwa chakuti pali chipembedzo chamayanjano chochuluka.” Iye akuwonjezera kuti “ambiri amakonda chipembedzo chomwe nchabwino kwa iwo ndipo chimawasangalatsa . . . Munthu wina anachitcha icho kukhala chipembedzo chosankha mogwirizana ndi chikondwerero cha munthuwe.”
5 Ena anganene kuti, “Chipembedzo changa nchabwino kwa ine.” Ndithudi, funso lenileni liyenera kukhala lakuti, “Kodi chipembedzo changa nchwabwino kwa Mulungu?” Zowonadi, anthu ambiri a m’Chikristu Chadziko ndi Chihindu ngokhutira ndi kulambira mafanizo ndi mafano awo. Anthu ambiri odzitcha Akristu amapeza kuti mulungu Wautatu wopanda dzina ngwokwanira kwa iwo. Ndipo Asilamu oposa 900 miliyoni amakhulupirira Allah. Kumbali ina, mamiliyoni a osakhulupirira Mulungu amati kulibeko Mulungu.
Awo Amene Amafunikira Thandizo
6. Kodi aŵerengi ambiri a Nsanja ya Olonda atumba chiyani?
6 Koma bwanji za ife amene timaŵerenga mokhazikika maganizi ano? Tafunafuna Mulungu wowona ndipo tampeza. Tawatsimikizira mawu awa a Yakobo 4:8 kukhala owona: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” Mwakuyanjana mokangalika ndi mpingo Wachikristu, tayandikira chifupi ndi Mulungu, ndipo tadziwonera tokha mmene Yehova akuyandikirira pafupi nafe.—Yohane 6:44, 65.
7. Kodi timadziŵa bwanji kuti padakali anthu ambiri omwe adakali okondweretsedwa ndi kukhala okangalika m’chowonadi?
7 Komabe, tikudziŵa kuti padakali ambiri omwe ali achimwemwe kuyanjana mwa apa ndi apo ndi anthu a Yehova komatu sanachitepobe kanthu kuyandikira chifupi ndi Yehova mwakudzipereka ndi ubatizo. Kodi ichi tachidziŵa bwanji? Pafupifupi anthu mamiliyoni khumi anapezekapo pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu mu 1990. Koma kodi ndiangati omwe akufalitsa mokangalika mbiri yabwino Yaufumu? Oposa mamiliyoni anayi okha. Ichi chikutanthauza kuti tiri ndi mabwenzi a chowonadi pafupifupi mamiliyoni asanu ndi limodzi omwe nthaŵi zina amasangalala kugwirizana nafe koma omwe sanayambebe kugwiritsira ntchito chinenero choyera mwakulalikira mbiri yabwino Yaufumu. Mosakaikira, m’zochitika zamwadzidzidzi ambiri angamalankhulire Yehova ndi ulamuliro wa Ufumu wake. Komabe, iwo sanadzizindikiritsebe monga Mboni za Yehova. Awanso tikufuna kuwathandiza.—Zefaniya 3:9; Marko 13:10.
8, 9. (a) Kodi Yehova akutilimbikitsa kuchitanji? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kupanda nzeru kunyalanyaza uphungu wa Yehova?
8 Tikufuna kuŵalimbikitsa kukhala Mboni zachimwemwe, zokangalika za Yehova m’mbali yomalizira ya ntchito yaikulu yomwe ikukwaniritsidwa tsopano padziko lonse. Chonde tamvani chiitano chachikondi cha Yehova pa Miyambo 1:23 chakuti: ‘Tembenukani pamene ndikudzudzulani; tawonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga, ndikudziŵitsani mawu anga.’ (Yerekezerani ndi Yohane 4:14.) Nkolimbikitsa chotani nanga kudziŵa kuti Yehova adzavomereza kutenga kwathu masitepe abwino a kudzizindikiritsa ife eni ndi dzina lake ndi kulambira! Ndithudi, sitifuna kuphatikizidwa pakati pa omwe akulongosoledwa pa Miyambo 1:24, 25 kuti: ‘Chifukwa ndaitana, ndipo munakana; ndatambasula dzanja langa, ndipo panalibe analabadira; koma munapeputsa uphungu wanga wonse; ndi kukana kudzudzula kwanga.’
9 Awo amene amanyalanyaza uphungu wa Yehova wakuti amfunefune pamene adakapezeka ndi awo amene amaleka kupanga chosankha chawo kufikira atadzachiwonadi chisautso chachikulu chitayamba adzapeza kuti adikirira kwa nthaŵi yaitali kwambiri. Kachitidwe koteroko kakasonyeza kusoŵeka kwa chikhulupiriro ndi nzeru ndipo kukakhala kulakwira chisomo cha Yehova.—2 Akorinto 6:1, 2.
10. Kodi nchifukwa ninji mphwayi ndi kusakondweretsedwa ziri zowopsa?
10 Kuti tichitire fanizo kufunika kwa kuchitapo kanthu mofulumira, kodi mungatsatire malangizo a dokotala kokha pamene muli kale ndi chibayo? Kapena, pamene munazindikira zizindikiro zoyamba za matendawo? Pamenepo kodi nchifukwa ninji mukadikirira kwa nthaŵi yaitali osadzipatula nokha ku dziko lodwala la Satana ndikukhala kumbali ya Yehova ndi Mboni zake? Zotulukapo za kuchita mphwayi, kusakondweretsedwa, ndi kunyalanyaza zamveketsedwa bwino lomwe pa Miyambo 1:26-29: ‘Inetu ndidzachitira chiphwete tsoka lanu, ndidzatonyola pakudza mantha anu . . . Pamenepo adzandiitana, koma sindidzavomera; adzandifunatu, osandipeza ayi; chifukwa anada nzeru, sanafuna kuopa Yehova.’ Lolani kuti tisadzapezedwe ‘tikufuna Yehova’ pamene kudzakhala kuchedwa!
11. Kodi pali thandizo lotani kwa anthu amene akufuna kutumikira Mulungu?
11 Anthu ena amene amaŵerenga magazini ano angakhale adakafunafunabe Mulungu wowona. Ndife osangalala kuti mukuumirirabe m’kufunafuna kwanu. Tikupemphera kuti chidziŵitso chanu cha Baibulo chikusonkhezereni kupanga kachitidwe kabwino kuchilimika kaamba ka chowonadi. Khalani otsimikiziridwa kuti mpingo uliwonse wa Mboni za Yehova ngwokonzekera kukuthandizani m’kufunafuna kwanu.—Afilipi 2:1-4.
Nthaŵi ya Changu ndi Kuchitapo Kanthu
12, 13. Kodi nchifukwa ninji tifunikira kuchitapo kanthu ponena za kulambira kowona?
12 Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti onse achitepo kanthu kudzizindikiritsa iwo eni ndi Yehova Mulungu ndi kulambira kwake kowona? Chifukwa chakuti zochitika zadziko zikunka kuchimake. Zochitika za mbiri yadziko zikusintha mofulumira kuposa pakuzindikira kwa munthu. Ino sindiyo nthaŵi yakuima chiliri kapena kukhala wofunda. Yesu anafotokoza momvekera bwino kuti: “Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.” Iye ananenanso kuti: ‘Pakuti amene aliyense adzachita manyazi chifukwa cha ine ndi mawu anga, Mwana wa munthu adzachita manyazi chifukwa cha iye, pamene adzafika ndi ulemerero wake ndi wa Atate, ndi wa angelo oyera.’—Mateyu 12:30; Luka 9:26.
13 Ino ndiyo nthaŵi yofunikira changu ndi kuchitapo kanthu! Tikudziŵa kumene zochitika zadziko zikunka, ndipo Armagedo ikuyandikira kwabasi. Chotero, chiitano nchakuti funani Yehova tsopano lisanafike ‘tsiku la mkwiyo wake,’ pamene iye angapezeke. Pa chisautso chachikulu kudzakhala kuchedweratu.—Zefaniya 2:2, 3; Aroma 13:11, 12; Chibvumbulutso 16:14, 16.
14. Kodi tiri ndi zifukwa zotani zofunira Mulungu?
14 Ndithundi, anthu onse ayenera kumafuna chiyanjo cha Mulungu tsopano. Mtumwi Paulo analongosola moyenerera pa Machitidwe 17:26-28 motere: ‘Ndi mmodzi [Mulungu] analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zawo, ndi malekezero a pokhala pawo; kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife; pakuti mwa iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu.’ Mawu omalizirawo akuti, ‘pakuti mwa iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda ndi kupeza mkhalidwe wathu,’ amatipatsa chifukwa chokwanira cha kufunira Mulungu. Tithokoza chisomo cha Yehova, tikukhala m’mbali yachilengedwe yokhala ndi zamoyo yaing’ono koma yofunika ya dziko lapansi laling’onong’onoli. Kodi sitiyenera kukhala oyamikira kwa Mfumu Ambuye wa chilengedwe chonse? Ndipo kodi sitiyenera kusonyeza chiyamikiro chathu m’njira zogwira ntchito?—Machitidwe 4:24.
15. (a) Kodi katswiri wa mbiri yakale Arnold Toynbee analingalira chiyani kukhala chifuno cha chipembedzo chapamwamba? (b) Kodi tiyenera kuchitanji kuti tikhale okhoza kulemekeza Mulungu?
15 Katswiri wa mbiri yakale Arnold Toynbee panthaŵi ina adalemba kuti: “Cholinga chenicheni cha chipembedzo chapamwamba ndicho kuwunikira uphungu wauzimu ndi chowonadi chomwe chiri mbali yeniyeni m’miyoyo yambiri yomwe ingachifikire, kotero kuti moyo uliwonse ungakhale wokhoza kukwaniritsa cholinga chenicheni cha Munthu. Cholinga chenicheni cha munthu ndicho kulemekeza Mulungu ndi kusangalala Naye kosatha.” (An Historian’s Approach to Religion, masamba 268-9) Kuti tilemekeze Mulungu, tiyenera choyamba kumfuna ndikupeza chidziŵitso cholongosoka cha iye ndi zifuno zake. Chotero, chiitano ichi cha Yesaya nchoyenerera: ‘Funani Yehova popezeka iye, itanani iye pamene ali pafupi; woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwerere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti iye adzakhululukira koposa.’—Yesaya 55:6, 7.
Kodi ndi Thandizo Logwira Ntchito Lotani Limene Tingapereke?
16. (a) Kodi ndichitokoso chotani chomwe chikuyang’anizana ndi mpingo Wachikristu? (b) Kodi ndi m’njira zogwira ntchito zotani mmene tingathandizire ena kutumikira Yehova?
16 Mamiliyoni a anthu okondwerera omwe sanakhalebe ofalitsa okangalika amapereka chitokoso kwa tonsefe. Kodi nchiyani chomwe tikuchita m’njira yogwira ntchito monga akulu, atumiki otumikira, apainiya, ndi ofalitsa kuthandiza mabwenzi achowonadi amenewo kukhala otengamo mbali okangalika m’kulambira kowona limodzi nafe? Njira imodzi yoperekera thandizo logwira ntchito pamene kuli kofunika ndiyo kufika panyumba zawo ndi kuwatengera ku misonkhano pa Nyumba Yaufumu kotero kuti nawonso angasangalale ndi mapindu a mzimu wa Yehova pamaziko okhazikika. Uphungu wa Paulo kwa Ahebri, m’mutu 10, mavesi 24 ndi 25, ngwofunika koposa lerolino monga mmene unaliri panthaŵiyo: ‘Ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muwona tsiku liri kuyandika.’ Tikulimbikitsa onse amene akufuna kudziwonera okha ubwino wa Yehova kusonkhana ndi Mboni za Yehova mokhazikika pa Nyumba Yaufumu yawo yakumaloko.
17. Ngati tikufuna kuthandiza ophunzira Baibulo kupita patsogolo m’kufunafuna kwawo Yehova, kodi ndimafunso otani omwe afunikira kuyankhidwa?
17 Ngati timaphunzira Baibulo ndi munthu wina amene amapezekapo mokhazikika pamisonkhano, kodi tingamuthandize iye kuyeneretsedwa monga wofalitsa wa mbiri yabwino? (Onani Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 97-9.) Ndipo iye atakhala wofalitsa wosabatizidwa, kodi chiitano chakupita nafe m’ntchito yolalikira poyera yokhazikika ndi kumaphunziro ndi maulendo obwereza chimaperekedwa? (Onani kope la December 1, 1989, la Nsanja ya Olonda, tsamba 31.) Kufotokoza m’mawu ŵena, achatsopano oterowo atayeneretsedwa, kodi timaŵalimbikitsa mwakuwalola kudziwonera okha zotulukapo zabwino za ntchito yathu yolalikira?—Mateyu 28:19, 20.
Yehova Ngwoyenerera Kufunidwa
18. Kodi Yehova wasonyeza motani chifundo chake kwa anthu?
18 Chifukwa cha nsembe yadipo ya Kristu Yesu, Yehova samasunga machimo athu akale motsutsana nafe ngati tilapa ndi kusonyeza chikhulupiriro. Onani mawu awa a Davide: ‘Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Pakuti monga m’mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuwopa iye. Monga kum’mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuwopa iye. Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.’—Salmo 103:10-14; Ahebri 10:10, 12-14.
19. Kodi pali chilimbikitso chotani kwa awo amene angakhale anachoka m’chowonadi?
19 Yehova alidi Mulungu wooloŵa manja ndi wachifundo. Ngati tipita kwa iye modzichepetsa ndi molapa, iye amakhululuka ndi kuiwala. Iye samasunga zinthu kukhosi kosatha ndi chotulukapo cha chizunzo cha moto wamuyaya wa helo. Ayi, ziri monga momwe Yehova analongosolera kuti: ‘Ine, inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha ine mwini; ndipo ine sindidzakumbukira machimo ako.’ Ha, chimenecho chiyenera kukhala cholimbikitsa chotani nanga kwa omwe angakhale anachoka m’chowonadi ndipo ananyalanyaza unansi wawo ndi Yehova! Nawonso akulimbikitsidwa kufunafuna Yehova tsopano ndikubwerera m’mayanjano okangalika ndi anthu a dzina lake.—Yesaya 43:25.
20, 21. (a) Kodi nchitsanzo cholimbikitsa chotani chimene tiri nacho mu Yuda wakale? (b) Kodi nzika za Yuda zinafunikira kuchitanji kuti zipeze dalitso la Yehova?
20 Mogwirizana ndi zimenezi tiri ndi chitsanzo cholimbikitsa cha Mfumu Asa wa Yuda wakale. Iye anathetseratu kulambira konyenga mu ufumu wake, koma ziyambukiro za kulambira kwachikunja zinatsalirabe. Cholembedwacho pa 2 Mbiri 15, mavesi 2 mpaka 4, chikutiuza zimene mneneri Azariya anauza Asa monga chokumbutsa kuti: ‘Yehova ali nanu; mukakhala ndi iye, mukamfuna iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani. Masiku ambiri tsono Israyeli anakhala wopanda Mulungu woonayo, . . . koma pamene anatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israyeli m’kusautsidwa kwawo, ndi kumfuna, anampeza.’
21 Yehova sanaseŵere chibisalirano ndi Mfumu Asa koma ‘anapezeka.’ Kodi ndimotani mmene mfumuyo inachitira ndi uthengawo? M’mutu umodzimodziwo, mavesi 8 ndi 12 akuyankha motere: ‘Ndipo pakumva Asa mawu aŵa, . . . , analimbika mtima, nachotsa zonyansazo m’dziko lonse . . . nakonza guwa la nsembe la Yehova lokhala pakhomo pa likole la Yehova. [Yuda] naloŵanso chipangano chakufuna Yehova Mulungu wa makolo awo ndi mtima wawo wonse, ndi moyo wawo wonse.’ Inde, iwo anafuna Yehova mofunitsitsa ‘ndi mtima wawo wonse, ndi moyo wawo wonse.’ Kodi chinatulukapo nchiyani kwa mtunduwo? Vesi 15 likutiuza kuti: ‘Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wawo wonse, namfunafuna ndi chifuno chawo chonse; ndipo anampeza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo.’
22. Kodi nchiyani chimene chimatilimbikitsa kukhala okangalika tsopano mu utumiki wa Yehova?
22 Tsopano, kodi chimenecho sichilimbikitso chakuti tonsefe tichitepo kanthu ponena za kulambira koyera kwa Yehova? Tikudziŵa kuti pali kuthekera kwakuti mamiliyoni ambiri angamalemekeze Yehova. Mosakaikira ambiri a iwo akupanga masinthidwe m’miyoyo yawo kotero kuti afikiritse ziyeneretso Zamalemba kaamba ka utumiki wa Yehova. Ena akukula m’chidziŵitso ndi chikhulupiriro, akumfuna Yehova, ndipo posachedwapa adzasonkhezeredwa kugawana chinenero choyera ndi ena mwakuwapatsa kumvetsetsa kwakuya kwa chowonadi chonena za Yehova ndi Ufumu wake. Ndipo kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti tonsefe tifunefune Yehova tsopano pamene iye adakapezeka? Chifukwa chakuti dziko lake latsopano lolonjezedwa liri pafupi kwenikweni!—Yesaya 65:17-25; Luka 21:29-33; Aroma 10:13-15.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Kodi ndani amasonyeza kusakondweretsedwa kulinga kwa Mulungu wowona, Yehova?
◻ Kodi chipembedzo chimayambukira mkhalidwe kumlingo wotani?
◻ Kodi pali kuthekera kotani kwa kuwonjezeka pakati pa Mboni zokangalika?
◻ Kodi nchifukwa ninji ino ili nthaŵi ya changu ndi kuchitapo kanthu?
◻ Kodi nchifukwa ninji Yehova ali woyenerera kumfunafuna?
[Chithunzi patsamba 10]
Mabwenzi ambiri a Mboni za Yehova amene amafikapo pa Chikumbutso ngothekera kudzakhala atumiki a Mulungu
Chiŵerengero cha opezekapo pa Chikumbutso mu 1990: 9,950,058
Chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa: 4,017,213
[Chithunzi patsamba 12]
M’tsiku la Mfumu Asa, mtunduwo unatembenukira kwa Yehova