Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 6/15 tsamba 22-26
  • Kuchitira Umboni m’Falansa Dziko la Zinthu Zosiyanasiyana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchitira Umboni m’Falansa Dziko la Zinthu Zosiyanasiyana
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • ALSACE
  • BRITTANY
  • MAPIRI A ALPS
  • CHIGWA CHA LOIRE
  • CORSICA
Nsanja ya Olonda—1991
w91 6/15 tsamba 22-26

Kuchitira Umboni m’Falansa Dziko la Zinthu Zosiyanasiyana

FALANSA ndidziko la zinthu zosiyanasiyana zambiri. Mapiri aatali, zitunda zokwezeka ndi zotsika, materezi amatanthwe osesedwa ndi mphepo yamkuntho, magombe ofunda a mchenga, minda ya dzinthu, mafamu aang’ono ochinjirizidwa, minda yaikulu ya mpesa, kodyetsera ziŵeto, nkhalango za mitengo ya nkungudza yobiriŵira nthaŵi zonse ndi mitengo yogwetsa masamba ake, timidzi, midzi, matauni, mizinda yaikulu yamakono​—Falansa iri nzonsezi, ndi zina zowonjezereka.

Chinkana kuti mbali yaikulu ya dera la kumidzi yakhalabe ndi kukongola kwake, zochitika za chitaganya cha Falansa zasintha kwambiri m’zaka zaposachedwapa. “Chitaganya cha Falansa sichiri m’nyengo ya vuto,” likutero kope la 1989 la Francoscopie, “koma chiri m’chipwirikiti chenicheni. Zomangira za chitaganya, makhalidwe, miyezo yamwambo, ndi malingaliro zikusintha kwakukulukulu pa liŵiro lofulumira.”

Masinthidwe amwadzidzidzi ameneŵa ayambukiranso zipembedzo. Ngakhale kuti Chikatolika chidakali chipembedzo cha anthu ochuluka, icho tsopano ndimwambo kuposa chipembedzo chokhala ndi chiyambukiro chenicheni pa moyo wa ziŵalo zambiri. Kuipidwa komawonjezereka kwa anthu ndi makhalidwe auzimu kwaimitsa kufutukuka kwa matchalitchi.

Mosiyana kwenikweni, ntchito ya Mboni za Yehova m’Falansa yapita patsogolo mofulumira m’zaka zoŵerengeka zapitazo. Kuchokera ku Alsace kumpoto koma chakum’maŵa mpaka ku Brittany wa ku Atlantic, kuchokera ku mapiri aatali a Alps mpaka ku Chigwa cha Loire chotsika, ngakhale pa chilumba cha Mediterranean cha Corsica, Mboni zimayang’anizana ndi mikhalidwe yosiyanasiyana ndi kukumana ndi anthu okhala ndi makulidwe osiyanasiyana. Tiyeni tipite paulendo wa zithunzithunzi ndi kuwona mmene kuliri kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu m’Falansa, dziko la zinthu zosiyanasiyana.​—Mateyu 24:14.

ALSACE

Yochita malire ndi Jeremani, Alsace ndi gawo lodziŵika kaamba ka minda yake ya mpesa ndi midzi yodzala maluŵa okongola. Strasbourg, likulu lake, lakhala malikulu a Chiprotestanti kuyambira nyengo ya Kusintha, ndipo anthu a ku Alsace mwachisawawa amalilemekeza kwakukulu Baibulo. Mboni za Yehova zakhala zikulalikira mbiri yabwino ya Ufumu m’derali kuyambira kuchiyambi cha zaka za zana lino. Lerolino, ntchitoyo njokhazikitsidwa bwino, monga kwasonyezedwa ndi chokumana nacho cha msungwana wina wachichepere wotchedwa Sylvie, yemwe anagwiritsira ntchito mwaŵi wolalikira kusukulu.

Pokambitsirana ndi anzake amkalasi angapo, Sylvie anatchula chifuno cha moyo ndi ziyembekezo za mtsogolo. Mnyamata wina anakondweretsedwa kwabasi kulola Sylvie ndi Mboni ina kumfikira kunyumba. “Ngakhale kuti wachichepere Wachikatolikayu anali mnyamata wotumikira pa guwa, anali ndi mafunso ambiri amene sanayankhidwepo,” anatero Sylvie. “Tinagwiritsira ntchito Baibulo kuyankha mafunso ena, ndipo analola phunziro Labaibulo lokhazikika.” Mnyamatayo anabatizidwa pambuyo pa chaka chimodzi ndipo atayeneretsedwa analoŵa muuminisitala wanthaŵi zonse monga mpainiya wokhazikika. Sylvie nayenso watenga mwaŵi wa utumiki umenewo kuyambira pamenepo.

BRITTANY

Loloŵerera m’Atlantic, Brittany ndi gawo la mwambo Wachikatolika wolimba. Komabe, kupyolera m’zoyesayesa zosalekeza za Mboni, chiŵerengero cha anthu chomawonjezereka m’derali chikulandira uthenga wa Ufumu. Nachi chitsanzo cha zimene zikuchitika m’chigawo chakumpoto koma chakumadzulo kwa Falansa chimenechi.

“Okwatirana achichepere anasamukira m’nyumba yosanja pamwamba pa yathu,” ikusimba motero Mboni yakumaloko. “Nthaŵi ina pambuyo pake, ndinakumana ndi mkazi wachichepereyo pamasitepe, atanyamula mwana wake wamwamuna. Podziŵa kuti dzina lamwanayo linali Jonathan, ndinafunsa ngati iye anadziŵa magwero a dzinalo. ‘Ndiganiza kuti nlochokera m’Baibulo, koma ndizokhazo zimene ndimadziŵa,’ anayankha motero. Iye anamvetsera kulongosola kumene ndinapereka, ndipo anati onse aŵiri iye ndi mwamuna wake anakondweretsedwa ndi Baibulo. Ngakhale kuti tinali ndi makambitsirano owonjezereka, panalibe zotulukapo zenizeni panthaŵiyo.

“Pambuyo pake, okwatiranawo anandipempha uphungu pa mavuto akutiakuti. Ndinagwiritsira ntchito Baibulo kuŵayankha, ndipo anakondweretsedwa ndi chidziŵitso chimene linapereka. Ndinaŵapemphanso kuphunzira Baibulo. Tsiku lotsatira mkazi wachichepereyo anavomera. Milungu ingapo pambuyo pake, mwamuna wake anagwirizana nafe m’phunziro. Tsopano onse aŵiri ndi Mboni zobatizidwa.”

MAPIRI A ALPS

Mapiri a Alps ngotchuka chifukwa cha mawonekedwe okongola. Anthu amapita kumeneko kukakhumbira mapiri aatali, makamaka Mont Blanc, phiri lalitali koposa Kumadzulo kwa Yuropu. M’chigawo chinonso, chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu amene amalemekeza Mlengi chikuwonjezeka. Anthu a misinkhu yonse ndi a mitundu yonse akuloŵa m’ntchito yawo, monga momwe cholembedwa chotsatirachi chikusonyezera.

Achichepere anayi m’deralo anali ndi mbiri yoipa kwenikweni. Iwo anali kuba magalimoto ndi katundu wina, ankaledzera kaŵirikaŵiri, anagwiritsira ntchito ndi kugulitsa mankhwala ogodomalitsa, ndipo anali oloŵetsedwa m’kuchita uchiwerewere ndi kukhulupirira mizimu. Iwo anali alova ndipo nthaŵi zambiri anali m’vuto kwa apolisi, ndipo onse anakhalapo m’ndende. Komabe, onse anayi anamva za chowonadi muubwana wawo chifukwa chakuti mabanja awo adaphunzira ndi Mboni za Yehova nthaŵi ndi nthaŵi.

Pambuyo pa zaka zingapo zokhala ndi moyo woipa, mmodzi wa achicheperewo anasintha mtima nasankha kutumikira Yehova. Chimenechi chinachititsa zochitika zoyambukirana. Tsiku lina apolisi anali kufufuza monga mwanthaŵi zonse, ndipo anafunsa mmodzi wa anyamatawo kutsegula chola chake. Poyembekezera kupeza mankhwala ogodomalitsa kapena katundu wobedwa, iwo anadabwa kupeza Baibulo lokha ndi timabuku. Mnyamatayo anagwiritsira ntchito Baibulolo kufotokoza zimene zinadzetsa masinthidwe m’moyo wake. Popeza zimenezo kukhala zovuta kukhulupirira, wapolisi wina anafunsa kuti: “Kodi ukutanthauza kuti sumasutanso, kumwa, kapena kugwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa?” Apolisi pomalizira pake anavomereza kufotokozako ndipo anamlola kupita popanda kumvutitsanso. Lerolino anyamata anayi ameneŵa ngobatizidwa, onse akutumikira monga atumiki otumikira mumpingo, ndipo atatu ndi apainiya okhazikika.

CHIGWA CHA LOIRE

Chigwa cha Loire chimatchedwa munda wa Falansa. Chimachokera ku Orléans, makilomita 110 kum’mwera kwa Paris, kufika ku matsiriro a Mtsinje wa Loire ku Gombe la Atlantic. Chigawo chimenechi nchodziŵika chifukwa cha nyumba zazitali zambiri zokhala ndi malinga olimba, malo akale okhalamo mabanja achifumu ndi ogonamo posaka nyama. Muli mipingo ya Mboni za Yehova m’matauni onse aakulu m’derali.

Tsiku lina mkati mwakupuma kusukulu, Emma, msungwana wamng’ono wokonda kucheza ndi wachikondi wa zaka zisanu ndi chimodzi zakubadwa, anabwerera m’kalasi kukapatsa moni mphunzitsi wake. Pokhala wodabwa kuwona mphunzitsi wake akusuta, iye anagwetsa misozi nathaŵa. Mphunzitsiyo anamtsatira namfunsa chifukwa chake iye anali kulira, koma Emma sananene kanthu. Mphunzitsiyo atafunsitsitsa, Emma anasisima nayankha kuti: “Nchifukwa chakuti mukusuta. Mudzadwala ndi kufa!”

Tsiku lotsatira mphunzitsiyo anaitana amayi a Emma kuŵauza mmene anakhudzidwira ndi kachitidwe ka mwana wamkaziyo. Chotero amayiwo anafotokoza kaimidwe ka Mboni ponena za fodya. Ndiyeno mphunzitsiyo anaulula kuti banja lake linampemphapo kuleka kusuta, koma sizinagwire ntchito. Komabe, panthaŵi ino, iye anasonkhezeredwa ndi kachitidwe kowona mtima ka Emma chakuti analeka kusuta m’masiku aŵiri okha.

CORSICA

Chinkana kuti chilumba cha Corsica chimatchedwa “chilumba chonunkhira,” nchotchukanso chifukwa cha mzimu wankhalwe wa nzika zake, kaŵirikaŵiri wotulukapo nkhondo za mabanja zokhetsa mwazi. Kwazaka zambiri Mboni zinkawonedwa monga chipembedzo “chochokera Kumtunda.” Komabe, mphamvu ya chowonadi cha Baibulo ikusintha mitima ya anthu ambiri kumeneko.

Mboni ina yobatizidwa chatsopano inasimba kuti pamene inabwera kuchoka kutchuthi inapeza kuti ziŵiya zonse zokhoza kunyamulidwa pa famu yake zinabedwa. Iye anafotokoza kuti: “Mwakukhulupirira Yehova, ndinali wokhoza kuchita mosiyana ndimmene ndikanachitira kumbuyoku.” Pamene ankalankhula kwa anansi ake apafupi, iye mokhazika mtima anafotokoza kutaikiridwa kwake.

“Pambuyo pake, anansi apafupi anali ndi mavuto. Ndinasiya ntchito yanga kupita kukaŵathandiza. Masiku angapo pambuyo pake, ndinalandira foni kuchokera kwa mmodzi wa iwo kundipempha kupita mofulumira. Poganizira kuti iye analinso m’vuto, ndinapita pamenepo. Iye anandipatsa pokhala nandifunsa kuti: ‘Kodi mukudziŵa chifukwa chimene ndakuitanirani? Ndakuitanirani ziŵiya zanu. Ndine amene ndinaziba. Koma pamene ndinawona mkhalidwe wanu wachifundo ndi waubwenzi, ndinati, “Sindingawachitire zimenezo!” Ndipo pambuyo potithandiza, sindinakhozenso kugona tulo usiku.’” Chikristu chowona chogwira ntchito chinatsogolera ku zotulukapo zabwino.

Kumapeto a nkhondo yadziko yachiŵiri, pamene ntchito yochitira umboni wa Ufumu inayambanso m’Falansa, munali Mboni zokwanira 1,700 zokha m’dziko lonselo. Ntchito yofikira anthu onse ndi uthenga wa Ufumu inawoneka yosatheka. Komabe, m’kupita kwa zaka, Yehova wadalitsa anthu ake m’Falansa ndi ziŵiya zofunikira​—malo osindikizira, Nyumba Zaufumu, Nyumba Zosonkhanira, ndi zina zotero​—ndi mzimu wofunitsitsa kukwaniritsa ntchitoyo. Lerolino, pokhala ndi alaliki achangu oposa 117,000, uthenga wakuti Ufumu wa Yehova mwa Kristu ndiwo chiyembekezo chokha cha anthu ukulalikidwa m’dziko lonse limeneli la zinthu zosiyanasiyana.

[Mapu/​Zithunzi patsamba 23]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

FALANSA

BRITTANY

CHIGWA CHA LOIRE

MAPIRI A ALPS

ALSACE

NYANJA YAMCHERE YA ATLANTIC

NYANJA YA MEDITERRANEAN

ENGLISH CHANNEL

CORSICA

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena