Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 6/15 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Yendani Monga Momwe Mwalangizidwa ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kulemekeza Moyo ndi Mwazi Mwaumulungu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
Nsanja ya Olonda—1991
w91 6/15 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Kodi Mkristu ayenera kukana mwamphamvu chotani kuthiridwa mwazi komwe kwalamulidwa kapena kuvomerezedwa ndi khoti?

Mkhalidwe uliwonse umakhala wosiyana, chotero palibe lamulo lokwaniritsa mikhalidwe yonse pankhaniyi. Akristu ngodziŵika chifukwa chopereka mwaulemu ‘zake za Kaisara kwa Kaisara,’ kumvera malamulo a boma. Komabe, iwo amazindikira kuti thayo lawo lalikulu ndilo kupereka ‘zake za Mulungu kwa Mulungu,’ osati kuswa lamulo lake.​—Marko 12:17.

Aroma 13:1-7 amafotokoza unansi wa Akristu kwa ‘maulamuliro aakulu’ aboma. Maboma oterowo ali ndi ulamuliro wakupanga malamulo kapena kupereka zitsogozo, kaŵirikaŵiri kuti apititse patsogolo ubwino wa anthu. Ndipo maboma ‘amagwira lupanga’ kuti akhwimitse malamulo awo ndi ‘kukwiyira wochita choipa mogwirizana ndi malamulo awo.’ Pokhala ogonjera ku maulamuliro aakulu, Akristu amafuna kumvera malamulo ndi zigamulo za khoti, koma kugonjera kumeneku kuyenera kukhala ndi poimira. Ngati Mkristu wapemphedwa kugonjera ku chinachake chimene chikaswa lamulo lapamwamba la Mulungu, lamulo laumulungu limakhala loyamba; ndilo loyambirira.

Malamulo ena amakono omwe mwa iwo okha ali abwino angagwiritsiridwe ntchito molakwa kuvomereza kukakamiza kuthira mwazi Mkristu. M’chochitikachi Akristu ayenera kutenga kaimidwe kamodzimodziko kamene mtumwi Petro anakatenga: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”​—Machitidwe 5:29.

Yehova analamula Aisrayeli kuti: ‘Mulimbikepo ndi kusadya mwaziwo; popeza mwazi ndiwo moyo, nimusamadya moyo pamodzi ndi nyama yake.’ (Deuteronomo 12:23) Matembenuzidwe a Baibulo Lachiyuda a mu 1917 amati: “Tangolimbikani mtima m’kusadya mwazi.” Ndipo Isaac Leeser anamasulira vesili motere: “Tangolimbanipo kuti musadye mwazi.” Kodi zimenezo zikumvekera ngati kuti atumiki a Mulungu anafunikira kukhala osasamala kapena osaikako mtima posunga lamulo lake?

Ndi chifukwa chabwino, Akristu akhala otsimikiza mtima kotheratu kumvera Mulungu, ngakhale ngati boma linawalamula kuchita zosiyana. Profesa Robert L. Wilken akulemba kuti: “Akristu sanakane kokha utumiki wankhondo [Wachiroma] koma anakananso kuvomera udindo waunyinji kapena kutenga thayo lolamulira mizinda.” (The Christians as the Romans Saw Them) Kukanako kukanatanthauza kutchedwa akuswa lamulo kapena kuponyedwa m’bwalo lazilombo Lachiroma.

Lerolino Akristu ayenera kukhalanso ochilimika, ogamulapo molimbika mtima kusaswa lamulo laumulungu, ngakhale ngati kuchita tero kukawaika paupandu winawake ku maboma akudziko. Lamulo lapamwamba koposa m’chilengedwe chonse​—lamulo la Mulungu​—limafuna kuti Akristu asale mwazi, monga momwedi akulamulidwa kupeŵa dama (mkhalidwe woipa wachisembwere). Baibulo limazitcha ziletso zimenezi kukhala ‘zoyenera.’ (Machitidwe 15:19-21, 28, 29) Lamulo laumulungu loterolo silifunika kuwonedwa mopepuka, kukhala chinthu choyenera kulabadiridwa kokha ngati kuli kothekera kutero kapena ngati silipereka mavuto. Lamulo la Mulungu liyenera kulabadiridwa!

Pamenepo, tingamvetsetse chifukwa chimene Mkristu wachichepere wotchulidwa patsamba 17 anauzira khoti kuti “anakulingalira kuthiridwa mwazi kukhala kulakwira thupi lake ndipo anakulinganiza ndi kugwiriridwa chigololo.” Kodi mkazi Wachikristu aliyense, wachichepere kapena wachikulire, angagonjere kugwiriridwa chigololo popanda kuyesayesa kudzichinjiriza, ngakhale ngati panali chilolezo chalamulo chakuti dama logwiriridwa chigololo lingachitidwe?

Mofananamo, msungwana wazaka 12 zakubadwa wogwidwa mawu patsamba limodzimodzilo sanasiye chikaikiro chirichonse kuti ‘iye akhoza kulimbana ndi kuthiridwa mwazi kulikonse kololedwa ndi khoti ndi nyonga yake yonse imene angakhoze, kuti akafuula ndi kupalapata, kuti akachotsa chiwiya chothirira mwazicho pamkono pake ndikuti akayesayesa kutaira mwazi wokhala m’thumbamo pakama pake.’ Iye anatsimikiza mtima zolimba kumvera lamulo laumulungu.

Yesu anathaŵa m’dera lina pamene anthu anafuna kumpanga kukhala mfumu. Mofananamo, ngati kukuwoneka kukhala kotheka kuthiridwa mwazi kovomerezedwa ndi khoti, Mkristu angasankhe kusankhalapo kaamba ka kuswa lamulo la Mulungu koteroko. (Mateyu 10:16; Yohane 6:15) Panthaŵi imodzimodziyo, Mkristu ayenera kufunafuna mwanzeru thandizo lamankhwala losiyana, mwakutero kupanga kuyesayesa kwenikweni kwakusunga moyo ndikupezanso thanzi labwino.

Ngati Mkristu anapanga kuyesayesa kwamphamvu kupeŵa kuswa lamulo la Mulungu pa mwazi, olamulira angamulingalire kukhala wakuswa lamulo kapena kumpangitsa kuloŵa m’milandu. Ngati chilango chingatulukepodi, Mkristuyo ayenera kukuwona kukhala kuvutika chifukwa cha chilungamo. (Yerekezerani ndi 1 Petro 2:18-20.) Koma m’zochitika zambiri, Akristu apeŵa kuthiridwa mwazi ndipo ndi chisamaliro chabwino chamankhwala anachira, kotero kuti panalibe mavuto alamulo otulukapo. Ndipo chofunika koposa, iwo asunga umphumphu wawo kwa Mpatsi wa Moyo ndi Woweruza Waumulungu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena