Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 7/1 tsamba 32
  • “Kodi Nchifukwa Ninji Makanda Amafa?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kodi Nchifukwa Ninji Makanda Amafa?”
  • Nsanja ya Olonda—1991
Nsanja ya Olonda—1991
w91 7/1 tsamba 32

“Kodi Nchifukwa Ninji Makanda Amafa?”

Ichi nchimene banja lomwe linaferedwa ana aang’ono aŵiri linafuna kudziŵa. Mwamuna wa ku Willowick, Ohio, U.S.A., analongosola kuti:

“Posachedwapa, tsoka linachitika m’banja langa. Mchemwali wanga anaferedwa ana ake aang’ono aŵiri m’ngozi yoipitsitsa yagalimoto. Ndithudi, banja lonselo linakanthidwa ndi chisoni ndikusoŵa chochita. Minisitala wawo wa Baptist sanapereke chitonthozo Chamalemba chirichonse. Iye ankangoti, ‘Chinali chifuniro cha Mulungu’ ndikuti, ‘Mulungu anafuna angelo aŵiri owonjezereka.’

“Chinkana kuti panali nthaŵi yochepa kwambiri yakufufuza, ndinatembenukira ku bukhu la Kukambitsirana za m’Malemba pansi pa mutu wakuti ‘Kodi Nchifukwa Ninji Makanda Amafa?’ M’masiku ndi milungu yotsatirapo, mkazi wanga ndi ine takhala okhoza kugaŵana ndi banja langa mayankho owona a mafunso awo ambiri, monga ngati, ‘Kodi nchifukwa ninji makanda amafa?’ ‘Kodi chiri chifuniro cha Mulungu kumalanda makolo ana awo?’ ndipo, lofunika kwambiri, ‘Kodi pali chiyembekezo chanji chakuwawonanso ana okondedwa ameneŵa?’ Makolo anga anena kuti akakonda kubwera ku Nyumba Yaufumu mtsogolo.”

Bukhu la Kukambitsirana za m’Malemba liri ndi mitu yankhani zazikulu yoposa 70. Kuphatikizapo “Imfa,” “Helo,” “Moyo,” “Kutengedwa m’Thupi,” “Kudziveka Thupi Lanyama,” “Kugonana,” “Kukhulupirira Mizimu,” ndi ina yambiri. Zosonyezera zake nkhani ndi malemba zokuta masamba asanu ndi aŵiri zingakuthandizeni kupeza mayankho mofulumira. Kuti mulandire kope, chonde dzazani ndi kutumiza kapepalaka.

Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba, lamasamba 448 la Kukambitsirana za m’Malemba. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 2.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena