Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 7/15 tsamba 3
  • Kufunafuna Dongosolo Ladziko Latsopano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufunafuna Dongosolo Ladziko Latsopano
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Sikufunafuna Kopanda Mavuto
  • Zolinganiza za Munthu Mkufuna Kudzetsa Chisungiko cha Padziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Mtundu wa Anthu Ulakalaka Dziko Latsopano
    Galamukani!—1992
  • “Dongosolo La Dziko Latsopano”—Chiyambi Chake Chinali Chosalimba
    Galamukani!—1996
  • Dziko Latsopano—Kodi Lidzadza Konse?
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 7/15 tsamba 3

Kufunafuna Dongosolo Ladziko Latsopano

“PALIBE mamapu otitsogolera kumene tikumkako, ku dziko ili latsopano lodzipangira tokha. Pamene dziko liyang’ana kumbuyo zaka makumi asanu ndi anayi za nkhondo, chidani, kukaikirana, tiyeni tiyang’anenso kutsogolo​—ku zaka za zana latsopano, ndi zaka chikwi zatsopano, za mtendere, ufulu ndi kukhupuka.”

George Bush, pulezidenti wa ku United States anathirira ndemanga zimenezo pa January 1, 1990. Muuthenga wofananawo, Mikhail Gorbachev, pulezidenti wa ku Soviet Union anapereka lingaliro la kugwirizana m’ma 1990 kuchotsapo “dziko la mantha ndi kusadalirana, zida zosafunika, malingaliro achikale andale zadziko ndi ziphunzitso za nkhondo, ndi zopinga zopeka pakati pa anthu ndi maboma.” Inasimba motero Mainichi Daily News ya ku Japan ya January 3, 1990.

Mwachidziŵikire, ziyembekezo zinali zazikulu. Zinkaterobe chaka chimodzi pambuyo pake. Mu uthenga wa State of the Union pa January 29, 1991, Pulezidenti Bush anasonya ku nkhondo ya ku Persian Gulf nati: “Chimene chiri pachiswe nchoposa dziko limodzi laling’ono [Kuwait], ndichinthu chachikulu​—dongosolo ladziko latsopano mmene mitundu yosiyanasiyana igwirizanitsidwa ndi cholinga chimodzi cha kufikira ziyembekezo za dziko lonse za anthu: mtendere ndi chisungiko, ufulu ndi kugwira ntchito kwa lamulo.”

Sikufunafuna Kopanda Mavuto

Mavuto ambiri amalepheretsa munthu kufunafuna kwake dongosolo ladziko latsopano. Kulimbana kwazida kumakhaladi chopinga. Akuloza ku nkhalwe zochitika mu Iraq ndi Kuwait panthaŵiyo, magazini a Time a January 28, 1991, anati: “Pamene mabomba ndi mamisaelo ankaponyedwa, ziyembekezo za dongosolo ladziko latsopano zinangokhala chipwirikiti chozoloŵereka.” Magaziniwo anawonjezera kuti: “Palibe amene ayenera kukhulupirira chinyengo chirichonse chakuti dongosolo ladziko latsopano lotamandidwa koposalo liripo kapena layandikira.”

Kugwirizana kwamitundu yonse sikunafikiridwepo, ndipo zimenezi zimalepheretsa zoyesayesa za anthu zakukhazikitsa dongosolo ladziko latsopano. M’lipoti lowonekera m’magazini akuti The World & I (January 1991), akatswiri anasanthula “malamulo akunja omabuka a maulamuliro amphamvu koposa ndi ziyambukiro zawo zothekera pa dongosolo ladziko latsopano.” Mkonzi anagamula kuti: “Mbiri imapereka lingaliro lakuti mpata wokhala pakati pa nkhondo ndi mtendere ngwabwino panthaŵi yabwino koposa. Kugwirizana kwamitundu yonse, makamaka pakati pa mphamvu zazikulu, nkofunika koposa kaamba ka kusintha kwachipambano kuchokera ku Nkhondo Yoputana ndi Mawu kumka ku dongosolo ladziko latsopano.”

Mavuto a malo okhala nawonso amatsekereza dongosolo ladziko latsopano limene anthu ambiri amalilingalira. Mu State of the World 1991 (lipoti la Worldwatch Institute), Lester R. Brown anati: “Palibe amene anganene motsimikizira mmene dongosolo latsopano lidzakhalira. Koma ngati titi tipange mtsogolo mwabwino kaamba ka mbadwo wotsatira, pamenepo kuyesayesa kwakukulu kofunikira kukonzanso kunyonyotsoka kwa malo okhala a pulaneti lino kudzatenga chisamaliro chonse cha zinthu zadziko kwazaka makumi ambiri zirinkudza.” Lipotilo linafotokoza kuti kuipitsidwa kwa mpweya “kunafika pamlingo wowopsa thanzi m’mazana a mizinda ndi wowononga zomera m’maiko ambiri.” Lipotilo linawonjezera kuti: “Pamene chiŵerengero cha anthu okhala pa pulaneti lino chikukwera, chiwerengero cha mitundu ya zomera ndi zinyama chikutsika. Kuwonongedwa kwa malo okhala ndi kuipitsa kukuchepetsa zamoyo zosiyanasiyana za dziko lapansi. Kutentha komawonjezereka ndi kuwonongedwa kwa chifunda thambo kukhoza kuwonjezera zowonongedwa.”

Mwachiwonekere pamenepa, kufunafuna dongosolo ladziko latsopano kwa anthu kuli kodzala ndi mavuto. Kodi kufunafunaku kudzatsimikizira kukhala kwachipambano? Kodi kukhoza kunenedwa kuti dziko latsopano layandikira? Ngati nditero, kodi zidzachitika motani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena