Dziko Latsopano—Kodi Lidzadza Konse?
PA APRIL 13, 1991, George Bush, amene panthaŵiyo anali prezidenti wa United States, anakamba nkhani mu Montgomery, Alabama, yamutu wakuti: “Kuthekera kwa Dongosolo la Dziko Latsopano.” Pomaliza, iye anati: “Dziko latsopano limene layandikira . . . , lili dziko labwino koposa la zotumbidwa zatsopano.”
Miyezi iŵiri pambuyo pake The Bulletin of the Atomic Scientists inati pamene maboma Achikomyunizimu anagwa Kummaŵa kwa Ulaya, “dongosolo la dziko latsopano lozikidwa pamtendere, chilungamo, ndi demokrase linaoneka kukhala litayandikira.”
Nkhani zoterozo za dziko latsopano zapitirizabe mpaka mu 1993. The New York Times inasimba mu January za chipangano chimene chinapangidwa cha kuchepetsa zida za nyukliya. Nyuzipepalayo inati: “Zimenezo zimaika Amereka ndi Russia ‘pamphembenu pa dziko latsopano,’ malinga ndi mawu osankhidwa bwino a Prezidenti Bush.”
Milungu iŵiri pambuyo pake prezidenti watsopano wa United States, Bill Clinton, analengeza m’nkhani yake yoyambirira kuti: “Leroli, pamene dongosolo lakale likupita, dziko latsopano lili laufulu kwambiri komanso losakhazikika kwambiri.” Iye ananenadi kuti: “Dziko latsopano limeneli lalemeretsa kale miyoyo ya mamiliyoni a anthu a ku Amereka.”
Chotero pakhala manenanena ambiri ponena za dziko latsopano—losiyana ndi labwinopo. Malinga nkunena kwa nduna ina, mkati mwa nyengo yaifupi chabe, George Bush analankhula kwanthaŵi 42 m’ndemanga zake zapoyera ponena za “Dongosolo la Dziko Latsopano.”
Koma kodi nkhani yoteroyo njachilendo? Kodi inamvedwapo kale?
Palibe Chatsopano Kwenikweni
M’May 1919, pambuyo penipeni pa Nkhondo Yadziko I, gulu la Federal Council of the Churches of Christ in America linachita msonkhano mu Cleveland, Ohio, kumene ‘kuthekera kwa dziko latsopano ndi labwinopo’ kunalengezedwa. Wolankhula wina ananenetsa kuti: “Lidzakhala dziko latsopano mmene mkhalidwe wa mpikisano udzakhala utaloŵedwa m’malo ndi mkhalidwe wa mayanjano ndi ubale. Lidzakhala dziko latsopano mmene mkhalidwe wa umodzi udzakhala utaloŵa m’malo mkhalidwe wa magawano . . . Lidzakhala dziko latsopano mmene ubale ndi ubwenzi zidzakhala zitaloŵa m’malo mikangano iliyonse kusiyapo kokha nkhondo ya kulimbana ndi kuipa.”
Kodi matchalitchi anakhulupirira kuti dziko latsopano limeneli likabwera mwanjira yanji? Kodi ndimwanjira ya boma la Ufumu wa Mulungu lolonjezedwa m’Baibulo? Ayi. Iwo anayembekezera gulu la ndale zadziko kuti libweretse dziko latsopano loterolo. Mtsogoleri watchalitchi wina ananena kuti: “Chimene leroli timachitcha Chigwirizano cha Mitundu ndicho chotulukapo chosapeŵeka cha chikhulupiriro chathu chonse Chachikristu ndi cha zoyesayesa zake m’dziko lino.” Atsogoleri atchalitchi a m’nyengo imeneyo anachirikizadi Chigwirizano cha Mitundu monga “chisonyezero cha ndale zadziko cha Ufumu wa Mulungu padziko lapansi.”
Kumbali ina, wolamulira wamphamvu m’Germany, Adolf Hitler, anatsutsa Chigwirizano cha Mitundu ndipo m’ma 1930 anakhazikitsa Ulamuliro Wachitatu wa Germany. Iye ananena kuti Ulamuliro wake ukakhala kwa zaka chikwi ndipo ukakwaniritsa zimene Baibulo limanena kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo ungazikwaniritse. “Ndikuyamba ndi achichepere,” anatero Hitler. “Mwa kuwagwiritsira ntchito ndikhoza kupanga dziko latsopano.”
Hitler anamangitsa bwalo lalikulu kwambiri mu Nuremberg losonyezeramo mphamvu za Nazi. Motero, zipilala zazikulu zokwanira 144 zinamangidwa paguwa mamita pafupifupi 300 m’litali mwake. Nchifukwa ninji zipilalazo zinali 144? Baibulo limanena za anthu 144,000 amene akalamulira limodzi ndi “Mwanawankhosa” Yesu Kristu, ndi kuti ulamuliro wawo ukakhala kwa zaka chikwi. (Chivumbulutso 14:1; 20:4, 6) Mwachionekere, sikuti zinangochitika chabe kuti zipilala zomangidwa mu stediyamu ya Nuremberg zinali 144, popeza kuti zolembedwa zimasonyeza bwino lomwe kuti nduna za Nazi zinakonda kugwiritsira ntchito chinenero cha Baibulo ndi mawu ake ophiphiritsira.
Kodi nchiyani chinali chotulukapo cha zoyesayesa za anthu za kukwaniritsa chimene Baibulo limati Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo udzachikwaniritsa?
Kulephera kwa Zoyesayesa za Munthu
Zochitika za m’mbiri zimachitira umboni bwino lomwe kuti Chigwirizano cha Mitundu chinalephera kudzetsa dziko latsopano lamtendere. Gulu limenelo linagwa pamene mitundu inagwera m’Nkhondo Yadziko II. Ndiponso, pambuyo pa zaka 12 zokha, Ulamuliro Wachitatuwo unakhala bwinja. Kunali kulephera kotheratu, konyazitsa banja la mtundu wa anthu.
Kupyola m’mbiri yonse zoyesayesa za anthu za kupanga dziko latsopano lamtendere zalephera kotheratu. Henry Kissinger, mlembi wakale wa boma la United States anati: “Kutsungula kulikonse kumene kwakhalapo kwagwa potsirizira pake. Mbiri yangokhala nthano ya zoyesayesa zimene zinalephera, ya ziyembekezo zimene sizinakwaniritsidwe.”
Tsopano bwanji ponena za dongosolo la dziko latsopano limene atsogoleri adziko akhala akulilengeza posachedwapa? Kubuka kwa chiwawa cha mafuko kwachititsa manyazi lingaliro lenilenilo la dziko latsopano loterolo. Mwachitsanzo, pa March 6 wapitayu, wolemba nkhani William Pfaff ananena monyodola kuti: “Dongosolo la dziko latsopano lafika. Likugwiradi ntchito ndipo nlatsopanodi, limadalitsa kuukira ena, limavomereza nkhanza ndi kukangana kwa mafuko kukhala mkhalidwe wololedwa padziko lonse.”
Mikangano yoipitsitsa ndi nkhanza zimene zachitika chiyambire kugwa kwa Chikomyunizimu nzochititsa kakasi. Ngakhale George Bush, atatsala pang’ono kutula udindo wake pansi mu January, anavomereza kuti: “Dziko latsopano likhoza, m’kupita kwanthaŵi, kukhala lowopsa mofanana ndi lakale.”
Kodi Pali Chifukwa Chokhalira ndi Chiyembekezo?
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti mkhalidwewo uli wopanda chiyembekezo? Kodi dziko latsopano langokhala loto chabe? Mwachionekere, anthu alephera kupanga dziko latsopano. Koma bwanji ponena za lonjezo la Mlengi la kuchita zimenezo? “Koma monga mwa lonjezano lake [Mulungu] tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano,” limatero Baibulo.—2 Petro 3:13.
Miyamba yatsopano imene Mulungu akulonjeza ndiyo ulamuliro watsopano wolamulira dziko lapansi. Ulamuliro watsopano umenewu ndiwo Ufumu wa Mulungu, boma lake lakumwamba limene Yesu anaphunzitsa anthu kulipempherera. (Mateyu 6:9, 10) Boma lakumwamba limenelo panthaŵiyo lidzaumbidwa ndi Yesu Kristu ndi olamulira anzake okwanira 144,000, ndipo dziko lapansi latsopanolo lidzakhala chitaganya chatsopano cha anthu. Inde, iwo adzakhala m’dziko latsopano laulemerero akumachilikiza ulamuliro wa Mulungu mokhulupirika.
Boma la Ufumu wa Mulungu lidzalamulira dziko latsopano lolonjezedwalo. Chotero dziko latsopano limeneli silidzakhala lopangidwa ndi munthu. “Ufumu wa Mulungu sumatanthauza konse chochitika chochitidwa ndi anthu kapena ulamuliro umene akhazikitsa,” ikulongosola motero insaikulopediya ina ya Baibulo. “Ufumuwo ndiwo chochitika chaumulungu, osati chokwaniritsa cha anthu kapena chokwaniritsa cha Akristu odzipatulira.”—The Zondervan Pictorial Encyclopedia of the Bible.
Dziko latsopano lokhala pansi pa Ufumu wa Mulungu liridi lotsimikizirika kudza. Mukhoza kudalira lonjezo la kudza kwake chifukwa chakuti lonjezolo laperekedwa ndi “Mulungu, wosanamayo.” (Tito 1:2) Chonde talingalirani kuti dziko latsopano la Mulungu lidzakhala la mtundu wotani.
[Mawu a Chithunzi patsamba 24]
Chithunzithunzi cha NASA