Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 11/8 tsamba 11-12
  • Mtundu wa Anthu Ulakalaka Dziko Latsopano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtundu wa Anthu Ulakalaka Dziko Latsopano
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndidziko Latsopano Lotani?
  • Kodi Anthu Angadzetse Mtendere Wosatha ndi Chisungiko?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Dziko Latsopano—Kodi Lidzadza Konse?
    Galamukani!—1993
  • Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Angaichititse Ndani?
    Galamukani!—2004
  • Kodi Ndani Amene Angabweretse Mtendere Wokhalitsa?
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 11/8 tsamba 11-12

Mtundu wa Anthu Ulakalaka Dziko Latsopano

KULAKALAKA dziko latsopano sikunakhale kwakukulu koposa tsopano. Zaka makumi asanu ndi atatu zapita za nkhondo, zipwirikiti, njala, miliri, upandu, ndi kuipitsidwa kwa mpweya zakhala zowopsa. Mtundu wa anthu ukufuna kulowa m’dziko latsopano lamtendere. Molabadira chikhumbo chimenechi, atsogoleri adziko ayamba kulankhula za kupanga dziko latsopano loterolo.

Mosakaikira mwamva kapena kuwerenga mawu olankhulidwa ndi anthu otchuka akuti dziko latsopano liri pafupi. Pulezidenti George Bush wa United States anati polankhula mu September 1991: “Usiku uno, pamene ndiwona zochitika za demokrase zikufunyululuka padziko lonse lapansi, mwinamwake—mwinamwake tikuyandikira kwambiri dziko latsopano limenelo koposa ndi kale lonse.”

Monga umboni wakuti dziko latsopano liri pafupi, atsogoleri adziko akusonya kukutha kwa Nkhondo Yapakamwa ya pakati pa maiko a Kummaŵa ndi maiko a Kumadzulo. Ndithudi, dziko lapeza mpumulo pang’ono pamene maprogramu a kuchepetsa zida akugwira ntchito. Kuchepetsedwa kwa zida zanyukleya kumalimbikitsa chiyembekezo cha anthu ambiri cha kudza kwa dziko latsopano lamtendere ndi chisungiko.

Mu April wachaka chino, George McGhee, wachiŵiri kwa nduna yowona zakunja panthaŵi ya ulamuliro wa malemu John F. Kennedy yemwe anali pulezidenti wa United States, analengeza kuti: “Ife tsopano tiri ndi mpata—ndithudi, kufunika—kwa kujambula chitsanzo cha dongosolo la dziko latsopano lozikidwa pa malingaliro atsopano a chisungiko.” Iye anawonjezera kuti: “Ndikhulupirira kuti, chiyembekezo chothekera kopambana cha dongosolo la dziko latsopano lachipambano, chimadalira pa kulimbikitsa zomangira chitaganya cha m’maiko onse.”

McGhee ananena kuti kuleka kwa Falansa kwa kuyesa zida zanyukleya mkati monse mwa 1992 kunali “kupereka chisonkhezero ku maiko ena azida zanyukleya kuchita chimodzimodzi.” Iye anasonyanso ‘kukuyamba kwa Russia kwa kuchepetsa nkhokwe zazida zanyukleya ndi kusiya mkhalidwe wowopsa wa kukonzekera chandamale cha mphamvu zanyukleya.’

Ndiponso, pamsonkhano wa atsogoleri adziko m’London m’July 1991, asanu ndi aŵiri a iwo analengeza kuti mgwirizano wa ankhondo ku Persian Gulf “unatsimikizira kukhoza kwa chitaganya cha m’mitundu yonse kwa kugwirira ntchito pamodzi ‘kubwezeretsa mtendere ndi chisungiko za mitundu yonse ndi kuthetsa nkhondo.’”

Kodi Ndidziko Latsopano Lotani?

Zonsezi zikumvekera kukhala zolimbikitsa. Koma dzifunseni kuti, Kodi ndidziko latsopano lotani limene mitundu ikuyembekezera kupanga? Kodi ndidziko lopanda zida zankhondo, lopanda nkhondo?

McGhee akuyankha kuti: “Amereka iyenera kusunga zida zokwanira kuchitira kuti ikhoze kudzachita mbali yake kukuyesayesa kulikonse kwa kugwirizanitsa magulu ankhondo, kapena kulaka ngati nkhondoyo iri yosapeweka.” Chotero atsogoleri adziko sakulengeza kutuliratu zida zankhondo, ndipo sali kukana kuthekera kwa zoyesayesa zankhondo ngati, monga mwe McGhee adanenera, “nkhondo iri yosapeweka.” Mabomawo sangalonjeze konse dziko latsopano lopanda nkhondo. Kwenikweni, iwo amadziŵa kuti sangathe kupanga dziko loterolo.

Mwachitsanzo, tayang’anani zimene zachitika kale. Pamutu wakuti “Dongosolo la Dziko Latsopano” mu New York Times ya May 17, 1992, mkonziyo Anthony Lewis analemba kuti: “Kupenyerera zithunzithunzi za pawailesi yakanema zamabomba ogwera pa [Sarajevo, Bosnia ndi Herzegovina,] ndi alaiya akumanthunthumira mwamantha, ndinalingalira kuti kutsungula sikunapitebe patsogolo kuyambira pamene mabomba a Anazi anagwera pa Rotterdam. Palibe dongosolo la dziko latsopano.”

Komabe, kuphatikiza pa kuthetsa nkhondo, pali mavuto ena ambiri amene afunikira kuthetsedwa kuti dziko latsopano lokhutiritsa lipangidwe. Talingalirani za kuipitsa malo kwakupha kumene kukuwononga mwapang’onopang’ono mpweya wathu, mtunda, ndi nyanja; ntchito zaupandu kwambiri ndi ntchito zogulitsa anamgoneka zimene zimabera anthu mamiliyoni ambiri chuma chawo ndi thanzi; kuwononga dala nkhalango zimene zimathandizira kuvumba kwa mvula zimene zimawonjezera kukukokololedwa kwa nthaka yachonde ndipo potsirizira pake ku maliyambwe amene amawononga dzinthu.

Ndiponso, zofunikira kuthetsedwa ndizo nthenda zowopsa zakuthupi, kuphatikizapo nthenda yamtima, kensa, AIDS, kensa ya m’magazi, ndi nthenda yashuga. Ndipo bwanji za mavuto a umphaŵi, kusowa nyumba, kuperewera kwa chakudya ndi madzi, kudya mokwanira, umbuli, kuwonongedwa kwa mpweya wa mumlengalenga? Ndithudi, mpambowo ulibe mapeto. Mavuto owopsa amenewa ali ngati mulu wa mabomba otcheredwa. Anthu ayenera kuwachotsa asanaphulike kukhala masoka otsatizanatsatizana amene akatsogolera kukupululutsidwa kwawo. Kodi iwo angakhazikitse dziko latsopano m’nthaŵi yokwanira kuchita zimenezi?

Kwazaka zambiri magulu ndi anthu osonkhana akhala akugwira ntchito zolimba kuthetsa mavuto a dziko lapansi. Komabe, sikokha kuti mavuto awanda komanso atsopano ndi ocholowana kwambiri abuka. Kodi kusakhoza kwa munthu kuthetsa amenewa kumatanthauza kuti kulakalaka kwa munthu dziko latsopano lamtendere, lotetezereka kuli kosaphula kanthu? Tingathe kuyankha mwachidaliro kuti ayi! Chonde lingalirani chifukwa chimene tikunenera zimenezi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena