Lipoti Losangalatsa Kuchokera ku Soviet Union
Kufika Pachimake Kosangalatsa kwa Zaka Zana Limodzi za Kuchitira Umboni
“KULEMBETSA Tchata cha Malo Oyendetsa Ntchito a magulu achipembedzo a ‘Mboni za Yehova mu U.S.S.R.’”
Uku ndiko kutembenuzidwa kwa mawu oyamba a chikalata cha chinenero cha Chirussia cholembedwanso patsamba lino. Zowonadi, mawu ameneŵa amaimira yankho la mapemphero ambiri. Chikalatacho chinasainidwa ndi kusindikizidwa mu Moscow ndi nduna yaikulu ya Unduna wa Zachiweruzo wa R.S.F.S.R. (Russian Soviet Federated Socialist Republic). Izi zitanthauza kuti Mboni za Yehova ndigulu lachipembedzo lozindikiridwa mu U.S.S.R. Chotero, izo zafika posinthira m’mbiri yawo ya zaka zana limodzi m’dziko lalikululo.
Chiyambi Chaching’ono Kwambiri
Mbiri ya zaka zana limodzi? Inde. M’nthaŵi zamakono, wolalikira woyambirira koposa wodziŵika wa mbiri yabwino m’dziko limenelo anali Charles Taze Russell, yemwe anasimba za kuchezera kumeneko mu 1891. M’kope la September 1891 la Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence, iye akufotokoza kuti anapita ku Kishinev, Russia, mkati mwa ulendo woyendera Yuropu. Kumeneko anakumana ndi Joseph Rabinowitch, yemwe anakhulupirira mwa Kristu ndipo ankayesa kulalikira ku mabanja Achiyuda m’deralo. Russell akusimba zambiri ponena za ulendo wake ndi Rabinowitch ndi kukambitsirana kwawo kwakuya, kosangalatsa konena za Ufumu.
Mbiri Yabwino Imvedwa Kachiŵirinso
Pambuyo pa ulendo wa Russell, zochepa zikumvedwa ponena za kuchitira umboni mu yomwe tsopano ndi U.S.S.R., koma zimenezo sizikutanthauza kuti palibe chimene chinakwaniritsidwa. Mu 1927 mipingo itatu mu Soviet Union inatumiza ku Sosaite malipoti awo a misonkhano ya Chikumbutso. Koma kupita patsogolo sikukuwonekera kukhala kunali kofulumira kufikira nkhondo yadziko yachiŵiri. Nkhondo imeneyo inatulukapo kusamutsidwa kwakukulu kwa anthu ambiri m’Yuropu. Chotulukapo chimodzi chosawonedweratu cha kusamukasamuka kumeneku chinali kulowerera kwakukulu kwa alaliki a Ufumu mu Soviet Union.
Mwachitsanzo, kope la February 1, 1946, la The Watchtower limasimba kuti: “Ofalitsa oposa chikwi chimodzi omwe kalelo analalikira m’chinenero cha ku Ukraine m’mbali yakum’maŵa ya Poland tsopano asamutsidwira mkati mwa Russia. . . . Ndiyenonso, abale mazana ambiri omwe ankakhala ku Bessarabia, yomwe kale inali mbali ya Rumania, tsopano ndi nzika za Russia ndipo akupitiriza ntchito yawo yopanga ophunzira m’mitundu yonse.”
Ndiponso, mkati mwa nkhondo yadziko yachiŵiri, nzika zambiri za ku Soviet Union zinavutika m’misasa yachibalo ya Nazi. Kwa ena chokumana nacho chovuta chimenechi chinatsogolera ku madalitso osayembekezereka. Lipoti lina likusimba za chiŵerengero cha akazi achichepere Achirussia amene anaponyedwa m’ndende ku Ravensbrück. Kumeneko anakumana ndi Mboni za Yehova, anavomereza chowonadi, ndipo anapanga kupita patsogolo kufikira ubatizo. Zinthu zofananazo zinachitika m’misasa ina. Pamene Mboni zobatizidwa chatsopanozi zinamasulidwa pamapeto a nkhondo, zinatenga mbiri yabwino Yaufumu kubwerera nayo ku Soviet Union. Mwanjirayi nkhondo yadziko yachiŵiri inatulukapo chiwonjezeko chofulumira cha chiŵerengero cha olalikira Ufumu m’gawo la Soviet Union. Mu 1946 kunayerekezeredwa kuti ofalitsa 1,600 anali okangalika kumeneko.
Kulalikira m’Ndende
Ndende zinapitiriza kuchita mbali yaikulu m’kufalitsa mbiri yabwino mu Soviet Union. Pambuyo pa nkhondo, olamulira anaziwona molakwika Mboni kukhala chiwopsezo, ndipo zambiri zinaponyedwa m’ndende. Koma zimenezi sizinaimitse kulalikira kwawo. Kodi zikanatero motani, pamene izo zinakhulupirira mowonadi kuti uthenga wonena za Ufumu wa Mulungu ndiwo mbiri yabwino koposa kwa anthu? Chotero kwa zambiri za izo, ndende inakhala gawo lawo, ndipo akaidi osaŵerengeka omwe anawamva anavomereza. Lipoti la mu 1957 limati: “Pa onse amene ali odziŵika kukhala m’chowonadi lerolino m’Russia kwatsimikiziridwa kuti maperesenti makumi anayi analandira chowonadi m’ndende ndi m’misasa yachibalo.”
Kodi Mbonizo zinakhwethemulidwa ndi chiwopsezo chosalekeza chakuponyedwa m’ndende chimenechi? Kutalitali! Lipoti la mu 1964 limati: “M’misasa imeneyo muli mboni za Yehova zomwe zaloŵamo kwa nthaŵi yachiŵiri kapena yachitatu, popeza kuti sizinaleke kulalikira uthengawo pambuyo pakumasulidwa.” Ena, lipotilo likupitiriza kutero, anali apandu omwe anaponyedwa m’ndende kapena msasa wachibalo ndipo anakumana ndi Mboni pamene anali kumeneko. Iwo anavomereza chowonadi ndipo anapita patsogolo kufikira kubatizidwa asanamasulidwe.
Kuchepekera kwa Chitsenderezo
Mkati mwa ma 1960, olamulira anakhala ndi maganizo ofeŵerapo kulinga kwa Mboni. Mwachidziŵikire, iwo anazindikira kuti anthu a Yehova sanali chiwopsezo konse ku lamulo ndi dongosolo la anthu. Chotero pamene kuli kwakuti ntchito za Akristu odzichepetsa ameneŵa sizinali zozindikiridwa mwalamulo, iwo anakumana ndi kumangidwa ndi kufufuzidwa kwa m’nyumba zawo kocheperapo, ndipo anali oyamikira kaamba ka kucheperako kwa chitsenderezo kumeneku. Chikhumbo chawo chachikulu chinali chakuti apitirize moyo wawo Wachikristu ndi ntchito m’mkhalidwe wodekha, wachete, ndi mwamtendere monga momwe angakhozere.—Aroma 12:17-19; 1 Timoteo 2:1, 2.
Mu 1966 onse amene anaikidwa muukapolo ku Siberia kwanthaŵi yaitali anamasulidwa ndipo analoledwa kupita kumalo kulikonse kumene anafuna m’dzikolo. Ambiri anabwerera kwawo pambuyo posakhalako kwa zaka zambiri, koma ena anasakha kutsalira m’munda wobala zipatso umenewo. Ndipo sionse amene anabwerera omwe anasankha kukhalirira. Mlongo wina, yemwe anathamangitsidwira ku Siberia ndi banja lake ali msungwana wachichepere, anabwerera ndi makolo ake kumadzulo kwa Russia. Koma iye anakhala kwa kanthaŵi kochepa. Iye anakonda kwambiri anthu odzichepetsa, ochereza a ku Siberia kwakuti anasiya banja lake nabwerera kum’maŵa kukapitiriza kulalikira kwa anthu omvetsera amenewo.
Chokumana nacho chapadera cha nthaŵi imeneyi chimaphatikizapo mbale yemwe anasamukira ku mzinda wina. Patapita kanthaŵi anapeza Mboni zina ziŵiri. Atatuwo anapempherera thandizo ndipo posakhalitsa anafikira mkazi wachichepere wa Greek Orthodox. Iye anavomereza chowonadi mofulumira ndipo anatsogoza abalewa kwa okondwerera ena aŵiri—amayi ake ndi mchemwali wake wamng’ono. Lipotilo likutsiriza kuti: “Lerolino pali anthu makumi anayi omwe amagwirizana ndi abalewo, makumi atatu a iwo aphunzira chowonadi m’miyezi isanu ndi umodzi yapitayi.”
Chikhalirechobe, Mboni za Yehova zinali zotsekerezedwa m’ntchito zawo chifukwa chakukhala zosazindikiridwa mwalamulo. Misonkhano inkachitidwa mochenjera. Kulalikira kunachitidwa mosamalitsa. Kuponyedwa m’ndende kunali kothekerabe, ndipo kuchitira umboni kunyumba ndi nyumba kwapoyera kunali kosatheka. Komabe, mosasamala kanthu za zonsezi, Akristu okhulupirika a ku Soviet Union ameneŵa anapitiriza kutumikira Mulungu wawo mokhulupirika ndikukhala nzika zabwino za dziko lawo. (Luka 20:25) Pofotokoza mkhalidwe wawo, mmodzi wa iwo analemba kuti: “Ndimwaŵi waukulu kupirira ziyeso zonse ndikukhalabe wokhulupirika kwa Yehova Mulungu, kutamanda Mulungu kosatha m’moyo wonse wa munthuwe kotero kuti upeze moyo wosatha kwa Yehova kupyolera mwa Yesu Kristu.” Ha, Mboni za ku Soviet Union zimenezi zakhala zitsanzo zabwino zotani nanga za kukhulupirika!
Kuzindikiridwa Mwalamulo Pomalizira Pake!
Mu 1988 zinthu zinayamba kusintha m’maiko ogwirizana ndi Soviet Union. Mkhalidwe wa ufulu wokulirako unayamba, ndipo maiko omwe analetsa ntchito za Mboni za Yehova anayamba kupanga malamulo atsopano. Poland, Hungary, Romania, ndi maiko ena anapatsa Akristu owona mtima ameneŵa kuzindikiridwa kwalamulo, kuwalola kuchita ntchitoyo poyera osawopa kulangidwa. Zaka zitatu zapitazi zakhala zosangalatsa chotani nanga Kum’maŵa kwa Yuropu! Ha, abalewo agwiritsira bwino motani nanga ufulu wawo wopezedwa chatsopanowo kufalitsa uthenga wamtendere Waufumu! Ndipo Mboni za Yehova padziko lonse zimasangalala nawo motani nanga!
Mboni za ku Soviet Union zapindula kale ndi ufulu wawo wofutukuka. Zikwi zambiri—zina zochokera kutali kwambiri monga ku gombe la Pacific la Asia—zinafikapo pa misonkhano yopanga mbiri mu Poland mu 1989 ndipo kachiŵirinso mu 1990, pamene Mboni 17,454 zochokera ku Soviet Union zinalipo mu Warsaw. Ha, ndizikumbukiro zotani nanga zimene anabwerera nazo kwawo! Ambiri anali asanalambirepo ndi Akristu anzawo ochuluka. Tsopano anali pakati pa makamu zikwi makumi ambiri!
Iwo anabwerera ku Soviet Union yomwe inali kukhala yololera. Mboni padziko lonse zinapenya ndi kuzizwa kuti: Kodi Mboni za Yehova mu Soviet Union zidzazindikiridwa liti mwalamulo? Eya, zinachitika mu 1991—ndendende pambuyo pa zaka zana limodzi kuyambira pamene Charles Taze Russell anapitako! Pa March 27, 1991, “Malo Oyendetsa Ntchito a Magulu Achipembedzo a Mboni za Yehova mu U.S.S.R.” analembedwa m’chikalata chosainidwa mu Moscow ndi Nduna ya Chiweruzo ya R.S.F.S.R. Kodi ndiufulu wotani umene unaperekedwa kwa Mbonizo?
Tchata chalamulo cha bungwe lolembetsedwa chatsopanolo chimaphatikizapo chilengezo chotsatirachi: “Cholinga cha Gulu Lachipembedzo ndicho kuchita ntchito yachipembedzo yodziŵikitsa dzina la Yehova Mulungu ndi makonzedwe ake achikondi kaamba ka anthu kupyolera mwa Ufumu wake wakumwamba mwa Yesu Kristu.”
Kodi zimenezi zidzachitidwa motani? Njira zondandalitsidwa zimaphatikizapo kulalikira poyera ndi kuchezera nyumba za anthu; kuphunzitsa chowonadi Chabaibulo kwa anthu amene ali ofunitsitsa kumvetsera; kuchita nawo maphunziro Abaibulo aulere mwa chithandizo cha mabuku ophunzirira Baibulo; ndi kupanga makonzedwe a kutembenuza, kuitanitsa, kufalitsa, kusindikiza, ndi kugaŵira Mabaibulo.
Chikalatacho chimandandalitsanso gulu la Mboni pansi pa Bungwe Lolamulira, kuphatikizapo mipingo yokhala ndi mabungwe a akulu, Komiti Yotsogoza [Yanthambi] yokhala ndi ziŵalo zisanu ndi ziŵiri ya dzikolo, ndi oyang’anira dera ndi chigawo.
Mwachiwonekere, Mboni za Yehova tsopano zikhoza kuchita zinthu mwaufulu ndiponso poyera mu Soviet Union monga mmene zimachitira m’maiko ena ambiri. Tangoyerekezerani chisangalalo cha zisanu mwa ziŵalo zisanu ndi ziŵiri za Komiti Yotsogoza ndi akulu ampingo asanu otumikira kwa nthaŵi yaitali omwe anali ndi mwaŵi wapadera wakusaina chikalata chopanga mbiri chimenechi ndikuwona chikutsimikiziridwa ndi chisindikizo chalamulo ndi Mkulu wa Dipatimenti ya Registration of Public and Religious Associations! Moyenerera, Milton Henschel ndi Theodore Jaracz a Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova analiponso kuchitira umboni chochitika chokondweretsa chimenechi. Pakati pa magulu amene anavomerezedwa ndi R.S.F.S.R., Mboni za Yehova zinali zoyamba kulandira chikalata chawo chalamulo cha kulembetsedwa. Ha, ndi mphotho yotani nanga kaamba ka abale okhulupirika a ku Russia amenewo pambuyo pa zaka zambiri za kupirira moleza mtima!
Mboni za Yehova kulikonse zikuyamikira olamulira a ku Soviet Union amene anapereka kuzindikiridwa kwalamulo kumeneku. Izo zikuyamikira kwenikweni Yehova ndi mtima wawo wonse chifukwa cha ufulu watsopano wa abale awo a ku Soviet Union. Zimasangalala ndi Mboni zinzawo za ku U.S.S.R. ndi m’maiko onse a Kum’maŵa kwa Yuropu omwe tsopano akutumikira Yehova Mulungu mwapoyera kwenikweni. Yehova awadalitsetu molemera pamene akugwiritsira ntchito ufulu umenewu mokwanira m’kutamanda dzina lake loyera.
[Chithunzi patsamba 9]
Kremlin mu Moscow
[Chithunzi patsamba 10]
Nthumwi za ku Russia pamsonkhano wa mu 1990 kunja kwa Soviet Union