M’mawa wa Bata
Zimenezo ndi zimene woŵerenga wa ku Illinois, U.S.A., ananena kuti magazini a Galamukani! amapereka. “Ndinadabwa mosangalatsidwa pambuyo poŵerenga kope la chofalitsidwa chanu cha Galamukani!” analemba motero munthuyo. “Mkazi wina ndiye anandipatsira magaziniyo m’mawa uno pa sitesheni ya sitima. Inandipangitsa kukhala wosanguluka ndi wamtendere, ndipo inali ndi chidziŵitso chothandiza. Chonde ndidziŵitseni mmene ndingamalandirire makope ameneŵa mokhazikika.
“Ndikuthokozaninso kaamba kondipatsa mmawa umodzi wa bata.”
Tikulingalira kuti nanunso mudzapindula ndi nkhani zosangalatsa za mu Galamukani! Ngati mungakonde kulandira magaziniŵa, tangodzazani ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Ndingakonde kuti mudzinditumizira magazini a Galamukani! kunyumba kwanga. (Kunja kwa Zambia, lemberani ku nthambi ya Watch Tower yakumaloko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 2.)