Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 8/15 tsamba 29-31
  • Kodi Mumazikana Zikhoterero Zauchimo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumazikana Zikhoterero Zauchimo?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Kukana Kuli Kwakupha
  • Dzichinjirizeni Inu Eni!
  • Vomerezani Ndipo Chitanipo Kanthu
  • Kodi Iripo Njira Imene Anthu Angatulukire Mumkhalidwe Wawo Wauchimo?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Baibulo Likusinthabe Moyo Wanu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Muzimva Mawu a Yehova Nthawi Zonse
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Tiyenera Kukhala Maso Kuti Tizipewa Mayesero
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 8/15 tsamba 29-31

Kodi Mumazikana Zikhoterero Zauchimo?

‘NDIPO chotero ndipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna chabwino, choipa chiriko. Pakuti monga mwa munthu wa mkati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiwona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lirikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziŵalo zanga.’​—Aroma 7:21-23.

Panafunikira kudzichepetsa kuti Paulo avomereze ziri pamwambapa. Komabe, mwakuchita tero, iye anakhoza kuchinjiriza zikhoterero zake zopanda ungwiro kumlaka.

Kuli kofanana ndi Akristu owona lerolino. Pamene tinalandira chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi Chabaibulo, tinapanga masinthidwe ofunikira m’njira yathu yamoyo, kuigwirizanitsa ndi miyezo ya Yehova. Komabe, zikhoterero zauchimo zimakhalapobe, ‘pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake.’ (Genesis 8:21) Kodi ndife owona mtima mokhoza kuvomereza zikhoterero zathu zakutizakuti zomwe zimatipsinja? Kapena kodi timakana kuti tiribe, mwinamwake nkugamula kuti, ‘Izi zingakhale mbali zovuta kwa ena koma osati kwa ine’?

Kudzinyenga kwaumwini koteroko kungakhale kwakupha. Fanizo lozikidwa pa Baibulo lingatithandize kuzindikira kufunika kwa kuvomereza zikhoterero zathu zauchimo ndi kuzilamulira.

Chifukwa Chake Kukana Kuli Kwakupha

M’nthaŵi Zabaibulo mizinda yambiri inkatetezeredwa ndi malinga. Zitseko zachipata​—kaŵirikaŵiri zopangidwa ndi matabwa​—zinali mbali zosavuta zokhoza kuloŵeredwa ndi adani za linga lamkati la mzinda; chotero, zinkachinjirizidwa mwamphamvudi. Nzikazo zinangomanga zitseko zazipata zochuluka zofunikira kaamba ka kayendedwe m’nthaŵi yamtendere. Zitseko zamatabwa kaŵirikaŵiri zinkakutidwa ndi chitsulo, kupeŵa kuwonongeka ndi moto. Nsanja zinkamangidwa m’malingawo kotero kuti alonda oikidwa pa izo akakhoza kuwona adani omadza patali.

Tsopano talingalirani: Kodi chikachitika nchiyani ngati nzika za mzinda zinatsutsa chiwopsezo cha kuloŵeredwa kupyola pa zipata zamzinda ndipo motero osazitetezera mokwanira? Asirikali achidani akaloŵa mosavuta mumzinda, ndi kuugonjetsa mzindawo.

Kulinso motero ndi ife. Yehova amadziŵa mbali zathu munthu payekha zokhoza kuloŵereredwa. ‘Ndipo Palibe cholengedwa chosawonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa iye amene tichita naye.’ (Ahebri 4:13) Satana nayenso amazindikira zikhoterero zauchimo zomwe ziri mwa ife, kaya zikhale zakupotoza chowonadi, kukwiya msanga, kukondweretsedwa ndi chisembwere chakugonana, kukondetsa zinthu zakuthupi, kunyada, kapena china chirichonse. Ngati timakana kuti tiribe zikhoterero zauchimo, timadzipangitsa tokha kukhala okhoza kuloŵeredwa koposa ndi ziukiro za Satana pa chikhulupiriro chathu. (1 Petro 5:8) Tingalakidwe pamene zikhumbo zoipa zikula nizipyola pa zikhoterero wamba ndi kubala uchimo. (Yakobo 1:14, 15) Tifunikira kukhala ngati Paulo, kuvomereza mowona mtima ‘zitseko za matabwa’ zimene tingakhale nazo.

Dzichinjirizeni Inu Eni!

Kukakhala kopanda pake kuzindikira zikhoterero zoipa koma osachitapo kanthu. Uku kukafanana ndi munthu yemwe amadziyang’ana m’kalirole, awona mbali zofunikira chisamaliro, nachokapo popanda kupanga kuwongolera kofunikirako. (Yakobo 1:23-25) Inde, tifunikira kuchitapo kanthu kudzichinjiriza kuti tisagonjetsedwe ndi zikhoterero zauchimo. Kodi ndimotani mmene tingachitire zimenezi?

M’nthaŵi Zabaibulo, mizinda yaing’ono kapena “miraga,” inali yopanda malinga kaŵirikaŵiri. (Numeri 21:25, 32; Oweruza 1:27; 1 Mbiri 18:1; Yeremiya 49:2) Nzika za mizinda imeneyi zikathaŵira mumzinda wamalinga m’nthaŵi yakuukiridwa ndi adani. Mizinda yamalinga inatumikira monga kobisala anthu a m’dera lapafupi.

Baibulo limamfotokoza Yehova Mulungu kukhala nsanja, pobisalira, linga kumene tingathaŵire kaamba ka chitetezo. (Miyambo 18:10; Zekariya 2:4, 5) Chotero Yehova ndiye chitetezo chachikulu cha atumiki ake. Kupemphera kosalekeza kwa iye kuli kofunika kwambiri. (1 Atesalonika 5:17) Chithandizo china ndicho Baibulo. Pogwiritsira ntchito Mawu a Mulungu, tidzachita bwino kuchita phunziro lapadera la mbali zimene tiri ofooka. Tikhozanso kuika padera nkhani zozikidwa pa Baibulo zomwe zimakhudza ‘zitseko [zathu] zamatabwa’ kaamba ka kuzisanthula mobwerezabwereza.

Ndiponso, mofanana ndi alonda pa nsanja, nafenso tikhoza kuwona adani patali, titero kunena kwake, ndi kuchitapo kanthu moyenera. Motani? Mwakupeŵa mikhalidwe m’mene tingakumane ndi chiyeso kapena chitsenderezo. Mwachitsanzo, munthu wogwirira ntchito pa kukhala wachikatikati m’kumwa zakumwa zoledzeretsa mwanzeru adzasankha kupeŵa malo kumene zakumwa zimenezi zimapezeka mosavuta kapena kumene zimalimbikitsidwa.

Zonsezi zimafunikira kuyesayesa. Komabe, ngati Paulo anachita ‘kupumpuntha thupi lake’ kuti atsutse zikhoterero zopanda ungwiro, kodi nafenso sitifunikira kupanga kuyesayesa? Kupereka chidwi chosamalitsa choterocho ku zikhoterero zathu zauchimo kudzasonyeza kuti tikutsatira uphungu wa mtumwi Petro wakuti: ‘Chitani changu kuti mupezedwe ndi iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chirema.’​—1 Akorinto 9:27; 2 Petro 3:14.

Vomerezani Ndipo Chitanipo Kanthu

Osalefulidwa ngati, mosasamala kanthu za zoyesayesa zanu, zikhoterero zopanda ungwiro sizizimiririka zonse. Malinga ngati tiri opanda ungwiro, zikhoterero zoipa zidzakhalapobe kumlingo wakutiwakuti, monga momwe zinaliri ndi Paulo. Koma tifunikira kupitirizabe kumazipondereza zimenezi, kuzilepheretsa kubala uchimo.

Komabe, zindikirani kusiyana kokhala pakati pa kuvomereza kukhalako kwa kupanda ungwiro ndi kukulekerera. Zimenezi zingafotokozedwe mwafanizo ndi munthu yemwe ali ndi mtima wofooka. Iye ayenera kuyang’anizana ndi chenicheni chimenechi mwakuyesayesa kusunga mtima wake mumkhalidwe wabwino monga momwe angathere. Iye samalingalira kuti popeza kuti mtima wake weniweniwo uli wofooka, kungakhale bwino kwa iye kutaya chitetezo chonse ndi kukhala ndi moyo mulimonse mmene afunira.

Pamenepa, dziŵani kuti, nyonga yathu siiri m’kukana zikhoterero zauchimo mosadziŵa koma kuzivomereza ndi kuchitapo kanthu motsutsana nazo. Chotero musawope kuvomereza kwa nokha ndi kwa Yehova mbali zimene mumayesedwa mosavuta ndi kupsinjidwa. Simuyenera kudzida inu mwini chifukwa cha kuchita motero, ndipo chikondi cha Yehova pa inu sichidzazimiririka. Kwenikweni, pamene muyandikira pafupi ndi Mulungu pofunitsitsa chivomerezo chake, iye adzayandikira pafupi kwenikweni ndi inu.​—Yakobo 4:8.

[Chithunzi patsamba 31]

Chifaniziro ichi cha Megido chimafotokoza mwafanizo zitseko zachipata zochinjirizidwa ndi malinga otetezera mizinda yamakedzana

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena