Ngachimwemwe Chotani Nanga Ofatsa!
“Achimwemwe ali ofatsa, pakuti adzalandira dziko lapansi.” —MATEYU 5:5, NW.
1. Kodi nchiyani chimene chiri kufatsa kumene Yesu anakunena mu Ulaliki wake wa pa Phiri?
MUULALIKI wake wa pa Phiri, Yesu Kristu anati: “Achimwemwe ali ofatsa pakuti adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) Kufatsa kumeneku, kapena kudekha, sindiko chisonyezero chakufatsa kwachinyengo, ndipo sikuli mkhalidwe wachibadwa chabe wamunthu. Mmalomwake, ndiko kufatsa kwenikweni kwa mkati ndi kukhala wamtendere zosonyezedwa kwakukulukulu molabadira chifuniro cha Yehova ndi chitsogozo. Anthu ofatsa mowona alidi ndi lingaliro lakudalira pa Mulungu limene limasonyezedwa mumkhalidwe wofatsa kulinga kwa anthu anzawo.—Aroma 12:17-19; Tito 3:1, 2.
2. Kodi nchifukwa ninji Yesu ananena kuti ofatsawo ngachimwemwe?
2 Yesu anatcha ofatsawo achimwemwe chifukwa chakuti adzalandira dziko lapansi. Monga mwana wa Mulungu wofatsa mwangwiro, Yesu ndiye Wolandira dziko lapansi Wamkulu. (Salmo 2:8; Mateyu 11:29; Ahebri 1:1, 2; 2:5-9) Koma monga “mwana wamunthu” Waumesiya, anayenera kukhala ndi olamulira anzake mu Ufumu wake wakumwamba. (Danieli 7:13, 14, 22, 27) Monga “olowa nyumba anzake” a Kristu, odzozedwa ofatsa ameneŵa adzakhala ndi phande m’cholowa chake cha dziko lapansi. (Aroma 8:17) Anthu ena ofatsa onga nkhosa, adzasangalala ndi moyo wamuyaya m’Paradaiso m’malo a Ufumuwo apadziko lapansi. (Mateyu 25:33, 34, 46; Luka 23:43) Chiyembekezo chimenecho chimawapangitsadi kukhala achimwemwe.
3. Kodi Mulungu ndi Kristu anapereka chitsanzo chotani ponena za kufatsa?
3 Wolandira Wamkulu wofatsayo akulandira dziko lapansi kuchokera kwa Atate wake, Yehova, chitsanzo chachikulu cha kufatsa. Ndimobwerezabwereza chotani nanga mmene Malemba amanenera kuti Mulungu ali “wolekeleza ndi waukoma mtima wochuluka”! (Eksodo 34:6; Nehemiya 9:17; Salmo 86:15) Iye ali ndi mphamvu zazikulu koma amasonyeza kudekha kotero kuti olambira ake amfikire mopanda mantha. (Ahebri 4:16; 10:19-22) Mwana wa Mulungu, amene anali “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima,” anaphunzitsa ophunzira ake kukhala ofatsa. (Mateyu 11:29; Luka 6:27-29) Motsatizana, akapolo ofatsa ameneŵa a Mulungu ndi Mwana wake anatsanzira ndi kulemba za “kufatsa ndi kukoma mtima kwa Kristu.”—2 Akorinto 10:1, NW; Aroma 1:1; Yakobo 1:1, 2; 2 Petro 1:1.
4. (a) Malinga ndi Akolose 3:12, kodi nchiyani chimene chachitidwa ndi awo amene alidi ofatsa? (b) Kodi ndimafunso otani amene tiyenera kupenda?
4 Lerolino, onse aŵiri Akristu odzozedwa ndi atsamwali awo apadziko lapansi afunikira kukhala ofatsa. Pokhala atasiya kuipa kulikonse, bodza, chinyengo, chisiriro, ndi kujedana, athandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu kukhala atsopano mwa “mphamvu yosonkhezera maganizo awo.” (Aefeso 4:22:24, NW; 1 Petro 2:1, 2) Iwo amafulumizidwa kudziveka “mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.” (Akolose 3:12) Koma kwenikweni kufatsa kumaphatikizapo chiyani? Kodi nchifukwa ninji kukhala ofatsa kuli kopindulitsa? Ndipo kodi mkhalidwe umenewu ungawonjezere motani chimwemwe chathu?
Kupenda Kufatsa Mosamalitsa
5. Kodi kufatsa kungalongosoledwe motani?
5 Munthu wofatsa ali wodekha m’kulingalira ndi khalidwe. Mumatembenuzidwe ena a Baibulo, ali mfotokozi wakuti pra·ysʹ yemwe amatembenuzidwa “woleza mtima,” “wachikatikati,” “wofatsa,” ndi “wodekha.” M’Chigiriki choyambirira, mfotokoziyo pra·ysʹ angagwire ntchito kukamphepo kayaziyazi kapena liwu lodekha. Angatanthauzenso munthu amene ali wokoma mtima. Katswiri W. E. Vine akunena kuti: “Kugwiritsidwa ntchito kwa [dzinalo pra·yʹtes] kuli choyamba ndi kwakukulukulu kulinga kwa Mulungu. Uli mkhalidwe wa mzimu umene timavomereza kuchita kwake ndi ife kukhala kwabwino, ndipo motero popanda kutsutsa kapena kukana; uli wogwirizana mwathithithi ndi liwu lakuti tapeinophrosunē [kudzichepetsa].”
6. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti kufatsa sikuli kufooka?
6 Kufatsa sikuli kufooka. “Muli kudekha mu praus,” analemba motero katswiri William Barclay, “koma mkati mwakudekhako muli nyonga yachitsulo.” Kumafunikira nyonga kuti tikhale wofatsa. Mwachitsanzo, nyonga imafunikira kuti tikhale wofatsa titakwiitsidwa kapena pamene tikuzunzidwa. Mwana wa Mulungu wofatsayo, Yesu Kristu, anapereka chitsanzo chabwino m’nkhani imeneyi. “Amene pochitidwa chipongwe sanabwezere chipongwe, pakumva zowawa sanawopsa, koma anapereka mlandu kwa Iye [Yehova Mulungu] woweruza kolungama.” (1 Petro 2:23) Mofanana ndi Yesu wofatsayo, tingakhale achidaliro kuti Mulungu adzalanga otitonza ndi otizunza. (1 Akorinto 4:12, 13) Tingakhale abata, monga momwe anachitira Stefano wozunzidwayo, tikumazindikira kuti ngati tikhala okhulupirika, Yehova adzatisamalira ndipo sadzalola chirichonse kutivulaza kosatha.—Salmo 145:14; Machitidwe 6:15; Afilipi 4:6, 7, 13.
7. Kodi Miyambo 25:28 imasonyezanji za munthu wopanda chifatso?
7 Yesu anali wofatsa, komabe anasonyeza nyonga m’kuimabe nji pa chimene chiri cholungama. (Mateyu 21:5; 23:13-39) Aliyense wokhala ndi “mtima wa Kristu” adzakhala wofanana naye m’nkhaniyi. (1 Akorinto 2:16) Ngati munthu saali wofatsa, iye ali wosafanana ndi Kristu. Mmalomwake, amayenererana ndi mawu awa: “Wosalamulira mtima akunga mudzi wopasuka wopanda linga.” (Miyambo 25:28) Munthu wosafatsa wotero ali wosavuta kulowedwa ndi malingaliro olakwika amene akhoza kumpangitsa kuchita mwanjira zosayenerera. Pamene kuli kwakuti Mkristu wofatsa saali wofooka, amadziwabe kuti “mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mawu owawitsa aputa msunamo.”—Miyambo 15:1.
8. Kodi nchifukwa ninji sikuli kosavuta kukhala wofatsa?
8 Sikuli kosavuta kukhala wofatsa, popeza tiri ndi cholowa chakupanda ungwiro ndi uchimo. (Aroma 5:12) Ngati tiri atumiki a Yehova tiyeneranso kulimbana ndi mphamvu ya mizimu yoipa imene ingayese kufatsa kwathu mwachizunzo. (Aefeso 6: 12) Ndipo ambirife timagwira ntchito pakati pa awo amene ali ndi mzimu wasontho wadziko limene liri pansi pa ulamuliro wa Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Chotero kodi tingakulitse motani kufatsa?
Mmene Tingakulitsire Kufatsa
9. Kodi ndilingaliro lotani limene lidzatithandiza kukulitsa chifatso?
9 Chitsimikiziro chozikidwa pa Baibulo chakuti timafunidwa kusonyeza kufatsa chidzatithandiza kukulitsa mkhalidwe umenewu. Tsiku ndi tsiku tiyenera kuyesayesa kukulitsa kufatsa. Apo phuluzi, tidzakhala ngati anthu amene amawona kufatsa monga kufooka ndipo amalingalira kuti chipambano chimachokera m’kukhala wodzikuza, wovuta, ngakhale wankhanza. Komabe mawu a Mulungu amatsutsa kunyada ndipo mwambi wanzeru umati: “Wachifundo achitira moyo wake zokoma; koma wankhanza avuta nyama yake.” (Miyambo 11:17; 16:18) Anthu amatalikirana ndi munthu waukali, wosakoma mtima, ngakhale ngati amatero kwakukulukulu kuti apewe kuvulazidwa ndi nkhanza yake ndi kusadekha.
10. Ngati titi tikhale ofatsa, kodi tiyenera kugonjera kuchiyani?
10 Kuti tikhale ofatsa, tiyenera kugonjera ku chisonkhezero cha mzimu woyera, kapena mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. Monga momwedi Yehova anatheketsera dziko lapansi kubala zipatso, amatheketsanso atumiki ake kubala zipatso za mzimu wake, kuphatikizapo chifatso. Paulo analemba kuti: “Chipatso cha mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.” (Agalatiya 5:22, 23) Inde, kufatsa kuli chimodzi cha zipatso za mzimu wa Mulungu zosonyezedwa ndi awo amene amamkondweretsa. (Salmo 51:9, 10) Ndipo ha, ndi masinthidwe otani nanga amene kufatsa kumatulutsa! Mwachitsanzo: Panali wachifwamba wotchedwa Tony yemwe ankamenya, kubela anthu, kuzembetsa mankhwala ogodomalitsa maganizo, kutsogoza gulu lanjinga za moto, ndipo anakhala nthaŵi ali m’ndende. Komabe, mwakulandira chidziŵitso cha Baibulo ndipo mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, iye anasintha nakhala mtumiki wofatsa wa Yehova. Nkhani ya Tony iri yeniyeni. Pamenepa kodi munthu angachitenji ngati kusadekha kwakhala mbali yaikulu ya umunthu wake?
11. M’kukulitsa chifatso, kodi ndi mbali yotani imene pemphero limachita?
11 Pemphero lochokera mumtima lopempha mzimu wa Mulungu ndi chipatso chake chakufatsa lidzatithandiza kukulitsa mkhalidwewu. Tingafunikire ‘kumangopemphabe,’ monga momwe Yesu ananenera, ndipo Yehova Mulungu adzatipatsa zofuna zathu. Pambuyo pakulongosola kuti atate aumunthu amapatsa ana awo zinthu zabwino, Yesu anati: “Ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wakumwamba adzapatsa mzimu woyera kwa iwo akumpempha iye?” (Luka 11:9-13) Pemphero lingathandize kupangitsa kufatsa kukhala mbali yachikhalire yaumunthu wathu—mkhalidwe wowonjezera chimwemwe chathu ndi chija cha mabwenzi athu.
12. Kodi nchifukwa ninji kukumbukira kuti anthu ali opanda ungwiro kungatithandize kukhala ofatsa?
12 Kukumbukira kuti anthu ali opanda ungwiro kungatithandize kukhala ofatsa. (Salmo 51:5) Sitingalingalire kapena kuchita mwangwiro, monga momwe anthu ena angachitire, chotero tiyenera kukhaladi achifundo ndi kuwachitira monga momwe tikafuna kuchitiridwa. (Mateyu 7:12) Kuzindikira kuti tonsefe timapanga zolakwa kuyenera kutichititsa kukhala okhululukirana ndi ofatsa pochita ndi ena. (Mateyu 6:12-15; 18:21, 22) Ndiiko komwe, kodi sindife oyamikira kuti Mulungu amasonyeza chikondi ndi kufatsa kulinga kwa ife?—Salmo 103:10-14.
13. Kodi tingathandizidwe motani kukulitsa chifatso ngati tizindikira kuti Mulungu walenga anthu amene ali ndi ufulu wakudzisankhira?
13 Kuzindikira kuti Mulungu anapanga anthu okhala ndi ufulu wakudzisankhira kungatithandizenso kukulitsa kufatsa. Zimenezi sizimalola aliyense kunyalanyaza malamulo a Yehova ndi kusalangidwa, koma kumaloladi kusiyanasiyana m’zofuna, zokondedwa, ndi zosakondedwa pakati pa anthu ake. Chotero tiyenitu tizindikire kuti palibe aliyense ali ndi thayo lakuyenerana ndi umunthu umene tingalingalire kukhala wabwino koposa. Mkhalidwe umenewu udzatithandiza kukhala ofatsa.
14. Ponena za kufatsa, kodi kutsimikiza kwathu kuyenera kukhala kotani?
14 Kutsimikiza kusasiya kufatsa kudzatithandiza kukulitsabe mkhalidwe umenewu. Kugonjera ku chisonkhezero cha mzimu wa Yehova kunadzetsa kusintha m’kulingalira kwathu. (Aroma 12:2) Mkhalidwe wofatsa, wonga wa Kristu umathandizira kutiletsa kulowa “m’kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, mamwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaleka.” Sitiyenera konse kusiya kufatsa kaamba ka zifukwa zachuma, zamayanjano, ndi zina zotero kapena chifukwa chakuti anthu amanena mawu onyoza ponena za kupembedza kwathu. (1 Petro 4:3-5) Sitiyenera kulola kalikonse kutipangitsa kuchita ntchito zathupi, kotero kuti nkutaya kufatsa kwathu ndi kulephera kulandira Ufumu wa Mulungu kapena kusangalala ndi madalitso ake. (Agalatiya 5:19-21) Tiyenitu nthaŵi zonse tiugwiritsitse mwaŵi wakukhala anthu ofatsa a Mulungu, kaya tikhale odzozedwa okalandira moyo wakumwamba kapena okhala ndi chiyembekezo cha padziko lapansi. Ndicholinga chimenecho, tiyenitu tipende mapindu ena a kufatsa.
Mapindu a Kufatsa
15. Malinga ndi Miyambo 14:30, kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kukhala wofatsa?
15 Munthu wofatsa ali ndi mtendere wamtima, maganizo, ndi thupi. Zimenezi ziri choncho chifukwa chakuti iye salowa m’makangano, sakwiitsidwa ndi zochita za ena kapena kudzivutitsa ndi nkhaŵa zosalekeka. Kufatsa kumamthandiza kulamulira malingaliro ake, ndipo zimenezi ziri zopindulitsa mwamaganizo ndi mwakuthupi. Mwambi umati: “Mtima wabwino ndiwo moyo wathupi.” (Miyambo 14:30) Kusoweka kwa kufatsa kungatsogolere kumkwiyo umene ungakweze kuthamanga kwamwazi kapena kuchititsa mavuto a kudzimbidwa, phumi, mavuto amaso, ndi mavuto ena. Mkristu wofatsa amasangalala ndi mapindu osiyanasiyana, kuphatikizapo “mtendere wa Mulungu” umene umatetezera mtima wake ndi mphamvu zake zakulingalira. (Afilipi 4:6, 7) Ha, ndi kwanzeru chotani nanga mmene kuliri kukhala wofatsa!
16-18. Kodi kufatsa kumakhala ndi chiyambukiro chotani pa unansi wathu ndi ena?
16 Mkhalidwe wakufatsa umawongolera unansi wathu ndi ena. Mwinamwake panthaŵi ina tinali ndi chizolowezi cha kuumirira pa zinthu kufikira titapeza chimene tikufuna. Anthu angakhale atakwiya nafe chifukwa chakuti tinasowa kudzichepetsa ndi kufatsa. M’mikhalidwe yoteroyo, sikunayenera kutidabwitsa ngati tinalowetsedwa mumikangano yotsatizanatsatizana. Komabe, mwambi umati: “Posowa nkhuni moto ungozima; ndipo popanda kazitape makangano angoleka. Monga makala ozizira pa makala akunyeka ndi nkhuni pamoto; momwemo munthu wamakangano autsa ndewu.” (Miyambo 26:20, 21) Ngati ndife ofatsa, mmalo ‘mowonjezera nkhuni pamoto,’ ndi kuputa ena, tidzakhala ndi unansi wabwino ndi iwo.
17 Munthu wofatsa ali wothekera kukhala ndi mabwenzi abwino. Anthu amasangalala kuyanjana naye chifukwa chakuti iye ali wamaganizo abwino ndipo mawu ake ngotsitsimula ndi ozuna ngati uchi. (Miyambo 16:24) Zinali choncho ponena za Yesu, yemwe anakhoza kunena kuti: “Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wamiyoyo yanu. Pakuti goli langa liri lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:29, 30) Yesu sanali waukali, ndipo goli lake silinali lotsendereza. Awo odza kwa iye anachitiridwa mwabwino ndi kutsitsimulidwa mwauzimu. Mkhalidwe uli wofanana pamene timayanjana ndi bwenzi Lachikristu lofatsa.
18 Kufatsa kumatichititsa kukondedwa ndi okhulupirira anzathu. Mosakaikira, Akristu ambiri ku Korinto anakokeredwa kwa Paulo chifukwa chakuti iye anawadandaulira “mwakufatsa ndi ulele wa Kristu.” (2 Akorinto 10:1) Ndithudi Atesalonika ayenera kukhala atalabadira mtumwiyo, popeza kuti anali wodekha, mphunzitsi wofatsa. (1 Atesalonika 2:5-8) Mosakaikira akulu a ku Efeso anaphunzira zochuluka kuchokera kwa Paulo ndipo anamkonda kwabasi. (Machitidwe 20:20, 21, 37, 38) Kodi mumasonyeza kufatsa kumene kumakuchititsani kukondedwa ndi ena?
19. Kodi ndimotani mmene kufatsa kumathandizira anthu a Yehova kusunga malo awo m’gulu lake?
19 Kufatsa kumathandizira anthu a Yehova kukhala ogonjera ndi osunga malo awo m’gulu lake. (Afilipi 2:5-8, 12-14; Ahebri 13:17) Kufatsa kumatikaniza kufunafuna ulemerero umene uli wozikidwa pakunyada ndipo kuli konyansa kwa Mulungu. (Miyambo 16:5) Munthu wofatsa samadzilingalira kukhala woposa okhulupirira anzake ndipo samayesa kupambana mwakuŵadyera masuku pamutu. (Mateyu 23:11, 12) Mmalomwake, iye amazindikira mkhalidwe wake wauzimu ndi kufunikira kwa makonzedwe a Mulungu a dipo.
Kufatsa Kumapititsa Patsogolo Chimwemwe
20. Kodi kufatsa kumakhala ndi chiyambukiro chotani pamoyo wabanja?
20 Atumiki onse a Mulungu ayenera kukumbukira kuti kufatsa kuli chipatso cha mzimu wake chimene chimapititsa patsogolo chimwemwe. Mwachitsanzo, chifukwa chakuti anthu a Yehova amasonyeza mikhalidwe yotero yonga chikondi ndi chifatso, mabanja achimwemwe amasefukira pakati pawo. Pamene mwamuna ndi mkazi amachitirana mwachifatso, ana awo amaleredwa m’malo okhala abata, osati m’banja lolamuliridwa ndi mawu aukali ndi zochita. Pamene atate apereka uphungu kwa ana mofatsa umakhala ndi chiyambukiro chabwino pamaganizo awo achibwana, ndipo mzimu wakufatsa uli wothekera kukhala mbali yaumunthu wawo. (Aefeso 6:1-4) Kufatsa kumathandiza amuna kupitirizabe kukonda akazi awo. Kumathandizira akazi kukhala ogonjera kwa amuna awo ndipo kumasonkhezera ana kumvera makolo awo. Kufatsa kumachititsanso ziŵalo zabanja kukhala ndi mzimu wokhululukira umene umawonjezera chimwemwe.—Akolose 3:13, 18-21.
21. Kwakukulukulu, kodi ndiuphungu wotani umene mtumwi Paulo anapereka pa Aefeso 4:1-3?
21 Mabanja ndi anthu ofatsa amapititsa patsogolo chimwemwe mumipingo imene amagwirizana nayo. Chotero, anthu a Yehova afunikira kupanga kuyesayesa kwamphamvu kukhala ofatsa. Kodi inu mukutero? Mtumwi Paulo anadandaulira Akristu anzake odzozedwa kuyenda moyenerera chiitano chawo chakumwamba, akumatero “ndi kuwonetsera kudzichepetsa konse ndi chifatso, ndi kuwonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwachikondi; kusamalitsa kusunga umodzi wa mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.” (Aefeso 4:1-3) Akristu okhala ndi chiyembekezo chapadziko lapansi ayeneranso kusonyeza kufatsa ndi mikhalidwe ina yaumulungu. Imeneyi ndiyo njira imene imadzetsa chimwemwe chenicheni. Alidi achimwemwe chotani nanga ofatsa!
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji anthu ofatsa ngachimwemwe?
◻ Kodi kukhala wofatsa kumatanthauzanji?
◻ Kodi kufatsa kungakulitsidwe motani?
◻ Kodi mapindu ena a kufatsa ndiotani?