‘Ntchito Yaukatswiri Yeniyeni’
Mmenemo ndimmene woŵerenga wa ku Argentina anafotokozera bukhu lofalitsidwa posachedwapa la Mankind’s Search for God. “Ilo liri ndi mbali zosiyanasiyana, mofanana ndi ntchito yaukatswiri,” iye analemba motero. “Monga momwedi ntchito yaukatswiri iriri ntchito yopangidwa ndi zinthu zosiyanasiyana zambiri, bukhuli liri ndi nkhani ndi mafotokozedwe osiyanasiyana achipembedzo kwakuti limadabwitsa woŵerengayo.”
“Kaŵirikaŵiri, anthu Akumadzulo sadziŵa kalikonse ponena za zikhulupiriro za ku Kum’maŵa ndi ziyambi zawo.” Komabe, monga momwe woŵerenga woyamikirayu akusonyezera, bukhu limeneli limafotokoza “Chihindu ndi Chiziyoni, Chibuda ndi timagulu tampatuko ta Chikristu Chadziko, ndi malingaliro ena osaŵerengeka achipembedzo. Ilo liri ntchito yaukatswiri yothandiza aliyense amene akusanthula zipembedzo,” iye akufotokoza motero.
Anthu ambiri amangodziŵa chipembedzo cha makolo awo ndipo kaŵirikaŵiri amadziŵa zochepa. Koma kodi chipembedzo chanu chiyenera kukhala chokhacho chomwe munabadwiramo, kapena kodi muyenera kupanga chosankha chanzeru pambuyo pakuyerekezera chipembedzo chanu ndi za ena? Bukhu lamasamba 384 la Mankind’s Search for God lidzakuthandizani kupanga kuyerekezera kumeneku. Lingakuyandikitseninso kwa Mulungu wowona.
Ndingakonde kulandira bukhu lamasamba 384, lokhala ndi zithunzithunzi zokongola la Mankind’s Search for God. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 2.)