Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 4/15 tsamba 18-22
  • Chitokoso Chakulalikira M’limodzi la Madoko Aakulu Koposa Padziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitokoso Chakulalikira M’limodzi la Madoko Aakulu Koposa Padziko Lonse
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • “Ntchito Yaumishonale Yongokhala”
  • “Tchalitchi Chapanjinga”
  • Kucheza kwa Panthaŵi Yake ndi Uthenga wa Panthaŵi Yake
  • Nkhani za Amalinyero Zolimbikitsa
  • “Ponya Zakudya Zako”
  • Kodi Mungakhalemo ndi Phande?
Nsanja ya Olonda—1992
w92 4/15 tsamba 18-22

Chitokoso Chakulalikira M’limodzi la Madoko Aakulu Koposa Padziko Lonse

ROTTERDAM, wokhala pamatsiriro oloŵera mu nyanja ya North Sea, a mtsinje wa Rhine wotanganidwa kwambiri wa ku Yuropu, amatchedwa limodzi la madoko aakulu koposa padziko lonse. Pokhala ndi zombo za makampani osiyanasiyana okwanira pafupifupi 500 zomabwera kunoko, Rotterdam amachita malonda mwachindunji ndi malo oposa 800 padziko lonse. Ndithudi, liri doko la dziko lonse.

Komabe, doko Lachidatchi limeneli la zaka 650 siliri chabe mphambano ya zombo. Lirinso pokumanira anthu. Khamu la amalinyero limabwera usana ndi usiku uliwonse kuchokera kungodya zonse za dziko. Amalinyero ameneŵa sanasiidwe ndi Mboni za Yehova mu Netherlands. Mofanana ndi Mboni za kwina kulikonse, zimafunafuna njira zolalikirira mbiri yabwino koposa ya dziko lonse​—yakuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzasanduliza dziko lapansi kukhala Paradaiso​—wa anthu a mtundu uliwonse, kuphatikizapo amalinyero.​—Danieli 2:44; Luka 23:43; 1 Timoteo 4:10.

“Ntchito Yaumishonale Yongokhala”

Zaka zingapo zapitazo, Watch Tower Society mu Netherlands inapempha alaliki anthaŵi zonse, kapena apainiya asanu ndi mmodzi, kukalalikira kuchombo ndi chombo m’doko lonse la Rotterdam. Apainiyawo anatenga mwaŵi umenewu mwachimwemwe. Anatenga chidziŵitso kwa akulu a dokolo, kupenda madoko, ndipo mosapita nthaŵi anazindikira kuti anali ndi ntchito yopereka chitokoso yoti aichite.

“Kuli ngati ntchito yaumishonale yongokhala,” akutero Meinard, mgwirizanitsi wa ulaliki wa padokolo. Kodi akutanthauzanji? “Kaŵirikaŵiri mishonale amayenda ulendo wautali kupita kwa anthu, koma kwa ife anthu amayenda ulendo wautali kubwera kwa ife.” Akuwonjezera kuti, “gawo limene timalalikiramo nlapadziko lonse monga momwe mungalipezere.” Bukhu lapachaka la Rotterdam Europoort la mu 1985 linanena kuti mu 1983, chaka chimene apainiyawo anayamba ntchito yapadera imeneyi, doko la Rotterdam linalandira zombo zapanyanja 30,820 zochokera kumaiko osiyanasiyana okwanira 71. Zimenezo ziridi za padziko lonse!

Moyenerera, “amishonale apadoko”​—monga momwe amalinyero anayamba kutcha apainiyawo​—alinso apadziko lonse. Geert, Peter, ndi mkazi wake Karin, ndi Adatchi, Daniël ndi Meinard anachokera ku Indonesia; ndipo Solomon ndi wa ku Ethiopia. Pokhala ochokera ku Yuropu, Asia, ndi Afirika alaka vuto lakudziŵa zinenero zisanu ndi zitatu zowapinga, koma kuti apambane m’ntchitoyi, anafunikira kulaka zopinga zina.

“Tchalitchi Chapanjinga”

“Sungangoyenda pamlatho, kukwera pamtantho, ndi kuloŵa m’chombo,” akutero Peter, wazaka 32, yemwe kale anali mmalinyero. “Umafunikira chiphaso cha malowo.” Zimenezo zitanthauza chiphaso choloŵera pamlatho ndi chiphaso choloŵera m’zombo. “Kutenga ziphasozo kunachitika mochedwa,” akukumbukira motero Peter, “koma pambuyo pake tinatenga ziphaso zisanu ndi zitatu, zokwanira, zokhala ndi zithunzithunzi zathu ndi zisindikizo zaboma.” Iwo anagaŵa doko lamilatholo la makilomita 37 m’zigawo zitatu, chirichonse choyang’aniridwa ndi apainiya aŵiri.

Komabe, ndimotani mmene mungachitire ndi unyinji wa zinenero zolankhulidwa ndi amalinyero ochokera kumaiko ambiri? Ngakhale kuti apainiyawo anakundika mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero 30 nanyamula ochuluka monga anathera panjinga zawo, mabukuwo anawoneka kukhala osakwanira. “Sumadziŵa kwenikweni zinenero zomwe zidzafunikira,” akunena tero Solomon wazaka 30 akumwetulira. “Kaŵirikaŵiri zimachitika kuti amalinyero amafuna mabuku m’zinenero zimene sitinanyamule, ndiyeno nkutiuza kuti chombo chawo chidzanyamuka m’maola pafupifupi atatu.” Posafuna kulefula amalinyerowo, mpainiya mmodzi amachoka mofulumira, nakatenga mabuku oyenera, nabwerera mofulumira, nawapereka kwa amalinyero olakalakawo. “Pamene vuto limodzimodzilo linabuka pamene tinali kulalikira m’mbali zina za doko lokhala pamtunda wotenga ulendo wa maola atatu panjinga,” akutero Peter, “kunali kwachiwonekere kuti tinafunikira njira ina yochitira ndi vutolo.”

Tsiku lina Mboni ina yokhala m’dera la dokolo inadabwitsa apainiyawo mwakuwapatsa ngolo ziŵiri zokhoza kukokedwa ndi njinga, iriyonse yaukulu wa bafa. Apainiyawo anadzaza ngolozo ndi mabuku azinenero zonse zomwe zinalipo, nazikoloŵeka kunjinga zawo, namka kudokolo. Mosapita nthaŵi ngolozo zinadziŵika kwambiri. “Zinakhala chizindikiro chathu,” akutero mmodzi wa apainiyawo. “Mlonda wapachipata atatiwona tikubwera, amatsegula chipatacho, kutikodola kuti tiloŵe, nafuula nati: ‘Tawonani tchalitchi chapanjinga chikuyenda!’” Nthaŵi zina, mlondayo atawona “tchalitchi chapanjingacho” chikubwera kumbali yake, amatsegula chipata nafuula nati: “Pali zombo ziŵiri za ku Poland ndi chimodzi cha ku Tchaina!” Mawu othandiza amenewo amatheketsa apainiyawo kukwera m’zombozo ndi mabuku a zinenero zoyenerera. Koma ayeneranso kufika panthaŵi yoyenerera. Chifukwa ninji?

Kucheza kwa Panthaŵi Yake ndi Uthenga wa Panthaŵi Yake

Apainiyawo angalankhule kwa antchito m’zombozo kokha panthaŵi yakupuma m’maŵa ndi masana kapena pakudya chakudya chamasana. Komabe, wophika zakudya ali ndi maola osiyana ogwirira ntchito, ndipo kazembe wa chombo ndi maofisala ena amapezeka tsiku lonse. Ndiponso, apainiyawo amadziŵa kuti zombo za Briteni zokocheza pa Rotterdam zimamamatira ku nthaŵi ya Briteni (yosiyana ndi nthaŵi ya Chidatchi ndi ola limodzi), kotero kuti antchito awo amapita kukadya pamene antchito osakhala aku Briteni amabwerera pantchito. Nzodziŵikiratu kuti, mpainiya wakudoko amafunikira watchi yodalirika.

Komabe, kodi amalinyero ali ofunitsitsa kugwiritsira ntchito nthaŵi yawo yakupuma kukambitsirana Baibulo? “Kaŵirikaŵiri, ndimawapeza kukhala ofunitsitsa kukambitsirana uthenga wa Ufumu,” akutero Geert, wazaka 31. “Mwina nchifukwa chakuti amakhala oyamba kuwona kulephera kwa maboma aumunthu.” Mwachitsanzo, amalinyero ena anauza Geert kuti atabweranso padokolo pambuyo pa miyezi yambiri, anapeza kuti miulu ya dzinthu dza anthu aku Ethiopia okanthidwa ndi njala zimene anatsitsa zinalipobe, ndipo panthaŵiyo dzinthuzo zinali zitawola kale ndipo zinali ndi makoswe ochuluka. “Nchifukwa chake amalinyero ambiri ataya chiyembekezo chawo m’ndale,” akutero Geert. “Choncho lonjezo la Baibulo la boma limodzi kaamba ka anthu onse limawakopa.”

Peter akuvomereza. “Kazembe wina wa chombo cha Jeremani anati zaka khumi zapitazo antchito ake akanandithamangitsa m’chombocho, koma kusintha kwa mikhalidwe ya dziko kwa lerolino kunadzutsa chikondwerero chawo muuthenga wa panthaŵi yake wa Baibulo.” Wophika chakudya m’chombo cha Korea anasimba kuti pamene nkhondo pakati pa Iran ndi Iraq inali mkati, chombo chonyamula mafuta chimene anali kugwiramo ntchito chinakanthidwa ndi bomba la roketi ndi kuyaka moto mu Persian Gulf. Analumbira kuti ngati akakhala ndi moyo, adzafunafuna Mulungu. Anapumulukadi. Pamene apainiyawo anakumana naye pambuyo pake ku Rotterdam, anatenga mabuku onse omwe iwo anambweretsera m’chinenero cha ku Korea.

Zombo zambiri zimakhala zokocheza padoko kwa masiku angapo. Zimenezi zimalola apainiya kubwererako kwa nthaŵi ziŵiri, zitatu, kapena zoposerapo kuti apitirize makambitsirano a Baibulo pambuyo pa ntchito. Komabe, ngati injini ya chombo sikugwira bwino ntchito, chombocho chingakhale chokocheza kwa milungu itatu. “Zimenezo zimaipira kampaniyo,’ akutero mpainiya akumwetulira, “koma zimakomera ntchito yathu.” Ndipo, pambali pa kupitiriza makambitsirano a Baibulo, apainiyawo amalinganiza kusonyeza imodzi ya maprogramu amasilaidi a Sosaite ya mutu wakuti, “The Bible​—A Book for This Generation” (Baibulo​—Bukhu la Mbadwo Uno), m’chipinda chodyera. Ndiponso amalinyero ena amabwera kumisonkhano ya Mboni za Yehova ya magulu ochuluka olankhula zinenero za maiko ena mu Rotterdam. Zimenezi zimachitika kufikira injini itakonzedwanso. Pamenepo Baibulo limatsekedwa. Nsambo zolunzanitsa chombo ndi doko zimamasulidwa, ndipo chombocho chimachoka padokolo​—koma sichimachoka m’maganizo a apainiyawo.

Nkhani za Amalinyero Zolimbikitsa

Mwakugwiritsira ntchito ndandanda za m’nyuzipepala kapena dongosolo lamakompyuta a anthu onse la oyang’anira dokolo, apainiya apadokowo amasunga cholembedwa cha zombo zimene anachezera zobwera ndi zopita. Chimodzi cha zombozo chitangofika kachiŵiri, apainiyawo amafunitsitsa kufikira amalinyero kuti adziŵe zimene zinachitika kuyambira pakucheza kwapapitapo. Ha, nkhani zimene amalinyero amasimba nzolimbikitsa chotani nanga!

Mmalinyero mmodzi anapereka bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi kwa anzake asanu chombo chitayamba ulendo wapanyanja, ndipo asanu ndi mmodziwo anachita phunziro Labaibulo. Iye anajambulanso mutu wonena za moyo wabanja pakaseti nauseŵeranso m’chipinda chodyera kuti antchito onse apindule. M’chombo china, mmalinyero wina yemwe anapezeka pa Nyumba Yaufumu m’doko lapafupi la Antwerp anaika chikwangwani kukhoma la chipinda chodyera chomwe analembapo mawu azilembo zazikulu akuti “Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova.” Ndipo anaitanira antchito anzake kumeneko pochititsa msonkhano wa Baibulo. Asanatsitse chikwangwanicho, anaitaniranso antchito anzake kumsonkhano wotsatira. Mlungu wotsatira, chikwangwanicho ndi antchitowo anali pamalo amodzimodziwo.

Apainiyawo anapezanso kuti amalinyero ena sanasiye mabuku awo. “Titaloŵa m’chipinda cha Isaac, ofisala wa njira zolankhulirana ndi wailesi wa Kumadzulo kwa Afirika, tinavutika kupeza pokhala,” akusimba tero Meinard. “Magazini a Sosaite, mabuku, ndi makonkodansi anali paliponse​—otsegulidwa.” Ndiponso Isaac anali ndi ndandanda ya mafunso a Baibulo okonzeratu, pakuti anali kuyembekezera kubweranso kwa apainiyawo.

Komabe, amalinyero ena samayembekezera kuti apainiya awafikire. Usiku wina foni ya Geert inaimba iye atagona.

“Kodi ameneyo angakhale ndani usiku uno?” anang’ung’udza motero Geert akupapasira foniyo.

“Moni, ndine bwenzi lako!” linatero liwulo mwachimwemwe.

Geert anayesa kukumbukira amene munthuyo angakhale.

“Bwenzi lako la m’chombo,” linateronso liwulo.

“Ndi 3 koloko mbandakucha!” anatero Geert.

“Inde, komabe munandiuza kuti ndidzakuimbireni foni chombo changa chitangofika ku Rotterdam. Eya, ine ndafika!” Mwamsanga pambuyo pake, Geert anauyamba ulendo wake wokakumana ndi bwenzi lakelo lokhala ndi chikondwerero m’Mawu a Mulungu.

“Ponya Zakudya Zako”

Chiyamikiro kaamba ka mabuku ofotokoza Baibulo chikusonyezedwanso m’makalata omwe amalinyerowo analembera apainiya. Nazi ndime zotsatira zogwidwa mawu:

‘Ndayamba kuŵerenga bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi . . . Tsopano ndikumvetsetsa zinthu zina zomwe sindinazidziŵe. Ndikhulupirira kuti chombo chathu chidzabweranso ku Rotterdam.’​—Angelo.

‘Ndinaliŵerenga bukhu lija, ndipo ndatumiza mafunso kotero kuti mudzawayankhe pondilembera makalata.’​—Alberta.

‘Tsopano ndimaŵerenga Baibulo tsiku lirilonse. Ndine wokondwa kukhala bwenzi lako. Kupeza mabwenzi onditsogoza kwa Mulungu ndichinthu chabwino kwambiri chomwe chandichitikira m’moyo.’​—Nickey.

Makalata ochititsa nthumanzi otero amakumbutsa apainiyawo zomwe Baibulo limanena pa Mlaliki 11:1 kuti: “Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri.” Amasangalala kwambiri atadziŵa kuti amalinyero ena atenga kaimidwe kawo kumbali ya Yehova.

Stanislav, mmalinyero Wachipolish, anachita chidwi ndi zimene anaphunzira m’mabuku a Sosaite. Anasonkhanitsa mofulumira kalaibulale kakang’ono ka mabuku ofotokoza Baibulo ndipo, ali paulendo wapanyanja, anaŵerenga bukhu lirilonse. “Pamene anatilemberanso kalata,” akutero Meinard, “anatiuza kuti anabatizidwa.”

Folkert, mkulu wa zombo zoyenda m’dzikolo, anayamba kumva uthenga wa Ufumu ali ku Rotterdam. Pambuyo pa miyezi iŵiri iriyonse ankabweranso kudokolo kwa mlungu umodzi naphunzira Baibulo kwa masiku asanu ndi aŵiri otsatizana. Ndiyeno, asanapite paulendo wina wamiyezi iŵiri, apainiya anampatsa ndandanda ya makeyala a Nyumba Zaufumu zamunjira ya zombo yaulendo wake. Folkert anaima pamaholowo ndipo anasonkhezeredwa ndi mmene analandiridwira mwachikondi. Posapita nthaŵi, mkulu ameneyu anabatizidwa ndipo tsopano amatumikira Yehova mwachangu.

Mike, ofisala wa Gulu Lankhondo Lapanyanja la Briteni, anakumanapo ndi Mboni ndipo anali kuphunzira Baibulo ali paulendo wapanyanja. Nthaŵi ina, pamene chombo cha nkhondo chimene anagwiramo ntchito chinakocheza pa Rotterdam, anagwiritsira ntchito njinga yake yokhoza kupindidwa kupita ku Nyumba Yaufumu. Anachita chidwi ndi chikondi ndi umodzi zimene anawona ndipo anauza mabwenzi ake kuti wasankha kusiya ntchito yake. Ngakhale kuti kunatsala zaka zinayi zokha kuti alandire penshoni yokhala ndi malipiro aakulu, anamamatira ku chosankha chake nabatizidwa pambuyo pake.

Meinard akunena kuti: “Changu cha Mike, Stanislav, Folkert, ndi ena chakutumikira Yehova chimatisonkhezera kupitirizabe kufunafuna amalinyero onga iwo padokolo.”

Kodi Mungakhalemo ndi Phande?

Atapenda zaka zokwanira pafupifupi khumi zakulalikira m’limodzi la madoko aakulu koposa padziko lonse, “amishonale apadoko” asanu ndi mmodziwo akuvomereza ndi mtima wonse​—ntchitoyo yakhala yopereka chitokoso koma yofupa. “Titamaliza kulalikira tsiku lirilonse,” akunena tero Meinard, “timatchova njinga kubwerera kunyumba ndi lingaliro lakuti ena a amalinyerowo akuyembekezera ulendo wathu wotsatira.”

Kodi pangakhale amalinyero omwe akuyembekezera kuchezeredwa padoko lakwanuko? Mwina akulu mumpingo mwanu angapange makonzedwe kotero kuti mukhale ndi phande m’ntchito imeneyi yopereka chitokoso koma yofupa.

[Bokosi patsamba 20]

KUFIKA KUMAGAWO KUMENE NTCHITO YATHU NJOLETSEDWA

M’chaka china posachedwapa, zombo zoposa 2,500 za kumaiko kumene ntchito ya Mboni za Yehova njoletsedwa zinakocheza pa Rotterdam. Ndipo apainiya apadoko anawona zimenezo kukhala mwaŵi wakufika kumagawo amenewo ndi uthenga wa Baibulo.

M’chimodzi cha zombo zoyambirira za ku Asia chomwe anafikira, apainiyawo anagaŵira mabuku awo onse okwanira 23, nasiya antchito ena okwiya chifukwa chophonya kupeza kope. Mnyamata wina wogwira ntchito m’kitchini ya chombo china cha ku Asia anachita mochenjera. Atalandira bukhu kwa mpainiya, analibweza atalikuta m’pepala lomwe analembapo keyala. Mpainiyawo anaiwona mfundoyo. Kunyamula bukhulo kukamuika paupandu kwambiri mnyamatayo. Tsiku limenelo mpainiyayo analitumiza ku Far East.

M’chombo china chochokera ku Afirika munali mmalinyero wina yemwe anali ndi ndandanda ya mabuku omwe Mboni zakwawo zinafuna. Kuyambira pamenepo, nthaŵi iriyonse imene mmalinyero ameneyo abwerera kwawo, sutukesi yake imadzazidwa ndi mabuku. Mmalinyero wa kudziko lina la m’Afirika anagwiritsidwa mwala kwambiri pamene mpainiya yemwe amaphunzira naye anampatsa makope atatu okha a bukhu la Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. “Zimenezo sikanthu!” anafuula motero mmalinyeroyo, akumatukula mikono yake posoŵa chochita. “Abale akwathu afuna mabuku 1,000!” Kuti akhale wotetezereka, apainiyawo anamfulumiza kutenga makope 20 okha panthaŵi imodzi.

Mwina yosangalatsa inali nthaŵi imene apainiyawo anadziŵa kuti chombo china chidachokera kudziko kumene Mboni zinali kuzunzidwa chifukwa cha zikhulupiriro zawo, ndikuti ambiri anataya ntchito zawo ndi katundu. Atadziŵa kuti kapitawo m’chombocho anali Mboni, anafikira kazembe wake nampempha chilolezo chakutumiza chithandizo cha osoŵa pachombo chake. Kazembeyo anavomera, ndipo pambuyo pa masiku oŵerengeka, matumba aakulu okwanira zana limodzi a zovala, nsapato, ndi katundu wina anatumizidwa kwa Mboni m’dzikolo.

[Bokosi patsamba 21]

KULALIKIRA KUCHOMBO NDI CHOMBO​—LINGALIRO LA MKAZI

“Poyamba, ndinazengereza kutsagana ndi Peter,” akukumbukira motero Karin, mkazi yekha mwa apainiyawo, “chifukwa ndinamva mbiri yakuti amalinyero kaŵirikaŵiri ngankhanza ndi oledzera. Komabe, ndapeza kuti ambiri ali aulemu. Kaŵirikaŵiri, mmalinyero atadziŵa kuti ndife okwatirana, amatulutsa chithunzithunzi cha mkazi wake ndi ana nayamba kutifotokozera za banja lake. Mwanjira yotero, takhoza kugaŵira makope ochuluka a bukhu la Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe.”

Kuyendera zombo monga mwamuna ndi mkazi okwatirana kumakupangitsanso kukhala kosavuta kufikira akazi a antchito ndi akazi ena amene nthaŵi zina amagwira ntchito monga anesi. “Kaŵirikaŵiri samakhala omasuka kwa alendo,” akutero Karin, “koma atandiwona, amafunitsitsa kulankhula nane.”

Kodi nchiyani chomwe chinali chitokoso chachikulu m’ntchito yakeyo? “Makwerero ansambo,” akuyankha tero Karin. “Ndinada zinthu zopsapsala zimenezo.” Kodi anawalaka mantha akewo? “Inde. Nthaŵi ina pamene ndinazengereza kukwera, gulu la amalinyero a ku Paraguay anangondipenya nafuula nati: ‘Udzakhoza. Tangodalira mwa Mulungu.’ Ndithudi,” akutero Karin apo akuseka, “atandiuza zimenezo, ndinalibe chochita koma kungokwera basi.” Mwamuna wake wochita chidwiyo akuti: “Pambuyo pa zaka zinayi za makwerero ochuluka ansambo, iye tsopano amakwera mofanana ndi mmalinyero.”

Karin ndi mwamuna wake, Peter, analoŵa kalasi la 89 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ku United States. Pa September 28, 1990, anapita kugawo lawo latsopano, ku Ecuador, dziko lokhala ndi doko. Ayenera kuti amawona monga ngati ali kwawo kwenikweni.

[Bokosi patsamba 22]

KODI NDINU MMALINYERO?

Kodi mufuna kupezekapo pamsonkhano Wachingelezi wa Mboni za Yehova pamene chombo chanu chakocheza palimodzi la madoko aakulu padziko lonse? Pamenepo khalani nayo pafupi ndandanda yotsatirayi ya makeyala a pakali pano a Nyumba Zaufumu ndi nthaŵi za misonkhano:

Hamburg, Schellingstr. 7-9; Loŵeruka, 4:00 p.m.; foni: 040-4208413

Hong Kong, 26 Leighton Road; Sande, 9:00 a.m.; foni: 5774159

Marseilles, 5 Bis, rue Antoine Maille; Sande, 10:00 a.m.; foni: 91 79 27 89

Naples, Castel Volturno (makilomita 40 kumpoto kwa Naples), Via Napoli, corner of Via Salerno, Parco Campania; Sande, 2:45 p.m.; foni: 081/5097292

New York, 512 W. 20 Street; Sande, 10:00 a.m.; foni: 212-627-2873

Rotterdam, Putsestraat 20; Sande, 10:00 a.m.; foni: 010-41 65 653

Tokyo, 5-5-8 Mita, Minato-ku; Sande, 4:00 p.m.; foni: 03-3453-0404

Vancouver, 1526 Robson Street; Sande, 10:00 a.m.; foni: 604-689-9796

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena