Amwenye Achigoajiro Alabadira
ALIKHALE pamthunzi wa mtengo waukulu atavala mkanjo wakuda wautali, mkazi wachikulireyo anawoneka ngati wa kudziko lina. Analankhulanso chinenero chachilendo kwa ife. “Mukabwerenso,” iye anatero mwachimwemwe. Akuloza anthu okwanira 50 a fuko lake omwe anamzinga, anawonjezera nati: “Tonsefe tifuna kuti mukabwerenso. Mudzibwera mlungu uliwonse!”
Kodi anthuwa anali ayani? Kodi nchifukwa ninji anali ofunitsitsa kuti tikabwerereko, ngakhale kuti sanakumanepo nafe? Lekani tikuuzeni za tsiku limene tinali ndi Amwenye Achigoajiro okhala ku La Guajira Peninsula kumpoto koma chakum’maŵa kwa Colombia ndi kumpoto koma chakumadzulo kwa Venezuela.
Zimene Tinawona Poyamba
Titanyamuka ku Caracas, likulu la Venezuela, siteshoni yathu yoyamba inali Maracaibo. Poloŵa m’tauniyo, tinawona asungwana atatu akuyenda pamsewu atavala mikanjo yaitali yowoneka bwino. Nkhope zawo zinali zosiyana ndi za nzika zambiri za Venezuela—mafupa a m’masaya otundumuka, khungu lodera, tsitsi lakuda lowongoka. Powona kuyenda kwawo kosangalatsa kwapang’onopang’ono, tinachita chidwi kuwona Amwenye Achigoajiro nthaŵi yoyamba.
Tsiku la ulendo wathu wa ku La Guajira Peninsula linacha bwino ndipo linali labata. Kusanatenthe kwambiri m’maŵa, ifeyo okwanira 50 tinakwera basi, osangalala pokhala ndi phande m’ndawala yapadera ya dziko lathu lino yopereka uthenga wa Baibulo kumadera akutali a Venezuela. Tinali kupita ku tauni ya Paraguachón, kumalire ogaŵana ndi Colombia.
Titachoka mumzinda wa Maracaibo, tinadutsa matauni aang’ono ambiri ndi midzi, iriyonse yokhala ndi msika ndi masitolo ogulitsira nsapato zoluka ndi mikanjo yaitali yamawonekedwe abwino yotchedwa mantas. Mudzi uliwonse unali ndi bwalo lapakati laudongo ndi tchalitchi chopakidwa chikule, kuchititsa malo onsewo kuwoneka bwino. Anthu onse anali amawonekedwe Achimwenye. Ngakhale kuti anali osiyana kwambiri ndi ife, tinakumbukira kuti ameneŵa anali ena a nzika zoyambirira za Venezuela.
Kufunafuna Nyumba
Potsirizira pake tinafika kumene tinali kupita. Basi yathu inaima m’mbali mwa msewu pafupi ndi khoma lalifupi pamthunzi wa mtengo waukulu. Kumbali ina ya khomalo kunali sukulu ya m’mudzimo—yotseka chifukwa chakuti panali pa Sande.
Titadzigaŵa m’magulu aŵiri, tinapita mbali zosiyana kufunafuna nyumba. Tinali kukaitanira aliyense kunkhani Yabaibulo yodzakambidwa m’chinenero cha Chigoajiro pa 3 koloko masanawo m’bwalo la sukulu. Evelinda, Mwenye Wachigoajiro mwachibadwa, anatsagana nafe. Tinakhulupirira kuti zimenezi zikatipangitsa kulandiridwa bwino, pakuti ngakhale kuti tikakhoza kulankhula Chispanya, sitinachidziŵe mpang’ono pomwe Chigoajiro.
Titangotuluka m’mudzi, tinataya nthaŵi kwambiri kuyenda pakati pa nyumbazo. Pamene tinali kuyenda pamsewu wautali wowongoka wokhala ndi zitsamba zoŵirira kumbali zonse ziŵiri, kamnyamata ka zaka pafupifupi khumi kanagwapo kuyenda nafe nikamatiyang’ana mwachidwi ndithu. Evelinda anakamwetulira nafotokoza m’Chigoajiro cholinga cha ulendo wathu m’deralo. Dzina lake linali Omar, ndipo anathaŵa titamuitanira kunkhani.
Titapambuka pamsewuwo, tinatenga kanjira kafumbi kochita matope ndi mvula yaposachedwa. Tinauzidŵa kuti timeneti tinali tinjira tozembetsera katundu pakati pa Colombia ndi Venezuela. Mpweya unadzala fungo la msipu wobiriŵira. Ngakhale kuti tinavutika ndi chitungu, changu chathu sichinafooke. Komabe, kuvutika konse kunaiŵalika pamene kanjira kodzera m’nkhalango yoŵirira yotentha, kanatulukira mwadzidzidzi pamalo aakulu atetete—famu yeniyeni ya Agoajiro.
Kuyang’anizana ndi Agoajiro
Pafupifupi mbuzi khumi ndi ziŵiri, zamatonthomatontho okongola oyera, akuda, ndi ofiirira, zinaligone pamthunzi, zikutafuna pang’onopang’ono. Pamachira otansidwa pakati pa mitengo iŵiri, panagona mkazi akuyamwitsa mwana wake. Tiana tingapo tinali kuseŵera pafupi. Mkaziyo anali kunja kwa nyumba yomata yofolera ndi udzu yotchingidwa ndi mpanda wa mitengo ndi nsambo. Panalinso timisasa tina pamalopo. Mowonekeratu kena kanali kakitchini, kumene moto wankhuni unali kuyaka pansi pa miphika yaikulu yonga nkhali. Zikopa za mbuzi zinali zolenjekeka chapafupi kuti ziume.
Atatiwona, mwamuna yemwe anaima pafupi ndi chipata anathamanga nakatiikira timipando tiŵiri pafupi ndi mkazi wogona pamachira. Evelinda anapereka moni kwa mwamunayo ndi mkaziyo m’chinenero chawo nafotokoza chiyembekezo cha m’Malemba cha mtsogolo mwakugwiritsira ntchito brosha ya zithunzithunzi ya Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Mikhalidwe yamtendere m’malowo inatisonyeza kuti maupandu a dziko lonse kapena kuwonjezereka kwa masoka m’mizinda yapafupi sizikakhala nkhani zoyenerera kunoko. Mboni ina m’gulu lathu inali itafotokoza kuti popeza kuti Amwenye Achigoajiro ngamanyazi mwachibadwa, nkofunika kusonyeza chikondi ndi nkhaŵa yeniyeni kaamba ka ubwino wawo poyambirira. “Kaŵirikaŵiri timafunsa za umoyo wa banja, za zokolola, ngati kudagwa mvula posachedwa, ndi zina zotero,” iye anatero. “Zimenezi zimatitsegulira njira yowauzira za Ufumu wa Mulungu ndi kuwasonyeza kuti posachedwapa Yehova adzachotsa kuipa konse ndi Satana Mdyerekezi, yemwe iwo amamuwopa kwambiri.”
Pamene Evelinda analankhula, omvetsera ake anavomereza, ndipo posapita nthaŵi mkazi wina ndi ana angapo anaphatikana nafe. Tidauzidwa poyamba kuti lamulo la Agoajiro limalola mwamuna kukhala ndi akazi ambiri. Kodi zimenezo ndizo zili kunoko? Zimenezo zinatikumbutsa za Yenny, Mgoajiro wokongola wa zaka 21 yemwe amakhala ku Maracaibo. Mwamuna wachuma Wachigoajiro anapereka malowolo aakulu kaamba ka msungwanayo. Koma makolo ake, amene saali Mboni za Yehova, anasemphana. Ngakhale kuti amayi ŵa Yenny anavomereza ukwati, atate ŵake anakana. Wofunsirayo anali atakwatira kale mkulu wa Yenny!
Pamene Evelinda anamaliza ulaliki wake, mwamunayo anagulako brosha. Ndiponso mkazi yemwe anaima kumbuyo kwake anapempha imodzi, ndipo tinampatsa mokondwera. Panthaŵiyo anzathu omwe tinali nawo anali atapita. Choncho tinaitanira banjalo kunkhani yamasana ndiyeno nkupita, poti sitinafune kusoŵa m’dera lakumidzi lachilendolo.
Mboni ina m’gulu lathu inasimba zimene zinamchitikira. Mwamuna yemwe anali pamachira anamvetsera mosamalitsa pamene mkazi wake anabweretsa zakumwa—matambula aŵiri a chicha, wophikidwa ndi chimanga chosinja. Mwaulemu, mbale wathu analandira namwa. Pambuyo pake, Magaly, mnzake Wachigoajiro anafotokoza mmene chakumwacho amachipangira. Kaŵirikaŵiri, chimangacho amachisinja ndi mano! Mlongoyo analephera kudziletsa naseka atawona kuti nkhope ya mbaleyo yasintha ndi kudabwa.
Mwamuna wina Wachimwenye, yemwe anachita chidwi ndi kuyesayesa kwa abale kumfikira ndi uthenga wa Baibulo, anatsika pamachira ake. Atavala malaya, anawatsogolera kumudzi wina wobisika umene iwo anaphonya.
Pakudutsa pa famu ina pamene anzathu anali kukambitsirana ndi achikulire m’banjalo, tinawona kagulu ka ana aang’ono amaliseche ndi mimba zotumuka ataima du pansi pa mtengo. Tinadzadziŵa kuti mkhalidwe umenewu uli chifukwa cha manyutirishoni ndi tizilombo. Anthu ambiri mwa ameneŵa alibe madzi akumpopi ndi magetsi. Ndithudi, zimenezi zikutanthauza kuti alibe mafiriji, mafani, kapena magetsi m’nyumba.
Chiŵerengero Chosayembekezereka
M’maŵa unatha mofulumira kwambiri. Pobwerera kumene kunali basi kukadya chakudya chamasana, sitinadziŵe unyinji wa anthu oitanidwa amene akadza kudzamvetsera nkhani Yabaibulo masana.
Pa 2:45 p.m., sitinadziŵe ngati gulu lathu lokha ndilo likakhala omvetsera a mbale wathu Wachigoajiro, yemwe anakonzekera nkhani yoti idzakambidwe m’mphindi 45 m’chinenero chakumaloko. Koma sizinali choncho! Banja laling’ono loyamba kubwera linafika mwamanyazi m’bwalo la sukulu. Ayenera kuti anadabwa pamene aliyense anawalandira bwino. M’mphindi zingapo zotsatira, ambiri anafika, mwachiwonekere ena anayenda mtunda wautali. Banja lokhala pafamu yokhala ndi mbuzi khumi ndi ziŵiri nalonso linalipo! Hi, mkazi uja yemwe analigone pamachira anawoneka wosiyana chotani nanga atavala manta yake yakuda yochititsa kaso! Ngakhale Omar wachichepere, yemwe tidalankhula naye pamsewu, anadza, mwachiwonekere ali yekha. Pamene ena anafika, sitepe lalitali lakonkiri lomwe linatumikira monga benchi m’bwalo la pasukulupo linadzala. Litawona zimenezo, bwenzi lathu loyendetsa basi linagulula mipando m’basimo kuti anthu akhalepo pomvetsera nkhani.
Amwenye Achigoajiro okwanira 55 anakhala namvetsera pamene Eduardo anali kukamba nkhani Yabaibulo. Komabe, sanakhale chete kotheratu. Ngati anavomereza mfundo yomwe wokamba nkhaniyo anatchula, anadzuma kapena kung’ung’udza. Pomwe analankhula za mapeto akuipa omwe alinkudza, mkazi wachikulire wotchulidwa poyamba anafuula amvekere: “Inde, pali kuipa kochuluka. Kunena zowona, alipo pano anthu ena oipa. Ndikhulupirira kuti akumvetsera!” Mbale Eduardo anavomereza ndemangayo mwaluso napitiriza ndi nkhani yake.
Pamene nkhani inatha, mbale mmodzi m’gulu lathu anajambula chithunzithunzi. Agoajiro anakonda zimenezo kotero kuti anapempha ngati angatukule mikono yawo m’mwamba atanyamula mabrosha a Sangalalani ndi Moyo kaamba ka chithunzithunzi chotsatira. Ndiyeno ena anachoka pang’onopang’ono napita, koma pafupifupi okwanira theka anatsala natiwona tikukwera basi. Anatikakamiza kulonjeza kuti tikabweranso, ndiyeno anaima natitsazika kufikira pamene basi inaleka kuwoneka.
Pamene tinali kupita, tinauwonadi kukhala mwaŵi kupereka mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu kwa anthu ameneŵa. Ambiri anaumva kwa nthaŵi yoyamba. Mboni za ku Maracaibo zinali kale kulankhula za ulendo wawo wotsatira. Kodi pakakhala zotulukapo za nkhaniyi?
Zotulukapo Zabwino
Abalewo anabwereranso pambuyo pa milungu iŵiri. Anagaŵira mabuku ochuluka ofotokoza Baibulo, anapanga maulendo obwereza kwa okondwerera, ndipo anayambitsa maphunziro Abaibulo. Ndiponso, Amwenye 79 anapezekapo pamsonkhano wapoyera wapanja. Pachochitikacho abale anafotokoza kuti akabweranso pambuyo pa milungu itatu mmalo mwa iŵiri chifukwa cha msonkhano wadera. Amwenyewo anadabwa. “Mwina tidzafa nthaŵiyo isanafike!” anatero mmodzi wa iwo. Iwo anafunsa zimene msonkhano wadera umatanthauza. Zinamveka zabwino kwambiri moti ananena kuti nawonso afuna akapezekeko! Makonzedwe anapangidwa, ndipo okwanira 34 anakhoza kupezekapo pamsonkhano ku Maracaibo, kumene abale olankhula Chigoajiro anawathandiza kumvetsera programu Yachispanya.
Chifuno cha Yehova nchakuti ‘anthu onse . . . afike pozindikira chowonadi.’ (1 Timoteo 2:3, 4) Nkodzetsa chimwemwe chotani nanga kuwona kulabadira koteroko mwa Amwenye ameneŵa ofuna chowonadi okhala ku La Guajira Peninsula!
[Bokosi patsamba 26]
Miyoyo Ilemeretsedwa ndi Chowonadi cha Baibulo
Iris ndi Margarita, achichepere aŵiri Achigoajiro, anakondwera kuwona brosha ya Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Koma anali ndi vuto limodzi. Sanadziŵe kuŵerenga. Mboni yomwe inawachezera inadzipereka kuwathandiza mwakugwiritsira ntchito kabukhu ka Learn to Read and Write. Posakhalitsa, asungwanawo anasangalala pokhala okhoza kulemba ndi kutchula dzina la Yehova molondola.
Pamene anapita patsogolo, anazizwa ndi chiyembekezo chodabwitsa choperekedwa ndi Baibulo. Anachita chidwi kwambiri ndi lonjezo lakuti anthu onse adzasangalala ndi ufulu. “Kwathu kuno moyo ngomvetsa chisoni kwa achicheperefe,” iwo anafotokoza tero. “Kaŵirikaŵiri amatikwatitsa kwa mwamuna wongopezeredwa tikali aang’ono kwenikweni, ndipo kugwirira chigololo nkofala.”
Chokondweretsa kwambiri kwa Iris ndi Margarita chinali kupezeka kwawo pamsonkhano wadera ku Maracaibo. Nkhope zawo zinasonyeza chimwemwe chomwe anali nacho m’mitima mwawo, makamaka poimba nyimbo. Nthaŵi zonse ankaima pakhomo molakalaka patsiku limene Mboni ikabwera kuphunzira nawo Baibulo, ndipo sanaphonye nkhani yapoyera imene inakambidwa m’mudzi mwawo. Asungwana ameneŵa awona kuti miyoyo yawo yalemeretsedwadi ndi chidziŵitso cha Yehova Mulungu ndi zifuno zake.