Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 9/15 tsamba 24-27
  • Akupeza Chimwemwe Chenicheni mu “Paradaiso”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akupeza Chimwemwe Chenicheni mu “Paradaiso”
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Kuwopa Imfa Kulakidwa
  • Akopeka ndi Chikristu Chowona
  • Apeza Mtendere ndi Chimwemwe
  • Kudzimana ndi Mfupo
Nsanja ya Olonda—1992
w92 9/15 tsamba 24-27

Akupeza Chimwemwe Chenicheni mu “Paradaiso”

PARADAISO! Kaŵirikaŵiri liwulo limabwera m’maganizo pamene anthu aganiza za Hawaii​—ndipo pazifukwa zabwino. Zinthu zabwino zopezeka kwambiri kunoko ndizo mkhalidwe wakunja wabwino, thambo loti ngwe, peyupeyu wa mingwalangwa, kamphepo kotsitsimula kayaziyazi, ndi madoko a mchenga​—mikhalidwe imene anthu ambiri angalingalire kukhala yaparadaiso.

Zinthu zimenezi zakopa anthu akutali ndi apafupi. Iwo abwera kuchokera ku Asiya, chigawo cha Pacific, zigawo za Amereka, ndipo ngakhale kumalo onga zisumbu za Caribbean ndi Ulaya. Ambiri abwera kudzakhala kuno chifukwa cha mkhalidwe wakunja wabwino wa chaka chonse. Ena abwera kudzafuna chuma​—ndiponso, chimwemwe. Chotulukapo chakhala chitaganya cha anthu a mitundu ndi mafuko osiyanasiyana, ndi kusiyana kwakukulu kwa miyambo ya kakhalidwe ndi zikhulupiriro zachipembedzo.

Komabe, sizabwino zokhazo zimene ziri kunoko. Mofanana ndi malo ambiri okongola padziko lapansi, Hawaii ngwodzala ndi upandu, anamgoneka, kupulupudza kwa ana, kuipitsa, ndi mavuto ena ochuluka ogwera mtundu wa anthu mosasamala kanthu za kumene wina angakhale. Chifukwa cha kusasamala kwa anthu ndi dyera lawo, kukongola kwa zisumbu za Hawaii kukuwonongeka pang’onopang’ono. Anthu amafuna paradaiso, koma sionse okhala kuno amene amafunadi kupanga kapena kuyesa kusunga zisumbuzi kukhala paradaiso. Pamafunikira zoposa malo okongola ndi mkhalidwe wakunja woyenerera kuti paradaiso apangidwe.

Komabe, pali gulu lina lomakulakula la anthu okhala kuno amene akupeza chimwemwe chenicheni m’mikhalidwe yonga paradaiso imeneyi. Ameneŵa ndianthu amene alandira chowonadi cha Baibulo ndipo amakhulupirira lonjezo labwino kwambiri la Mulungu lakuti: “Ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima.” Anthu ameneŵa mwachimwemwe akuyang’ana mtsogolo akumakumbukira mawu a mtumwi Petro akuti: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.” (Yesaya 65:17; 2 Petro 3:13) Kodi anthu ameneŵa ndani? Kodi anaphunzira motani chiyembekezo chabwino kwambiri chopezeka m’Baibulo? Ndipo kodi apanga masinthidwe otani m’miyoyo yawo?

Kuwopa Imfa Kulakidwa

Isabel ndi mwamuna wake, George, ndi Afilipino. Iye anakula akuphunzitsidwa kutsatira chipembedzo cha makolo ake cha Roma Katolika ngakhale kuti sanaŵerengepo Baibulo. Isabel anaphunzitsidwa kuti moyo wa munthu ngwosakhoza kufa. Kodi anayambukiridwa motani ndi chiphunzitso chonyenga chimenechi? Eya, iye anawopa kufa chifukwa chakuti anali ndi lingaliro lakukwiriridwa wamoyo kwamuyaya m’bokosi lamaliro, moyo wake ukulephera kutulukamo. Komabe, mu 1973, Isabel anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Pamene anaphunzira kuti moyo wa munthu ukhoza kufa ndi kuti Mulungu adzagonjetsa imfa mwa chiukiriro, anakondwera kwambiri napeza chitonthozo chachikulu kwambiri. (Ezekieli 18:4, 20; Yohane 5:28, 29) Chowonadi cha Baibulo chinakhomerezedwa kwambiri mwa iye kotero kuti anapita patsogolo mofulumira.

Nanga bwanji za George? Nayenso anapezekapo pokambitsirana Baibulo koma ndi cholinga cha kupeza chifukwa ndi Mboni. Komabe, sanathe kupeza cholakwa chirichonse pa zimene iye ndi mkazi wake anali kuphunzitsidwa. Kwenikweni, atangoyamba kuphunzira, panabuka nkhani ya mwazi. Kufikira panthaŵiyo, George ankakonda kudya zakudya zosanganizidwa ndi mwazi. Koma pamene anawona kuti Baibulo momvekera bwino limatsutsa kudya mwazi, anasiya. (Genesis 9:3, 4; Levitiko 17:10-12; Machitidwe 15:28, 29) Iye anapitiriza kutenga mbali m’phunziro Labaibulo ndipo anakondwa kuti pomalizira anapeza chowonadi. Lerolino, George, Isabel, ndi ana awo anayi akusangalala ndi chimwemwe chenicheni mwakukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu.

Akopeka ndi Chikristu Chowona

Mwamuna wina Wachijapani wotchedwa George ndi mkazi wake Mpwitikizi, Lillian, ali m’zaka zawo zapakati pa 60 ndi 70. Onse aŵiriwo anabadwira ndi kukulira m’Hawaii. Popeza kuti George sanamphunzitsidwe malangizo achipembedzo alionse ndi makolo ake, iye sanatenge chipembedzo mwamphamvu mpang’ono pomwe. Komabe, nthaŵi zonse iye wakhala wokhulupirira mwa Mulungu. Kumbali ina, makolo a Lillian anamlerera m’chipembedzo chawo, monga Mroma Katolika.

Ngakhale kuti George sanali woŵerenga Baibulo wachangu, anali kuŵerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa zaka 30. Motero anaphunzira zambiri ponena za Baibulo. Komabe, pokhala wosuta fodya womwerekera ndi chidakwa, anazengereza kupanga masinthidwe m’moyo wake. Pamene zaka zinali kupita, George anapitiriza kuŵerenga magaziniwo ndi kupezeka mwakamodzikamodzi pamisonkhano Yachikristu pa Nyumba Yaufumu. Chifukwa ninji? Malinga ndi kunena kwake, chifukwa chakuti “zipembedzo zina nzachinyengo kwambiri” pololera zinthu zambiri zoipa zotsutsidwa ndi Baibulo. Iye anawona kuti Mboni za Yehova zinali zosiyana.

Kodi chinakopa mkazi wokhulupirika wa George, Lillian, nchiyani kuti alandire chowonadi cha Mawu a Mulungu ngakhale kuti anali wokhwima kwambiri m’chipembedzo cha makolo ake? Eya, mchemwali wake anamuitanira kumisonkhano ku Nyumba Yaufumu. “Ndinasangalala kuwona mkhalidwe wachimwemwe wonga wa banja ndi anthu omwetulirana mwaubwenzi,” anakumbukira motero Lillian. Chikondi chenicheni chimene anawona chosonyezedwa pakati pa anthu a Yehova chinamkhutiritsa kuti anapezadi chowonadi. (Yohane 13:34, 35) Anavomereza phunziro Labaibulo, mkupita kwanthaŵi anapatulira moyo wake kwa Yehova Mulungu, ndipo anabatizidwa miyezi ingapo pambuyo pakubatizidwa kwa mwamuna wake.

George samasutanso kapena kuledzera, ndipo Lillian anataya mafano ake onse achipembedzo. Ndi mitima yodzala chikondi, iwo akugaŵana ndi ena zimene aphunzira, kuphatikizapo adzukulu awo 25 ndi dzidzukulu 4. Tangopenyani nkhope zawo, ndi kuwona mmene George ndi Lillian aliri achimwemwe!

Apeza Mtendere ndi Chimwemwe

Onse aŵiri, Patrick, Mwairishi wa zaka zapakati, ndi mkazi wake Nina, Myuda, anatsamukira kuno ku Hawaii kuchokera kummwera chakumadzulo kwa United States. Kumbuyoko, iwo anali ndi moyo woluluzika wa kumwa anamgoneka, kufufuza zipembedzo, ndi makhalidwe akusadzisungira. Anathanso zaka zambiri monga ziŵalo za kagulu kachipembedzo kampatuko, akumakalimira kupeza chidziŵitso chapamwamba kupyolera mwa anamgoneka, kusinkhasinkha, ndi phungu wawo waumwini. Mkupita kwa nthaŵi, Patrick anatopa ndi kaduka, zotetana, ndi ndewu zosatha mwa ziŵalo za kagulu kachipembedzoko zimene zinkanena kuti zinapeza ‘chidziŵitso chapamwamba koposa.’ Iye anachoka m’kaguluko nabwereranso ku Hawaii, kumene anali kukhala kalelo, akumayembekezera kupeza mtendere wa maganizo. Pambuyo pake, Patrick anakokosa Nina, amene anali msungwana wake panthaŵiyo, kumchezera. Potsiriza, anakwatirana nakhala m’Hawaii.

Patrick ndi Nina sanayembekezere kuti kufunafuna kwawo mtendere ndi chimwemwe potsirizira kukawachititsa kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Nina analidi wosakhulupirira kukhalako kwa Mulungu m’moyo wake wonse, koma anayamba kupeza mayankho a Baibulo okhutiritsa a mafunso ovuta onga onena za chifukwa chake pali kuipa ndi chifukwa chake zoipa zimachitika kwa anthu abwino. Mofananamo, zaka khumi za kufunafuna chowonadi kwa Patrick zinatha bwino. Mwamsanga, zimene iye ndi Nina anali kuphunzira m’Baibulo zinayamba kusintha lingaliro lawo ponena za makhalidwe. Pambuyo pomenya nkhondo yovuta kwa nthaŵi yaitali, Patrick anakhoza kulaka vuto lake lalikulu lakumwerekera ndi fodya. Tsopano, kwazaka pafupifupi khumi, iye ndi mkazi wake akhala ndi moyo woyera, wamkhalidwe wodzisungira mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu. Pokhala ndi mtima ndi chikumbumtima choyera, iwo akusangalala ndi mtendere umene akhala akuufunafuna.

Kudzimana ndi Mfupo

“Yesetsani kuloŵa pakhomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kuloŵamo, koma sadzakhoza.” (Luka 13:24) Mawu amenewo a Yesu Kristu amasonyeza bwino lomwe kuti nkovuta kutumikira Mulungu ndi kukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo Yamalemba. Aliyense wofunitsitsa kutero samangofunikira kuyesetsa kokha komanso kudzimana koyenerera. Ndimmene zakhalira kwa anthu otchulidwa m’nkhaniyi. Koma ameneŵa afupidwa modabwitsa chotani nanga!

Mwachitsanzo, talingalirani Patrick ndi Nina, amene angotchulidwa kumene. Iwo anapanga masinthidwe aakulu kusiya moyo umene unawadzetsera ndalama zochuluka nayamaba uminisitala Wachikristu wanthaŵi yonse wochirikizidwa ndi ntchito yaganyu. Komabe, iwo ali okhutiritsidwa kuti mapindu auzimu aposa kutalitali kudzimana kulikonse kwakuthupi kumene iwo apanga. Ndipo iwo alidi achimwemwe.

Chifukwa cha msinkhu wawo, sikunakhale kwapafupi kwa George ndi Lillian kupanga masinthidwe. Kupezeka pamisonkhano Yachikristu ndi kukhala ndi phande muuminisitala kumafuna nthaŵi, chisamaliro, ndi nyonga. Komabe, iwo ali okondwa kuti thanzi lawo lawongokera, ndipo moyo umene ali nawo tsopano ungangofotokozedwa kukhala wabwino koposa, wokhutiritsa, ndi wachimwemwe.

Ponena za George ndi Isabel, vuto lawo lalikulu koposa liri pakuphunzitsa ana awo ndi kuwathandiza kupeza njira ya ku moyo. Nthaŵi ndi kuyesayesa kwakukulu nzofunika pokonzekeretsa ana anayi kaamba ka misonkhano Yachikristu kapena kupita nawo muuminisitala Wachikristu. Panthaŵi ina chitsenderezo chosalekeza chimenecho chinachititsa George ndi Isabel kufookera pamathayo awo aukholo. Koma nkhani ya Baibulo yamutu wakuti “Kudzutsanso Mzimu wa Kudzimana” inawasonkhezera kuwonjezera zoyesayesa zawo zakupereka chisamaliro ndi chiphunzitso choyenera chonse kwa ana awo anayi kuti ‘awalere m’maleredwe ndi chilangizo cha Yehova.’ Ndithudi, zoyesayesa zotero zadzetsa mfupo zochuluka.​—Aefeso 6:4.

Saali malo okongola, mkhalidwe wakunja wabwino, kapena moyo wabata umene umabweretsa chimwemwe chenicheni kwa anthu ameneŵa ndi ena ambiri. Mmalomwake, kuli kudziŵa kwawo kuti akugwiritsira ntchito moyo wawo mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo akutsatira miyezo ya Mawu ake, Baibulo. (Mlaliki 12:13) Ndiponso, chimwemwe chenicheni chimasefukira m’mitima yawo pamene asinkhasinkha za nthaŵi yosangalatsa pamene paradaiso wadziko lonse adzabwezeretsedwa padziko lapansi.​—Luka 23:43.

[Chithunzi patsamba 25]

George, Isabel, ndi ana awo amakondwa kuŵerenga Baibulo

[Chithunzi patsamba 26]

George ndi Lillian amapeza chimwemwe muunisitala Wachikristu

[Chithunzi patsamba 27]

Patrick ndi Nina akusangalala ndi mtendere weniweni muutumiki wa Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena