Mawonekedwe Angakhale Onyenga
“PALIBE mawonekedwe odalirika,” anatero woseŵera drama Wachiairishi Richard Sheridan. Zimenezi nzowona kumitengo ndiponso kwa anthu.
Tsiku lina chakumapeto kwa March m’chaka cha 33 C.E., Yesu Kristu anawona mtengo wamkuyu pamene iye ndi ophunzira ake anali kuyenda kuchokera ku Betaniya kumka ku Yerusalemu. Mtengowo unali wodzala ndi masamba, koma kuuyang’anitsitsa kosamalitsa kunavumbula kuti uwo unalibe zipatso konse. Chifukwa chake Yesu anati kwa mtengowo: “Munthu sadzadyanso zipatso zako nthaŵi zonse.”—Marko 11:12-14.
Kodi nchifukwa ninji Yesu anatemberera mtengo umenewu popeza kuti, monga momwe Marko akufotokozera, “siinali nyengo yake yankhuyu”? (Marko 11:13) Eya, pamene mtengo wamkuyu uphukira masamba, kaŵirikaŵiri umatulutsanso nkhuyu zoyamba kucha. Kunali kosazoloŵereka kuti mtengo wamkuyu ukhale ndi masamba panthaŵi imeneyo yachaka. Koma popeza kuti unali ndi masamba, Yesu moyenerera anayembekezera kupeza nkhuyu pamtengowo. (Wonani chithunzithunzi pamwambapo.) Chenicheni chakuti mtengowo unangotulutsa masamba chinatanthauza kuti uwo ukakhala wosabala zipatso. Mawonekedwe ake anali onyenga. Popeza kuti mitengo ya zipatso inali kukhomeredwa msonkho, mtengo wosabala zipatso unali chothodwetsa m’zachuma ndipo unafunikira kudulidwa.
Yesu anagwiritsira ntchito mtengo wamkuyu wosabala zipatso umenewo kufotokoza mwafanizo phunziro lofunika lonena za chikhulupiriro. M’mawa mwake, ophunzira ake anadabwa kuwona kuti mtengowo unali utafota kale. Yesu anafotokoza kuti: “Khulupirirani Mulungu. . . . Zinthu zirizonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.” (Marko 11:22-24) Kuwonjezera pakufotokoza mwafanizo kufunika kwa kupemphera m’chikhulupiriro, mtengo wamkuyu wofotawo unasonyeza mwamphamvu chimene chikachitika kumtundu wopanda chikhulupiriro.
Miyezi ingapo kalelo Yesu anali atayerekezera mtundu wa Ayuda ndi mtengo wamkuyu umene sunabale zipatso kwa zaka zitatu ndipo ukadulidwa ngati ukakhalabe wosabala zipatso. (Luka 13:6-9) Mwakutemberera mtengo wamkuyuwo masiku anayi okha imfa yake isanachitike, Yesu anasonyeza mmene mtundu wa Ayuda sunabalire zipatso zoyenera kulapa ndipo chotero unali wofunikira chiwonongeko. Ngakhale kuti mtunduwo—mofanana ndi mtengo wamkuyu—mwachiphamaso unawonekera ngati wathanzi, kuupenda mosamalitsa kunausonyeza kukhala wopanda chikhulupiriro kumene potsirizira pake kunauchititsa kukana Mesiya.—Luka 3:8, 9.
Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anachenjeza za “aneneri onyenga” ndipo anati: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? Chomwecho mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Mtengo uli wonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Inde chomwecho pa zipatso zawo mudzawazindikira iwo.” (Mateyu 7:15-20) Mawu a Yesu amenewa ndi nkhani ya kutembereredwa kwa mtengo wa mkuyu zimasonyeza bwino lomwe kuti tifunikira kukhala maso mwauzimu, chifukwa chakuti mawonekedwe achipembedzo angakhalenso onyenga.