Zimenezi Ziri Zosatheka!
“NKWAPAFUPI kuti ngamira ipyola diso lasingano, koposa mwini chuma kuloŵa Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 19:24) Yesu Kristu ananena izi kuphunzitsa otsatira ake phunziro. Wolamulira wachichepere wachuma anali atakana kumene chiitano chakukhala wotsatira wa Yesu ndi kukhala ndi phande m’mipata yauzimu yabwino kwambiri yochuluka. Mwamunayo anasankha kunonomera kuchuma chake chambiricho mmalo mwakutsatira Mesiya.
Yesu sanali kunena kuti kuli kosatheka kotheratu kwa munthu wachuma kupeza moyo wosatha m’kakonzedwe ka Ufumu, chifukwa chakuti anthu ena achuma anadzakhala otsatira ake. (Mateyu 27:57; Luka 19:2, 9) Komabe, kupeza moyo kuli kosatheka kwa munthu wachuma aliyense amene amakonda kwambiri chuma chake kuposa zinthu zauzimu. Kuli kokha mwakukhala wozindikira chosoŵa chake chauzimu ndi kufunafuna chithandizo cha Mulungu kuti munthuyo angalandire chipulumutso choperekedwa ndi Mulungu.—Mateyu 5:3; 19:16-26.
Fanizo la ngamira ndi diso la singano silifunikira kuwonedwa monga momwe lalembedwera. Yesu anali kugwiritsira ntchito mawu okuluŵika kugogomezera vuto loyang’anizana ndi anthu okhupuka amene amayesa kukondweretsa Mulungu pamene akusungabe njira yawo yamoyo yachuma, ndi yokondetsa zinthu zakuthupi.—1 Timoteo 6:17-19.
Ena amanena kuti diso la singano linali chipata chaching’ono cha linga la mzinda pa chimene ngamira inali kupitapo movutikira ngati yatulidwa katundu wake. Koma liwu Lachigiriki lakuti rha·phisʹ, lotembenuzidwa “singano” pa Mateyu 19:24 ndi Marko 10:25, likuchokera ku mneni wotanthauza “kusoka.” Pa Luka 18:25 liwu lakutilo be·loʹne likusonya kusingano yosokera, ndipo pamenepo New World Translation imati: “M’chenicheni, kuli kosavutirapo, kwa ngamira kupyola diso lasingano yosokera kuposa munthu wa chuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.” Akatswiri osiyanasiyana amachirikiza matembenuzidwe amenewa. W. E. Vine amati: “Lingaliro lakugwiritsira ntchito ‘diso lasingano, ku zipata zazing’ono likuwonekera kukhala lamakono; palibe umboni wosonyeza kuti nlakalekale.”—An Expository Dictionary of New Testament Words.
Ngamira yaikulu yoyesa kupyola diso la singano yosokera yaing’onong’ono “ikusonyeza kalankhulidwe ka voko ka Akummaŵa,” likutero bukhu lina lamaumboni. Ndipo ponena za ena ochenjera kwambiri kotero kuti anawonekera kuchita zosatheka, The Babylonian Talmud imati: “Iwo amapyoza njovu padiso lasingano.” Yesu anagwiritsira ntchito mawu okuluŵika odziŵika ndi kusiyanitsa kwamphamvu kugogomezera kusathekera. Kuli kosatheka kwa ngamira, kapena njovu, kupyola diso lasingano yosokera. Komabe, mwachithandizo cha Mulungu, munthu wachuma angathe kusiya lingaliro lake lokondetsa zinthu zakuthupi ndi kufunafuna moyo wosatha. Angateronso onse okhala ndi chikhumbo chochokera pansi pa mtima chakuphunzira ndi kuchita chifuniro cha Mulungu Wam’mwambamwamba, Yehova.