Kufikira “Anthu Amitundu Yonse” m’Belgium
MTUMWI Paulo anakumbutsa Akristu odzozedwa anzake za chifuniro cha Mulungu chakuti “anthu amitundu yonse ayenera kupulumutsidwa ndi kufika pachidziŵitso cholongosoka cha chowonadi.” Kuti izi zitheke iwo akafunikira kupemphera kuti apatsidwe ‘moyo wodekha ndi wachete’ kotero kuti akakhoze kulengeza mbiri yabwino ya Ufumu kwa onse okhala ndi khutu lakumva.—1 Timoteo 2:1-4, NW.
Lerolino, kufikira “anthu amitundu yonse” ndi mbiri yabwino kuli ndi tanthauzo lapadera kwa Mboni za Yehova m’Belgium. Kuyambira mapeto a Nkhondo Yadziko II, dziko laling’ono limeneli, limene liri ndi ukulu wokhoza kuloŵa mosavuta m’Nyanja ya Tanganyika kapena theka la Nyanja ya Michigan, lakhala nawo masinthidwe aakulu mumpangidwe wake wa mafuko a anthu ndi mwambo. Kuwonjezera pa zitaganya zake zitatu zakalekale—Aflemi (Adatchi), Afalansa, ndi Ajeremani—tsopano m’Belgium muli timagulu ta anthu olankhula zinenero zosiyanasiyana ndi miyambo. Muli Aluya, Ateki, Amwenye, Atchaina, Afilipino, Aafirika, ndi nzika za ku Amereka, kungotchula ochepekera chabe. Kukuyerekezeredwa kuti munthu 1 mwa 10 alionse mu Belgium ngwochokera kudziko lachilendo.
Chotero, Mboni m’Belgium, mofanana ndi Akristu anzawo padziko lonse lapansi, zikuyang’anizana ndi chitokoso cha kufikira “anthu amitundu yonse” ndi mbiri yabwino. Kodi mkhalidwewo uli wotani polalikira mitundu yosiyanasiyana yotere? Kodi munthu angafikire motani anthu amene ali ndi chiyambi cha makhalidwe ndi cha chipembedzo chosiyana kotheratu? Ndipo kodi amalabadira motani uthenga wa Baibulo?
Kuyambitsa Kumadzetsa Zotulukapo
Kulankhula kwa “anthu amitundu yonse” za mbiri yabwino ya Ufumu ndiko chokumana nacho cha chimwemwe ndi chokondweretsa. M’makwalala odzala anthu, pa malo amsika, pa zoyendera za anthu onse, kuchokera kunyumba ndi nyumba, anthu ochokera ku makontinenti onse amapezedwa. Mwakuyamba kochepekera, wofalitsa wa Ufumu angayambitse mosavuta kukambitsirana, ndipo kaŵirikaŵiri kutero kumakhala ndi zotulukapo zopindulitsa.
Pa malo oimira basi, Mboni inayambitsa kukambitsirana ndi dona wa ku Afirika, mwakumwetulira kwa ubwenzi chabe. Mwamsanga donayo anasonyeza chisangalalo chake cha kumva za Ufumu wa Mulungu, ndipo anafuna kudziŵa zowonjezereka za Baibulo. Iye analandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! napatsa Mboniyo keyala yake. Pamene Mboni inanena kuti ikamfikira msanga, donayo anatsutsa. “Ayi! Ayi! Tiyenera kupanga pangano lotsimikizirika kuchitira kuti ndidzakhale panyumba pamene mufika.”
Masiku atatu pambuyo pake, pamene Mboniyo inali kudzapanga ulendowo, inapeza kuti inali itataya keyala ya donayo. Koma popeza inakumbukira dzina la khwalalalo, Mboniyo inapita nifika pa nyumba iriyonse kuwona ngati ikanapeza dzina la munthu Wakuda. Anafika kumapeto akhwalalalo popanda kupeza zimene anali kufuna. Anagwiritsidwa mwala kwambiri chotani nanga! Mwadzidzidzi, akukonzekera kubwerera, anangowona mbwee, dona weniweniyo amene anali kumfunafuna anali chiriri patsogolo pake, ndipo inali nthaŵi yeniyeniyo imene anapangana ya kuchezako! Phunziro la Baibulo linayambidwa.
Bwanji za zizoloŵezi, zikhulupiriro, ndi miyambo zosiyanazo? Mwachitsanzo, bwanji za chikhulupiriro cha Ahindu? Eya, mpainiya mmodzi anakumbukira zimene anaziŵerenga m’bukhu la Kukambitsirana za m’Malemba. Ilo limati: “Mmalo mwa kuyesayesa kuyang’anizana ndi zocholowana za nthanthi Yachihindu, perekani chowonadi chokhutiritsa maganizo chopezedwa mu Baibulo lopatulika. . . . Chowonadi chomvekera bwino m’Mawu ake chidzafikira mitima ya akumva njala ndi ludzu lachilungamo.”
Zimenezo ndizo zimenedi mpainiyayo anachita pamene anakumana ndi Kashi, mkazi wa ku Indiya amene anavomereza phunziro la Baibulo. Kashi anapita patsogolo bwino lomwe, ndipo mwamsanga anali kulankhula kwa mabwenzi ake onse ponena za zimene anali kuphunzira. Tsiku lina mpainiya anakomana ndi mkazi wa nduna yaukazembe, amene anafunsa kuti: “Kodi ndinu amene mumaphunzitsa Kashi Baibulo?” Mpainiyayo anadabwa chotani nanga pamene donayo anati: “Iye ndimphunzitsi wogwira mtima chotani nanga! Wafikira pakundikhutiritsa pamfundo zambiri. Tayerekezerani, iye, Mhindu, kuphunzitsa Baibulo ine, Mkatolika!”
Pamene mukumana ndi Afilipino, mwamsanga mumazindikira kuti unyinji wa iwo umakonda Baibulo. Iwo ndianthu aubwenzi ndi ochereza, ndipo kuli kosavuta konse kuyambitsa makambitsirano ndi iwo. Dona wina Wachifilipino analandira mosavuta magazini aŵiri, koma pokhala Mkatolika, anawataya. Masabata angapo pambuyo pake analandiranso magazini aŵiri, amene anawasiya m’chola chake. Usiku wina anakhala ndi chikhumbo cha kuŵerenga. Atatha kusanthulasanthula zimene zikamkondweretsa, anapeza magaziniwo. Mozengereza, anayamba kuwawerenga, ndipo chikondwerero chake chinawonjezereka. Mwamsanga pambuyo pake, Mboni ina inafika panyumba pake, ndipo donayo anafunsa mafunso ambiri. Iyi inali nthaŵi yoyamba imene donayo anayamba kuyerekezera zikhulupiriro zake Zachikatolika ndi zimene Baibulo limanena. Ulaliki Wamalembawo womvekera bwino, unamkhutiritsa donayo kotero kuti potsirizira pake anapeza chowonadi.
“Ponya Zakudya Zako”
Nzika zochuluka zachilendo zimafika ku Belgium pazifukwa za bizinesi kapena kugwira ntchito pa imodzi ya nyumba zaukazembe 150 za m’menemo kapena Gulu Lachitaganya cha Yuropu. Unyinji wa iwo amakhalako zaka zochepekera zokha. Kuchitira umboni kwa anthuwa ndi kuchita phunziro nawo la Baibulo kungawonekere kukhala kosaphula kanthu poyamba. Koma Baibulo limatikumbutsa kuti: “Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri.” (Mlaliki 11:1) Kaŵirikaŵiri zotulukapo zake zimakhala zofupa modabwitsa.
Izi zinali choncho ndi mkazi wina wa ku Amereka amene analandira magazini mokhazikika kuchokera kwa Mboni ina. M’kupita kwa nthaŵi Mboniyo inasonyeza phindu lakuphunzira Baibulo mokhazikika, ndipo Mboniyo inampempha kuphunzira naye. Mkaziyo anavomereza pempholo napanga kupita patsogolo kofulumira. Mwamsanga mkaziyo anawona kusiyana pakati pa chipembedzo chowona ndi chonyenga. Motero iye anachotsa m’nyumba mwake mafano onse achipembedzo. Ndiyeno nthaŵi inafika yoti abwerere ku United States. Kodi izi zinatanthauza mapeto akupita patsogolo kwake kwauzimu? Tayerekezerani chisangalalo ndi kudabwa za Mboniyo pamene inalandira telefoni kuchokera kwa Mboni ina ku United States ikumamuuza kuti donayo anapitiriza ndi phunziro lake, anapatulira moyo wake kwa Yehova Mulungu, ndipo anabatizidwa! M’chenicheni, iye anali kutumikira kale monga minisitala mpainiya wothandiza.
Zofananazo zinachitikanso kwa Kashi, mkazi wa ku Indiya, ndi kwa dona Wachifilipino wotchulidwa poyambapo. Pamene Kashi anabwerera ku Indiya, iye ndi mwamuna wake anayambiranso phunziro lawo la Baibulo. Potsirizira pake iwo onse anadzipatulira kwa Yehova nagawanamo m’ntchito yolalikira. Popeza kuti ankakhala m’chigawo chimene munalibe Mboni zina, iwo anapereka nyumba yawo kuchitiramo Phunziro Labukhu Lampingo. Kashi anatumikira monga mpainiya wothandiza kumlingo umene thanzi lake linamulola, ndipo wakhala akuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba asanu ndi limodzi, ophatikizapo chiwonkhetso cha anthu 31. Mofananamo, mkupita kwanthaŵi mkazi Wachifilipinoyo anasamukira ku United States, anapita patsogolo nadzipatulira ndi kubatizidwa, nakhala mpainiya wokhazikika. Zotulukapo zosangalatsa zotere ziri pakati pa zambiri zimene ofalitsa a Ufumu m’Belgium akusangalala nazo pamene akupitirizabe kulalikira kwa anthu m’gawo lawo.
Chitokoso cha Zinenero
Kuti ichite mwachipambano ntchito yakulalikira kwa “anthu amitundu yonse,” ofesi ya nthambi imafunikira kukhala ndi mabukhu ofotokoza Baibulo m’zinenero zoposa zana limodzi. Tsopano mipingo ya m’Belgium iri ndi zinenero khumi. Pamipingo 341, yokwanira 61 iri m’zinenero zachilendo, ndipo mwa ofalitsa Ufumu 26,000 okwanira 5,000 ali amitundu yachilendo. Mpingo umodzi umaphatikizapo amuna ndi akazi ochokera ku maiko osiyanasiyana 25. Tayerekezerani kusiyanasiyana m’mawonekedwe ndi m’miyambo pa misonkhano yawo! Komabe chikondi ndi chigwirizano pakati pa abale chiri umboni wamphamvu wakukhala ophunzira owona Achikristu.—Yohane 13:34, 35.
Popeza kuti pali nzika zambiri m’Belgium zofunikira kumva mbiri yabwino m’zinenero zachilendo, ofalitsa ena avomereza chitokoso chakuphunzira zinenero zovuta, monga Chiteki, Chiluya, ndi Chitchaina. Zoyesayesa zawo zafupidwa molemerera.
Awo amene amagwira ntchito pakati pa Aluya amapeza kuti kaŵirikaŵiri angadzutse chikondwerero m’Baibulo mwakutchula phindu lake lothandiza. Wofalitsa wina wa Ufumu anali ndi makambitsirano okondweretsa ndi profesa Wachiluya, ndiyeno kwa zaka zitatu pambuyo pake sanakhoze kupezanso profesa ameneyu. Posataitsidwa mtima mofulumira, wofalitsayo anasankha kusiya pepala lolembedwa mafunso a Baibulo kwa profesayo. Mafunsowa anamdzutsira chisangalalo kwambiri kotero kuti anali wofunitsitsa kuchita kapendedwe ka Baibulo kokhala ndi chifuno. Iye anadabwa kwambiri ndi zimene anapeza zakuti profesayo ndi mkazi wake, aŵiri onsewo Asilamu, anapatula madzulo ena kuŵerenga Baibulo pamodzi.
Awo oyesayesa kuthandiza chitaganya chachikulu cha Atchaina m’mizinda yaikulu ali ndi chopinga china chakuchigonjetsa kuwonjezera pachopinga chachinenero. Atchaina ambiri samakhulupirira Mulungu monga Mlengi kapena Baibulo kukhala Mawu a Mulungu. Komabe, iwo ali ndi chidwi ndipo amafuna kudziŵa chimene limanena. Iwo alinso oŵerenga achangu. Sikwachilendo kuti iwo amalize kuŵerenga bukhu lirilonse lofotokoza Baibulo limene muwasiira, kapena ngakhale mbali yaikulu ya Baibulo, m’masiku ochepekera chabe. Ngati mtima wawo uli wolungama, iwo amasonkhezeredwa ndi mphamvu ya Mawu a Mulungu.
Dona wina wa ku Tchaina anakupeza kukhala kovuta kwambiri kuvomereza lingaliro lakuti kuli Mlengi. Koma paphunziro lachiŵiri, misozi inalenjera m’maso mwake pamene anati: “Tsopano ndakhulupirira mwa Yehova Mulungu, chifukwa chakuti ngati Baibulo linalembedwa kwanyengo ya zaka 1,600 ndi anthu osiyanasiyana 40 ndipo komabe liri logwirizana kotheratu ndi mutu wankhani umodzi, pamenepo ayenera kukhala Yehova Mulungu amene anali kutsogolera kulembedwako. Zimenezi nzosavuta kuwona!”
Dona wina wa ku Tchaina anafikiridwa ndi Mboni ina pa treni yamkhwalala. “Kodi ndinu Mkristu?” Iye anafunsa Mboniyo. Pamenepo mkaziyo ananena kuti anali wogwiritsidwa mwala kwakukulu kuwona kutsutsana kwambiri pakati pa odzinenera kukhala Akristu. Mboniyo inavomereza zimene mkaziyo ananena koma inafotokoza kuti Baibulo silimadzitsutsa. Pamenepo donayo anatsika mu treniyo. Anapatsa Mboniyo keyala yake, ndiyeno pamene Mboniyo inamchezera, donayo anadzuma kuti: “Ngati kokha ndikanadziŵa, mwenzi ndikanakwera treniyo chaka chimodzi chapitacho!” Atafunsidwa zimene anatanthauza, donayo anafotokoza kuti: “Ijayo inali nthaŵi yanga yoyamba kupita ku yunivesite ndi treni yamkhwalala. Kodi mungayerekezere? Ndinawawanya chaka chimodzi!” Mkaziyo anali wachimwemwe kwambiri kuti anakhoza kuphunzira Baibulo ngakhale kuti kunali kwa miyezi yoŵerengeka chabe asanabwerere ku Tchaina.
Zokumana nazo zofanana ndi zimenezi zaphunzitsa Mboni za ku Belgium phunziro. “Mamaŵa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako,” limatero Baibulo, “pakuti sudziŵa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi ngakhale izozo, kaya zonse ziŵiri zidzakhala bwino.” (Mlaliki 11:6) Zoyesayesa zochitidwa kugonjetsa zopinga za chinenero, chizoloŵezi, ndi mwambo zimayenerana ndi zotulukapo zake. Kuposa zonse, kulabadira kwaubwenzi kumatsimikizira, kuti ndithudi Mulungu “alibe tsankhu, koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”—Machitidwe 10:34, 35.