Kodi Chinapangitsa Kuphunzitsa kwa Yesu Kukhala Kogwira Mtima Mwapadera Nchiyani?
NGAKHALE kuti mwachiwonekere atsogoleri achipembedzo Achiyuda sanali owona mtima pakumutcha kuti “Mphunzitsi [Chigiriki Di·daʹska·los],” Yesu Kristu anazindikiridwa monga wotero ndi ponse paŵiri okhulupirira ndi osakhulupirira omwe (Mateyu 8:19; 9:11; 12:38; 19:16; 22:16, 24, 36; Yohane 3:2) Adindo otumidwa kukammanga anachita chidwi kwambiri ndi kuphunzitsa kwake kotero kuti anabwerera manja kapa, akumati: ‘Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero.’ (Yohane 7:46) Yesu anaphunzitsa “monga mwini mphamvu, wosanga alembi awo.” (Mateyu 7:29) Magwero a kuphunzitsa kwake anali Mulungu (Yohane 7:16; 8:28), ndipo Yesu anapereka chidziŵitsocho mokhweka, chigomeko chosatsutsika, mafunso osonkhezera maganizo, mawu okuluŵika ochititsa chidwi, ndi mafanizo othandiza otengedwa ku zinthu zozoloŵereka kwa omvetsera ake. (Mateyu 6:25-30; 7:3-5, 24-27) Yesu anagwiritsiranso ntchito kuphunzitsa mwakuchita zinthu, panthaŵi ina anasambitsa mapazi a ophunzira ake kuti awaphunzitse kuti iwo ayenera kutumikirana.—Yohane 13:2-16.
Chidziŵitso cha Yesu chinakulitsidwa ndi kukhala kwake ndi unansi wapafupi ndi Atate wake ndi Mulungu asanadze kudziko lapansi. Chifukwa chake iye anadziŵa Mulungu kuposa mmene anachitira munthu wina aliyense, ndipo izi zinamkhozetsa kuphunzitsa mwaukumu ponena za Atate wake. Monga momwe Yesu mwiniyo ananenera: ‘Palibe munthu adziŵa Mwana, koma Atate yekha; ndi palibe wina adziŵa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.’—Mateyu 11:27; Yohane 1:18.
Yesu analinso wozoloŵerana kwambiri ndi Mawu Olembedwa a Mulungu. Pamene anafunsidwa kuti nliti linali lamulo lalikulu koposa m’Chilamulo, mosazengereza iye anafotokoza mwachidule Chilamulo chonse m’malamulo aŵiri, akumagwira mawu kuchokera pa Deuteronomo (6:5) ndi Levitiko (19:18). (Mateyu 22:36-40) Mkati mwa nthaŵi yauminisitala wake, iye amadziŵika kukhala atasonya kapena kutchula ziganizo zimene zimafanana ndi malemba ochokera mu pafupifupi theka la mabukhu a Malemba Achihebri.
Mbali zina zimene zinapangitsa kuphunzitsa kwa Yesu kukhala kwaukumu ndi kogwira mtima zinali kuzindikira kwake munthu ndi nkhaŵa yake yachikondi pa ena. Luntha lake lakuthwa linakulitsidwa ndi chidziŵitso chake chozizwitsa chakuzindikira ziyambi ndi kuganiza kwa anthu ena. (Mateyu 12:25; Luka 6:8; Yohane 1:48; 4:18; 6:61, 64; 13:11) “Iye anadziŵa anthu onse.” (Yohane 2:25) Mtima wake unamvera chifundo anthu kumlingo wakuti anadzimana mpumulo wofunika kuti awaphunzitse. Panthaŵi ina Yesu ndi ophunzira ake anatenga bwato nayamba ulendo wopita kumalo akutali kukapuma pang’ono. “Ndipo anthu anawawona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikira, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ochokera m’midzi monse, nawapitirira. Ndipo anatuluka Iye, nawona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.”—Marko 6:31-34.
Yesu anachitira ophunzira ake mokoma mtima. Pamene ophunzira ake sanazindikire tanthauzo lafanizo lina, iye anawafotokozera fanizolo moleza mtima. (Mateyu 13:10-23) Pozindikira zopereŵera zawo, iye sanapereke kwa iwo chidziŵitso chochulukitsitsa. (Yohane 16:4, 12) Pamene kunali kofunika, Yesu anabwereza pafupifupi mawu ofananawo. (Marko 9:35; 10:43, 44) Kaŵirikaŵiri Yesu, poyankha mafunso anachirikiza yankho lake mwamafanizo kapena zinthu zowoneka, mwakutero anali kukhomereza mwakuya pa maganizo a omvetsera ndi kusonkhezera mphamvu yawo ya maganizo.—Mateyu 18:1-5, 21-35; Luka 10:29-37.