Wodzuka Mamaŵa
PAKATI pamitengo yazipatso kuchigawo cha Mediterranean, mtengo wamchiwu uli umodzi wa mitengo yochititsa chidwi koposa. Chakumapeto kwa January kapena February—nthaŵi yaikulu kwambiri mitengo yambirimbiri isanatero—umagalamuka kukusagwira kwake ntchito kwa m’chisanu. Ndipo nkugalamuka kotani nanga! Mtengo wonse umavala chovala chazitsamba zaupofu wokongola kapena zoyera, zotsirizirazi zimafanana ndi imvi zankhalamba—Yerekezerani ndi Mlaliki 12:5.
Ahebri akale anatcha mtengo wamchiwu kuti “wodzuka mamawa,” akumasonya ku kutuŵa kwamaluŵa kwake koyambirira. Mkhalidwe umenewo unagwiritsiridwa ntchito ndi Yehova kufotokoza mwafanizo uthenga wofunika. Pachiyambi pa uminisitala wake, Yeremiya anasonyezedwa masomphenya a nthambi yamchiwu [katungulume]. Kodi anatanthauzanji? Yehova anafotokoza kuti: “Ine ndidzadikira mawu anga kuwachita.”—Yeremiya 1:12.
Monga momwedi mtengo wamchiwu ‘umadzukira’ mamawa, chotero Yehova mophiphiritsira anali “kudzuka mamaŵa” kutumiza aneneri ake okachenjeza anthu za zotulukapo zakusamvera. (Yeremiya 7:25) Ndipo sankapuma—ankapitirizabe ‘kukhala maso’—kufikira mawu ake aulosi akwaniritsidwa. Zinatero kuti mu 607 B.C.E., panthaŵi yoikidwiratu, chiweruzo cha Yehova chinadza pamtundu wopatuka wa Yuda.
Mawu a Mulungu amaneneratu kuti chiweruzo chofanana chidzadza motsutsana ndi dongosolo loipa mu limene tikukhala. (Salmo 37:9, 10; 2 Petro 3:10-13) Posonya ku mchitidwe wachiweruzo umenewu, mneneri Habakuku akutipatsa chitsimikiziro kuti: ‘Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.’ (Habakuku 2:3) Kuphukira kokongola kwa mchiwu kumatikumbutsa kuti Yehova adzakhalabe maso ponena za mawu ake kuti awakwaniritse.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.