Amishonale a ku Micronesia
NGAKHALE kuti analekanitsidwa ndi mitunda yaikulu yowonekera kukhala yosatha ya Nyanja ya Pacific, amishonale a ku Micronesia amakhozabe kusonkhana chaka chirichonse pa “kugwirizanitsidwa kwa banja.” Ndipo kodi alaliki onse amenewa ochokera kuzilumba zakutali amakumana kuti? Moyenerera, pamalo amene boma lam’malowo lawatcha kuti Jehovah Street—malo amene ali ofesi yanthambi ya Guam imene iwo akutumikira pansi pake.
Mu June 1992, amishonale 56 anasonkhana panthambi kuti afike pa Msokhano Wachigawo wakuti “Onyamula Kuunika.” Kuseka ndi nkhani zothutsa mtima zinadzaza malowo pamene anakumbutsa maubwenzi akalekale ndi kuyambitsanso atsopano. Monga mwa chizoloŵezi, iwo onse anakonzekera kuti ajambulidwe chithunzi pamakwerero a Nyumba ya Ufumu monga kagulu ndiyeno anaseyama pamagome aatali atatu amadyerero kuti adyere pamodzi chakudya cha chaka ndi chaka cha amishonale, chimene chaka chino chinapangidwa kukhala chapadera ndi kuchezetsa kwa Albert Schroeder, chiwalo cha Bungwe Lolamulira.
Kwa amishonale ambiri, kusonkhana kwa chaka ndi chaka kumeneku m’Guam ndiko mwaŵi wokha umene amakhala nawo kuchoka pa nyumba zawo zazing’ono zam’malo otenthaŵa. Ndipo nyumbazi nzazing’onodi. Ebeye Island, chimodzi cha zilumba zotchedwa Marshall Islands, chiri ndi mahekitala 32 okha. Nyumba ya a mishonale pa chilumba cha Majuro mu Marshall ndi kunyumba ya ku Kiribati mu Gilbert Islands zonse ziŵiri zamangidwa pa makhwaŵa aatali, aang’ono amene kutakata kwake kuli kilomita 0.8. Chotero amishonalewo amapanga ulendo wawo wochititsa nthumanzi koposa wopita ku Guam.
Pamene lingaliro lakulalikira ku chilumba chakutali ndi chotentha lingamvekere kukhala lokondweretsa, m’chenicheni ndiko chitokoso chimene ochepekera okha ndiwo ali okonzekeretsedwa kuthana nacho. Mokondweretsa, 7 okha mwa amishonale 56 achokera ku Sukulu ya Baibulo ya Gilead ya Watchtower. Unyinji wawo unachokera ku Hawaii kapena ku Filippines kumene anali aminisitala apainiya ozoloŵerana kale ndi moyo wam’malo otentha, ndipo anapita mwachindunji kuchokera kumaiko akwawo kumka kumagawo awo aumishonale.
Chifukwa chakuti zilumba za Micronesia ziri pafupi kwambiri ndi mzera woyerekezera wapakatikati padziko lapansi, amishonale amalimbana ndi kutentha koŵaula ndi chitungu kuti afikire anthu ndi mbiri yabwino. Kulankhulirana kungakhaledi chitokoso chachikulu kwambiri. Chilumba chirichonse kapena zilumba zingapo ziri ndi chinenero chake chake—zina zosadziŵika ndi zosalembedwa konse m’mabukhu omasulira mawu—ndipo pangapite zaka zambiri mlendo asanachilankhule mwa myaa. Kuthandiza anthu m’zitaganya zazilumba zosiyasiyana zimenezi kuti azindikire Baibulo, nthambi ya Guam imasindikiza mabukhu m’zinenero 11, zimene 9 za zimenezi zimalankhulidwa m’Micronesia mokha.
Zilumba zina ziri kutali kwambiri kotero kuti zingafikiridwe kokha pabwato. Nyumba ya amishonale yaku Tol mu Chuuk (Truk) iri pachilumba chotero, ndipo amishonale kumeneko amadalira pa makina okoka mphamvu yadzuŵa kuŵapatsa magetsi kwamaola ochepekera chabe tsiku lirilonse.
Zonse pamodzi, pali nyumba za amishonale 14 m’Micronesia yonse, imene ikuphatikizapo zigawo pafupifupi ukulu wa United States. Mwa anthu oposa 400,000 amene amakhala m’chigawocho, okwanira 1,000 ali ofalitsa a mbiri yabwino, olinganizidwa m’mipingo 20 ndi magulu akutali 3.
Pamene kuli kwakuti kaŵirikaŵiri anthu a ku Micronesia ngaubwenzi kwambiri, miyambo ya m’malowo ndi chitsenderezo cha banja zimalefula ambiri kulandira chowonadi cha Ufumu wa Mulungu. Chotero ngakhale kuti ntchito yolalikira ikupeza chipambano onse pamodzi (ofalitsa a Ufumu 1,000 akuchititsa maphunziro a Baibulo ochuluka 2,000), mipingo ina ndi timagulu takutali idakali yaing’ono. Mwachitsanzo, pali ofalitsa 5 okha pachilumba cha Tinian, ofalitsa 7 okha pachilumba cha Nauru, ndipo mpingo wa ku Yap, Kosrae, [wodziŵikanso monga Kusaie], ndi Rota uliwonse uli ndi ofalitsa osakwanira 40. Komabe, amishonale ena akhala m’magawo awo kwa zaka zoposa 20. Chokondweretsa mwapadera, amishonale asanu ndi modzi onse pachilumba cha Belau akhala konko zaka zosachepera 12.
Kwa awo amene akupirira, mfupozo nzazikulu. Pali mipata yatsiku ndi tsiku yakudabwa ndi kukongola kwa chilengedwe cha Yehova. Zilumba zobiriŵira za Micronesia ziri zomwazikana mofanana ndi majuwelo aang’ono obiriŵira pa nsalu yazojambula ya bluu ya Pacific. Makilomita ambirimbiri a magombe osapanikizana ndi mathanthwe ofiira a m’mbali mwa nyanja odzala ndi nsomba zamitundumitundu zimene zimakopa ochita maseŵera omira ndi kusambira kuti atulukire ena a malo abwino koposa ochitirako maseŵera akumira padziko lonse. Ndipo pamapeto a tsiku lirilonse, pamakhala kuwonerera kochititsa chidwi kwa kuloŵa kwadzuŵa m’nyanja yamchere.
Komabe, mfupo yaikulu koposa, ndiyo mwaŵi wa kutumikira Yehova mwakuuza ena za malonjezo ake odabwitsa amtsogolo. Chifukwa chakuti amishonale a ku Micronesia amapitirizabe kukalimira mfupo imeneyo, iwo akukwaniritsa mawu a Yesaya 42:12 akuti: “Apereke ulemerero kwa Yehova, anene matamando ake m’zisumbu.”
[Mapu/Chithunzi patsamba 31]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Barrigada, Guam
Santa Rita, Guam
Koror, Belau
Chuuk (Truk) Islands
Tarawa, Kiribati
Kosrae
Ebeye
Marshall Islands
Majuro
Kolonia, Pohnpei
Songsong, Rota
Saipan
Yap
MICRONESIA
MELANESIA
CAROLINE ISLANDS
PACIFIC OCEAN
PHILIPPINES
NEW GUINEA
EQUATOR
[Chithunzi]
Amishonale asonkhana m’Guam, June 1992