“Asanabadwe Mapiri”
“INU mwakhala mmalo athu okhala m’mibadwo yonse. Mapiri asanabadwe kapena musanabweretse dziko lapansi ndi dziko, kuyambira kuumuyaya kufikira kuumuyaya ndinu Mulungu.” (Salmo 90: 1, 2, New International Version) Mawu amenewo analunjikitsidwa kwa Mlengi wathu, ndipo ngotonthoza chotani nanga—makamaka lerolino, pamene kalikonse kawonekera kukhala kosakhazikika!
Mu mkhalidwe woipiraipira wachuma, ngochepekera amene ali ndi chidaliro chamtsogolo. Kuwonjezereka kochititsa mantha kwa upandu ndi kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa kwasanduliza mizinda ina kukhala zigawo zomenyera nkhondo. Ngakhale gulu lakalekale limenelo, banja, likudzandira. Timamva za zinthu zachilendo zonga maukwati a aziwalo zofanana. Chiŵerengero cha mabanja akholo limodzi chikuwonjezereka, kumene kaŵirikaŵiri kholo limodzi lifunikira kuthana ndi chitsenderezo chachikulu. Mtendere wamabanja ambiri ukuwonongedwa ndi zonyansa, zonga kumenyana kwa okwatirana ndi kuchitira nkhalwe ana.
Kodi ndani adzatitsogolera kupyola nthaŵi zovuta zimenezi? Eya, pali uphungu wambirimbiri wochokera kwa akatswiri a zamaganizo, aphunzitsi, ndi ena, koma unyinji wa uphunguwo ngwotsutsana. Kwa mbadwo wathunthu Kumadzulo, Dr. Benjamin Spock anali phungu woposa onse pankhani ya kuphunzitsa ana. Ndiyeno anavomereza kuti uphungu wake unali wolakwa!
Nkwanzeru kwambiri chotani nanga kuti Mulungu akhale “malo okhala” athu! M’nthaŵi zachipolowe zino, Iye ali thanthwe lokhazikika, wokhalako “kuyambira kunthaŵi yosatha kufikira nthaŵi yosatha.” Iye anati za Iye mwini kupyolera mwa mneneri Malaki: “Ine Yehova sindisinthika.” (Malaki 3:6) Miyezo ya Mulungu, monga momwe yalembedwera mu Baibulo, njodalirika kotheratu. Iye analiko “mapiri asanabadwe,” ndipo uphungu wake, wopezeka m’Malemba Opatulika, ngwozikidwa panzeru yake yamuyaya. Ndiyo imene tifunikiradi kuti tipeze chimwemwe ndi chipambano.
Pamenepa, kuli kwanzeru, kukhala ndi chidaliro m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Liphunzireni kuti mupindule ndi nzeru ya Mulungu. Dalirani zimene muphunzira, ndipo ziloleni kuti zikhale kuunika kokutsogolerani panjira yanu ya moyo. (Salmo 119:105) Awo okha amene amatero ali ndi chifukwa chakukhalira achidaliro ponena za mtsogolo ndi mtendere wowona ndi wamaganizo.